Mitambo yaku England idalira ndikutulutsa magazi tsiku la Ashura.
Mitambo yaku England idalira ndikutulutsa magazi tsiku la Ashura.
Nkhani imeneyi idatchulidwa mu bukhu lotchedwa “ zochitika za nthawi ya Anglosaxon” lomwe lidatulutsidwa mchaka cha 1996 kunena kuti tsiku la Ashura ( nkhani yomwe idachitika mchaka cha 61 hijir) mitambo yaku England idalira ndikutulutsa magazi. Nkhaniyi ndi imodzi mwa nkhani zomwe zilipo mu nkhani za kale(history), koma yokhayi ndiyodabwitsa komanso ndiyosaiwalika mu history.
Bungwe lofalitsa nkhani lotchedwa Aljawar pambuyo pofalitsa nkhaniyi adalemba kuti: bukhu la “ zochitika za nthawi ya Anglosaxon” ndilimodzi mwa mabuku odalilika mu nkhani za kale lomwe lidatanthauziridwa ndi Michael Swanton.
Bukhuli lidafalikira ku England mchaka cha 1996 ndipo mchaka cha 1998 lidatulutsidwa munzinda wa Newyork ndi University ya Exeter. Mutsamba la 38 mubukhuli muli mau awa: Here in Britain there was Bloody rain, and milk and butter were turned to blood, (685).
Mchaka cha 685 kuno ku Britain kudali mvula ya magazi, mkaka ndi butter zidasanduka magazi. Nkhani yake ili chonchi mu bukhuli tsamba 38:
A.D. 685. This year King Everth commanded Cuthbert to be
consecrated a bishop; and Archbishop Theodore, on the first day
of Easter, consecrated him at York Bishop of Hexham; for Trumbert
had been deprived of that see. The same year Everth was slain by
the north sea, and a large army with him, on the thirteenth day
before the calends of June. He continued king fifteen winters;
and his brother Elfrith succeeded him in the government. Everth
was the son of Oswy. Oswy of Ethelferth, Ethelferth of Ethelric,
Ethelric of Ida, Ida of Eoppa. About this time Ceadwall began to
struggle for a kingdom. Ceadwall was the son of Kenbert, Kenbert
of Chad, Chad of Cutha, Cutha of Ceawlin, Ceawlin of Cynric,
Cynric of Cerdic. Mull, who was afterwards consigned to the
flames in Kent, was the brother of Ceadwall. The same year died
Lothhere, King of Kent; and John was consecrated Bishop of
Hexham, where he remained till Wilferth was restored, when John
was translated to York on the death of Bishop Bosa. Wilferth his
priest was afterwards consecrated Bishop of York, and John
retired to his monastery (21) in the woods of Delta. This year
Were there was in Britain a bloody rain, and milk and butter turned to
blood
Nkhani ndi yoti chaka cha 685 chimenechi chikugwirizana ndi chaka cha 61hijir,Qamar chomwe Imam Husain(a) adaphedwa pamodzi ndi anthu ake.
Pali nkhani zina zomwe tikuzipeza mu mahadith kuti tsiku limeneli la Ashura mitambo idalira ndikutulutsa magazi, mwachitsanzo,Hazrat Zainab adanena kuti
"أو عَجبتم أن مَطَرت السماء دماً"
Kodi mukudabwa zoti kumwamba kudalira ndikutulutsa magazi!
Angakhale mu mabuku ahalu sunnah mudanenedwa nkhaniyi pomwe olemba nkhani akuti:
"لما قتل الحسین اسودّت السماء وظهرت الکواکب نهاراً حتى رأیت الجوزاء عند العصر وسقط التراب الأحمر"
Husain ataphedwa kumwamba kudachita mdima ndipo nyenyezi zidaoneka mpaka ndidaona nyenyezi yotchedwa Jauzai masana atsikuli kenako kudagwa dothi lofiira kuchokera kumwamba.
Olemba nkhaniyi akupitiliza kunena kuti tsikuli ku Palestin (baitul maqdas) zidali zoti mwala wina ulionse omwe umatembenuzidwa umapezeka kuti uli ndi magazi atsopano pansi pake. Kudali kadansana kwa masiku okwana atatu.
Mulungu akudalitseni chifukwa cha kuwerenga kwanu.
Add new comment