Zoyenera kupanga tsiku la chisangalalo chachikulu cha Mulungu cha Ghadir
Zoyenera kupanga tsiku la chisangalalo chachikulu cha Mulungu cha Ghadir
Ife amathihabu a Imamiyyah (Shia) timakhulupirira kuti tsiku la pa 18 dthul hijah ndilachisangalalo pomwe timakumbukira kuti nditsiku lomwe Mtumiki wathu olemekezeka Muhammad (s.a.a.w) adamukhazikitsa ndikumulengezetsa Ali (a) kuti ndi mlowammalo pambuyo pake popanda kupezeka munthu wina pakati pawo.
cndikulitenga kukhala tsiku la lapamwamba ndi laulemerero monga mmene tikumvera mu ma aya ali mmusiwa:
وَإِذْ أَخَذَ اللَّـهُ مِيثَاقَ النَّبِيِّينَ لَمَا آتَيْتُكُم مِّن كِتَابٍ وَحِكْمَةٍ ثُمَّ جَاءَكُمْ رَسُولٌ مُّصَدِّقٌ لِّمَا مَعَكُمْ لَتُؤْمِنُنَّ بِهِ وَلَتَنصُرُنَّهُ قَالَ أَأَقْرَرْتُمْ وَأَخَذْتُمْ عَلَىٰ ذَٰلِكُمْ إِصْرِي قَالُوا أَقْرَرْنَا قَالَ فَاشْهَدُوا وَأَنَا مَعَكُم مِّنَ الشَّاهِدِينَ ﴿آل عمران: ٨١﴾
وَإِنَّ مِن شِيعَتِهِ لَإِبْرَاهِيمَ ﴿الصافات: ٨٣﴾
Koma kweni kweni nkhani ngati imeneyi amene angathe kuimvetsetsa ndi munthu amene ali ndichikhulupiriro cha Ahlubait, ndiye ngati munthu amene Sali muchikhulupirirochi angamvetsetse ndiye kuti kuyamikidwa konse ndikwa Mulungu.
Nkhani imeneyi ya Ghadir yomwe ili yofunikira kwambiri pakati asilamu chifukwa choti ikutifotokozera kufunikira kwa kupitirira chipembedzo cha chisilamu pambuyo pa Mtumiki wathu (s.a.a.w.) kudzera mwa atsogoleri okwana khumi ndi awiri (12) omwe ali ochokera mwa Mtumiki(s.a.a.w), tikuipeza mu bukhu lopatulika la Baibulo pomwe Ibrahim (a) adalikulongosola kwa ana ake Ishaq ndi Ismail za atumiki omwe adzabwere pambuyo pawo kuti kuchokera kwa Ismail kudzabwera atsogoleri okwana khumi ndi awiri(12).
Pali Riwayat lomwe likunena kuti Imam Swadiq(a) adafunsidwa kuti kodi asilamu ali ndichisangalalo china posakhala lachisanu, Qurubani ndi Fitir? Imam Swadiq adayankha kuti inde, pali chisangalalo chomwe chili chapamwamba kuposa zisangalalo zonse, ofunsa adati: nditsiku liti limeneli? Imam adati: nditsiku lomwe Mtumiki(s.a.a.w) adamupanga Ali (a) kukhala mlowammalo wake pambuyo pake ndipo adalengeza kwa anthu onse ponena kuti yemwe ine Mtumiki(s.a.a.w) ndidali tsogoleri ndi bwana wake adziwe ndikuvomereza kuti uyu Ali (a) ndi tsogolweri komanso bwana wake, tsikuli lidali pa 18 dthul hijah. Munthuyu adati: kodi ndintchito zanji yomwe tingapange tsikuli? Imam adayankha kuti muyenera kusala, kupembedza, kumukumbukira Mtumiki(s.a.a.w) ndi akunyumba kwake ndikuwafunira mafuno abwino ndi mtendere, litengeni tsikuli kukhala lachisangalalo chifukwa Mtumiki adamulangiza Ali kukhala kuti azilitenga tsikuli kukhala lachisangalalo. Angakhale atumiki ena adali kuwalangiza alowammalo awo kuti tsiku ngati limeneli aziltenga kukhala lachisangalalo.
Hadith ina yachokera kwa Ibn Abi Nasir Bazantiy yomwe adainena kuchokera kwa Imam Ridtha(a) kuti Imam adanena kwa iye kuti e! iwe mwana wa Abi Nasir, kwina kuli konse komwe ungakhale likafika tsiku la chisangalalo cha Ghadir uziyetsetsa kukafika ku manda olemekezeka a Amir muminina Ali (a) chifukwa tsiku limeneli Mulungu amakhululuka machimo a munthu okhulupirira wamwamuna kapena wamkazi omwe adawapanga zaka makumi asanu ndi limodzi (60), amamupulumutsa kuchokera ku moto kuposa momwe adamupulumutsira mu mwezi wa Ramadthan, usiku wa mphamvu (laylatul qadir) ndi usiku wa eidul fitir, Kupereka ndalama zokwana diriham imodzi kwa m’bale okhulupirira tsiku limeneli kuli ndi ubwino okwana madiriham chikhwi chimodzi kuposa kupereka masiku ena, uyenera kuchitira zabwino ndi zosangalatsa m’bale okhulupirira tsikuli mwamuna kapena mkazi, ndikulumbira mwa Mulungu kuti zidakakhala kuti anthu ubwino watsikuli amaudziwa monga momwe zikufunikira kuti adziwe ndiye kuti angelo adzakhala akugwirana nawe dzanja kakhumi patsiku.
Chomwe tiyenera kudziwa pankhaniyi ndichoti tiyenera kupanga zinthu zosonyeza kuti tsikuli ndilalikulu.
Ntchito zomwe zili zofunikira kuzichita tsikuli ndi izi:
1. kusala komwe mphoto yake ndichikhululuko cha machima omwe udawapanga zaka zokwana makumi asanu ndi limodzi.
2. kusamba.
3. Kumuyendera Amir uminina Ali(a) kukaona manda ake, ndizabwino kuti munthu ayenera kuyetsetsa kukafika ku manda ake oyerawa. Pali ziyara ya mitundu itatu yomwe tikuipeza mumariwaya; yoyamba ndiyomwe imatchedwa “amin allah” yomwe itha kusomedwa pafupi kapena kutali.
4. kupemphera pemphero la maraka awiri, ndipo ikatha muyenera kupita pa sajidah( kuika mphumi pansi) ndikuthokoza Mulungu kokwana ka zana (100), kenako muweramuka kuchokera pa sajidah ndikukhala ndikunena dua iyi:
اَللّهُمَّ اِنِّى اَسْئَلُكَ بِاَنَّ لَكَ الْحَمْدَ وَحْدَكَ لا شَريكَ لَكَ وَاَنَّكَ
E! ambuye Mulungu, ine ndikukupemphani inu chifukwa choti ndinu mwini matamando onse komanso palibe wina yemwe tingamupembedze muchoonadi koma inu nokha ndipo mulibe othandizana naye mu Umulungu wanu
Mtumiki olemekezeka (s.a.a.w) adali kulongosola ubwino omwe Msilamu angapeze ngati atapanga ntchito za tsikuli, choncho ankafika polongosola upamwamba wake iye. Nthawi zina iye akafuna kuzilongosola amalongosola ubwino ndi upamwamba wa Ali (a), mwachoncho zimakhala ngati akuzilongosola mwini wake chifukwa choti Ali Mphunzitsi wake wamkulu ndi iye Mtumiki.
Ma Shaikh ena Ahlu sunnah wal jama’a adanena hadith yomwe ikuti: tsiku lina Mtumiki adafunsidwa kuti kodi munthu yemwe ali wapamwamba kuposa iye ndindani? Mtumiki adayankha kuti Abubakar ndi Umar. Fatwimatu Zahrah (a) adafunsa kuti nanga Ali bwanji? Mtumiki adati: kodi Ali ndi ine pali kusiyana? Kusonyeza kuti anthu awiri amenewa akubwera pambuyo pa Mtumiki ndi Ali. Kodi ngati Mtumiki(s.a.a.w) akumulongosola Ali ndi upamwamba otere nanga mwini wake ali bwanji?
واحِدٌ اَحَدٌ صَمَدٌ لَمْ تَلِدْ وَلَمْ تُولَدْ وَلَمْ يَكُنْ لَكَ كُفُواً اَحَدٌ وَاَنَّ
Inu amene muli nokha komanso mmodzi ndipo simufunikira china chilichonse, inu amene mulibe mwana komanso simunachite kuberekedwa, palibe chinthu chomwe chingafanane nanu.
Tanthauzo la Wahid ndi Ahad ndiye kuti monga mmene chilili cholembera kuti nthawi yomwe chisanalembe china chilichonse chimakhala kuti mwa iye zonse zomwe zalembedwazi ( inki yomwe yatulutsidwa ndikupanga bukhu) idalipo ndipoyamba pomwe sikuti yapezeka nthawi yomwe lalembedwa bukhu ayi, kumasulira kuti Mulungu ndi iye yekhayo yemwe adalipo ndiponso pambuyo pakupezeka zopezeka ndimmodzi yekha yemwe ali ndimphamvu zopezeketsa izozi choncho palibe kunenenso kuti Mulungu ali ndichiyambi, komanso Mulungu popanga chinthu sizifunikira pakhale chiyambi chake koma kuti iye ndi amene ali opezekeza zonsezi, iye ndimwini kupezeka zopezeka zonse.
مُحَمّداً عَبْدُكَ وَرَسُولُكَ صَلَواتُكَ عَلَيْهِ وَ الِهِ يا مَنْ هُوَ كُلَّ يَوْمٍ فى
Ndithudi Muhammad(s.a.a.w) ndi kapolo wanu komanso Mtumiki wanu ( mtendere wanu ukhale kwa iye ndi akubanja kwake, e! Inu amene tsiku lina lililonse mumakhala otanganidwa ndi ntchito
شَاْنٍ كَما كانَ مِنْ شَاْنِكَ اَنْ تَفَضَّلْتَ عَلَىَّ بِاَنْ جَعَلْتَنى مِنْ اَهْلِ
ndipo chifukwa cha ntchito zanu zabwino mwandipatsa ine mtendere otha kukhala
اِجابَتِكَ وَاَهْلِ دِينِكَ وَاَهْلِ دَعْوَتِكَ وَوَفَّقْتَنى لِذلِكَ فى مُبْتَدَءِ
Munthu ovomereza chifuniro, chipembedzo, kuitana kwanu ndipo mudandikwaniritsira zonse kumayambiriro kwa chilengedwe changa
خَلْقى تَفَضُّلاً مِنْكَ وَكَرَماً وَجُوداً ثُمَّ اَرْدَفْتَ الْفَضْلَ فَضْلاً وَالْجُودَ
Zonsezi chifukwa cha ubwino, mtendere,kupereka mowolowa manja ndikukoma mtima kwanu kenako pambuyo pa ubwino
mwabweretsanso ubwino wina, pambuyo pa kupereka mowolowa manja mwabweretsanso kuolowa manja kwina o
Mtendere umenewu ndikupezeka kwa Mtumiki(s.a.a.w), Ali, Hasan ndi Husain omwe ali atsogoleri pambuyo pa Mtumiki, Mulungu ndiodziwa kukhonza ndikuika chinthu china chilichonse mofunikira kuti akapolo ake athe kugwiritsa ntchito mwachitsanzo Mulungu adapanga madzi omwe adapangidwa ndi zinthu ziwiri hydrogen ndi oxygen kukhala othandiza munthu muzinthu zina ndi zina, koma hydrogen yemweyo akangogwiritsidwa ntchito payekha amasanduka kukhala owopsa kwa munthu monga amatha kuotcha chimodzi-modzi oxygen koma ataphatikiza mukupezeka mpumulo kuchokera mu iwo
جُوداً وَالْكَرَمَ كَرَماً رَاْفَةً مِنْكَ وَرَحْمَةً اِلى اَنْ جَدَّدْتَ ذلِكَ الْعَهْدَ
Zonsezi chifukwa cha chifundo ndichisoni chanu mwakutero mwabwerezanso lonjezo
لى تَجْديداً بَعْدَ تَجديدِكَ خَلْقى وَكُنْتُ نَسْياً مَنْسِيّاً ناسِياً ساهِياً
langa pambuyo poti mwabwezeretsa ndikukhonzanso chilengedwe change pamene ine mwini wanga ndidali oiwala ndikuiwalidwa komanso osazindikira chilichonse,
غافِلاً فَاَتْمَمْتَ نِعْمَتَكَ بِاَنْ ذَكَّرْتَنى ذلِكَ وَمَنَنْتَ بِهِ عَلَىَّ وَهَدَيْتَنى
mwakwaniritsa mtendere wanga pondikumbutsa, kundipatsa mtendere komanso mwandiongola
لَهُ فَليَكُنْ مِنْ شَاْنِكَ يا اِلهى وَسَيِّدى وَمَولاىَ اَنْ تُتِمَّ لى ذلِكَ وَلا
Ndipo chifukwa cha ubwino ndi ntchito zanu zabwino ndikwaniritsireni ine mtendere umenewu e! inu bwana ndi Mulungu wanga,
تَسْلُبَنيهِ حَتّى تَتَوَفّانى عَلى ذلِكَ وَاَنتَ عَنّى راضٍ فَاِنَّكَ اَحَقُّ
Musandilande mtendere omwe mwandaipatsawu mpaka kuti mudzanditenge ndidakali mu iwo ndipo inu muli osangalala nane.
Asakani yemwe ndi mwini wa bukhu lotchedwa “Shawahid tanzil”, akunena kuti tanthauzo la “mustaqim” ndi Ali(a). Kusonyeza kuti munthu akhale muchiongoko ndikupeza mtendere ngati umenewu akufunikira kuti akhale otsatira njira ya Ali (a). Inde, tiyenera kupempha Mulungu kuti tisachoke mubwato limeneli la ahlubait (a) chifukwa pali zitsanzo zina zomwe zidapatsidwa mtendere ngati umenewu koma mapeto ake adaluza. Kodi satana sadali munthu wamkulu, nanga Qaruna sadalinso munthu wamkulu koma tapeza onsewa kuti adagonja ndikugwa pansi komanso kutulutsidwa mumtendere wa Mulungu, choncho ife nthawi zonse pempho lathu lizikhala loti tisadzatuluke mu mtendere umenewu kufikira nthawi yomwe Mulungu adzatitenge.
المُنعِمينَ اَنْ تُتِمَّ نِعمَتَكَ عَلَىَّ اَللّهُمَّ سَمِعْنا وَاَطَعْنا وَاَجَبْنا داعِيَكَ
Inu ndi opereka mtendere weniweni pachifukwachi ndinu amene mungakwaniritse mtendere wanga, ambuye Mulungu, chifukwa cha chifundo chanu tamva,tamvera ndipo tavomera oitanira wanu,
بِمَنِّكَ فَلَكَ الْحَمْدُ غُفْرانَكَ رَبَّنا وَاِلَيكَ المَصيرُ امَنّا بِاللّهِ وَحدَهُ لا
Matamando onse ali kwa inu ndipo tikupempha chikhululuko chanu e! inu bwana wathu ndipo kwa inu ndikobwerera, ife takhulupirira mwa Mulungu mmodzi yekha
شَريكَ لَهُ وَبِرَسُولِهِ مُحَمَّدٍ صَلَّى اللّهُ عَلَيْهِ وَ الِهِ وَصَدَّقْنا وَاَجَبْنا
Yemwe alibe othandizana naye mu Umulungu wake komanso Mtumiki wake olemekezeka Muhammad (s.a.a.w) pomuvomereza ndikumuyankha zomwe adabwera nazo
داعِىَ اللّهِ وَاتَّبَعْنَا الرَّسوُلَ فى مُوالاةِ مَوْلينا وَمَوْلَى الْمُؤْمِنينَ اَميرِ
Komanso oitanira munjira ya Mulungu, tamutsatira Mtumiki wathu mu ubale ndikumvera tsogoleri wanthu ndi tsogoleri wa anthu okhulupirira,
المُؤْمِنينَ عَلِىِّ بْنِ اَبيطالِبٍ عَبْدِاللّهِ وَاَخى رَسوُلِهِ وَالصِّدّيقِ الاْكْبَرِ
Ali bin Abi Twalib (a) yemwe ndi kapolo wa Mulungu komanso nzake wa Mtumiki(s.a.a.w) ndi odalilika wamkulu,
وَالحُجَّةِ عَلى بَرِيَّتِهِ المُؤَيِّدِ بِهِ نَبِيَّهُ وَدينَهُ الْحَقَّ الْمُبينَ عَلَماً لِدينِ
Komanso mboni kwa zolengedwa zake ndipo Mtumiki ndi chipembedzo chake choonadi chowonekera paderachi chidalimbikitsidwa ndi iye amenenso ali mbendera ya chipembedzo
اللّهِ وَخازِناً لِعِلْمِهِ وَعَيْبَةَ غَيْبِ اللّهِ وَمَوْضِعَ سِرِّ اللّهِ وَاَمينَ اللّهِ عَلى
Cha Mulungu, nkhokwe ya nzeru zake ndi zobisika za Mulungu komanso odalilika wake pakati pa zolengedwa zake,
خَلْقِهِ وَشاهِدَهُ فى بَرِيَّتِهِ اَللّهُمَّ رَبَّنا اِنَّنا سَمِعْنا مُنادِياً يُنادى
Mboni mu zolengedwa zake, e! ambuye Mulungu amene muli bwana wathu ife tamumva oitanira kwa inu akuitana
للا يمانِ اَنْ امِنُوا بِرَبِّكُمْ فَامَنّا رَبَّنا فَاغْفِرْ لَنا ذُنُوبَنا وَكَفِّرْ عَنّا
Kuitanira kuchikhulupiriro ndicholinga choti tikhulupirire ndipo ife takhulupirira choncho ambuye Mulungu tikhululukireni machimo athu
سَيِّئاتِنا وَتَوَفَّنا مَعَ الاْبْرارِ رَبَّنا وَ اتِنا ما وَعَدْتَنا عَلى رُسُلِكَ وَلا
Ndipo mutitenge ife tidakali anthu abwino komanso tipatseni zinthu zomwe mudatilonjeza kudzera mwa Mtumiki wanu olemekezeka
تُخْزِنا يَوْمَ الْقِيمَةِ اِنَّكَ لا تُخْلِفُ الْميعادَ فَاِنّا يا رَبَّنا بِمَنِّكَ وَلُطْفِكَ
musadzatichititse manyazi tsiku lomaliza ndithu inu simuononga lonjezo lanu, ife chifukwa cha ubwino ndi chifundo chanu
اَجَبْنا داعِيَكَ وَاتَّبَعْنَا الرَّسُولَ وَصَدَّقْناهُ وَصَدَّقْنا مَوْلَى الْمُؤْمِنينَ
tavomera kuitana komwe amaitanira oitanira wanu, tatsatira Mtumiki wanu ndikumukhulupirira komanso tsogoleri wa okhulupirira
وَكَفَرْنا بِالجِبْتِ وَالطّاغُوتِ فَوَلِّنا ما تَوَلَّيْنا وَاحْشُرْنا مَعَ اَئِمَّتِنا فَاِنّا
Ife takanira anthu ozikweza ndi odumpha malire (anthu omwe adalanda udindo kuchokera kwa iye) choncho tipangeni ife kukhala pansi pa ulamuliro wake monga momwe ife tafunira kuti tikhale mu ulamuliro wake ndipo mudzatizutse kuchokera mmanda ndi atsogoleri athu amenewa
Imam Swadiq (a) adanena kuti ngati munthu angachikonde chinthu angakhale mwala tsiku lomaliza adzadzukitsidwa nawo. Choncho munthu amene angawakonde akunyumba kwa Mtumiki(s.a.a.w) ndiye kuti tsiku lomaliza adzaukitsidwa nawo
بِهِمْ مُؤْمِنُونَ مُوقِنُونَ وَلَهُمْ مُسَلِّمُونَ امَنّا بِسِرِّهِمْ وَعَلانِيَتِهِمْ
Chifukwa ife takhulupirira mwa iwo ndikugonjera, takhulupirira angakhale zinthu zobisika ndi zoonekera zawo zomwe,
وَشاهِدِهِمْ وَغائِبِهِمْ وَحَيِّهِمْ وَمَيِّتِهِمْ وَرَضينا بِهِمْ اَئِمَّةً وَقادَةً
Anthu opezeka pakati pawo ndi osapezeka, amoyo awo ndi okufa, ndipo tasangalala ndi iwo pakukhala kwawo atsogoleri,
وسادَةً وَحَسْبُنا بِهِمْ بَيْنَنا وَبَيْنَ اللّهِ دُونَ خَلْقِهِ لا نَبْتَغى بِهِمْ بَدَلاً وَلا
Iwowa atikwanira kukhala atsogoleri athu pakati pathu ndi Mulungu ndipo sitikufuna ena mmalo mwawo
نَتَّخِذُ مِنْ دُونِهِمْ وَليجَةً وَبَرِئْنا اِلَى اِلله مِنْ كُلِّ مَنْ نَصَبَ لَهُمْ حَرْباً
ndipo sitingamulowetse wina mmitima mwathu, tithawira kwa Mulungu kuchokera kwa anthu omwe adakhazikitsa kwa iwo nkhondo,
مِنَ الْجِنِّ وَالاِنْسِ مِنَ الاْوَّلينَ وَالاْ خِرينَ وَكَفَرْنا بِالْجِبْتِ
Kuchokera majini, anthu oyambirira ndi omalizira ndipo takanira anthu ozikweza,
وَالطّاغُوتِ وَالاَوثانِ الاَرْبَعَةِ وَاَشْياعِهِمْ وَاَتْباعِهِمْ وَكُلِّ مَنْ
Opsola malire, mafano anayi, owatsatira awo ndi ena onse
والاهُمْ مِنَ الْجِنِّ وَالاِنْسِ مِنْ اَوَّلِ الدَّهرِ اِلى آخِرِهِ اَللّهُمَّ اِنّا
Omwe ali pansi pa ulamuliro wawo kuyambira ziwanda ndi anthu pachiyambi mpaka pamathero, e! ambuye Mulungu,
نُشْهِدُكَ اَنّا نَدينُ بِما دانَ بِهِ مُحَمَّدٌ وَ الُ مُحَمَّدٍ صَلَّى اللّهُ عَلَيْهِ
Ife tikuikira umboni kuti takhala anthu opembedza monga momwe amapembedzera Muhammad(s.a.a.w) ndi akunyumba kwake(a),
وَعَلَيْهِمْ وَقَوْلُنا ما قالُوا وَدينُنا ما دانُوا بِهِ ما قالُوا بِهِ قُلْنا وَما دانُوا
Zolankhula zathu ndizokhazo zomwe iwo amalankhula, chipembedzo chathu ndichomwecho chipembedzo chawo, zomwe adanena tanena ndipo kupembedza kwawo ndikomwe tikupembedza
بهِ دِنّا وَما اَنْكَرُوا اَنْكَرْنا وَمَنْ والَوْا والَيْنا وَمَنْ عادَوْا عادَيْنا وَمَنْ
Zomwe adazikanira tazikanira, omwe adawakonda ifenso tawakonda, omwe adawada tawadanso,
لَعَنُوا لَعَنّا وَمَنْ تَبَرَّؤُا مِنْهُ تَبَرَّاْنا [مِنْهُ] وَمَنْ تَرَحَّمُوا عَلَيْهِ تَرَحَّمْنا
omwe adawatemberera tawatembereranso, omwe adazitalikitsa kuchokera kwa iwo ifenso tazitalikitsa kuchokera kwa iwo, omwe adawachitira chisoni ifenso tawachitira chisoni,
عَلَيْهِ آمَنّا وَسَلَّمْنا وَرَضينا وَاتَّبَعْنا مَوالِيَنا صَلَواتُ اللّهِ عَلَيْهِمْ
Ife takhulupirira,tagonjera,tasangalala ndiponso tatsatira atsogoleri athu (mtendere wa Mulungu ukhale kwa iwo),
اَللّهُمَّ فَتَمِّمْ لَنا ذلِكَ وَلا تَسْلُبْناهُ وَاجْعَلْهُ مُسْتَقِرّاً ثابِتاً عِنْدَنا وَلا
e! ambuye Mulungu tikwaniritsireni ife zinthu zimenezi ndipo musatilande koma muzipange zimenezi kukhala zokhazikika ndi zolimba kwa ife,
تَجْعَلْهُ مُسْتَعاراً وَاَحْيِنا ما اَحْيَيْتَنا عَلَيْهِ وَاَمِتْنا اِذا اَمَتَّنا عَلَيْهِ الُ
Musazipange zinthuzi kukhala za nthawi yochepa kapena zongobwerekera, tipatseni ife moyo tidakali ndi zinthuzi monga momwe mudawapatsira akunyumba ya Mulungu(s.a.a.w) ndi izo,
مُحَمَّدٍ اَئِمَّتُنا فَبِهِمْ نَاْتَمُّ وَاِيّاهُمْ نُوالى وَعَدُوَّهُمْ عَدُوَّ اللّهِ نُعادى
Omwe ndi atsogoleri athu amene timawatsatira ndikuwakonda, adani awo omwenso ndi adani a Mulungu timawada,
فَاجْعَلْنا مَعَهُمْ فِى الدُّنْيا وَالاَّخِرَةِ وَمِنَ الْمُقَرَّبينَ فَاِنّ ا بِذ لِكَ ر اضُونَ
Tipangeni ife kukhala limodzi ndi iwo pano pa dziko lapansi ndi tsiku lomaliza komanso kukhala anthu oyandikana nanu chifukwa ife tili osangalala ndi zimenezi.
يا اَرْحَمَ الرّاحِمينَ
E! inu amene muli achisoni kuposa achisoni onse.
Kenako mupitanso pa sajidah ndikunena mau oti “ Alhamudulillah” ndi “ Shukuranilillah” kokwana kazana.
Zidanenedwa kuti munthu yemwe angapange ntchito zomwe zili zoyenera kuzichita tsiku limeneli la Ghadir ndiye kuti adzakhala ngati kuti adali limodzi ndi Mtumiki(s.a.a.w) tsiku la Ghadir, wagwirana chanza naye komanso ali limodzi ndi Imam Zaman mu mnyumba mwake.
Nthawi yabwino kupemphera pempheroli ndi nthawi yakuyandikira kupendeka kwa dzuwa chifukwa ndi nthawi yomwe Mtumiki(s.a.a.w) adamukhazikitsa Ali (a) pa ulowammalo ndi utsogoleri pambuyo pake. Ndibwino kuti raka yoyamba asome sura Qadir ndi Tauhid raka yachiwiri.
Zikomo kwambiri Mulungu akhale nanu ndikukupatsani zabwino za tsikuli.
Add new comment