Kuponderezedwa kwa Fatimah Al-zahra(a.s)

Bismillahi rahmani rahim

Kuponderezedwa kwa Fatimah Al-zahra(a.s)

Choyamba tikupepesa kwa onse chifukwa cha kuphedwa kwa mwana wa mkazi oyera wa Mtumiki wachisilamu yemwe ali Fatimatu al-zahra (a.s).

Chifukwa cha nkhani yodandaulitsa imeneyi, tikupepesanso kwambiri kwa mtima owala mudziko lolengedwali yemwe ali kuwala kwa khumi ndi ziwiri (10) pa utsogoleri wa uMulungu (Imamat), olemekezeka Imam Mahdiy Mulungu afulumizitse kubwera kwake.

Tiri ndi chikhulupiliro kuti zinthu zopangitsa kuti kuwonekera kwake kolemekezeka kuchitike mofulumira zipezeke mpakana kuti anthu adzapulumuke ndi chiwongoko cha iye osankhidwa ndi Mulunguyo.

Munthawi yomwe idadutsa kuchokera pomwe Mtumiki wachisilamu (s.a.a.w) adamwalira (adaphedwa) kufikira kuphedwa kwa mwana wake wamkazi (Fatimatu al-zahra), muchipembedzo mudachitika zinthu zikuluzikulu zofunika kwambiri ndipo zowona zake, zinthu ngati zimenezo ndi zofunika kwambiri pofuna kudziwa chilungamo chenicheni ndi bodza kwa munthu yemwe ali ofuna chilungamo.

Nkhani yokhudzana ndi zovuta zomwe adakumana nazo olemekezeka Zahra (mtendere ndi madalitso a Mulungu akhale kwa iye) pambuyo pa kumwalira (kuphedwa) kwa Mtumiki wa chisilamu (s.a.a.w), zowona zake ndi imodzi mwankhani zikuluzikulu muchipembedzo cha chisilamu.

Kuwadziwa magulu asanu (5) achisilamu kuti ndi gulu liti lomwe liri pa chilungamo ndipo ndi liti liri kunja kwa chisilamu, kungachitikenso kudutsira mukufufuza ndi mukuyang’ana umoyo wa olemekezeka Zahra (a.s) pambuyo pa kumwalira (kuphedwa) kwa bambo ake yemwe ali Mtumiki wachisilamu (s.a.a.w).

Kupitilira apo, pambuyo poti munthu wapeza njira ya chilungamo, uko ndiko kumakhala chiyambi cha kuyenda munjira ya chilungamo mpakana kukafika pa kukwana kweni kweni (chisangalalo chosatha pa tsiku lomaliza). Chonchonso olemekezeka Zahra (a.s) ali ndi gawo lalikulu pofuna kumuthandiza munthu kudziwa njira yachilungamoyi.

Mwachoncho ndikoyenera kuti tikumbutsane izi, kuti ife sitiripano ndi cholinga choti tingolongosola kuti chilungamo ndi chiti nanga bodza ndi liti. Koma kuti pambuyo popeza njira ya chilungamo pakhale chiyambi chokwera ndi kutsata njira yokwana ndi yapamwambayi.

Nkhani yokhudzana ndi olemekezeka Fatimatu al-Zahra (a.s) sikungodziwa chilungamo kuchokera ku bodza ayi, koma pambuyo podziwa za iye palinso kukwera kupita kudziko lokwera ndi kudziwandikitsa kwa Mulungu.

Ngati nditafuna kulongosola kwa chidule ndi nganene kuti:

Ulemelero wa olemekezeka Zahra (a.s) ndi wawukulu kwambiri kudutsira muzomwe zidanenedwa muchisilamu kuchokera kwa asilamu omwe ali a Shia komanso osakhala a Shia kuti:

Mulungu amakwiya chifukwa cha kukwiya kwa Fatimatu al-Zahra (a.s) ndipo amasangalala chifukwa cha kusangalala kwa iye (mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale kwa iye). Zomwe zikutsimikizira ulemelero ndi mbiri ya kusachimwa (Ismah) kwa iye.

Ndipo zikutsimikizira nkhani imeneyi ndi Ayah ya Tat’hiir ndi zomwe zidapangitsa kuti ayayi itsike polongosola ulemelero wa anthu osachimwa akunyumba ya mtumiki ndi kuyeretsedwa kwa Fatimatu al-Zahra (a.s).

Pankhani yokhudzana ndi ulemelero wa Olemekezeka Fatimatu al-Zahra (a.s), ma Ulama akuluakulu omasulira bukhu la Qur’an adatchulapo kuti pali ma Aya opitilira 200 okhudza iye. Koma mu Aya ya chikondi (Mawaddat), Mulungu adakakamiza msilamu wina aliyense kuti ngati akufuna kulipira pantchito yomwe mtumiki (s.a.a.w) adapanga (powawongola iwo kunjira ya chilungamo), ayenera kuwakonda anthu akunyumba ya Mtumiki (s.a.a.w) pomwe Qur’an ikunena kuti:

قل لا اسئلکم علیه اجرا الا المودة فی القربی[1]

Ndithudi Mayi olemekezeka ameneyu adali akulemezedwa ndi mtumiki wa chisilamu (s.a.a.w) kwambiri kufikira kuti Mtumiki (s.a.a.w) adamupatsa dzina loti (Ummu Abiiha).

Apa tikumbukirenso izi kuti mtumiki Muhammad (s.a.a.w) samalankhula zinthu zopanda pake ayi ndipo Qur’an potsimikizira ikunena kuti:

و ما ینطق عن الهوی ان هو الا وحی یوحی

kodi dzina loti Ummu Abiiha likutanthauza kuti chiyani?

Kodi zikutanthauza kuti Fatimatu al-Zahra (a.s) amamukonda kwambiri bwanji mtumiki, chikondi chomwe mayi amakhala nacho kwa mwana  ndicho chikondi chomwe olemekezekayu adali nacho kwa bambo ake.

Kapena kutanthauza kuti ngati momwe zimakhalira kuti ngati mayi sapezeka ndiye kuti mwana sangapezeke, kuti padakapanda Zahra (s.a) ndiye kuti dzina la mtumiki (s.a.a.w) silidakapezeka chifukwa choti akamberembere adakatha kuyesetsa kufafaniza dzina lake ndi kuthetsa chisilamu.

Kapenanso zikutanthauza kuti zinthu zonse zidalengedwa ndi cholinga choti zizimugwilira ntchito munthu ndipo munthu adalengedwa ndi cholinga choti kudutsira mukupembedza azamudziwe Mulungu ndipo kupembedza sikungatheke pokhapakha Malamulo a chisilamu atagwira ntchito ndi kuti tikhale ndi chikhulupiliro cha chisilamu ndipo ngati padakapanda Zahra (a.s) ndiye kuti chisilamu chidakatha ndipo sichikadafika kwa ife.

Ntchito zonse za anthu akunyumba ya Mtumiki (s.a.a.w) omwe ali osachimwa komanso oyera komanso omwe ali atsogoleri 11 ndi alowa m’malo a mtumiki wa chisilamu, zidali zikuchitika chifukwa cha kupezeka kwa Fatimatu al-Zahra (a.s). ngati usiku wa Qadr (Laylatul Qadr) ili nthawi yomwe Qur’an idatsika kupezeka kwa Zahra (a.s) mwaiyeyonso ndi momwe muli kutheka kuti ma Qur’an 11(ma Imam)olankhula atsike.

Chifukwa choti olemekezeka Zahra (a.s.) adali osunga chipembedzo, chonchonso ngati momwe adalili iye potsatila ndondomeko ya Mulungu polimbana ndi ulamulilo opondereza pambuyo pa Mtumiki wachisilamu, adamuwonetsera njira munthu ofuna chilungamo ndipo kudutsira mukuteteza kwake iye Fatima (a.s) pomuteteza Ali (a.s) adachiwonetsera poyera chisilamu choncho Mulungu amasangalala nacho kuchokera ku chisilamu chomwe samasangalala nacho. Ndipo iye adachisunga chisilamu kudutsira mukupeleka atsogoleri oyera okwana khumi ndi m’modzi omwe akupanga njira ya Imamah komwe omwe akupitiliza njira ya atumiki aMulungu.

Kapena kuti Mawu Ummu Abiiha ali ndi matanthauzo ena omwe Mulungu amatha kuwawonetsera anthu akuluakulu komanso omuwopa Mulungu.

Chabwino, ngati Mtumiki wa chisilamu adamupatsa Fatima al-Zahra (a.s) dzina loti Ummu Abiiha, ndiye udindo wa asilamu ndi otani kwa iye (kodi asilamu adzamupangira zotani?

Mawu amalonje oyamba amenewa ndithudi angakhale ovomerezedwa ndi asilamu onse.

Mawu oyambawo muwalumikize ndi mawu achiwiri, ndipo panthawi imeneyi mudzawona kuti kodi olemekezeka Fatimatu al-Zahra (a.s) adali ndi ntchito yaikulu bwanji pofuna kupeza njira yachilungamo kuchokera kunjira ya bodza.

Ndi kiyi kwa msilamu wina aliyense ndi cholinga choti munthu apeze zotsatira mofulumira, afufuze ndi kuwerenga mbiri ya umoyo wa Zahra (a.s) kuchokera pambuyo pomwalira Mtumiki (s.a.a.w) kufikira kuphedwa kwa Fatimatu al-Zahra (s.a).

Ndikoyeneranso kudziwa izi kuti anthu omwe siali otsatira njira yachilungamo, nthawi zonse amatsutsa kapena kukanira komanso kusokoneza kumene zomwe zidachitika mu mbiri ya umoyo wa Fatimatu al-Zahra (a.s) kuchokera pomwe Mtumiki adamwalira kufikira kuphedwa kwake.

Koma ine kapolo padakali pano ndikufuna ndikulongosolereni kuti nkhani imeneyi ndi imodzi mwa nkhani zikuluzikulu komanso yofunikira. Ndipo ndiri ndi chikhulupiliro kuti nsichi imodzi mwa nsichi zofuna kuzindikira za chipembedzo cha chisilamu. Mwachoncho paliphindu lalikulu kwambiri kwa msilamu wina aliyense kuti afufuze zokhudzana ndi Fatimatu al-Zahra (a.s).

Zomwe Shia akudziwa mu mbiri ya Fatimatu al-Zahra ndi izi;

Olemekezeka Zahra (s.a) adalangidwa ndi kuvutitsidwa ndi Ulamuliro wanthawi imeneyo.

Olemekezeka Zahra (s.a) adali odandaula pa ulamuliro wanthawi imeneyo pambuyo pa mtumiki wachisilamu (s.a.a.w) ndipo adamwalira ali okwiya ndi Khalifa oyamba ndi Wachiwiri (Abubakar ndi Umar).

Mwachoncho Fatimatu al-Zahra ndi cholinga choti nkhani imeneyi ikhale yomuwongola msilamu aliyense, adamuwuza Ali (a.s) kuti adzamuyike m’manda usiku kuti msilamu aliyense yemwe angapite ku mzinda wa Madinah omwe uli mzinda wa Mtumiki wachisilamu  ndi cholinga chokawona manda a anthu osankhika, opatulika komanso abwino a Mulungu azidzifunsa kuti:

Kodi manda  a Fatimatu al- Zahra (a.s) ali kuti?

Kodi ndi ndani adamuyika m’manda?

Ndichifukwa chiyani manda a Fatimatu al-Zahra (a.s) adabisika?

Koma kuti mafunso amenewa ndi mukufufuza za nkhani imeneyi muli chinsisi chosiyanitsa chilungamo ndi bodza.

Tidziwe izi kuti, imodzi mwa zolinga za gulu la Wahabiy mu mizinda ya Makkah ndi Madinah powononga manda akuluakulu a chisilamu komanso mpakana pano akulakalakanso atagumula manda onse, ndicholinga choti akufuna kuti adzafufute mafunso amene tanena aja kuti asadzapezeke m’mutu mwa munthu. Ngati mu mzinda wa Madinah simungakhale manda ena aliwonse ndiye kuti sipadzakhalanso funso kwa msilamu aliyense kuti kodi manda a Fatimatu al-Zahra (a.s) mwana wa mtumiki wachisilamu ali kuti?

Ndipo adayesetsa kuyamba kufafaniza manda ndi m’mene adathera kuti pasapezekenso manda kuti funsoli lichokeretu.

Ine pankhani imeneyi sindikufuna kuti ndibweretse ma Umboni akuphedwa ndi kunyozedwa kwa Mtumiki wa chisilamu kuchokera mu mabukhu a Shia ayi. Koma ndikufuna ndikulongosolereni inu akuluakulu Duwa iyi mwachidule ndi cholinga choti ofufuza njira ya chilungamo  apitilize kutero ndikuti apeze njira yachiwongoko mwachilungamo, chifukwa choti pali akuluakulu ambiri omwe adalemba mabukhu ambiri pofuna kutsimikizira za madandaulo ndi mavuto omwe adamufikira olemekezeka Zahra (a.s).

Komanso ndi kukumbutsaninso izi kuti mkwiyo kwa Fatimatu al-Zahra (a.s) zimafanana ndi mkwiyo wa Mulungu ndipo mkwiyo wa Mulungu uli ndi moto wa Gahena.

Chinthu chomwe chimatsimikizidwa mophweka kuchokera mu mabukhu omwe siali a Shia ndi cholinga chopeza njira yachilungamo kuchokera kubodza ndi ichi;

Fatimatu al-Zahra (a.s) adawopsezedwa ndi Khalifah wachiwiri (Umar ibn Khattab) zakuti adzawotcha nyumba yake.

Olemekezeka Zahra (s.a) adamwalira atakwiyitsidwa ndi Khalifah oyamba ndi wachiwiri.

Khalifah oyamba adavomereza kumapeto kwa umoyo wake kuti nyumba ya Olemekezeka Zahra (s.a) idanyozedwa ndi kupangidwa chipongwe.

Olemekezeka Zahra (s.a) adamuwuza Ali (a.s) kuti adzamuyike m’manda nthawi ya usiku ndipo onse omwe adamuvutitsa iye asadzakhalepo panthawi yokamuyika iye m’manda.

Khalifa oyamba ndi wachiwiri adamulanda Fatimatu al-Zahra munda omwe umatchedwa kuti Fadak ndipo Olemekezeka Zahra (s.a) adali okwiyanso kwambiri ndi zimenezi.

Adamenyedwa mambama Olemekezeka Zahra (s.a) ndi kulandira mavuto ambiri kuchokera kwa anthu antchito omwe adatumizidwa ndi ulamuliro wanthawiyo kuti akawononge nyumba ya olemekezekayo. Panthawi imeneyi nkuti Fatimatu al-Zahra (a.s) ali ndi pakati ndipo zomwe zidachitikazo kwa iye zidapangitsa kuti mwana wake wakhanda apite padera (mtayo) yemwe amatchedwa kuti Muhsin (mtendere wa Mulungu ukhale kwa iye).

Ngati msilamu aliyense atafufuza mulingo okhawu omwe ife talongosola apa ndi kupezanso zina zofanana ndi zimenezi zomwe ife sitinazitchule, adzapeza njira yachilungamo mosavuta ndipo zokhazi zikukwanira pofuna kudziwa chilungamo. Kutanthauza kuti sipakufunikiranso kuchita kufufuza kwambiri kuposera pamenepa.

Koma kuti pali nkhani zambiri kuposera pamenepa.

Komanso kwa munthu yemwe pang’ono pomwe alikale munjira ya chilungamo ndinso adayamba kale kugwiritsa ntchito bwino nyali yowala zomwe zili nzeru zake, kwa iye njira yachilungamo idzakhala yowonekera komanso yowala kwambiri ndipo adzayenda munjira imeneyi.

Chitsanzo chake chingakhale ngati galimoto yomwe ikufuna kuyenda mtunda wautali ndipo magetsi ake akungowalitsa pang’ono nsewu. Nthawi yomwe galimotoli likudutsa njira yomwe yawalitsidwa ija, mbali inanso ya njira pang’ono ndi pang’ono imawalitsidwa ndipo zikhala choncho mpakana kukafika. Koma ngati galimoto ija singayende munjira yomwe yawalitsidwako pang’ono ndiye kuti olo ndi pang’ono pomwe sidzasuntha kupita patsogolo.

Njira yachilungamo ilinso choncho. Ngati mwavomereza mulingo ochepa pa chilungamo ndiye kuti zina zonse zakhala pachilungamo kwa inu zizadziwika ndikukhala zowala mosavuta. Koma ngati simungataketake, ndikukhala ndi tsankho kapena osakhala ndi chidwi pofufuza njira ya chilungamo, olo ndi pang’ono pomwe palibe chomwe chidzawonekera kwa inu kuchokera muchilungamo. Zingakhale ngati galimoto yomwe magetsi ake ali chiwalire koma sikuyenda. Mwachoncho kukhala kwa magetsi owala palibe phindu lina lililonse kugalimotoyi.

Mwachoncho mbiri ya umoyo wa Olemekezeka Zahra (s.a) ikumufikitsa msilamu wina aliyense ofufuza chilungamo ku njira ya chiwongoko.

Zikomo kwambiri, nthawi zonse muzikhala anthu opambana. 

 




[1] Suratu al-Shura/23

Add new comment