Ziyaratu Ashura 1
Ziyaratu Ashura 1
MUDZINA LA MULUNGU MWINI CHIFUNDO NDI CHISONI CHA MUYAYA
Inde, adabweretsa zida, miyala ndi mikondo kuchokera ku nzinda wa Kufa,
Adabweretsa udani omwe udabindikira mmitima mwawo kuchokera tsiku la Ghadir,
Ataona kuti munthu ali yekha ndi dziko lakutali adamuthira nkhondo ndikumumenya,
Ataona kuti munthu ndi mlendo adamubweretsera mavuto ndi mazunzo.
M’bale olemekezeka usadabwe ndimmene kulankhula kwa mmwambaku kulili nkhani yake ndi ya Imam Husain (a) yemwe ndi mwana wa Ali(a) ndi Fatwimah (a) chomwe ndi chidzukulu cha Bwana wa Atumiki onse omwe adatumizidwa Muhammad (s.a.a.w).
Ndikulankhula kokhaku kukukwanira kwa munthu kuti adziwe kuti kodi Husain(a) adali ndani komanso adali otani, umoyo wake udali otani. Tisaiwale kuti Husain ndi munthu yemwe adasangalatsidwa ndi mwini wake Mtumiki kuti ndi mmodzi mwa mabwana achinyamata aku Jannah. Mauwa palibe amene angawakanire, tsono funso ndiloti kodi munthu yemwe walonjezedwa kukalowa ku Jannah ndi wabwino ndiowopa Mulungu kapena oipa?
Tsono zikutheka bwanji kuti munthu otereyu akuphedwa moponderezedwa ndimomvetsa chisoni chonchi? Kodi amene adamupha Husain yemwe ndi Yazid mwana wa Muawiyah ndi wabwino kuposa Husain olonjezedwa ndi agogo ake Mtumiki kuti akalowa ku Jannah? Kodi zingatheke kuti magulu awiri kukhala pachilungamo ndikuukirana kufika pomenyana posakhala kuti gulu limodzi limakhala pachilungamo pomwe limodzi limakhala losochera? Kapena inu muli ndikulankhula kwina koposa zomwe zanenedwazi? Ngatidi muli munthu ofuna chilungamo nkhani ndiyachionekere kuti chilungamo chidali ndi munthu wakuti, sichoncho?
Nkhani yomwe tikufuna kuti tikumbutsane pano ndiyokhudzana ndi Ziyarat ya Imam Husain (a) monga ife maShia ukafika mwezi umenewu wa Muharram timakumbukira mavuto omwe adagwera ku nyumba ya Mtumiki(s.a.a.w) komanso Asilamu onse dziko lapansi yomwe ndikuphedwa kopondereza ndikopanda chisoni kwa chidzukulu cha Mtumiki(s.a.a.w) Husain(a).
Tikamati ziyarat timatanthauza kumuyendera munthu wina wake kukamuona, tsopano ife mumwezi umenewu timakhala ndi ntchito yomuyendera Husain(a). Ena amapita ku Iraq dera lotchedwa Karibala malo omwe adaphedwera ndikuikidwa mmanda. Ena chifukwa choti sangathe kupita amakwaniritsidwa ndikuwerenga dua yomwe imatchedwa Ziyaratu Ashura.
Ubwino wa Ziyarat imeneyi ndi:
1. kupeza chichilitso kuchokera mwa iyo. Ngati munthu angakhale ndi vuto la nthenda ina yake akawerenga dua imeneyi Mulungu amatha kumuchiza.
2. Mavuto ndi zovuta zimachotsedwa kwa munthu. Ziyarat imeneyi imawerengedwa ndi Asilamu ambiri angakhale ndi Ahlu sunnah wal jamaa omwe.
3. Anthu adzazindikira choonadi cha Chisilamu chifukwa Husain(a) adaphunzira Chisilamu kuchokera kwa bambo ndi agogo ake. Phunzitsi wa bambo ake ndi Mtumiki(s.a.a.w), phunzitsi wa mai ake ndi Mtumiki (s.a.a.w) ,iye mwini phuzintsi wake ndi Mtumiki(s.a.a.w), kusonyeza kuti maphunziro omwe Husain(a) adali nawo amachokera kwa Mtumiki (s.a.a.w).Kodi ndi ndani yemwe angachidziwe chisilamu kuposa anthu amenewa?
Chinthu chomwe tiyenera kudziwa pa nkhaniyi ndichoti kupanda kuti Imam Husain(a) adaima ndikulimbana ndi Yazid bin Muawiyah, ndiye kuti chisilamu chidakaonongedwa angakhalenso zipembedzo zina. Chifukwa choti Yazid palibe chomwe amadziwa za dini ya chisilamu kwake kudali kupanga ntchito yosalongosoka, ngati wina akukanira nkhaniyi ayenera kufufuza umoyo wa Yazid mumabuku odalilika. Mapeto antchitoyi bwezi Mulungu asakuchitiridwa Ibadah.
Ndi uthenga kwa anthu omwe amapita kukapanga ziyarat ku manda a Imam Husain(a) kuti asafunikire kuti azikongoletse ndizovala zabwino kapena kusamba koma kuti atha kupita angakhale ali ndifumbi chifukwa choti munthu yemwe adagona pamalopo ndi oti adagwa pansi ndiponso adali fumbi lokhalokha chifukwa cha anthu osaopa Mulungu amenewa.
Ziyaratu ashura ndiya nthawi zonse ndi chifukwa chake amanena kuti (( كلّ يوم عاشورا وكلّ أرض كربلا )) (tsiku lina lililonse ndi ashura pomwe malo ena alionse ndi karibala)) kunena kuti munthu akakhala pachisangalalo kaya madandaulo ayenera kumukumbukira Imam Husain (a), kaya likhala lachisanu, Eidul fitir, Eidul Quruban, tsiku la Arafat ayenera kuwerenga ziyaratu ashura komwe ndikukumbukira Imam Husain(a).
Mwina wina atha kunena kuti ine ndili pachisangalalo cha kubadwa kwa Imam Mahdi choncho ndiyenera kukhala osangalala osati kudandaula ayi, kodi mwaiwala kuti Imam Zaman (Mahdi) (a) adanena kuti ((لابكينّ عليك صباحاً و مساءاً حتى أموت)) ((chifukwa choti masiku ndi nthawi zidandichedwetsa kuti ndisapezeke nthawiyi ndidzakhala ndikulira (kulilira Imam Husain) kummawa ndi madzulo ena alionse mpaka imfa yanga)). Kumasulira kuti Imam Zaman amakhala akudandaula za imfa ya Imam Husain (a) nthawi zonse.
Mfundonso ina yomwe ingapereke kuzindikira kwina kuti munthu athe kumudziwa Imam Husain(a) kuti kodi adali ndani ndi nkhani ya Mubahalah.
Mtumiki atagwirizana ndi ena mwa abusa kuti adzabwere ndicholinga choti aonetsane kuti kodi ndindani yemwe ali pachilungamo adagwirizana zoti wina aliyense abwere ndi anthu akubanja lake ndipo apemphe tembelero kuchokera kwa Mulungu kuti lipite kwa munthu wabodza. Zomwe mapeto ake zidali zoti Mtumiki adapita kumaloku ndi Ali, Fatwima, Hasan ndi Husain(a) . Komwe kuli kwauza Asilamu kuti akubanja kwake ndi anthu omwe adabwera nawowa. Monga momwe Mulungu akunenera mu Quran yolemekezeka kuti:
(( فمن حاجّك فيه من بعد ما جاءك من العلم فقل تعالوا ندع أبناءنا و أبناءكم و نساءنا و نساءكم و أنفسنا و أنفسكم ثمّ نبتهل وفنجعل لّعنة الله على الكاذبين )).
(( Munthu yemwe angalimbane nawe pambuyo poti kudziwa ndikuzindikira kwakufika nena kwa iwo kuti bwerani tiyitane ana athu ndi ana anu, akazi athu ndi akazi anu,ife ndi inu kenako tipemphe tembelero la Mulungu kuti likhale kwa amene ali onama)).
Add new comment