Mzimayi oyembekezera ndikutulutsa mwana ndikumudula mutu ndizo zotsatira za Jihad ya chiwerewere mudziko la Syria

Posachedwapa kwafalitsidwa nkhani ndi zithunzi kuchokera ku manyuzipepela olongosola za umoyo wapagulu, zomwe zikuwonetsera poyera atsikana ndi amayi opusitsidwa ndi ma MUFTI a gulu la Wahabiy powawuza zopita ku Syria ndikukapanga Jihad yachisembwere ndi anthu owukira dzikoli pofuna kukawapatsa mphamvu.

Mauthenga akuwonetsa kuti atsikana ndi amayi omwe akunamizidwa ndi kupusitsidwa ndi ma Wahabiy, tsiku lina lilironse akumagwiritsidwa ntchito molakwika popanga nawo zachisembwere ndipo akumakakamizidwa kutero popanda kutsatira malamulo a Shariyah.

 

Ena mwa anthu owukira ndi akupha mudziko la Syria omwe olo ndi pang’ono pomwe samatsatira malamulo, akadziwa za mzimayo oyembekezera, akumagwiritsa ntchito njira yowopsya ndi yoipitsitsa kwambiri yosemphana ndi umunthu pong’amba mimba ya mzimayi oyembekezerayo ndikutulutsa mwana oyembekezeredwayo ndikumudula mutu wake. Ndiuthenga ochokera ku nyuzipepela ya AWA, mabungwe oteteza za ufulu wamunthu adzikoli, pofuna kuthetsa zimenezi, apempha ku UN pozenga mlandu anthu oterewa ndicholinga chothetsa mchitidwe oipawu.

Add new comment