KUYIKIRA KUMBUYO MUNTHU ONYOZA ALI(A) NDI AHLUBAIT(A)
KUYIKIRA KUMBUYO MUNTHU ONYOZA ALI(A) NDI AHLUBAIT(A)
.
Imodzi mwa zintchito za makanema a Mawahabi ndikuyeretsa anthu omwe ali odziwikiratu ntchito zawo monga Muawiyah,Yazid, Ibn Taimiyyah ndi ena omwe adadzudzulidwa angakhale ndi maulama achisunni omwe pomunena iye kuti ndiotalikirana ndi Quran.Lero lino pamene ma ulama asunni ali kaliki-liki kudzudzula chikhulupiriro cha Ibn Taimiyyah kudzera muQuran ndi mahadith, nawo mawahabi atsekura makanema oyeretsera munthu onyoza Akunyumba kwa Mtumikiyu.Munthu wina adabwera pa kanema yachi wahabi imeneyi ndikumanena zoyeretsa Ibn Taimiyyah yemwe adanyoza Akunyumba ya Mtumiki ponena kuti zomwe maulama ena amanena podzudzula Ibn Taimiyyah sizoona ndipo anthu ayenera osazitengera zimenezi. Pofuna kumuyankha mkulu ameneyu tikunena kuti imodzi mwa njira zomwe timamudziwira munthu ndi chikhalidwe chake ndikuwerenga mabuku omwe adalemba.Kwakwana kwa ife kuti tiwerenge bukhu lomwe Ibn Taimiyyah adalemba lotchedwa “Minhajul sunnah” tione kuti kodi Ibn Taimiyyah ndi mdani nambala 1 wa Ahlubait(A) kapena ayi.
Add new comment