Uthenga wa mtsogoleri wamkulu wa dziko la Iran(Khamenei) pa zochitika za haji.
Hazrat Ayatullah Khamenei mtsogoleri wamkulu wa kusinthika kwa chisilamu (Inqilabu Islami) pa mwambo waukulu okhudzana nkhani ya haji wapereka uthenga oti kufika kwa nthawi ya haji imeneyi ndi chisangalalo chachikulu kwa asilamu onse komanso ndi mpata kwa iwo kuti athe kuthetsa mavuto omwe alipo pakati pa dziko la chisilamu limeneli lomwe lili loti limatha kukumana ndi mavuto nthawi zambiri.Tsogoleriyu walimbikitsa asilamu pankhani yolimbikira pofuna kulimbana ndi gulu lozikweza lomwe likufuna kuchotsa ndikuthetsa chisilamu ndi kutukuka kwake komanso kuchotsa mfundo ndi njira zomwe zilipo pofuna kuwombola palestine ndi asilamu kuchokera mmanja mwawo monga makanema onena ndikupanga zoipa a zionism ndi ena. Iye mukulankhula kwake wanena kuti: Ubale ndi mgwirizano wa asilamu wagona pankhani ya Tauhid( kusonyeza kuti asilamu onse ayenera kukhulupirira kuti ndi Mulungu yekha yemwe tingathe kumuyang’ana ndikumugwadira) komanso kumudziwa mdani ndikulimbana naye ndi chimodzi mwa ziphunzitso zikulu-zikulu za mwambo wa haji komanso kuonjezera apo chiphunzitso cha kudziwa mmene dziko likuyendera lero lino.
Uthenga onse wamkuluyu uli motere:
Mudzina la Mulungu mwini chifundo ndichisoni chosatha
Kuyamikidwa konse ndikwa Mulungu ndipo mtendere ndi madalitso akhale kwa bwana wa Atumiki onse (s.a.aw) ndi akunyumba kwake omwe ali anthu abwino komanso oyenera kulankhulana nawo osankhidwa.
Kufika kwa mwambo wa haji umenewu ndipofunikira kuti asilamu akutenge kukhala chisangalalalo chachikulu kwa iwo komanso ndi mtendere ndi mpata omwe wabwera kwa iwo mumasiku ndi zaka zimenezi. Mwachoncho ndipofunika kuti asilamu agwiritse ntchito mpata umenewu ndikuzindikira kufunikira kwake chifukwa kudzera mu haji imeneyi mavuto achisilamu adzachepetsedwa ndikuchizidwa. Haji ndi chitsime cha mtendere wa Mulungu choncho inu amene mwapeza mwayi opita ku haji muli muchisangalalo ndi mtendere wa Mulunguwu. Padakali pano mwavomera kuitana kwapamwamba kumeneku kuti muzochitika za mwambowu muthe kuzitsuka mitima yanu ndikukhala anthu abwino ndi mngwiro. Muyenera kutenga mtendere ndi kulemekezeka kuchokera ku bank imeneyi ndikuthandizika moyo wanu onse pophunzira izi: Kuzichepetsa ndikugonjera ku malamulo a Mulungu, kuvomereza udindo omwe muli nawo, kutakataka pa nkhani ya chipembedzo ndi dziko,kulolerana ndi kukhululukirana wina ndi mnzake,kuzidalira munthu pofuna kupanga zinthu zovuta, kudalira Mulungu muchithandizo,kulankhula pang’ono, kuzikhonza ndi kutha kukhalirana ndi asilamu ena. Mutha kuphunzira zinthu zosiyana siyana zokhudzana chipembedzo cha chisilamuchi ndikwatengera anthu ena omwe mwasiya kwanu ngati mphatso. Asilamu lero lino akufunikira anthu omwe kuganiza ndi ntchito zawo zikuchokera pa chikhulupiriro ndikuziyeretsa komanso ndikuti ayenera kukhala olimbana ndi adani ndikuyetsetsa kuziyeretsa mtima. Ntchito iyi idzatha kupulumutsa mtundu wachisilamu kuchokera ku mavuto omwe chisilamu chimakumana nawo moonekera kapena mobisika ndi adani. Ndizosakaikitsa kuti mtundu wa nthawi ino ndi oti uli mmaso komanso ozindikira angakhale asilamu omwe choncho choona chake ndichoti maiko ambiri achisilamu akumana ndikhaniyi ndipo inu mutha kuona zimenezi pa nthawi yomwe muli kuhajiyi. Kuchokera muzinthu izi zomwe zilikuchokera pa chikhulupiriro ndi kuyezamira kwa Mulungu ndi momwe asilamu atha kukhala opambana ndikupita patsogolo ndi zolinga zawo. Magulu olimbana ndikudzuka kwa chisilamu akuyetsetsa kufuna kugonjetsa asilamu pogwiritsa ntchito zida zomwe alinazo monga,kuchotsa chitetezo, kusokoneza kuganiza kwa anthu ndi nzeru zawo, kusokoneza magulu ankhondo, chuma, kufalitsa uthenga ndi zina. Nkhaniyi itha kumveka bwino kwa inu ngati mutaona mmene maiko akummawa kwa Asia monga pakistan,Afghanistan, Syria, Iraq, Palestine ndi maiko amphepete mwa khaliji Faris komanso kumpoto kwa Africa monga Libya,Egypt,Tunisia mpaka Sudan ndi ena komanso nkhondo za mmaiko, kunyozana kwa mipingo ya chisilamu, kusakhazikika kwa ndale, ziwembu ndikulimba mtima kwa anthu ena, kupezeka kwa magulu ena opsola muyezo popanga zinthu ndikupanda umunthu omwe akutumbula zidali za anthu ndikutafuna mitima yawo ndi mano, anthu okhala ndi zida omwe akumapha akazi ndi ana ndikutenga amuna ndikukamawazunza mosiyanasiyana. Zodandaulitsa ndikumvetsa chisoni ndizoti anthu oterewa akumanena kuti ndi asilamu. Koma zonsezi zikuchitika ndi anthu omwe ali ozikweza ndiotsatira satana omwe akupezeka maiko ambiri lero lino, anthuwa ndi omwe akuipitsa tsogolo ndikuononga umoyo wa anthu. Mukakhalidwe ngati aka tisayembekezere kuti maiko achisilamu apita patsogolo ndichitukuko, maphunziro ndikudzuka kuchokera mtulo lomwe ali nalo. Mchitidwe ngati uwu upangitsa kuti kudzuka kwa chisilamu kulephereke komanso ndikusowetsa chiyembekezo cha kudzukaku mpaka kufikira zaka zambiri. Nkhani yofuna kupulumutsa Palestine ndi asilamu ena kuchokera mmanja mwa Zionist ndi America idzaiwalika pakati pawo.
Nkhani yofuna kuthetsa mavutowa nditha kungogawa pawiri yomwe ikuchokera pa mwambo umenewu wa haji:
Choyamba: mgwirizano wa asilamu kuchokera pa umodzi wa Mulungu (Tauhid).
Chachiwiri: kumudziwa mdani ndikulimbana ndi njira zake pofuna kulimbana ndi chisilamu.
Kulimbikitsa ubale ndichiphunzitso chachikulu mumwambo wahaji umenewu. Nkhani ikafika apa ndiye kuti kulankhulana ndikukambirana nkhani zachipembedzo mokhala ngati mukulimbana wina ndi mnzake ndikoletsedwa. Kuvala zovala zofanana, ntchito yofanana,kuyenda kofanana, khalidwe lofanana ndilachikondi nditanthauzo la chikhulupiriro cha umodzi wa Mulungu kwa asilamu onse. Uwu ndi tsutso wa chisilamu kwa maganizo ndichikhulupiriro cha mtundu omwe taulongosola omwe ndi owonongeka omwe asilamu onse ayenera kudziwa kuti mtunduwu uli kunja kwa chisilamu. Asilamu ayenera kudziwa kuti chida chomwe angathe kukudzumula nacho anthu amaganizo ngati awa omwe akuphetsa ndikuketsa mwazi wa asilamu ndi anthu osalakwa ndi mwambo wa haji umenewu. Zodabwitsa ndizoti anthu omwe mwambo wakuzitsuka kuchokera kwa anthu ophatikiza Mulungu ndi zinthu zina umenewu omwenso ndi ntchito ya Mtumiki(s.a.aw), akupanga kukambirana pankhani ngati zimenezi kukhala zoletsedwa (haraam).
Ine monga tsogoleri wa asilamu monganso atsogoleri ena achisilamu ndikulengeza kuti zolankhula, ntchito zomwe zingapangitse kusiyana maganizo pakati pa asilamu ndikukolezera moto komanso kunyoza zinthu zoyeretsedwa za gulu lina lilonse la chisilamu kapena kukanira gulu lina lililonse la chisilamu, kuthandizira magulu okanira ndi ophatikiza Mulungu, kuchita chipongwe chisilamu lamulo lake ndi haraam.
Kumudziwa mdani ndi nsichi yachiwiri yomwe sifunikira kuyiwalidwa ndipo nthawi yomwe tikuponya miyala pamwambo wa rajimu jamrat tiyenera kukumbukira nsichi imeneyi.
Choyamba kupezeka kwa mdani pakati pathu kusatipangitse kuiwala nkhaniyi. Chachiwiri ndichoti kumudziwa mdani lero lino ndi makanema ama Zionists ndi anthu ozikweza omwewa moti sipakufunikira kuti tilakwitse chilichonse pankhaniyi. Chachitatu ndichoti njira za anthuwa ndiko kubweretsa kugawikana pakati pa asilamu, kufalitsa ntchito zoipa,ndale zosakhala bwino,chuma ndi zina.
Chimene iwo ayenera kudziwa ndichoti ife asilamu sitibwerera mmbuyo muchifuniro cha Mulungu koma tipitiriza kulimbana nawo, koma tikayiwala adaniwa ndiye kuti ntchito yathu idzatikulira kwambiri.
Ine ndili ndichikhulupiriro kuti nkhani yolimbana ndi adaniwa muno dziko la Iran taiona ndipo zinatheka chifukwa choti chilingaliro chathu ndi kugwira ntchito kwathu kudali kusatopetsa.Inunso asilamu azathu amaiko ena muyeneranso kugwiritsa ntchito ndikutengera nzeru pankhaniyi.
Pomaliza ndikupempha Mulungu kuti adalitse haji imeneyi ndikuti ikhale njira yothetsera zolinga za adani ndikuti Mulungu avomere ndikulandira haji yanu komanso kukupatsani matupi ndi moyo wathanzi.
Wasalamu alaikum warahamatullah ta’ala wabarakatuh.
Sayyid Ali Khamenei
5 dthili hijjah,1434, mofanana ndi 19, mihir 1392.
Add new comment