Kugwiliridwa kwa mwana wa zaka zisanu ndi shaikh (mufut) wa chiwahabi wa ku Saud
Kugwiliridwa kwa mwana wa zaka zisanu ndi shaikh (mufut) wa chiwahabi wa ku Saud
Mkulu wina yemwe amazitenga kuti ndi munthu ophunzira chipembedzo cha chisilamu wa chiwahabi dzina lake Faihan Alghamidi walamulidwa kuti akwapulidwe zikwapu zokwana mazana asanu ndi atatu (800) ndikukakhala kundende zaka zisanu ndi zitatu chifukwa chopezeka olakwa pa mlandu ogwilirira mwana wamkazi wazaka zisanu mdziko la Saud Arabia.
Mu kulankhula kwa Tv Shia nkhani ikuti mkuluyu kuonjezera pa chilango chomwe walandira wauzidwanso kuti alipire ndalama zokwana 1 million Rial Saudi kukhala ngati chindapusa, ndalama zomwe zikukwanira 270 Dollars. Pali chiyembekezo choti ndalamazi ziperekedwa kwa mai amwanayu yemwe ndi mkazi wake wakale.
Mai wa mwanayu akufuna kuti mkuluyu ayenera kupereka ndalama zina zokwana 10 million Rial Saud chifukwa cha imfa ya mwanayu. Mkazi wachiwiri wamkuluyu yemwe naye akuzengedwa mlandu othandizira mwamuna wake pankhaniyi walamulidwa kuti akwapulidwe zikwapu zokwana 150 ndikukakhala kundende zaka zokwana khumi.
Dzina la mwanayu lidali Lami yemwe adali mwana wake mkuluyu ( kusonyeza kuti chitsiru cha bambo ngati ichi chidagona ndikugwilirira mwana wake) yemwe pa 25 December 2011 adamutengera kuchipatala atavulazidwa kwambiri pa nthawi yomwe mkuluyu amamugwilirira, kenako mukudutsa kwa miyezi ingapo mwanayu adamwalira.
Tiyeni azibambo tikhale achisoni kwa ana athu.
Add new comment