MAHADITH OKWANA 40 OCHOKERA KWA IMAM HUSAIN (A)
MUDZINA LA MULUNGU MWINI CHIFUNDO NDI CHISONI CHOSATHA.
MAHADITH OKWANA 40 OCHOKERA KWA IMAM HUSAIN (A)
KUMUDZIWA IMAM HUSAIN MWACHIDULE
DZINA: Husain.
MAINA OPATSIDWA: Sayyid Shuhada.
DZINA LOTCHUKA NALO:Abu Abdullah.
DZINA LA BAMBO: Ali (A)
DZINA LA MAYI: Fatimah (a).
TSIKU LOBADWA: 3 Shaban mchaka cha 4 Hijir.
MALO OBADWIRA: Madinah Munawwarah.
ZAKA ZAKE: 57.
ZAKA ZA UTSOGOLERI WAKE: 10.
TSIKU LA KUFA: 10 Muharram mchaka cha 61 Hijiri.
MALO OFERA NDI MANDA:Karbala.
OLAMULIRA ANTHAWIYO:Muawiyah ndi Yazid.
AMENE ADAMUPHA: Shimur ndi Sinan molamulidwa ndi Ubaidullah bin Ziyad
ndi Yazid bin Muawiyah( Mulungu awatembelere).
ANA AKE: 6, anayi amuna awiri akazi ( mukulankhula kwa
Shaikh Mufid). 10, asanu ndi mmodzi amuna anayi
akazi( mukulankhula kwa shaikh Maruhum Aribili
mubukhu lotchedwa Kashiful ghammah).
1- قال الامام الحسين عليه السلام :
البخيل من بخل بالسلام.
Imam Husain (a) adanena kuti: Munthu waumbombo ndi amene amaumira kupereka salaam.
Chimene tiyenera kudziwa ndichakuti salaam ndichinthu chofunikira kwambiri muchipembedzo cha chisilamu chifukwa chakuti chisilamu chimaphunzitsa zabwino zokha-zokha. Chisilamu chimatiphunzitsa kuzichepetsa pomwe tikayang’anitsitsa tipeza kuti kuzichepetsa kwagona mu salaam.Mukulankhula kwina tikuti chisonyezo chakuzichepetsa ndi salaam. Pofuna kulimbikitsa kufunikira kwa nkhani ya salaam imeneyi tikupeza kuti mu Quran muli kupereka ndikupatsidwa salaam kwa ena mwa aneneri monga: Nuhu (safat:79) (( Mtendere ukhale kwa Nuhu )) (salaam ala Nuhu), Ibrahim( Ibrahim:109) (( salaam ala Ibrahim)) (mtendere ukhale kwa Ibrahim), Mtumiki Muhammad ndi akunyumba kwake (s.a.a.w) ((salaam ala ali Yasin)) (mtendere ukhale kwa ali Yasin), Atumiki(a) ((salaam ala murisalin)).
Konsekuti kufuna kunena kufunikira kwa salaam. Tsono ngati atumiki (a) akutha kupereka ndikupatsidwa salaam chonchi kuli bwanji ife.
2- قال عليه السلام :
للسلام سبعون حسنة، تسع و ستّون للمبتدء و واحدة للرّاد.
Imam Husain (a) adanena kuti: Salaam ili ndi ubwino okwana makumi asanu ndi awiri (70), ubwino okwana makumi asanu ndi limodzi ndi mphambu zisanu ndi zisayi (69) umakhala kwa munthu oyamba kupereka salaam pomwe ubwino umodzi okha umakhala kwa oyankha.
Apa akufuna atiuze kuti kuyambirira popereka salaam ndichinthu chabwino kwambiri chifukwa choti chili ndi zabwino zambiri kuposa kuyankha salaam. Choncho ife tiyeni tikhale oyambirira popereka salaam kuti zabwinozi tizipeze. Ndibwinonso kwa ife asilamu kuti tizikonda kutumiza salaam kwa anthu akulu-akulu athu muchipembedzo , kwambiri kwake ma Imam monga Imam Husain amene akutiphunzitsa nkhani ya salaam imeneyi. Wina atha kunena kuti tingapereke bwanji salaam kwa iye? Tidziwe kuti munthu monga Imam Husain salaam wathu amamva chifukwa chonena kuti salaam ya iwo ndiyoti imapezeka muthupi mwawo pamene ife tikupereka salaam mwaiwo imakhala kuti ikadalipo kusonyeza kuti kwaife kumakhala kuti tikuyankha salaam yawo osati ndife oyamba kupereka salaam kwa iwo (salaam yawo ndi ya Takiwiniyy) (muchilengedwe chawo). Komanso Mulungu akunena kuti (wala tahasabanna ladthina qutilu fi sabilillah amuwata bali ahayau…………………)) ((Musaganize kuti anthu omwe amafera munjira ya Mulungu ndi okufa ayi koma dziwani kuti anthu amenewa adakali moyo……)). Ndiye kuti salaam wathuyu amamumva. Imfa simathero azonse ayi koma kuti imfa ndiulendo , imfa ndikubadwa kwatsopano, imfa ndikuvundukuka kwa tsamba lina la moyo, imfa ili ngati kuti munthu akuvula chikopa chadziko lapansi akuvala chikopa china chadziko lina.
Add new comment