Ashura mukuyang’ana kwa Akirisitu

Ashura  mukuyang’ana  kwa  Akirisitu

Talongosola  mmbuyomu  kuti  tikamati  Ashura  timatanthauza tsiku  lomwe  Husain mwana  wa  Ali  chidzukulu  cha  Mtumiki(s.a.a.w)  chidaphedwa.  Nkhaniyi  ndiyoti  mu history  ilipo  ndipo  idakhazikika  angakhale  munthu  wina  atafuna  kuti  aibise  sizingatheke,  koma  mmalo  mwake  tikupeza  kuti  angakhale  akirisitu  adavomereza  za nkhaniyi  kuti  Imam  Husain (a)  adaphedwa  moponderezedwa  pofuna  kuteteza  chisilamu  kuchokera  kwa  anthu  omwe  amafuna  kuthimitsa  kuwala  kwake. Ena  mwa  akirisitu  akulankhula  motere:
1. Charlez Dikenz (Mlembi  otchuka  waku England)  adanena  kuti:  ngati  cholinga  cha  Imam  Husain(a)   pomenyana  ndi  adani  chidali  kufuna  za dziko  lapansi,  chimene  ine  sindikumvetsa  ndichoti  chifukwa  chani  iye  adatenga  azilongo,ana ndi akazi  ake?   Poona  zimenezi nzeru zanga   zikunena  kuti   iye  adapanga  izi  chifukwa  cha  chisilamu  basi.
2.Thomas  Carloil  (Philosopher  ndi  historian  waku England) adati: Chiphunzitso  chomwe  tikuchipeza  muzochitika  zodandaulitsa  za  pa  Karbala  ndi  zoti  Imam  Husain(a)  ndi  anthu  ake  adali  anthu  okhulupirira  Mulungu  ndipo  olimba  pofuna  kuteteza chipembedzo  cha   Mulungu. Zomwe  adapanga  iwo  zidaonetsera  poyera  nkhani  yakusiyana kwa  pakati  pa  chilungamo  ndi  bodza  ndipo  kupambana  kwake  angakhale  kuti  adali  ndi  anthu ochepa  kwandidabwitsa  kwambiri.
3.Edward  Brown (  Orientalist  waku  England)  adati:  kodi  pali  mtima  omwe  ungakhale  osadandaula  ndikumva  kuwawa  pambuyo  pomva nkhani  yomwe  idachitika  ku  Karbala? Angakhale  anthu  omwe  sali  Asilamu  sangathe  kukanira  kuyera  mtima  kwa   munthu(Husain)  yemwe  adamenya  nkhondo ya  chisilamu  imeneyi.
4.Fredrick  James  adati: Phunziro  la  Imam  Husain   komanso  munthu  wina  aliyense  yemwe  angafere  munjira  ya  Mulungu ndiloti  padziko lino  lapansi  pali  zinthu  zamuyaya  zomwe  zilipo  zoti  mkati  mwake  muli  chisoni,chifundo  ndi  chikondi   zomwe   sizingasinthe  choncho  munthu yemwe   angalimbane  ndi gulu  lina  lake  pofuna  kuchinjiriza  chinthu  china  chake  chomwe  ndichamtengo  wapatali  zinthu  zimenezi   zimatsalira padziko  lino  lapansi. 
5.Washington  Irewing (Historian  otchuka  waku America)  akuti:  Kudali  kotheka  kuti  Imam  Husain(a)  apulumutse  moyo  wake  pogonjera  zofuna  za  Yazid,  koma  chifukwa  cha  udindo  wa tsogoleri  ndi  chiphunzitso  cha  chisilamu  pa nkhani ya kulimbana  ndi  anthu  oukira  icho (Jihad)  sizidapereke  mwai  kwa  Imam  Husain(a)  kuti  amuvomere  Yazid  kuti  ndi mtsogoleri  wa Asilamu (Khalifah)  koma kuti  iye  adalolera  mavuto  ndi  mazunzo  onse  mmalo  mosiya  chisilamu  mmanja  mwa  mabani  umayyah.  Tiyenera  kudziwa  kuti  mzimu wa  Husain  udakalipo  pansi  pa  dzuwa  lowotcha  ndi malo  ouma (karbala). Kusonyeza  kuti  zotsatira  za  nkhondo  imeneyi  ndikupambana  kwa  Imam  Husain  yemwe  anthu  ma million   lero  lino amakhala  akumukumbukira  angakhale  omwe  sali Asilamu  pongoona  kuyera  kwa  cholinga  chake.
6.Thomas  Mosoric adati:  Angakhale  kuti  akulu akulu  ansembe   amasintha  mitima  ya  anthu  kufika  podandaula  kwambiri   potchula  mavuto  okhudza  Issah(a)  koma  kudabwitsa  ndikuzinzwa  kwa  zomwe  Husain  ndi  asikali  ake  adachita   sikungapezeke  mu mavuto  a  Issah  ndipo   mavuto  a Issah   ali  ngati  kamwala  kakang’ono  komwe  kaima  molingana  ndi phiri  lalikulu.
7. Morris  Dukbary adati:  malo  omwe  amasonkhana  ndikumakumbukira  mavuto  a Husain  amanena kuti  Husain  adalimbana  ndi  Yazid  posavomera  zofuna  zake   ndicholinga  chofuna  kuteteza   kulemekezeka,  ulemu   wa  anthu  ndi chipembedzo  cha  chisilamu. Choncho adalolera  kuti  chuma  chake, moyo  wake  ndi  ana  ake  zionongedwe  bola  ateteze  zinthuzi.  Tatiyeni   ifenso  tigwiritse  ntchito  njira  ya Husain  imeneyi  polimbana  ndi  anthu  opondereza  chifukwa choti  imfa  yolemekezeka  ili  bwino  kuposa  imfa  yonyozeka.
8. Marbin( odziwa  nkhani  zapa  middle  east waku Germany)  adati:  Zomwe  adachita  Husain  popereka  anthu  okondedwa  ake  adatsimikizira  za  kuponderezedwa  kwake  komanso  uchowona  wake.  Iye  adaphunzitsa  dziko lonse  lapansi  nkhani  yakuzipereka  ndipo adakhazikitsa  chisilamu  ndikufalitsa  dzina  lake  ndi  Asilamu. Msilikali  olungamayu  adauza  dziko  lapansi  kuti   kupondereza  kulibe  nthawi  yotalika  ayi   angakhale  kuti  kuoneke  ngati  kuli  ndi  mphamvu  koma  kumauluka  ndiphepo  mosakhalitsa.
9. George  Jurdock ( munthu  ophunzira  chilankhulo)  akuti:  Yazid   atawauza  anthu  ndikuwalimbikitsa  kuti  aphe  Husain, iwo  adali  kumufunsa  kuti  mutipatsa  ndalama  zochuluka  bwanji? Koma  asilikali  a Husain  adali  kunena kwa  iye  kuti  ife  tili  nawe  angakhale  tiphedwe  kokwana  kakhumi  ndi kasanu  ndi  kawiri (70)  tikhalabe  mu gulu  lako  mpaka  timenye  nkhondo  ndikuphedwa. Kodi  kusiyana kumeneku  kukuchokera  pati?
10. Anttony  Bara  adati:  adakakhala   Husain(a)  wa ife (mkirisitu)  tidakaika  malo ena  alionse  mbendera  yake ndipo  mmudzi  wina  ulionse tidakakhazikitsa   tchalitchi  ndikumaitanira  anthu  mudzina  lake.
M’bale  olemekezeka  awa  ndi akirisitu  omwe  atha  kuona  ndikuzindikira  choonadi  chenicheni  cha nkhani  ya  Imam Husain(a)  yomwe  idachitika  pa  Karbala, tsono  iwe m’bale  amene  uli  msilamu  ukukanika  bwanji  kuimvetsetsa  nkhaniyi?

Add new comment