Zionetsero za Husain(a) mu Quran 4
Mulungu subuhanah wata’ala akunena mu Quran yolemekezeka kuti:
يا أيتها النفس المطمئنة * ارجعى إلى ربك راضية مرضية * فادخلى فى عبادى و ادخلى جنتى؛ . الفجر: 27- 30
E! iwe mtima odekha ndikukhazikika, bwerera kwa mbuye wako uli osangalala komanso osangalalidwa ndi Mulungu, lowa mugulu la akapolo anga, lowa mu mtendere wanga.
Kodi pali mtima omwe uli odekha ndikukhazikika kuposa mtima wa kuwala kwa maso a Mtumiki(s.a.a.w) amene ali bwana wa anthu onse ofera mu njira ya Mulungu Husain (a)?
Yemwe adakumana ndi mavuto akulu oti vuto lina lililonse palokha limakwanira kugwedeza phiri lomwe laima molimba, monga asilikali ake onse, azibale ake ndi ana ake adaphedwa mwini wake akuona ndi maso ake.
Onena nkhaniyi akuti: nthawi ina iliyonse yomwe masiku amayandikira ku Ashura ( pa 10 mwezi wa Muharram) mavuto amenewa adali kukulirakulira kukhala ngati kuti kukumana kwake ndi Mulungu wake ali odekha ndi okhazikika mtima kudali kukuyandikira.
Inde, pali ma aya ambiri omwe anena za nkhani ya Husain, koma aya iyi yasankhidwa chifukwa choti ndi aya yomwe ikuonetsera kwambiri za Husain (a) zakudekha ndi kukhazikika kwake mtima.
Imam Swadiq (a) adanena kuti: Sura ya Fajir muyenera kuiwerenga nthawi yomwe mukupemphera mapemphero okakamizika(wajib) komanso osakakamizika( Mustahab) chifukwa sura imeneyi ndi ya Imam Husain(a) ndipo mitima yanu imangire za sura imeneyi, Mulungu akuchitireni chisoni ndikukhululukirani machimo anu.
Abu Usamah yemwe adali nawo pamalo omwe Imam Swadiq amanena izi adafunsa kuti kodi ndichifukwa chiyani sura imeneyi ikukhudzana ndi Imam Husain(a)? Imam adati: kodi iwe sukumva mau achoonadiwa omwe akunena kuti e! iwe mtima odekha ndi okhazikika, mauwa akutanthauza Imam Husain(a) chifukwa iye ndi “nafusil mutumainnah” ndipo ndiosangalalidwa ndi Mulungu. Sura imeneyi idatsikira iye ndi omutsatira ake ndi onse otsatira akunyumba kwa Mtumiki(s.a.a.w) ndipo munthu wina aliyense yemwe angawerenge sura imeneyi mowilikiza akakhala ndi Imam Husain malo amodzi ku mtendere, Mulungu ndi wamphamvu komanso ozindikira china chilichonse.
Monga momwe timakhala tikunong’oneza bondo kuti kalanga ine! ndidakakhala mugulu lanu ndikuphedwa limodzi nanu ndicholinga choti nafenso tikhale opambana kwakukulu, tiyeni tiyesetse kuti zochita zathu, zonena zathu zikhale zofanana ndi Imam Husain(a) kuti mwina Mulungu akakhale osangalala nafe monga momwe surayi ikunenera chifukwa
رضوان من الله اكبر ife tikudziwa kuti mphoto ya chisangalalo cha Mulungu chimenechi ndi yayikulu yomwe ndi mtendere.
Kuzipereka komwe Imam Husain(a) adaonetsa pamodzi ndi anthu ake kuli koti mbuyomu kudalibe ndipo sikudzapezeka angakhale mtsogolo momwe. Awa adali mayesero kwa iye. Chofunika pankhaniyi ndichakuti Asilamu alero lino ayenera kutengera phunziro pakuzipereka pofuna kuteteza chipembedzo ndikulimbana ndi anthu opondereza ndikuzikweza monga momwe tidaonera asilikali adziko la Iran polimbana ndi anthu omwe amafuna kubweretsa zinthu zosemphana ndi chisilamu, iwowa adatengera phunziro kwa Imam Husain(a) pofera munjira ya Mulungu ndikukhala opambana kwakukulu.
Tipemphe Mulungu kuti mtima ofuna kufera munjira yake usatichoke ndiponso tikhale anthu omvera akulu akulu achipembedzo omwe ali olungama (momwe zilili ku Iran kuti amamvera ndikutsatira mtsogoleri wamkulu Khamenei) kuti mtsogolo muno tidzakhale onyamula mbendela ya Imam wanthawi yathu ino Mahdi (a.f).
Add new comment