Zolankhula za Imam Baqir (a.s) 7.

Imam Baqir (a.s) adanena kuti: إيّاك والكَسَلَ والضَّجرَ فإنّهما مِفتاحُ كلِّ شرٍّ من كسل لم يُؤدِّ حقّاً ومن ضَجَرَ لم يصبر على حقٍّ. Key ya mavuto a munthu yagona muzinthu ziwiri: 1- Chinthu choyamba ndi ulesi. Munthu kukhala ndi malingaliro abwino polimbikira ntchito ndi zinthu zabwino kwa iye. Anthu ambiri omwe apita patsogolo amakhala oti adavutika komanso adalimbikira ntchito. 2-Chinthu chachiwiri ndicho kutaya mtima pachinthu. Zinthu ziwiri zimenezi zimamupangitsa munthu kupanga zinthu zoipa chifukwa choti iye amakhala ndi malingaliro atali atali koma chonsecho ali wawulesi komanso otaya mtima pa chinthu mapeto ake kuti apeze zinthu zomwe akufuna amapanga zoipa monga kuba, kupha, kulanda anthu katundu ndi zina. Tsono kuwopsa kwina ndikoti satana akalowelera nkhani imavuta chifukwa choti iye amamuwuza munthu zinthu zoyenera kuchita akamuwona kuti alibe chopanga chifukwa cha ulesi chifukwa satana amalamulira zinthu zoipa. -Munthu akakhala wawulesi amaphwanya ufulu wa anthu ena kuti apeze zofuna zake komanso akakhala otaya mtima pachinthu sapilira akafuna kupanga chinthu.

AttachmentSize
File 1dd92ecb2aad5d12b0a28ed1830236dc.mp429.16 MB

Add new comment