Zolankhula za Imam Baqir (a.s) 4
Imam Baqir (a.s) adanena kuti: الظلم ثلاثةٌ: ظلمٌ لا يغفره الله و ظلم يغفره الله و ظلم لا يَدَعُه الله فأمّا الظلم الذى لا يغفره الله فالشرك بالله وأمّا الظلم الذى يغفره الله فظلم الرجل نفسَه فيما بينه وبين الله وأمّا الظلم الذى لا يَدَعُه الله فالمُدايَنَة بين العباد ثمّ قال: ما يأخذ المظلوم من دَين الظالم أكثر ممّا يأخذ الظالم من دنيا المظلوم - Kupondereza kuli magulu atatu: 1. Kupondereza komwe Mulungu sadzakhululuka. 2. Kupondereza komwe Mulungu adzakhululuka. 3. Kupondereza komwe Mulungu sadzakudutsa ndikukusiya. - Tsono kupondereza komwe Mulungu sadzakhululuka ndipo munthu ngati angamwalire adakali mugululi, ndiye kuti malo ake ndikumoto, ndiko kumuphatikiza Mulungu ndi zinthu zina (Shirk). Munthu yumwe sadakhulupirire za umodzi wa Mulungu asayembekezere chikhululuko kuchokera kwa Mulungu. Kulankhula kokweza munthu wina kufika malo a uMulungu, kubweretsa ziphunzitso zabodza pakati pa anthu zomwe mapeto ake ndikuyambika kwa chipembedzo chosokonekera, ndikumuphatikiza Mulungu ndi zinthu zina. Kapena munthu wina kuzitenga kukhala wapamwamba odziwa chipembedzo ndikutulutsa zinthu zomwe Mulungu wazilamulira muchipembedzo ndikulowetsa zinthu zomwe Mulungu waziletsa muchipembedzo. -Tsono kupondereza kwachiwiri komwe Mulungu adzakhululuka ndikuchimwa kwa munthu kuchimwira Mulungu monga kumwa mowa ngati mwini wake angabwelere mwa Mulungu ndikusiya kumwa mowawu, Mulungu adzamukhululukira. - Tsono kupondereza kwachitatu ndikomwe munthu amamuchimwira munthu wina, monga kunyoza munthu wina kapena kukhala ndi ngongole ndi munthu wina koma ndikusamubwezera mwini wake zomwe zimatchedwa \"ufulu wa anthu\" ndiye kuti Mulungu sangakhululuke pokha pokha munthu amene udamuchimwirayo akhululuke. Poyikira ndemanga nkhaniyi, Pali nkhani yakuti: Munthu wina wake adali kumva kuwawa ndikuwotcha pachifuwa pake, tsiku lina mnzake adamufunsa kuti :\"Kodi ndichifukwa chiyani matenda ako sakuchizidwa?\"Adayankha kuti: \" Sindikudziwa koma zomwe zidachitika ndizoti: Tsiku lina ndidapita kunsika ogulitsa nyama. Nditafika ndidamufunsa mwini ogulitsa nyama kuti nyama yake akugulitsa pamtengo wanji? Ndimapanga izi ndikutosa nyamayi ndi chala changa, choncho mafuta anyamayi adatsalira kuchala changa, kenako ndidanyamuka ndikumuwuza ogulitsa nyama kuti sindigula nyamayi. Tsiku lina ndidapita kunsika omwewu koma ndidamupeza ogulitsa nyama uja atamwalira, ndidabwelera kunyumba, nditagona usiku ndidalota nditakumana ndi munthu ogulitsa nyama uja. Iye adati kwa ine: \" Achimwene inu, muli nane ngongole muyenera kundibwezera lero\" ndidati: \" ngongole yake iti?\" Adati: \" Inu tsiku lina mudabwera pamalo anga ogulitsira nyama ndikutosa nyama yanga ndipo mafuta anyama adatsalira kuchala chanu koma simudandipatse ndalama za mafutawo\" Ndidati: \" Pano ndalama ndilibe ndikubwezera bwanji?\" Adati: \" Poti ndalama mulibe ndiye inenso ndikutosani chala changa malingana ndimomwe mudatosera nyama yanga\". Kenako iye adatosa chala chake pachifuwa changa zitatero ndidadzidzimuka ndipo ndidawona kuti pachifuwa panga pakuwotcha ndikuwawa\". Kenako Imam akunena kuti: Pakati pamunthu opondereza ndi oponderezedwa amene amaluza kwambiri ndi opondereza chifukwa choti munthu oponderezedwa amatengeredwa zinthu zomwe zidali zoti zikhale zake pomwe opondereza amaona ngati wapambana polanda ndikutenga zinthu koma tsiku lomaliza adzafunsidwa ndikupatsidwa chilango chifukwa cha zinthu zimenezi. Tipemphe Mulungu kuti atitalikitse kuchokera ku kupondereza.
Attachment | Size |
---|---|
e87717f2224dbdc29c6fef30470c8de2.mp4 | 18.42 MB |
Add new comment