University yachisilamu yoyamba ku Malawi
Pofuna kulimbana ndi vuto lakusowekera maphunziro achisilamu, dziko la Malawi likufuna kutsekula University kuti achinyamata achisilamu akhale ndi mwayi okaphunzira maphunziro achisilamu. Polankhula pamsonkhano omwe adakumana akulu akulu a chisilamu, nduna yoyang’anira za paulendo ndi ntchito zapagulu olemekezeka a Sidik Mia adati: tili ndi cholinga chimodzi pofuna kukweza maphunziro adziko lino la Malawi choncho nkhani imeneyi ndiyotheka kudzera mu ulamuliro wabwino.
Iye adati ntchito imeneyi ichitika ndichithandizo chochokera ku bungwe la Direct AID Society laku Kuwait. Monga momwe tikudziwira kuti pali mauniversity angapo omwe akhazikitsidwa muno m’Malawi ndi anzathu achikirisitu monga African Bible College, Livingstonia University omwe ali mmanja mwa Church of Central Africa Presbytery, Seventh Day Adventist University ndi Catholic University. Kuonjezera apa tilinso ndi mauniversity aboma atatu. Kutsekulidwa kwa university imeneyi kudzachepetsa vuto la maphunziro mdziko muno. Ndunayi idalimbikitsa asilamu kuti ayenera kuzindikira kufunikira kothandiza kukwera kwa maphunziro mdziko komanso ndi anthu osowa chithandizo cha maphunziro. Ndunayi idapereka ndalama zokwana k2.5 million zoti amangire mabuloko ena asukulu ya derali ( sub mosque) m’boma la Mangochi. Komanso idapereka ndalama zoti zimangidwire mizikiti pa Mathanjesi mu nzinda omwewu wa Mangochi.
Chisilamu ndi chipembedzo chachiwiri kumwera kwa Africa pambuyo pa Chikirisitu.
Tiyeni asilamu tiikire chidwi pa maphunziro achipembedzo chathu.
Add new comment