kudziwa chowonadi

Mudzina la Mulungu wachifundo wachisoni chosatha
Mtendere ndi madalitso a Mulungu akhale kwa inu olemekezeka
Mulungu amene adatilenga, adatiyikira ife chipembedzo ndi cholinga choti tisadzakhale onong’oneza bondo chifukwa cha zolankhula ndi zichitochito zathu.
Mosataya nthawi ndikoyenera kuti tipeze chilungamo ndi njira yoyenera kuyendamo chifukwa choti ndife apaulendo, ulendo omwe uli wamuyaya.
Mukuyang’ana kwa umulungu, munthu sicholengedwa chopanda chiyambi ayi (kutanthauza kuti adalengedwa) koma ndi opanda mathero komanso wamuyaya ndipo kakhalidwe ka umoyo wathu osatha kakuyedzamira pa maganizo ndi zintchito zathu za masiku ochepa apadziko la pansiwa.
Imfa ndi nsamuko opita kudziko lina ndipo kakhalidwe ka umoyo wa dzikolo kakugwirizana ndi umoyo wadziko la pansili.
Dziko lino ndi munda wa tsiku lomaliza.
 Ngati padziko lino tingadzale mbewu yabwino, ndiye kuti patsikulo tidzakolola bwino koma ngati sitidzala kapena kudzala mbewu yowola komanso yosathandiza padziko lino ndiye kuti patsiku limenelo tidzakhala oluza komanso onong’oneza bondo.
Ndikupepesa chifukwa choti ndikulankhula mwachindunji, koma nthawi ndi yochepa pomwe koma yoyenera kudutsa ndi yaitali kwambiri.
Ife tilibe mpata wambiri.
Ine ndikufuna kukambirana ndi inu zokhudza chipembedzo cha chisilamu.
Zokhudzana ndi chisilamu chowonadi.
Kutanthauza kuti SHIA.
Sindikudziwa kuti mukudziwapo chiyani zokhudzana ndi chisilamu chowonachi?
Kodi muli ndi chigamulo chanji ndi maganizo otani pokhuna ndi chisilamu?
Koma ine kapolo amene ndakhala zaka 20 ndikuphunzira maphunziro achisilamu, ndikoyenera kuti ndikutsimikizireni abale anga okondedwa kuti kuchidziwa chisilamu ndikukhala munthu ozindikira za chisilamu ndi chinthu chovuta kwambiri.
Kumachita kuti kumvetsetsa za chisilamu chowonadi kwa munthu wachilungamo ndi omvetsetsa sikumafunikira nthawi yambiri.
Zikukwanira kwa iye kupempha kwa Mulungu (Dua) pofufuza njira ya chilungamo popanda udani wina uliwonse  mumtima mwake komanso posakhala ndi nsankho, ponena kuti Ee! Mulungu wanga ndigwireni dzanja langa  ndipo ndiwongolereni kunjira yomwe inu muli osangalatsidwa nayo.
Ngakhale kuti kupeza njira yachowonadi ndi kosavuta koma kulankhula zokhudza chisilamu ndi kovuta kwambiri.
Kodi ine ndi kuwuzeni zotani?
Kodi inu muli ndi chikhulupiliro chanji? Mukudziwapo chiyani zokhudza chisilamu?
Koma ndi kupempha kuchokera kwa Mulungu yemwe adalenga inu ndi ine kuti atipulumutse tonsefe ndikuti atiwongolere kunjira yowongoka.
Mulungu tiwongolereni ife kunjira ya chilungamo.
Kodi ndi chifukwa chiyani kulankhula zokhudza chisilamu ndikovuta?
Tikamati kulankhula zokhudza chisilamu tikutanthauza kuti kulankhula za chimbedzo chomwe Mulungu wa ine ndi inu ali osangalatsidwa nacho.
Kulankhula zokhudza chisilamu kukutanthauza kuti kulankhula zokhudza kutukuka ndi kupita patsogolo.
Chipembedzo chokwana chomwe chakumbatira maphunziro osiyanasiyana mkati mwake. Kakhalidwe ndi kalengedwe ka dziko, chikhalidwe cha munthu pa yekha, chikhalidwe cha m’banja, mgwirizano wa umoyo wa pagulu ndi kukhanzikitsa boma, zachipatala ndi odotolo, kuthetsa mavuto a muuzimu wa munthu ndi china chirichonse chomwe munthu amachifunikira pa umoyo wake watsiku ndi tsiku. Ndichifukwa chake kulankhula za chisilamu ndi kovuta.
Koma kuvuta kwina komwe kulipo komwe kukuwonjezera pa kuvuta kumeneku, ndiko kuwonetsera poyera mdima omwe udabwera muchisilamu kuchokera kwa anthu omwe siadali asilamu.
Ndipo kuvuta kwina koposera pamenepo ndiko kulankhula ndi kulongosola za chisilamu chenicheni kuchokera pamagulu onsewa omwe alipo muchimbedzo cha chisilamu.
Masiku ano mayiko ndi anthu odzikweza ndi opondereza akuyesetsa kuti kutsekereza kuti kuyitana kwa chisilamu chenicheni kusafike kwa anthu ofowoketsedwa ndipo kuti zofuna zawo zichitike, adakhazikitsa ndondomeko yoipa kwambiri. Adakhazikitsa chisilamu chabodza chomwe chikuyimira chisilamu chowonadi kuti wina aliyese owina aziti chisilamu koma ichi.
Ndichifukwa chiyani amatsutsana ndi chisilamu chowonadi chomwe chiri SHIA?
Ndifukwa chiyani amadana ndi SHIA?
Chifukwa choti zonena za SHIA nthawi zonse ndi zoti, sipakuyenera kuti papezeke gulu la anthu opondereza kuti azilamulira padziko la pansi ndikuti azidya gawo ndi chuma cha anthu osawuka ndi ofowoketsedwa.
Ndikoyenera kuti zipangizo ndi zinthu zidzifika mofanana kwa anthu onse adziko la pansi.
Ndikoyenera kulimbana ndikuthetsa kupondereza ndinso kumangosunga chuma chomwe chikungokhala osagwira ntchito yake moyenera.
Ndikoyenera kuti tirimbane ndi onse akuba. Ndikofunika kudula manja a anthu omwe akupisa m’matumba mwa anthu osauka. Ndikoyenera kuti chilungamo chikhale cholamula pa dziko.
Adayesetsa kutsekereza kuti mawu achisilamu chowonadi asamveke pakati pa anthu pogwiritsa ntchito zida zonse monga monga; makanema, filimu, nyuzipepala, mabukhu, intaneti ndi zina zotero.
Ngati titafuna kulongosola momveka bwino tinganene kuti:
Ngati pali cholinga choti ukhale mkhirisitu, ndiye kuti udzayenera kukhulupilira gulu limodzi kuchokera mu magulu a chikhirisitu. Mwachitsanzo udzakhala wa KATOLIKA, wa CCAP kapena wa MBONI za YEHOVA ndi zina zotero.
Muchisilamu muli magulu ambiri kuposa magulu a chikhirisitu. Muchisilamu mwina udzakhala HANAFIY, MALIKIY, HAM’BALIY, SHAFIY, WAHABIY kapena udzakhala SHIA, ndipo gulu la SHIA ndi lomwe liri lakalekale komanso loyamba pa magulu a chisilamu.
Koma tinenenso izi kuti, gulu la WAHABIY ndi gulu la kunja kwa chisilamu lomwe likupezeka ndi cholinga chofafaniza chisilamu chomwe chalowa mu chisilamu mwabodza.
Koma zoti magulu akuluakulu achisilamu alipo asanu (5) ndi zobisika kwa ambiri ndipo ndi ochepa omwe amadziwa zimenezi koma izi ndizo zowona zake.
Chifukwa cha mavuto ambiri omwe adachitikira magulu anayi (4) zidapangitsa kuti magulu anayiwa adzipatse dzina loti SUNNIY koma zowona zake ndi zoti muchisilamu muli magulu asanu ndipo loyambilira komanso lakale mwa magulu amenewa ndilo gulu la SHIA lomwe mtsogoleri wa gululi adali limodzi ndi mtumiki Muhammad (s.a.a.w) ndipo adakula ali ndi mtumiki komanso adaleredwa ndi mtumiki wathu okondedwa (mtendere ndi madalitso a Mulungu akhale kwa iye).
Kumachita kuti olo ndi m’modzi yemwe mwa akuluakulu komanso atsogoleri a magulu anayi aja, mtumiki sadamuwonepo komanso mtumikiyo sadalankhulepo zokhuna ndi iwo komanso utsogoleri wawo. Ena mwaiwo adabadwa patadutsa zaka zopitilira 100 chimwalilireni mtumiki (s.a.a.w).
Tsopano ndizotheka bwanji munthu amene olo mtumiki wa chisilamu sadamuwonepo kukwanitsa kulankhula zokhudza mtumiki Muhammad (s.a.a.w)?
Funso limeneli ndi funso lovuta kwambiri komanso ndi kiyi losiyanitsa pakati pa chilungamo ndi bodza.
Zifukwa zambiri ndi zomwe zidapangitsa kuti SATANA yemwe ali mdani olumbilira wa munthu, asokoneze zipembedzo zonse mpakana chisilamu kuchokera kunjira yowongoka ndikuzipititsa ku njira yosayenera ndipo mukudutsa kwa nthawi njira zambiri zosochera  zidalowa muchimbedzo cha chisilamu zomwenso zidapangitsa kuti kupeza njira yachowonadi kukhale kovuta.
Kapolo ine ndikuwalangiza onse omvetsetsa komanso ofunafuna njira ya chilungamo kuti ngati mwapeza zotsatira kuti mwafika pachilungamo ndibwino kuti mupilire musapupulume kutero ndikuti mudikire pang’ono ndinso yambani mwafufuza pakati pa magulu asanu osiyana omwe ali muchipembedzo cha chachisilamu.
Chodandaulitsa kwambiri ndi choti kuyitanira kuchisilamu komwe kulipo padakali pano kuli m’manja mwa anthu omwe ali adani a mtumiki wa Mulungu ndi chisilamu kumene ndipo kupezeka kwawo cholinga chake ndi kuyipitsa chisilamu.
Pambuyo pa olemekezeka mtumiki Musa (a.s), SATANA adasocheretsa chipembedzo cha chiyuda ndipo adawaongolera a YUDA kukugwadira ng’ombe ndipo adamusiya mulum’malo wa mtumiki Musa (a.s) ndipo zonsenzi zidachitika motsogoleredwa ndi munthu otchedwa SAMIRIY.
Anthu adamutsatira SAMIRIY koma zodabwitsa ndi zoti SATANA adamukankhira ntchito yoipa imeneyi HAROON (Aroni)  ndipo adamutenga SAMIRIY kukhala olakwa.
Zimenezi zidabwerezedwa mu chimbedzo cha chisilamu komanso chikhirisitu.
Chisilamu chidakumana ndi zisokonezo zosiyanasiyana. Zisokonezo zonse ziri mbali ina ndipo WAHABIYYAT irinso mbali ina.
WAHABIYYAT ndi gulu lomwe lilipo ndi cholinga chofuna kusocheretsa anthu, kuwononga ndi kuyipitsa chipembedzo chachisilamu.
Ndiye pomaliza ndikupempha kwa Mulungu kuti atipulumutse ife ndi kutiwongola ndi kuwala kwake.
Zikomo kwambiri nonse abale okondedwa. 
 

Add new comment