KUPANDA ULEMU KWA WAHABI POLANKHULANA NDI MASHIA.
.
KUPANDA ULEMU KWA WAHABI POLANKHULANA NDI MASHIA
Kulankhula ndi maganizo amenewa akuchokera kwa munthu yemwe amazitcha kuti ndi oyitanira anthu muchipembedzo cha Chisilamu, koma tikaonetsetsa tiona kuti khalidwe ndi zochitika zawo ndizosemphana ndi Quran komanso Sunnah ya Mtumiki(s.a.w.w).Kodi inu mungakhulupirire kuti anthu oterewa kukhala oyitanira muchipembedzo cha Chisilamu
Mawahabi nthawi zonse amazitcha  kuti ndioyitanira  ku Chisilamu koma funso ndilokuti chisilamu chomwe iwowa amachidziwa bwinochi chikuchokera pati? Chifukwa  chisilamu chomwe tikuchidziwa ndichomwe chikuphunzitsa chikondi, kukoma  mtima,kulemekezana ndi zina zotero,pomwe Mawahabi kwawo ndikupha,nkhanza, udani ndi zotero, choncho tikuona  kuti pakati pa chisilamu chimenechi ndichomwe Mtumiki(s.a.w.w) adaphunzitsa palikusiyana kumwamba ndi pansi
 
 
Add new comment