Ndakatulo yokhudza Imam Husain(a)
Ndakatulo yokhudza Imam Husain(a)
شیعتی ما ان شربتم ماء عذب فاذکرونی
اَو سَمعتم بغریب اَو شهید فَاندبونی
و انا سبط الذی من غیر جرم قتلونی
وبجرد الخیل بعد القتل عمدا سحقونی
لیتکم فی یوم عاشورا جمیعا تنظرونی
کیف استسقی لطفلی فابوا ان یرحمونی
ویلهم قد جرحوا قلب، لرسول الثقلین
فالعنوا هم ماستطعتم شیعتی فی کل حین
شیعتی ما ان شربتم ماءَ عذبٍ فاذکرونی
Zochitika zapa Karbala ndi mavuto akulu kwambiri omwe adagwa muchisilamu.
Imam Husain (a) ataphedwa thupi lake ndikugwera pansi, mau adamveka kuchokera mthupi lake lomwe lidali loti mutu wake udachotsedwa. Kuchokera muthupili mudamveka mau. Mutu wake omwe udaikidwa kunsonga kwa nkondo udali kulankhula mau ndikuwerenga Quran, komanonso thupi lidalankhula mau omwe ndindakatulo yomwe ili mmwambayi.
Mauwa adali otere:
شیعتی ما ان شربتم ماء عذب فاذکرونی
E! inu onditsatira anga ( mashia), nthawi yomwe mukumwa madzi ndikumbukireni ine, mukatero inu mukhala mu shia weni-weni.
Ndichifukwa chake nkhani ikuti Imam Sajjad(a) amati akaona madzi amalira kwambiri, amati akafuna kupanga udthu ndikuona madzi amalira kwambiri mpaka madzi amasanduka amudthafu(madzi oti achoka mulamulo la madzi monga momwe alili madzi azipatso oti sizingatheke kupangira udthu).
Munthu wina adafunsidwa kuti kodi ndintchito yabwino yanji yomwe wapanga usiku wa Qadr, iye adayankha kuti palibe ntchito yomwe wapanga kupatula kuti adangodzuka ndikumwa madzi ndikumukumbukira Imam Husain(a), kudanenedwa kwa iye kuti wagwira ntchito yayikulu kwambiri yomwe mwini wake Husain adaichemerera monga momwe tikumvera mu ndakatuloyi.
Mfundo yomwe tingaunikirane pamalopa ndiyoti tiyenera kusiyanitsa pakati pandakatulo zomwe timazimva zikunenedwa ndi anthu ena ndizomwe anthu ngati Imam Husain amanena. Ndakatulo zomwe anthu wamba amakhala akunena zimakhala zongosangalatsa kapena kupereka phunziro lina lake pang’ono pomwe ndakatulo za anthu monga Imam Husain ndichoonadi chokha chokha komanso chiphunzitso chachikulu kwa anthu.Mau a anthu amenewa alibe chikaiko mkati mwake, ngati inu mumamva mau awo ndikukhala ndichikaiko dziwani kuti mumtima mwanu mulibe chikondi ndikhulupiriro cha akunyumba kwa Mtumiki(Ahlubait). Chifukwa anthu amenewa akuchokera mnyumba mwa Mtumiki(s.a.a.w) amene samalankhula zinthu zammutu mwake koma amalankhula zochokera kwa Mulungu. لا ينطق عن الهوى ان هو الاّ وحي يوحى
Mukamuyang’ana Imam Husain(a) mumpeza kuti ndi munthu yemwe ali ndi ulemelero waukulu. Anthu omwe bambo ndi mai awo awiri ndi ma’asum (ochinjirizidwa ku kuchima) ndi Hasan ndi Husain(a) . Kusonyeza kuti Husain sadali munthu wamba oti ndikumufanizira ndi Yazid pa ubwino ndi upamwamba.
اَو سَمعتم بغریب اَو شهید فَاندبونی
Mukamva zinthu zodabwitsa ndi zovuta komanso kuphedwa kwa anthu ena ndikumbukireni ndikundidandaulira.
Mukaona zodabwitsa ndi mavuto (monga mmene anthu ambiri akuphedwera, ana, nkhalamba ndi anthu odwala ku Miyanmar,Pakistan,Afghanistan, Iraq ndi ena) ndikumanidwa madzi, kumbukirani kuti zinthu zimenezi ndizomwe zidandionekera ine Husain choncho khalani odandaula ndi izo.
و انا سبط الذی من غیر جرم قتلونی
Ine ndi chidzukulu chomwe chidaphedwa popanda tchimo lina lililonse.
Anthuni kutheka kuti mwina inu simukundidziwa kuti ine ndindani, ndikuuzani, ine ndi chidzukulu cha Mtumiki wa Mulungu (s.a.a.w) chomwe anthu oponderezawa adachipha popanda tchimo.Kodi inu mungandiuze kuti kodi Imam Husain adamupheranji? Husain ndi:
- Chidzukulu cha Mtumiki wa Mulungu.
- Mtumiki adanena za iye kuti ndichikongoletso cha chindanda cha Mulungu.
- Bwana wa anyamata a kumtendere.
- Mtumiki adati :حسين مني وانا من الحسين ((Husain ochokera mwa ine, inenso ochokera mwa iye))
- Ndi mwini wa aya ya Mawaddah.
- Ndi mwini wa aya ya Mubahalah.
- Ndi mwini wa sura ya Hal-ata.
Nthumwi ina yaku Rome yomwe idakhala nawo pa msonkhano wa Yazid idati kwa iye: iwe Yazid chipembedzo changa chili bwino kuposa chipembedzo chako chifukwa ine ndichidzukulu cha mmodzi mwa atumuki koma ndimalemekeza atumiki ndi azibale onse komanso sindinapange zomwe iwe wapanga popha mwana wa Mtumiki wanu ndikumasangalala chonchi.
Palibe chifukwa chomwe inu mungachitchule chomveka chomwe mudamuphera Husain kupatula chikhulupiriro chake choyera mu chisilamu.
وبجرد الخیل بعد القتل عمدا سحقونی
Munandipondaponda ndi hachi pambuyo pakundipha dala.
Chifukwa chimodzi chomwe chidachititsa kuti Imam Husain asaikidwe mmanda nthawiyo chidali choti thupi lake lidali loti lanyenyeka-nyenyeka chifukwa choliponda- ponda ndi hachi.
Pambuyo pakupha Imam Husain (a) Umar bin Saad adakuwa kuti kodi ndi ndani yemwe angaponde-ponde thupi la Husain kuti akalandire mphoto yayikulu? Kudapezeka anthu okwana khumi omwe adazipereka kuti agwira ntchito imeneyi, mmodzi wawo adali Usaid bin Malik yemwe atafika kwa Ubaidullah bin Ziyad adali kulongosola monyadira kuti ndife amene taponda-ponda thupi la Husain(a).
لیتکم فی یوم عاشورا جمیعا تنظرونی
Tsoka likhale kwa inu chifukwa cha zomwe mwachita tsiku limeneli la pa 10 mwezi wa Muharram pondipha ine uku mukuyanga’nira mavuto anga.
Anthu amenewa mitima yawo idalimba kuposa mwala posaganizira angakhale pang’ono mavuto omwe angakumane nawo pambuyo pakupha chidzukulu cha Mtumiki(s.a.a.w) , kodi iwowa adalibe manyazi kuti akakumana ndi Mtumiki wawo akamuyang’ana ndi khope yotani komanso akamuuza chani za Husain(a). Iyayi, satana akamupanika munthu pomutalikitsa ndichilungamo ndichoonadi zimakhala monga chonchi.
کیف استسقی لطفلی فابوا ان یرحمونی
Ndizotheka bwanji kuti ine ndipemphe madzi a mwana wanga koma ndikukana kundipatsa osandimvera chisoni.
Chisilamu ndichipembedzo chomwe chimatiphunzitsa nkhani ya chisoni kufikira pomwe chikunena kuti ngati munthu utakhala muchipululu ndipo uli ndi madzi ochepa okwanira kupangira udthu, ngati patabwera chinyama chaludzu akuti madziwo uchipatse chinyamacho iwe upange tayammam, ichi ndichisilamu chomwe ife tikuchidziwa, tsono anthu amenewa chisilamu chawo ndichotani chopanda chisoni angakhale kwa mwana wang’ono yemwe kumukaniza madzi? Chisilamu chawo ndichamtundu wanji chopanda chisoni kwa munthu wapamwamba ngati Husain(a) mpaka kumukaniza madzi? Ine chisilamu cha iwowa chikundidabwitsa kwambiri. Husain (a) nkhani itafika pothina adanena kwa iwo kuti:
منّوا على ابن المصطفى اما ترونه كيف يتلظى عطشانا؟
Muchitireni chifundo mwana wa Muhammad Musitafah, kodi inu simukuona momwe akuvutikira ndi ludzu?
Munthu yemwe angamukumbukire Imam Husain(a) nthawi yomwe akumwa madzi mphoto yake ndi yoti:
- Adzakhala ngati adali limodzi ndi Imam Husain(a) ku karibala ,adaphedwa naye limodzi.
- Adzakhala ngati kuti wapereka madzi kwa ana aludzu a Imam Husain(a) .
Imam Husain adalankhula kwa Shimr kuti:
يا شمر! اذا كان لابدّ من قتلي فاسقني جرءة من الماء
E! Shimr, ngati watsimikiza zofuna kundipha ine ndipatseko madzi pang’ono.
Imam Husain(a) adalikufuna kumukumbutsa Shimr kuti mwina akumbukira ndikubwerera mwa Mulungu ndicholinga choti mawa asadzanene kuti sindimadziwa chilichonse. Chifukwa Mulungu ndiokhululuka.
ویلهم قد جرحوا قلب، لرسول الثقلین
Tsoka likhale kwa iwo chifukwa choti adavulaza mtima wa Mtumiki wa zinthu ziwiri zolemera ( anthu ndi majini).
Mtumiki (s.a.a.w) adali kumukonda Imam Husain(a) ndipo tsiku lina adali kumupsopsona kwambiri kufikira poti adamufunsa kuti kodi zimenezi akupangilanji. Mtumiki adati: ndikupsopsona malo omwe mivi ndi mikondo idzakhala ikufikira.
Chabwino zomwe mukufuna kupangazo pangani, anawo iphani, akaziwo vutitsani, asilikali angwiro a Husain iphani, chidzukulu cha Mtumiki omalizachi iphani koma dziwani kuti Mulungu, Mtumiki ndi anthu okhulupirira adzaona ntchito zanuzo. قل اعملوا سيرى الله عملكم و رسوله و المؤمنون
Add new comment