Zolankhula za Imam Baqir (a.s) 3
Imam Baqir (a.s) adati: ثلاثةٌ من مكارم الدنيا والآخرة: أن تعفو عمّن ظلمك وتَصلَ من قطعك وتَحلُم إذا جُهِل عليك Pali zinthu zitatu zomwe zili makhalidwe abwino kwa munthu pano padziko lapansi ndipo malipiro abwino ali tsiku lomaliza. 1- Chinthu choyamba ndikumukhululukira munthu yemwe wakupondereza. Kupondereza komwe kuli apa ndikupondereza koti munthu kutheka wachita zimenezo chifukwa chakusadziwa kapena kulakwitsa ndipo pambuyo pakuzindikira wabwera ndikupepesa, ndiye kupondereza kukakhala kwamtunduwu munthu asawume mtima ayi koma ayenera kukhululuka. Tisayiwale kuti imodzi mwa mbiri za Mulungu ndi okhululuka kwambiri (Tawwab), munthu akachimwira Mulungu, Mulungu amamukhululukira. 2- Chinthu chachiwiri ndicho kulumikiza ubale ndi anthu omwe adula ubale. Chifukwa ubwino wakulumikiza ubale ndiwoti munthu amadziwa mavuto a anthu ena ndi maubwino ena, pomwe kuyipa kodula ubale ndikoti umoyo wa munthu umachepetsedwa. 3- Chinthu chachitatu ndichakuti munthu ayenera kukhala opirira nthawi yomwe munthu wina chifukwa cha umbuli wamupangira zinthu zoipa, tisayiwalenso kuti imodzi mwa mbiri za Mulungu ndi kupirira (halim), mwachoncho tiyenera kukhala anthu otsatira mbiri imeneyi.
Attachment | Size |
---|---|
e2a2225fb3e700230b64d59bb600a938.mp4 | 11.6 MB |
Add new comment