Ubwino wa Imam Husain 1
Ubwino wa Imam Husain 1
Mtumiki Muhammad(s.a.a.w) adanena kuti:
إنّ لقتل الحسين - عليه السلام - حرارة فى قلوب المؤمنين لا تبرد أبداً.
(( Kuphedwa kwa Imam Husain (a) ndi moto omwe wakolezedwa mmitima mwa anthu okhulupirira omwe sudzathimitsidwa mpaka kalekale)).
Mfunso lomwe likufunsidwa pamalopa ndi loti kuti Husain ndi ndani?
Kodi Husain ndi ndani oti kulimbana kwake ndi anthu ofuna kuononga chisilamu kulipo mpaka kalekale?
Husain ndi ndani yemwe magazi ake akuzutsa anthu pambuyo pakudutsa nthawi yayitali?
Husain ndi ndani yemwe chiphunzitso chake chili chosula anthu?
Husain ndi ndani oti dzina lake lili mkamwakamwa mwa zilankhulo zosiyanasiyana?
Husain ndi ndani oti makhalidwe onse abwino asonkhana mwa iye?
Husain ndi ndani yemwe ali sitima yachipulumutso komanso nyale yachiongoko?
Husain ndi ndani yemwe wakhazikitsa kukonda kufera mu njira ya Mulungu, kuopa Mulungu, kuzindikira, chikondi, chifundo ndi makhalidwe abwino dera la Karibala?
Husain ndi ndani yemwe kuphedwa, kupezeka ndi kulimba kwake kuli chinthu chozizwitsa nthawi zonse?
Husain ndi ndani yemwe sadakhale chete ndi kupondereza?
Husain ndi ndani yemwe mmalo mogonjera adasankha kufera munjira ya Mulungu?
Husain ndi ndani yemwe adalimbana ndi makhalidwe oipa ndi onyozeka?
Husain ndi ndani yemwe kulira pomukumbukira kuli ngati munthu akubwezeretsa thupi lake mmalo pambuyo poti lidaonongeka?
Husain ndi ndani yemwe pamanda pake ndi malo omwe anthu amapezera chichilitso?
Husain ndi ndani yemwe chikondi kwa iye zili ngati kuti munthu wateteza katundu wake wapadziko lapansi ndi tsiku lomaliza?
Husain ndi ndani yemwe pofuna kuti chipembedzo chipitilire adalolera kutsogoza ana ake okondedwa?
Husain ndi ndani yemwe agogo ake olemekezeka Muhammad(s.a.a.w) adanena kuti(( Husain ndi ochokera mwa ine ndipo ine ndiochokera mwa iye))?
Inde, uyu ndi Husain yemwe Mulungu adampatsa dzina loti
نفس المطمئنة (( mtima odekha ndikukhazikika)).
Uyu ndi Husain yemwe dothi lopezeka pa manda ake ndi chichilitso.
Uyu ndi Husain yemwe adaphedwa poitanira kuzinthu zabwino ndikuletsa zinthu zoipa.
Uyu ndi Husain yemwe kuphedwa kwake kuli kwa pamwamba.
Uyu ndi Husain yemwe zolankhula zake ndi zopereka phindu.
Uyu ndi Husain yemwe adasankha imfa ya ulemerero mmalo mwa imfa yonyozeka.
Uyu ndi Husain yemwe adaphunzitsa anthu nkhani ya kufuna ufulu ndikulemekezeka kwa munthu.
Uyu ndi Husain yemwe kumulilira iye kumabweretsa kuwala mumtima.
Uyu ndi Husain yemwe adalimbana ndi asilikali a adani okwana 30,000 popanda kugonjera iwo.
Uyu ndi Husain yemwe angakale kuti ana ake adadulidwa-dulidwa koma sadagonjebe.
Uyu ndi Husain yemwe adasiya zonse chifukwa cha chikondi kwa mbuye wake.
Uyu ndi Husain yemwe adalikuyamikabe Mulungu ndikupirira angakhale mwana wake wamiyezi isanu ndi umodzi adabaidwa ndi mkondo wansonga zitatu.
Uyu ndi Husain yemwe magazi ake adali mmalupanga a adani komabe kupambana ndikwake.
Husain ndi tsogoleri yemwe amakondedwa ndi Atumiki onse ndipo amakhala akumulilira.
Uyu ndi Husain yemwe pambuyo pakuphedwa kwake utsogoleri opanda pake wa mabani umayyah udazindikira kuti kulimba kwake atamwalira kuli koposa nthawi yomwe adali moyo.
Tiyeni ifenso titengere phunziro kuchokera kwa Husain (a) pokhala olimbana ndi adani achisilamu kuzipereka, mphamvu, kukonda chipembedzo,kufuna ufulu,kupirira,kulamulira zinthu zabwino ndikuletsa zinthu zoipa ndi kufuna kufera munjira ya Mulungu, ndipo ngati tingathe kukwanitsa kupanga izi titha kunena kuti ife tili limodzi ndi Husain(a).
Akulu akulu omwe adamvetsetsa nkhani imeneyi ya Husain amailongosola mwachikoka ndimopereka chidwi motero nkhani imeneyi idzapitilira mpaka mitundu yobwera mtsogolo adzaipeza.
Mulungu aipange imfa yathu kukhala ngati ya Husain pofera munjira yake ndikukhala yolemekezeka.
Add new comment