Imam Husain (a) adanena kuti:
4- قال عليه السلام :
إنّ قوماً عبدوا الله رغبةً فتلك عبادة التجار، و إنّ قوماً عبدوا الله رهبةً فتلك عباد العبيد، و إنّ قوماً عبدوا الله شكراً فتلك عبادة الاحرار وهي أفضل العبادة.
Imam Husain (a) adanena kuti: Ndithudi pali gulu lina limapembedza Mulungu chifukwa chofuna zinthu zina kuchokera kwa iye, mwachoncho kupembedza koteroku ndi kwa Malonda, palinso gulu lina lomwe limapembedza Mulungu chifukwa chomuopa iye, kupembedza koteroku ndi kwa kapolo, pomwe gulu lina limapembedza Mulungu chifukwa chofuna kumuthokoza ndikumuyamika chifukwa cha zomwe adamupatsa kapolo wake, kupembedza koteroku ndi kwa afulu komwenso ndikupembedza kwa pamwamba ndikwabwino kuponsa mitundu ina yonse yakupembedza.
Muhadithiyi tamva mitundu yakupembedza yomwe akapolo a Mulungu amakhala akupembedza pakati pawo.
Kupembedza koyamba ndikoti munthu amapembedza Mulungu chifukwa choti amalakalaka kukapeza zabwino zomwe Mulungu adamulonjeza kapolo wake monga mtendere, ndipo ku mtendere kumeneku kuli zabwino zambiri zomwe amene akalowe akakhala akupatsidwa monga zakudya zabwino, akazi okongola kolapitsa, zipatso zokoma, zakumwa zabwino ndi zina. Koma kupembedza koteroku kukufanana ndi munthu yemwe amachita malonda chifukwa choti wamalonda amatenga katundu wake ndikupititsa kunsika komwe kuli kuzipatsa ntchito yayikulu koma amadziwa kuti pali chomwe apeze kuchokera mu ntchito akhale akupanga.
Kupembedza kwachiwiri ndikoti munthu amapembedza Mulungu ndicholinga choti akumuopa iye. Kupembedza uku ndikwa kapolo, chifukwa choti kapolo amadziwa nthawi zonse kuti Mulungu ndiye bwana wake pomwe iye ndikapolo wa iye choncho amayembekezera kuti nthawi ina iliyonse bwana wake amulamula kugwira ntchito ina ili yonse choncho amakhala okonzeka nthawi yomwe akumulamula kuti amupembedze bwana wake iye nthawi yomweyo popanda kuyang’ana zolowa amapembedza.
Kupembedza kwachitatu ndikoti munthu amamupembedza Mulungu chifukwa choti akufuna kumuyamika ndikumuthokoza chifukwa choti akudziwa kuti iye ndi amene ali oyenerezeka kupembedzedwa posakhala wina komanso ndi mwini zonse zimene munthu amakhala nazo, chifukwa kuyamika kumakhala kuti munthu watsimikiza kuti ubwino onse komanso zochitika zonse ndi mtendere onse omwe iwe wakupeza panthawi imeneyi wachokera kwa uyo amene ukumuyamika, munthu yemwe amapembedza Mulungu amakhala kuti ali ndichikhulupiriro kwa Mulungu popanda kuperewera kwina kuli konse mkati mwake pachifukwa chimenechi kupembedza uku ndikwapamwamba kuposa kupembedza komwe kwatchulidwa.
Mfundo zomwe tikuzipeza mu hadithiyi ndi monga:
1. Munthu ayenera kupanga china chilichonse chifukwa cha Mulungu, kaya munthu akufuna kukapanga udhu kuti apemphere ayenera kupanga chifukwa cha Mulungu chifukwa akapanda kutero ndiye kuti udhu wake ukhala owonongeka, nthawi yomwe munthu akuima pamapemphero ena ali onse ayenera kuima chifukwa cha Mulungu.
2. Muhadith ina muli mau akuti: Mulungu adawauza akapolo ake omwe adali kumupembedza iye kuti akalowe kumoto, akapolowa chifukwa choti adali ndichikhulupirira chonse kwa Mulungu adanyamuka ulendo opita ku moto koma atafika kumoto kuja adapeza kuti moto kulibe koma mtendere, apa Mulungu adafuna kwayesa chikhulupiriro chawo koma kuti anthuwa adali ndichikhulupiriro chonse kwa Mulungu wawo motero adapambana.
3. Munthu ayenera kupembedza Mulungu posayang’ana kuti amulipira chiyani, inde mitundu ina yakupembedza sikuti palivuto loti yemwe akupembedza Mulungu chifukwa chofuna zomwe Mulunguyo adalonjeza ndiye kuti kupempherako ndikosalondola ayi koma apa pakungolongosoredwa mtundu omwe uli wabwino kwa kapolo kusankha kuti akapeze mtendere wapamwamba monga momwe tikudziwira kuti mtendere uli mmagulu angapo.
4. Munthu ayenera kupembedza Mulungu mwachikondi chake chonse kwa iye.
5. Tikafuna kutchula chitsanzo cha kapolo yemwe adasankha gulu lachitatuli ndiye ndi mwini wake amene akuti phunzitsa hadithiyi yemwe ali Imam Husain (a) chifukwa iye adali kupembedza Mulungu wake moyenerezeka monga momwe talongosolera mugulu lachitatu. Munthu wina otchedwa Hilalu ataona kuti Husain (a) wagwa pansi adapita pomwe iye adagona ndicholinga choti akamuone ngati wafa, atafika adamupeza kuti wagona pansi ndipo adali kulankhula mau ndimilomo yake youma, Hilalu akunena kuti ndidaganiza kuti mwina Husain akutembelera anthu omwe amupanga zinthu zoipa ngati zimenezi, koma nditamuyandikira ndikumvetsera zomwe amalankhula ndidamumva akunena mau awa "E! Mulungu wanga, chisangalalo changa chili muchisangalalo chanu, ine ndagonjera muchilamulo chanu ndipo ndili opilira ku mavuto anu palibenso Mulungu wina opembedzedwa koma inu nokha". Nditamva mauwa ndidazizwa kwambiri ndipo ndidafunsa kuti kodi iwe ndindani, kodi ndi Mtumiki kapena munthu wamba? Apatu taona mmene Imam Husain(a) chikhulupiriro chake chilili kumbali ya Mulungu komanso ndikupembedza kwake.
Zomwe zidachitika pamalowa zidali zoti Imam Husain(a) adali kubweza kwa Mulungu wake zinthu zomwe adasungitsidwa monga miyendo, mikono, mano, maso, makutu, thupi ndi zina chifukwa choti iye adalolera kuti adani athe kuli menya ndikulizunza thupi pofuna kuti chilamulo cha Mulungu chisabisike koma chioneke poyera, ndichifukwa chake Mulungu adasangalatsidwa naye pomwe akunena mu surat Fajir ma aya omalizira (27-30) kuti : "E! iwe mtima okhazikika ndichilamulo cha Mulungu, bwelera kwa Mulungu wako uli osangalala ndi osangalalidwa ndi Mulungu wako, lowa mu mtendere omwe akapolo anga alowa kale, inde lowa mu mtendere wanga."
Add new comment