Ziyaratu Ashura 3
Ziyaratu Ashura 3
Imam Swadiq (a) pofuna kulankhula za mavuto amenewa adanena kuti:
إنّ يوم عاشورا أحرق قلوبنا و أرسل دموعنا و أرض كربلا أورثتنا الكرب والبلاء فعلى مثل الحسين فليبك الباكون فإنّ البكاء عليه يمحو الذنوب أيّها المؤمنون.
Ndithudi tsiku la Ashura (tsiku lomwe Imam Husain(a) adaphedwa) limaotcha mitima yathu, limaketsa misozi yathu, ife tidalandira madandaulo ndi mavuto a Karibala pachifukwachi anthu olira ayenera kulilira Husain chifukwa kulilira Husain kumafufuta zochima za munthu e! inu anthu okhulupirira dziwani zimenezi.
Naye Imam Ridtha (a) adanena kuti:
إنّ يوم الحسين أقرح جفوننا و أسبل دموعنا و أذلّ عزيزنا بأرض كربلا....على مثل الحسين (ع) فليبك الباكون فإنّ البكاء عليه يحط العظام.
Kuphedwa kwa Imam Husain (a) kudapweteka maso athu, kudagwetsa misozi yathu ndipo munthu amene ali olemekezeka wathu adachepetsedwa pa Karibala, choncho anthu ayenera kumulilira Imam Husain(a) chifukwa kumulilira iye kumachotsa machimo akuluakulu.
Munthu wina otchedwa Abdullah bin Fudthail Hashimi adamufunsa Imam Swadiq (a) kuti: ndichifukwa chani kuti tsiku la Ashura lidasanduka tsiku la madandaulo, mavuto ndi mazunzo pomwe tsiku lomwe Mtumiki(s.a.a.w), Ali(a), Fatwimah (a) ndi Hasan(a) sizili chonchi kumachita kuti nawonso adaphedwa modandaulitsa pothiridwa mankhwala muzakudya kapena zakumwa? Imam adayankha kuti: zili chonchi chifukwa choti kuphedwa kwa Imam Husain (a) tsiku la Ashura tikakufanizira ndikuphedwa kwa ena onse omwe atchulidwawa tipeza kuti tsiku limeneli la Ashura ndi lalikulu kuposa masiku ena onse potengeranso kakhalidwe ka mavuto ake, chifukwanso choti Imam Husain (a) ndi munthu yemwe adatsalira mwa anthu asanu omwe amatchedwa kuti “Aswihabul kisai” ndiye kuphedwa ndikusowa kwa iye zidali ngati kusowa kwa anthu onsewa.
Inde, munthu akakhala ndikuganizira mozama mavuto omwe adachitika ku Karibala kuyambira tsiku loyamba mpaka lomaliza popanda kukhala ndi mtima wa sankho muchipembedzo adzavomereza kuti kuphedwa kwa Imam Husain (a) idali nkhani ndi mavuto akulu muchisilamu.
M’bale olemekezeka muchipembedzo cha chisilamu, kodi mudziwa kuti munthu Msilamu ali okakamizidwa kuchita kafukufuku muchipembedzo chimenechi cha chisilamu? Pomwe Mtumiki(s.a.a.w) akunena kuti: Kufunafuna maphunziro ndichikakamizo kwa Msilamu wina aliyense wamwamuna ndi wamkazi yemwe.
Choncho ngati munthu akufuna kudziwa zambiri za nkhani imeneyi ya kuphedwa kwa Husain bin Ali bin Abi Twalib yemwe ndi chidzukulu cha Mtumiki olemekezeka cholonjezedwa kukalowa ku mtendere, ayenera kuchita kafukufuku pa nkhaniyi.
Komanso ngati munthu sangakhale ndi mpata okwanira atha kukwaniritsidwa ndi “Site” imeneyi chifukwa mmenemu tikhale tikunena zambiri za nkhaniyi kapena inu mutha kutidziwitsa kuti tinenepo zambiri pankhaniyi.
Mulungu azikudalitsani nthawi zonse.
Wassalam alaikumu warahamatullah ta’ala wabarakatuh wamaghafiratuh.
Add new comment