Imam Husain (a)
5- قال عليه السلام:
أنا قتيل العَبرَة لا يذكرني مؤمن الاّ استعبر.
Imam Husain (a) adanena kuti: Ine ndi ophedwa yemwe ndili chitsanzo kwa ena ndipo munthu okhulupirira sangandikumbukire ine pokhapokha adzatengera chitsanzo changa.
Tikayang’ana kutanthauzira kwa sura ya Al imran aya ya 13 tipeza kuti liu loti “abarat” chiyambi chake likuchokera pa “Ubur” komwe ndikudutsa kakhalidwe kena kufika kena kapena malo ena kukafika ena. Nthawi zina misozi imatchedwa “abarat” chifukwa choti misozi imadutsa maso ndikumatsikira mmusi, mau omwe amadutsa pa lilime ndi makutu amatchedwanso “abarat”, ndiye kutengerapo phunziro ndichitsanzo kuchokera kuzochitika kumanenedwa kuti “Iburat” chifukwa choti munthu amazidutsa zomwe zachitika ndipo amazindikira zoona zeni zeni za zochitikazi.
Kodi kuchokera apa sizingatheke kuti Hadith yomwe Imam Husain adainena kuti: “Ine ndi ophedwa yemwe ndili chitsanzo kwa ena ndipo munthu okhulupirira sangandikumbukire ine pokhapokha adzatengera chitsanzo changa” timasulire kuti Imam Husain amanena kuti: Ine ndaphedwa ndicholinga choti ndikhale chitsanzo ndiphunziro kwa anthu ena.
Ine ndi ophedwa wa misozi amene ndidaphedwa ndikuti munthu wina aliyense okhulupirira akandikumbukira alire.
Mulungu amawakonda anthu omwe amabwerera kwa iye ndipo Imam Husain(a) adatipatsa ife pothawira pathu pankhani yakubwerera kwa Mulunguyi (kusonyeza kuti munthu panthawi yomwe amakumbukira mavuto omwe adamugwera Husain (a) ndikumalira amakhala kuti akubwerera kwa Mulungu ndikuziwandikitsa ndikukhalanso mugulu la mitima yokondedwa ndikulira).
Tikaonetsetsa tipeza kuti Imam Husain (a) adalimbana ndi adani amenewa ndi zolinga zingapo zina mwa izo ndi izi:
1. Kuongola anthu onse, chifukwa munthu amene angamve bwino bwino zomwe zidachitika ndikakhalidwe ka Husain polimbana ndi adani komanso zolankhula zake amavomereza kuti Husain adali pachilungamo ndipo ndioyenera kumutsatira chomwe ndi chiongoko kwa munthu.
2. Imam Husain (a) adaphedwa ndizolinga zina zomwe zili zofunikira osati kulira, malipiro ndi mphoto ayi koma kuti kuphedwa kwake kuli koti pambuyo pa zochitikazi padzabwera zotsatira zake zomwe anthu okumva adzakhalano akumapeza chilungamo cheni cheni cha nkhaniyi ndikukhala ndichikondi kwa iye kuchokera muchilengedwe chake.
Polongosola cholinga chake polimbana ndi adaniwa mu dua yotchedwa ziyarat ashura mwanenedwa mau oti:
وبذل مُهجَتَه فيك ليستنقذ عبادك من الجهالة و حيرة الضلالة وقد توازر عليه من غرّته الدنيا.
Iye adataya moyo wake munjira yanu ndicholinga choti apulumutse akapolo anu kuchokera ku umbuli,kusochera ndi kuzungulira malo amodzi posadziwa choonadi, zili choncho anthu omwe adanyengedwa ndi dziko adamuukira ndikumubweretsera mavuto.
Mtendere ukhale kwa Husain amene adaphedwa moponderezedwa, ophedwa olungama, ophedwa yemwe ndichitsanzo kwa ena ndipo kapolo wamavuto.
Ali (a) adanena kuti(يا عبرة كل مومن ) e! iwe amene umapangitsa kuti okhulupirira wina aliyense akakumbukira imfa yako aziketsa mizozi.
Imam Baqir (a) adanena kuti: ( ما ضرب عبد بعقوبة اعظم من قسوة القلب ) Palibe kapolo yemwe adakumana ndi mavuto oposa kuwuma kwa mtima.
Inde, ife tidawerenga nkhani ya Yusuf mmene idalili, bambo ake Yaqub adadandaula ndikulira mpaka maso ake kufika posaona , koma chonsecho sadaone zomwe adachitiridwa Yusuf, zoti adamenyedwa kapena kudzunzidwa kapena kuphedwa . Iye sadaone kuti Yusuf thupi lake lidamenyedwa kukhala mabala okhaokha, mutu wake udadulidwa ndikuikidwa kunsonga kwa mkondo.
Koma Husain (a) adamenyedwa thupi lake kukhala mabala okha-okha, adazunzidwa munjira zosiyana-siyana, mutu wake udadulidwa ndikuikidwa kunsonga kwa mkondo.
Kodi ngati Mtumiki Yaqub amafika polira chonchi mpaka maso ake kukhala akhungu nanga ife tililira pati kodi nanganso kulira kwathu kukukwanira ndi mavuto amenewa?
Mulungu akupatseni kuzindikira choonadi.
Add new comment