Zodabwitsa zomwe zidachitika pambuyo pakuphedwa Imam Husain(a)1
chidachitika ndi chani pambuyo pakuphedwa kwa Imam Husain(a) tsiku la Ashura?
Mashia amakhulupirira kuti kusankha kwa mtsogoleri (Imam) pambuyo pa Mtumiki(s.a.a.w) kuli mmanja mwa Mulungu ndipo munthu alibe chilolezo cholowerera pa nkhaniyi. Monga momwe zilili kuti kusankhidwa kwa Mtumiki kuli mmanja mwa Mulungu motero munthu alibe mphamvu yolowerera pankhaniyi.
Mu Quran muli ma aya omwe akuikira umboni za nkhaniyi: Mulungu pankhani ya utsogoleri (Imam) wa Ibrahim akunena kuti:
إِنِّي جاعِلُكَ لِلنَّاسِ إِماما . البقره / 124
Ine Mulungu ndikukupanga iwe kukhala mtsogoleri (Imam) wa anthu.
Komanso Mulungu akunena kuti:
وَهَبْنَا لَهُ إِسْحَاقَ وَ يَعْقُوبَ وَ كلاً جَعَلْنَا نَبِيًّا . مريم / 49
Ife tidampatsa Ibrahim Ishaqah ndi Yaqub (yemwe ndi mwana wa Ishaqah) ndipo tidapanga onse awiri kukhala atumiki.
Mu ma aya amenewa taona kuti kusankhidwa kwa Ibrahim kukhala mtsogoleri kuli mmanja mwa Mulungu komanso kukhala kwa Ishaqah ndi Yaqub atumiki kuli mmanja mwa Mulungu, palibe aya mu Quran yomwe ikunena kuti utumiki ndi utsogoleri uli mmanja mwa anthu.
Mashia amakhulupiriranso kuti monga momwe Mtumiki amayenera kuti aonetse zozizwitsa pofuna kutsimikizira za utumiki wake, mtsogolerinso ayenera kukhala ndi zozizwitsa kuti atsimikizire utsogoleri wake, kupanda kutero ndiye kuti utsogoleri wawo ukhala osavomerezeka ndi anthu.
Ahlubait(a) amene ali atsogoleri (ma Imam) pambuyo pa Mtumiki(s.a.a.w) adali ndi zozizwitsa zimenezi ndipo kuchokera mmenemu ndi momwe anthu amamvera ndikukhulupirira zokamba zawo komanso kuvomereza za wu Imam wawo.
Imam Husain(a) yemwe ndi Imam wachitatu mu mathihab a chishia adali ndi zozizwitsa zambiri munthawi ya umoyo wake angakhale pambuyo pa imfa yake zomwe zikusonyeza kuti munthuyu adali mtsogoleri weni-weni ndi osankhidwa ndi Mulungu komanso Imam oyenera pambuyo pa m’bale wake Hasan(a). Choncho ndizosatheka kuti Mulungu apereke zozizwitsa zimenezi kwa anthu omwe sali oyenera pa udindowu ndipo ndi zozizwitsa zimenezi ndikusocheretsa nazo anthu.(Tithawire kwa Mulungu ndi mau ngati amenewa).
Pano mwachidule tikufuna kuti tineneko zina mwa zozizwitsa zomwe zidachitika pambuyo pakuphedwa kwa Imam Husain(a). Zodabwitsa zomwe zikuchokera kwa munthu yemwe nzeru zidagonja ndi iye pa zochitika zazikulu zimenezi. Zosakaikitsa kuti zodabwitsa zimenezi zili zokwanira kuti choonadi ndi chilungamo chionekere kwa munthu yemwe akufuna chiongoko. Koma kuti munthu athe kumvesetsa zodabwitsa zimenezi ayenera kuchotsa mumtima mwake nkhani yatsango ndikunyoza kuti athe kuona nkhaniyi ndi mtima wake oyera.
Pomwe mashia akutsatira Imam Husain(a) yemwe ndi tsogoleri ochokera kwa Ahlubait(a) ndikukhulupirira zodabwitsa zake, pali anthu ena omwe safuna kutsatira utsogoleri wa mwana wa Mtumikiyu koma mmalo mwake akutsatira anthu omwe ali adani a akunyumba ya Mtumiki(s.a.a.w).
Tikufuna kutchula zodabwitsa zimenezi kuchokera mu mabuku ndi mashaikh odalilika kuti ukhale umboni kwa anthu onse ndikuti anthu okanira asakhale ndi mpata wina ulionse okanira.
Add new comment