Kutchula madandaulo akuphedwa kwa Ali Asghar (mwana wa Imam Husain(a)) pa karbala.
Kutchula madandaulo akuphedwa kwa Ali Asghar (mwana wa Imam Husain(a)) pa karbala.
Monga tikudziwa kuti mwezi wa Muharram umenewu ndi mwezi omwe nkhani yodandaulitsa ndi kumvetsa chisoni idachitika pa karbala komwe kuli kuphedwa kwa Imam Husain(a) ndi ana ake komanso abale ake, mmodzi mwa ana omwe adaphedwa pamalowa ndi Ali Asghar yemwe adali mwana wachichepere komanso oyamwa.
Pano tikufuna kulongosola zina mwa zinthu zomwe zidamuchitikira mwana ameneyu komwe kuli kudandaula ndi imfa yomvetsa chisoni imeneyi.
Inde zoona kuti mwana ameneyu adali wachichepere koma tikaganizira kwambiri tipeza kuti mwanayu adali mmodzi mwa othandiza Husain(a) chifukwa choti kuphedwa kwa mwanayu kukuonetsera poyera kupanda chilungamo, chisoni,kusalungama ndi kupondereza kwa anthu amenewa. Izi zikupereka umboni okwana kuti Imam Husain(a) adaphedwa moponderezedwa.Kusonyeza kuti imfa yamwanayu idatsekula thumba lalikulu lakupanda umunthu ndi chipembedzo kwa anthu ngati amenewa.
Ayatullah Haqi Chenasi adanena kuti muyenera kukumbukira ndikutchula madandaulo akuphedwa kwa Ali Asghar chifukwa ndi momwe kuphedwa koponderezedwa kwa Husain kukudziwika.
Ngati mukufuna kumukumbukira Imam Husain(a) muyeneranso kulakalaka kutchula mavuto a Ali Asghar kuti kukumbukira kwanu kukhale kokwanira.
Tsiku lina Imam Sajjad(a) adamufunsa Minhar (nthawi yomwe Mukhtar Thaqafi adaukira anthu opha Husain(a) )kuti kodi nkhani ya Harimalah ikuti bwanji? Minhar adadabwa nati e! inu mwana wa Mtumiki, ine ndidamva kuti amene adadula mutu bambo anu ndi Shimr osati Harimalah, ndipo Harimalah ameneyu adali kukhala ku Kufah. Imam Sajjad adayankha nati: Inde, ndizoona kuti Shimr ndiyemwe adadula mutu bambo anga ndipo Mulungu amuotche iye ndi moto waku jahannama. Koma ntchito yomwe adachita pa karbala idaotcha chiwindi cha bambo anga Husain(a).
Imam Sajjad(a) adamupangira Harimalah duwa kuti ambuye Mulungu muotcheni Harimalah ndi moto owopsa yomwe posadutsa masiku ambiri idayankhidwa pomwe Mukhtar Thaqafi adalimbana naye ndikumukumaniza kenako adamufunsa kuti talongosola zomwe udachita ndi Husain(a)?
Harimalah adayankha kuti ndikanena undisiya? Mukhtar adati dziwa kuti kunena kapena osanena uphedwa basi. Harimalah adati ndinena kuti zikupweteke. Ine ndidabweretsa ku karbala mivi itatu ya nsonga zitatu, umodzi mwa miviyi ndidaphera Ali Asghar omwe udazinga khosi lake kuchokera khutu lina kufikira khutu linanso
فذبحه من الاذن الى الاذن او من الوريد الى الوريد
Muviwu udazinga Ali Asghar kuchokera khutu lina kufikira khutu lina kapena kuchokera nsemba wina kufikira nsemba wina.
Chifukwa nthawi imeneyi Imam Husain adali atamunyamula Ali Asghar ndikumamuonetsa kwa adaniwa kuti mwanayu ali ndiludzu kwambiri mugawireni madzi chifukwa mukapanda kutero amwalira, iye wafika poti akuphupha-phupha monga momwe imapangira nsomba ikatuluka mmadzi ndikukhala nthawi yayitali. Imam Husain(a) adali kunena kuti:
يا قوم ان لم ترحموني فرحم هذا الطفل كيف يتلظى عطشاناً ، منّوا على ابن المصطفى اما ترونه كيف يتلظى عطشاناً
E! inu anthu, ngati simukufuna kundimvera ine chisoni palibe kathu koma mumvereniko chisoni mwana uyu, kodi inu simukuona momwe akuphuphira-phuphira chifukwa cha ludzu?
Mumvereniko chisoni mwana wa Muhammad Mustafah (s.a.a.w), kodi simukuona momwe akuphuphira-phuphira ndi ludzu?
Imam Husain akulankhula chonchi ndipomwe Harimalah adagenda muvi wake wa nsonga zitatu.
فرماه حرملة بن كاهل الاسدى بسهم فذبحه من الاذن الى الاذن فى حجر الحسين
Kenako Harimalah bin Kahil Asadiy adagenda muvi wake omwe udazinga Ali Asghar kuchokera khutu lina kufikira khutu lina ali mmanja mwa Husain(a).
Harimalah adapitiliza kunena nati muvi wina ndidamugenda nawo Imam Husain(a) pomwe wina ndidamugenda nawo Abdullah bin Husain(a). Apa Imam Sajjad(a) adati: رحم الله المختار (( Mulungu amuchitira chifundo Mukhtar))
و السلام على عبد الله بن الحسين الطفل الرضيع
ndipo mtendere ukhale kwa Abdullah bin Husain(a) mwana wang’ono oyamwa.
Nkhani ikuti nkhondo itafika pothina Imam Sajjad (a) adatenga lupanga ndikubwera malo ankhondo koma Imam Husain(a) atamuona adanena kuti mubwezeni iyeyo chifukwa choti mtundu wathu upitilira ndi iyeyo (komanso Imamat).
Imam Husain (a) adakuwa kuti kodi pali amene angandithandize? Koma tsoka kwa anthu ngati amenewa ndiloti sadamuyankhe Imam ameneyu angakhale anthu omwe amamulembera makalata kuti abwere ku kufah. Kenako kudamveka kukuwa kuchokera ku matenti ake. Atafunsa kuti zikukhala bwanji, Zainab adayankha kuti mwana yemwe adali muchikuta chake chifukwa chakumva mau anu wayamba kulira mpaka kugwera pansi. Husain(a) adali ndi ana ang’ono kwambiri omwe adali nawo ku karbala monga Ali Asghar, Abdullah ndi mwana yemwe adabadwa tsiku lomweli la Ashura ndipo adaphedwa ndi anthu owuma mitima ngati amenewa.
Nthawi yomwe Husain adali atamutenga Ali Asghar mmanja mwake akupempha madzi, Umar bin Saad adamuuza Harimalah kuti ndichifukwa chani sukuyankha Husain? Harimalah adati kodi ndiyambe kugenda bambo kapena mwana? Umar bin Saad adati kodi sukuona khosi loyera la Ali Asghar ? Mauwa ali ndi matanthauzo angapo, limodzi mwa iwo ndi ili:
- Ndiye kuti Imam Husain(a) adali atamutenga Ali Asghar kutsogolo kwake osati mmbali kapena kumbuyo.
Ali Asghar ataphedwa, Imam Husain(a) adali kutenga magazi ake ndikumaponya kumwamba, koma chodabwitsa ndichoti magazi amenewa samabwerera pansi. Imam Husain(a) adati: ambuye Mulungu malo a mwana wanga Ali Asghar ndi a pamwamba kuposa a mwana wa ngamiya yemwe adaphedwa inu ndikutumiza mavuto.
Zomwe Imam Husain (a) adapanga ndi mwana wake Ali Asghar zidali zosiyana ndi momwe adachitira ndi anthu ena. Mwanayu ataphedwa adatsika pa hachi ndipo adali kuyenda kupita kuma tenti ndikubwerera, kenako padabwera mzimayi wina kwa iye kenako adapemphera ndikumuika mmanda.
Mfunso ndiloti kodi ndichifukwa chiyani Imam Husain(a) adali kupempha madzi akudziwa kuti mwana wake wafika malo onga nsomba oti apatsidwe madzi kapena osapatsidwe amwalirabe?
Yankho ndiloti Imam Husain adachita izi kuti mwina papezeka munthu wina omva chisoni ndikubwerera munjira ya Mulungu ndikuongoledwa.Koma anthuwa adali olimba mitima kuti sadamve chisoni koma kupha mwana wang’ono ngati ameneyu. Angakhale pambuyo poti mwanayu adaikidwa mmanda adali kunena kuti chifukwa chiyani Husain waika mmanda mwana wake ndikusiya anthu ena osawaika? Inde, Imam Husain(a) amadziwa kuti anthu omwe aphedwe pamalowa mitu yawo idulidwa ndikuikidwa kunsonga kwa mikondo, kodi kamutu ka Ali Asghar kali ndikupirira koikidwa kunsonga kwa nkondo? Iye ankadziwa kuti thupi lake lipondedwa-pondedwa, nanga anthu inu kathupi ka Ali Asghar kali ndikupirira koti kapondedwe-pondedwe?
Padalinso chiyembekezo choti ngati anthu oipa amenewa achitira chisoni mwana wa miyezi isanu ndi umodzi mwina achitira chisoni ana a zaka zitatu, koma anthu oipisitsa ngati awa sadamvere chisoni mwana wa miyezi isanu ndi umodzi.
Abu Khalif yemwe ndi mmodzi mwa anthu omwe adali otenga ma fosholo ku karbala omwe (wamkulu wawo adali Abu Ayyub), adabweretsedwa kwa Mukhtar. Iye adamufunsa Abu Khalif kuti : kodi ungakumbukire nthawi yomwe udamvako chisoni ndi Husain? Iye adati: nthawi yomwe Husain adamutenga Ali Asghar ndipo adali mmanja namayenda naye kupita kumatenti ake ndikumabwerera, kenako ndidamuona mkazi wina adabwera kwa iye kenako Imam Husain adamuika mmanda Ali Asghar. Apa Mukhtar adasinthika nkhope chifukwa cha izi kenako adati palinso zina? Adati inde, ataikidwa mwanayu anthuwa adabwera ndikukumba malo omwe adaikidwa mwanayu ndikutulutsa mtembo wake.
Mulungu akudalitseni polilira Husain(a) ndi mwana wake.
Add new comment