Imamah (utsogoleri wa pambuyo pa Mtumiki) mu Quran 2

Imamah (utsogoleri wa pambuyo pa Mtumiki) mu Quran 2

 

Pokhudzana ndi Thawab za Surah imeneyi palinso ma Hadith odabwitsa kwambiri ponena kuti:
Munthu amene angawerenge Surayi mokweza, zili ngati munthu amene watenga lupanga ndipo akumenya nkhondo munjira ya Mulungu. Kodi imeneyi ndi nkhondo yake iti? Inu kunkhondo ya Mulungu m’makhala mukuwayitanira anthu kwa Mulungu. Ndiye kuti apa muwayitanira anthu kwa Mulungu ndi Surat Qadr. Muwayitanira anthu ku chimbedzo chowona komanso njira yachilungamo.
Kodi mu Surayi mwagona chiyani? Tilongosola zimenezo.
Akuti ngati mungawerenge Surayi motsitsa ndikudziwa zomwe ikunena, zili ngati kuti ukuzigudubuza m’magazi ako omwe munkhondo yomwe ukumenyayo. Kwa munthu owerengayo akuti zikukhala ngati kuti machimo ake akukhululukidwa. Chifukwa chiyani?
Inu mukudziwa kuti imodzi mwa mayina omwe Mulungu alinawo ndi:
یا مبدل السیئات بالحسنات
“Ee iwe Mulungu amene umasinthanitsa zoipa ndi zabwino”.
Kutanthauza kuti ngati munthu walakwa akapanga Tawbah umasinthanitsa choyipacho poyika chabwino.
Mu Hadith ina zidanenedwa pokhudzana ndi munthu amene angawerenge Surayi kuti: Machimo ako akhululukidwa ndipo yambiranso kupanga ntchito zako ndipo adzapulumutsidwa kuchokera ku zoipa.
Pankhani yoti iye adzapulumutsidwa kuchokera ku zoipa, mudziko lino lapansi chinthu choyipa kwambiri chomwe chingathe kumupeza munthu ndiko kusochera ndi kusemphana ndi njira yachilungamo ndinso kukumana ndi Shirk.
Chifukwa chakuti:
الدنیا دار بالبلاء محفوفة
“Dziko ndi nyumba yomwe yasakanizidwa ndi zipsyinjo”.
Akamati utetezedwa kuchokera ku zoipa ndiye kuti chiyani? Kutanthauza kuti tikhala otetezedwa kukalowa ku moto wa Jahannama.
Zowonadi munthu yemwe angawerenge Sura imeneyi adzatetezedwa ku zoipa pachinthu china chirichonse, chuma chake, banja lake ndi zina zotero.
Koma tsopano matanthauzo a Sura imeneyi.
Quran ikutsika mu usiki wa Qadr. Quran koyamba idatsika kwa Mtumiki wathu Muhammad (S.A.A.W) kamodzi ndi kamodzi kenako idayamba kumutsikira pang’ono pang’ono.
Quran ikuti:
إنا أنزلناه فی لیلة القدر
Apa tatiyeni tiwoneko matanthauzo a mawu.
Mawu oti: أنزل (Anzala) ndi mawu oti: نزل (Nazzala) ndi osiyana matanthauzo. Quran malo ena idagwiritsa ntchito mawo oti نزل (Nazzala) ndipo malo ena idagwiritsa ntchito mawu oti أنزل (Anzala).
Mawu oti Anzala akutanthauza kuti kutsika kwa Quran yonse kamodzi (Daf’iy) pomwe mawu oti Nazzala ndiye kuti kutsika pang’ono pang’ono (Tadrijiy).
Koma kuti ndichifukwa chiyani adawutcha usikuwu kuti usiku wa Qadr? Zidanenedwa kuti chifukwa chakuti usiku umenewu ndi usiku omwe zinthu zonse za dziko lapansi zimagawidwa komanso zimayesedwa ndi kuyikidwa mu mlingo wake.
Usiku wa Qadr ndi usiku omwe angelo akutsika ndipo dziko lapansi limadzadza ndi angelo.
لیلة القدر خیر من ألف شهر
Pokhudzana ndi ayayi kuti usikuwu ndi wabwino kuposa miyezi 1000, zinanenedwa mu Hadith kuti Mtumiki tsiku lina atagona adalota kuti kutsogolo kudzachitika zotani mu Chisilamu.
Ulamuliro opondereza wa Bani Umayyah udakwana miyezi 1000 ndipo iwo adawononga chisilamu m’miyezi imeneyi. Zinthu zoipitsitsa zomwe adapanga mudzina la Chisilamu. Adapha chidzukulu cha Mtumiki, bwana wa anyamata ku Jannah. Adalamula m’modzi mwa atsogoleri ankhondo ochokera mu ulamuliro umenewu panthawi yomwe adakapha anthu ambiri ku dziko la Iran pomwe adanena kuti:
Muwaphe anthu aku Iran kufikira kuti magazi ayendelere m’mitsinje ndipo magaziwo mukandire ufa ndikuphikira buledi, ndipo zimenezi zidachitikadi mudera la Gorgan kumpoto kwa dziko la Iran.
Adapanga zimenezi mudzina la chisilamu. Kodi ife apa tingayankhepo chiyani pa zomwe zidachitikazi? Palibe chomwe tingayankhe.
Mtumiki adalota kuti mbuzi zitakwera pa mwimbali pake ndipo Mtumiki adadandaula kwambiri chifukwa cha zimenezi. Mulungu pofuna kumusangalatsa Mtumiki posinthanitsa ndi madandaulo amenewa adati:
Ine ndi zakupatsa iwe usiku wa Qadr omwe ukadzapanga ntchito mu usiku umenewu, udzakhala opambana kuposa miyezi 1000.
Angelo amatsika usiku umenewu, kwina ndi cholinga chotsitsa Quran kwinanso chifukwa chakuti muchilengedwe cha ine ndi inu muli zinthu zomwe tingazikwanitse kuzipanga, mwachoncho zinthu zomwe ife tingazikwanitse kupanga, Mulungu amapereka chilolezo mu usiku umenewu kuti tipange.
Kodi tikamati mukulengedwa kwa wina aliyense muli kutheka koti atha kupanga zinthu zina ndipo sangapange zopitilira pamenepo, tikutanthauza chiyani?
Tikufuna kutanthauza kuti ngati Mulungu adachilenga chinthu china mukakhalidwe ka nyani, sizingatheke, mukupezeka kwake chiyenera kukwanitsa kungopanga zinthu zomwe nyani amapanga ndipo ngakhale ndi pang’ono pomwe nyani alibe chisankho komanso chifuniro komanso sizingatheke kumusintha kuti akhale munthu ophunzira. Mwachoncho mu usikuwu samachipatsa chilolezo choti chikhale ophunzira chifukwa chakuti muchilengedwe chake mulibe kutheka kumeneko.
 Koma mwa munthu yemwe akuphunzira muli chifuniro komanso kutheka koti atha kukhala ophunzira kapenanso atha kukhala osaphunzira chifukwa kutheka kwa zinthu ziwirizi mwa iye kulipo komanso chifuniro ndi chisankho. Mwachoncho mu usiku umenewu ndimomwe mumaperekedwa chilolezo kuti iwe upita mbali iti potengera chifuniro chomwe munthuyo ali nacho.
Mwachoncho kwa munthu wina aliyense zimalembedwa mu usikuwu kuti apite mbali iti? Nanga apange chiyani muchakamo.
Pali Hadith ina yomwe idanena kuti: Munthu amene angakanire ndi kutsutsa zomwe Surayi ikunena ziri chimodzi modzi kuti wakanira za Ahalbait (A.S).
Funso lomwe limakhala likufunsidwa mu Surah imeneyi ndi ili:
Angelo ndi Ruh omwe akufuna kuti ayende ulendo ofunikira umenewu kuchoka kumwamba kupita padziko lapansi, kodi amamutsikira ndani?
Tikawona tikupeza kuti mawu oti تنزل akulozera za chochitika chomwe chimakhala chikuchitika mopitilira, kutanthauza kuti kutsikaku kudakalipobe ndipo kumachitika chaka ndi chaka.
Kutsika kwa angelo kulipobe, kutsika kwa Quran kulipobe ndipo usiku wa Qadr ulipo chaka china chirichonse. Koma funso apa ndi loti kodi angelo ndi Ruh amamutsikira ndani?
Zikunenedwa kuti Ruh ndi mngelo wamkulu kuposa angelo ena onse mwachoncho ndi chifukwa chake wasiyanitsidwa ndi angelo mu Surayi pogwiritsa ntchito mawu oti Ruh.
Angelo amene adali kuwatsikira aneneri ochepa kwambiri ndipo ena mwa atumiki ankangomva mawu okha basi.
Ndiye angelo onse akutsika padziko la pansi mu usiku umenewu koma akumutsikira ndani? Nanga akutsika chifukwa chiyani ndipo akumutsitsira ndani Quraniyi?
Apa ndipomwe tikuwona kuti munthu amene ali otsatira Ahalbait (A.S) akumva komanso akuzindikira kuti pali cholengedwa china chake chomwe chili cha pamwamba kuposa angelo kufikira kuti akumutsikira iye.
Zowonadi ife chikhulupiliro chathu ndi chakuti angelo amamutsikira Imam yemwe padakali pano ndi Imam Mahdi (A.F) ndipo ma Ayanso ndi ma Hadith alipo omwe amalongosola zokhudzana ndi Imam ameneyu.
Angero akutsika.
Akutsikira chifukwa chiyani? من کل أمر pokhudzana ndi china chirichonse chomwe chidzachitika muchakacho.
Nanga akumutsikira ndani? Yankho lake likupezeka mu Surat Yasin kuti و کل شیئ أحصیناه فی إمام مبین ndipo china chirichonse tidachisunga mwa Imam owonekera poyera. Mwachoncho angelo akumutsikira munthu yemwe ali ndi kuzindikira pachina chirichonse muchifuniro cha Mulungu.
Mwachoncho Imam wathu ndi Imam amene amazindikira chinthu china chirichonse. Imam wathu ndi amene angelo amamutsikira.
Amawona chinachirichonse chomwe ife tingapange munthawi yomweyo.
و قل اعملوا فسیری الله عملکم و رسوله و المؤمنون
 Fundo ina ndi yakuti Wahay ulipo mpakana tsiku la Qiyama ndipo Quran mpakana tsiku la Qiyama ikutsikabe. Funso ndi loti kodi Ahalbait (A.S) umatsikira Wahay? Ee umatsikira. Wahay unkawatsikira mayi a Musa (A.S) komanso mayi a Mtumiki Isa (A.S) ndiye usawatsikire bwanji anthu osankhidwa ndi Mulungu omwe ali akunyumba ya Mtumiki? Kodi Wahay usamutsikire bwanji Khalifa wa Mulungu?
Mu Hadith ina m’modzi mwa atsogoleri athu (Imam) adafunsidwa kuti kodi usiku wa Qadr m’mawudziwa? Adayankha kuti: Ee tisawudziwe bwanji kumachita kuti angelo amatitsikira ife.
Chauta akudalitseni.

Add new comment