Ziyaratu Ashura 2
Ziyaratu Ashura 2
Pali anthu ena amanena kuti palibe kufunikira kofufuza nkhani yomwe idachitikira kale ndipo idatha, kulankhula kotero ndikosavomerezeka chifukwa chonena kuti angakhale anthu opanda chipembedzo amakhala akusunga ndikumakumbukira zinthu zakale kusonyeza kufunikira kwa izo, tsono ife Asilamu tisakumbukire bwanji mavuto omwe adatigwera muchipembedzomu.
Anthu amaganizo amenewa ndiye kuti amatsutsananso ndi Ziyaratu Ashura imeneyi, koma anthu oterewa Mulungu akuwatenga kuti ndi okanira pomwe akunena kuti:
((يا أيّها الذين أمنوا لا تتولّوا قوماً غضب الله عليهم قد يئسوا من الآخرة كما يئس الكفّار من اصحاب القبور))
((E! inu anthu amene mwakhulupirira, musawatenge anthu omwe Mulungu adawakwiira kukhala anzanu chifukwa anthu amenewa adataya mtima za nkhani ya tsiku lomaliza chifukwa cha ntchito zawo zoipa monga momwe adataira mtima anthu okanira omwe adaikidwa mmanda)).
Pachifukwa choti anthuwa ali okanira za Mulungu ndiye Mulungu akuwachotsa mu gulu la anthu ake okondedwa mukulankhula kwake mu Quran kuti:
(( و لا تصلّ على احد منهم مات ابداً ولا تقم على قبره انهم كفروا بالله و رسوله و ماتوا وهم فاسقون ))
)) Usawapemphere iwo akafa ndipo usaime pa manda awo chifukwa choti adakanira Mulungu ndi Mtumiki wake mpaka adamwalira adakali anthu owononga)).
Abale olemekezeka Ziyarat imeneyi imamupangitsa munthu kuti athe kumuzindikira Imam wake monga momwe zilili zofunikira kutero chifukwa Mulungu adasonkhanitsa zinthu zonse zomwe zikukhudzana ndi umoyo wa munthu pambuyo pa Mtumiki(s.a.a.w) kwa Imam monga momwe akunenera kuti:
((وكلّ شيء احصيناه فى امام مبين )) (( Zinthu zonse tazisonkhanitsa mwa Imam wachionekere)). Apa akufuna kutiunikira kuti Msilamu wina aliyense ayenera kukhala ndi Imam (tsogoleri) wa nthawi yake yemwe akhale akuthetsa mavuto ake.
Idalandiridwa nkhani mu bukhu la Uyun ndi Amali Swaduq kuchokera kwa Rayan Shabib , iye adanena kuti : tsiku loyamba la mwezi wa Muharram ndidapita kwa Imam Ridtha (a), Imamuyu adati kwa ine: kodi iwe mwana wa Shabib ukusala? Ndidati ayi, kenako Imam adayamba kulongosola nkhani ya mwezi umenewu wa Muharram ndi mavuto omwe adagwa mumweziwu omwe ndi kuphedwa kwa Imam Husain (a), mukulankhula kwake adali kunena kuti: e! iwe mwana wa Shabib, mwezi uno wa Muharram ndimwezi omwe anthu anthawi ya umbuli adali kuletsa kupondereza ndi kumenya nkhondo chifukwa cha kulemekezeka kwake koma gulu la asilamu ili silidathe kuzindikira ulemelero wa mweziwu ndi ulemeleronso wa Mtumiki (s.a.a.w) motero iwo adapha chidzukulu cha Mtumikiyu mmwezi umenewu wa Muharram, kuzunza ndikuvutitsa azimayi omwe adali nawo ndipo adatenga chuma chawo, Mulungu sadzawakhululukira iwo angakhale pang’ono.
E! iwe mwana wa Shabib ukafunira kulira chifukwa cha chinthu china chake uyenera kumulilira Imam Husain (a) chifukwa adamupha ngati momwe amaphera nkhosa. Adaphanso amuna okwana 18 (omwe ndi abale ake) omwe adalibe ofanana nawo.
Nthawi yomwe anthuwa amaphedwa kumwamba ndi pansi pano padali kuwalilira, angelo okwana zikhwi zinayi adatumizidwa kudzaikira umboni za kuphedwa kwawo ndipo atafika adawapeza kuti ndithu aphedwadi, pachifukwachi iwo adalamulidwa kuti aime pa manda a Imam Husain adakali ndifumbi mpaka tsiku lomaliza ndipo iwo adzakhala omuthandiza iye ndikumalankhula mau oti “ya latharatil Husain”.
E! mwana wa Shabib, bambo anga adanena mau omwe adawamva kwa bambo awo nawonso adamva kwa agogo awo kuti: Agogo anga Husain (a) ataphedwa kumwamba ndi dothi zidasanduka zofiira , e! mwana wa Shabib ngati ungalire kumulilira Husain mpaka misonzi kutsikira mmasaya ako dziwa kuti machimo onse omwe udawapanga akulu kapena ang’ono ambiri kapena ochepa adzakhululukidwa.
E! mwana wa Shabib, ngati ukufuna kuti udzakumane ndi Mulungu ulibe machimo uyenera kumuyendera Imam Husain (a) pa manda ake, e! mwana wa Shabib, ngati ukufuna kuti udzakhale limodzi mu nyumba yomwe Mtumiki adzakhale utemberere anthu omwe adapha Husain(a).
E! mwana wa Shabib, ngati ukufuna kuti udzapeze zabwino mofanana ndi momwe adapezera anthu omwe adaphedwa limodzi ndi Husain(a), uyenera kunena mau awa ((ya laitani kuntu mahumu fa afuzu fauzani a dthima))
((يا ليتني كنت معهم فافوز فوزاً عظيماً))(( kalanga ine! ndidakakhala limodzi nawo bwezi nditapambana kwakukulu))
E! mwana wa Shabib, ngati ukufuna kuti udzakhale nafe pamalo apamwamba ku mtendere khala odandaula nthawi yomwe ife tili odandaula, khala osangalala nthawi yomwe ife tili osangalala ndipo uyenera kutsatira ife ndikutikonda chifukwa choti munthu angakhale ataukonda mwala adzadzukitsidwa nawo tsiku lomaliza.
Add new comment