Nkhani yokhudzana ndi kusokonezeka kwa Qur’an
Chimodzi mwa zinthu zomwe adazifalitsa powanamizira ma Shia ndi choti Shia amakhulupilira kuti Quran idasokonezedwa ndipo amanena kuti gawo lochuluka la Quran lidafufutidwa. Chifukwa chakuti Quran yeniyeni idali ndi ma Aya okwana 18000 ndipo padakali pano adatsala ma Aya okwana 6236 okha basi.
Ndiye apa tikufuna tiwone kuti kodi ndi zowonadi ma Shia amakhulupilira za Quran ina kapena ayi ngati momwenso zimakhala zikunenedwera kuchokera kwa Ma Sheikh kuno ku Malawi kuti: ma Shia ali ndi Quran ya majuz 40 kapenanso 60 kumene. Zomwe tanena kale kuti komwe kuli kuwanamizira iwo.
Zimenezi ndi zofunikira kwambiri kuti zilongosoledwe ngakhale kuti kulongosola kwathu padakali pano kudzakhala kwachidule, chifukwa chakuti Quran ndi umboni waukulu kwambiri potsimikizira za utumiki wa mtumiki wathu Muhammad (S.A.A.W).
Mwachoncho ngati Quran idzapezeka ndi vuto ndiye kuti utumiki wake udzakhala wabodza komanso chisilamu chidzakhala chofunsidwa ndipo chidzafaniziridwa kuti ndi chipembedzo chabodza.
Sheikh Abdullah Jibrin akulongosola mu bukhu lake la Lu’ulu’ul Makin min Fatawa Sheikh Jibrin kuti:
Zinthu zinayi (4) ndi zomwe zikupangitsa kuti Shia akhale Kafir (okanira) mwachoncho ndi zinthu zinayizi, ndi chifukwa chake amayenera kuphedwa.
Kutanthauza kuti ngati munthu angafunse kuti ndichifukwa chiyani ma Shia amakhala akuphedwa? Yankho lake ndi loti chifukwa cha zinthu zinayi zomwe Sheikh Jibrin adanena.
Zinthu zinayizi ndi izi:
• Shia amakhulupilira kuti Quran idasokonezedwa ndipo amati Quran idali ndi ma Aya okwana 18000 koma padakali pano adangokhala 6236 basi.
• Shia ndi Kafir komanso ndi wa Najs chifukwa chakuti iye samagwiritsa ntchito ma Sunna amtumiki posagwiritsa ntchito bukhu la Sahih Bukhari ndi bukhu la Sahih Muslim, chifukwa chakuti:
من کان فی بیته صحیح بخاری کأن النبی یتکلم
“Munthu amene mnyumba mwake angakhale ndi Sahih Bukhari, zimakhala ngati kuti muli mtumiki akulankhula”.
Mabukhu amenewa ndi mabukhu omwe amabwera pambuyo pa Quran ndipo palibe mabukhu apamwamba komanso onena zowona pambuyo pa Quran kuposa amenewa.
Mwachoncho chifukwa choti Shia samatsatira ndi kugwiritsa ntchito ma bukhuwa ndiye kuti akutsutsana ndi Sunna ya mtumiki.
Kuwonjezeranso pa fundo imeneyi iwo samawalemekeza ndinso amawatembelera ma Swahaba kumachita kuti Quran yawachemelera maswahabawa koma shia ndi pomwe amawatembelera ndiye kuti iye ndi Kafir ndipo ayenera kuphedwa.
• Shia ndi Kafir chifukwa chakuti amawanena asilamu a Ahalsunna (Sunni) kuti ndi a Najs (nyasi) chifukwa chakuti amabadwa munjira yosavomerezeka.
• Shia ndi Kafir chifukwa chakuti amapyola muyeso pa chikhulupiliro pokhudzana ndi Ahalbait (A.S) – abale ake a mtumiki – chifukwa choti amawafikitsa pa mlingo wa Mulungu komanso amawagwadira.
Awa ndiwo mawu a Sheikh Abdullah Ibn Jibrin.
Tsopano mayankho athu pa fundo zimenezi ndi otani?
Yankho lathu mwachidule pa fundo yakuti Shia amakhulupilira kuti Quran idasokonezedwa.
Chikhulupiliro chathu (Shia) ndi chakuti, ndithudi bukhu lomwe liri padakali pano pakati pa asilamu ndi lomwelo lidabwera ndi mtumiki ndipo olo ndi pang’ono pomwe silidapungulidwe kapena kuwonjezeredwa ngakhale chilembo chimodzi kumene. Idatifika ife kuchokera kwa mtumiki mundondomeko yomwe padakali pano iripo mu Quraniyi ndipo mtumiki mwini wake ndi yemwe adayika ndondomeko imeneyi asadamwalire kudutsira mwa ma Swahaba ake. Mwachoncho mawu amenewa akungotinamizira ndi cholinga choti azitiphera. Ndithudi limeneli ndi bodza la mkunkhuniza. Ife timakhulupilira kuti china chirichonse chiri mu Quran ndi gawo la Quran ngakhale Bismillahi yemwe ali kumayambiliro kwa Sura ina iliyonse ndipo munthu akafuna kupemphera ayenera kuwerenga Bismllahi wake chifukwa kusatero ndiye kuti gawo lina la Quran likuchotsedwa. Kupatula asilamu ena monga a Ahalsunna omwe amanena kuti Bismillahi yemwe ali kumayambiliro kwa Sura ina iliyonse sigawo la Quran mwachoncho ndi chifukwa chake amaloleza kuti panthawi ya Swala atha kuyamba kuwerenga Sura popanda kuwerenga Bismillah.
Tawonani zimenezi kusiyana komwe tiri nako pachikhulupiliro pankhani ya Quran. Kodi kunena kuti Bismillahi yemwe akupezeka kumayambiliro kwa Sura sigawo la Quran, sindiko kukhulupilira kuti mu Quran muli zinthu zina zomwe zidangolembedwa ndi anthu ndipo sizochokera kwa Mulungu? Pomwe wina akukhulupilira kuti ngakhale Bismillahi kumene ndi gawo la Quran. Kodi ndi chifukwa chiyani anthu amatinenera bodza lomwe mapeto ake ndikumapezerapo mwayi otiphera?
Abale anga tatiyeni tiziganiza bwino mukulankhula kwathu makamaka ma Sheikh athu muyenera kumawawuza anthu zinthu za chilungamo osati zinthu zoyambitsa kuti asilamu azidana ndi kumayambana.
Chabe kuti bodzali ndi lalikulu ndipo lidafalitsidwa pena paliponse mwachoncho lidakhaladi ngati zowona kuti chikhulupiliro cha Shia ndi chimenechi kufikira kuti munthu yemwe wamva za Shia, nzeru zakenso sizimagwira ntchito bwino kapena kuganiza ngakhale ndi pang’ono pomwe.
Yankho lathu pa mawu oti Shia samalemekeza ma Swahaba ndipo amawatembelera komwe kuli kutsutsana ndi Sunna kumachita kuti Quran yawachemelera iwo mwachoncho Shia ndi Kafir ndipo ayenera kuphedwa.
Ilinso ndi bodza lachiwonekere. Kodi ife sitimamulemekeza Ali Ibn Abi Talib, Fatima al-Zahra mwana wa mtumiki, Hasan ndi Husein ana Fatima ndi Ali (A.S), Salman Farsi, Abu Dhar, Ammar, Miqdad ndi ena ambiri pokhala iwo maswahaba a mtumiki?
Ndizachidziwikire kuti ife ndi amenenso timawalemekeza maswahaba kwambiri mwachilungamo potengera ndi m’mene adaliri chifukwa chakuti adali anthu ovomerezedwa komanso osangalalidwa ndi mtumiki.
Koma kuti zomwe tinganene ndi zakuti: ife pokhudzana ndi anthu omwe adali m’mbali mwa mtumiki, timasiyanitsa pakati pa anthu omwe adali okhulupilira enieni ndi anthu omwe adali akamberembere (Munafiqiin).
Akamati Munafiq, ndi munthu amene amawonetsa nkhope yake ngati msilamu koma pomwe mu mtima simsilamu ayi ndipo amaziwandikitsa ndi mtumiki kapena asilamu kumene ndi cholinga choti awononge chisilamu ndi kuti amubweletsere vuto mtumiki.
Mwachoncho ife timasiyanitsa pakati pa maswahaba a mtumiki ngati momwe Mulungu akuwasiyanitsira mu Quran. Ma Aya ndi ambiri potsimikizira nkhani imeneyi koma poti padakali pano tikungoyankha mwachidule, Aya imodzi yokha idzatikwanira.
Mulungu mu Surat Tawbah Aya 101, akulankhula kuti:
و ممن حولکم من الأعراب منافقون و من أهل المدینة مردوا علی النفاق
“Ndipo ena mwa ma Arab omwe ali m’mbali mwanu ndi ma Munafiqiin komanso ena mwa anthu aku Madina akhazikika pa ukamberembere”.
Funso ndi lakuti kodi Mulungu akuwasiyanitsa magulu awiriwa ndiye ife tisawasiyanitse?
Kodi yemwe sakusiyanitsa ndi amene akusiyanitsa pakati pa magulu awiriwa ngati momwe wapangira Mulungu, ali wachilungamo ndi ndani?
Koma zomvetsa chisoni ndi zakuti chifukwa chakuti wina watsata njira yomwe Mulungu adatsata, akupatsidwa lamulo loti aphedwe. Mukuwona momwe nkhaniyi iliri kuwopsya kwake?
Mulungu mu Quran adayika Sura ina mudzina la Kafiruna ndipo adayikanso Sura ina mudzina la Munafiqun. Tikupeza kuti Surat Kafiruna ndi yaying’omo kwambiri poyerekeza ndi Surat Munafiqun ndipo ikulowamo kangapo konse.
Akamberembere nthawi ya mtumiki komanso nthawi ina iliyonse chiwelengero chawo chimakhala chochepa poyerekeza ndi ma Kafir, komanso ndi anthu omwe adali pafupi ndi mtumiki kukhala ngati asilamu. Bwanji sitikumadzifunsa kuti ndi chifukwa chiyani Mulungu akuchuluka mawu kwa anthu omwe adali pafupi ndi mtumiki m’mawonekedwe pomwe kwa anthu omwe adali ma Kafir akulankhula pang’ono?
Mulungu kumayambiliro kwa Surat Baqara akuwagawa anthu magulu atatu. Anthu okhulupilira (Muminiin, anthu okanira (Kafirin) ndi akamberembere (Munafiqiin). Mulungu akuwalongosola anthu okhulupilira ndi ma Aya atatu okha kuchokera Aya yachiwiri ya Surayi kufikira Aya yachisanu (5), akuwalongosola anthu okanira ndi ma Aya Awiri okha (6-7) pomwe tikuwona kuti akuwalongosola akamberembere – omwe amadziwonetsera ngati kuti ndi okhulupilira – ndi ma Aya okwana khumi ndi atatu (13).
Apanso funso ndi loti ndi chifukwa chiyani Mulungu akuchulukitsa mawu kwa akamberembere pomwe anthu okhulupilira ndi okanira akuwalongosola ndi mawu ochepa kwambiri?
Yankho lake ndi lowonekera poyera. Anthu okhulupilira muchowonadi ndi anthu omwe ali owonekera kwambiri komanso ndi odziwika kwa aliyense, chimodzimodzinso anthu okanira ndi odziwika bwino lomwe kwa aliyense kuti uyu ndi mkhirisitu ndipo uyu ndi mu Yuda komanso uyo ndi osakhulupilira kapena kuti alibe chipembedzo. Mwachoncho chifukwa choti anthu awa ndi odziwika bwino, ndikosavuta kuwatalikira komanso kupewa mavuto omwe angawabweletsere asilamu.
Pomwe munthu amene ali kamberembere (Munafiq) ndi amene ali owopsya kwambiri ndipo atha kuwononga chisilamu ndi kuwabweletsera vuto asilamu mosavuta kapenanso atha kumuwononga mtumiki mosavuta. Kuwopsya kwa munthu ameneyu ndi kwakukulu kwambiri ndi chifukwa chakenso Mulungu akuchulukitsa mawu potilongosolera ife za kuwopsya kwa munthu ameneyu kuti tikhale ochenjera kwambiri.
Ngatinso momwe zidakhalira mu mbiri ya zipembedzo zomwe zidapita kale. Zikupezeka kuti panthawi yomwe olemekezeka mtumiki Musa (A.S) adapita kuphiri la Tur, anthu omwe amawoneka kuti adali okhulupilira komanso apafupi ndi Musa (A.S) ndi omwe adasocheretsa anthu popanga ng’ombe ndikuwayitanira anthu kukugwadira ng’ombeyo ndipo adamukankhira kumbali munthu yemwe Musa (A.S) adawalamula kuti amumvere ndi kumutsatira yemwe ali Haroon (A.S), pambuyo pakuti mtumiki Musa (A.S) wagwira ntchito yaikulu motopetsa powayitanira anthu ku chilungamo.
Zowonadi, mavuto a kamberembere ndi ovuta kuwapewa kwake. Kamberembere pofuna kukwaniritsa zofuna zake ndi yemwe amayesetsa kutembenuza chilungamo ndi kukhala bodza ndipo bodza lake ndi kukhala chilungamo. Amagwiritsa ntchito njira zosiyana siyana monga kulanda ulamuliro, kukhala ndi mphamvu zochuluka, kuwopsyeza anthu, kupha anthu osalakwa ndi achilungamo, kuwaipitsa anthu omwe ali achilungamo, kutenga mbiri zabwino za anthu a chilungamo ndikuzimveka iwo eni ndi zina zotero kufikira kuti anthu ambiri chifukwa cha mantha, amavomereza zonena zake ndipo kudutsa kwa nthawi ana omwe akubadwa mtsogolo amapeza zinthu zomwe iye adazifalitsa ndipo anawo amaganiza kuti ichi ndicho chilungamo.
Mapeto ake munthu uja akamawuzidwa zowona ndikupatsidwa ma umboni ake, mofulumira amatsutsa popanda kuganiza komanso popanda umboni omveka komanso samawapatsa mpata makutu ake kuti amve kuti zomwe zikunenedwa ndi chiyani. Zonsezi ndi chifukwa choti adazolowera zomwe amapangazo ndipo adawapeza anthu ambiri akupanga zoterozo, pomwenso akuwona kuti zomwe zikunenedwa kuti ndi chilungamo, palibe yemwe akuzipanga komanso siambiri omwe amapanga.
Zotsatira zake ndipomwe umboni wake umakhala wakuti kuyambira kale makolo anga adali kupanga zomwe ndikupangazi komanso anthu ambiri amapanga chimodzimodzi.
Koma apa ndi pomwe tikumupeza munthu yemwe amagwiritsa bwino nzeru zake komanso ofuna chilungamo, akupilira ndi kuyika nthawi yake pofufuza ma umboni ndi cholinga choti adziwe kuti chilungamo ndi chiti ndipo amayang’ana mbali ina iliyonse kuti kodi awa akuti chiyani nanga umboni wawo ndi otani, nanga awonso akuti chiyani ndi umboni wawo ndipo nanga omwe akunena zowona ndi ati? mtima wake siwumakhazikika kufikira atadziwa zowona za nkhaniyo.
Abale anga asilamu okondedwa amene Mulungu wakulemekezani pokupangani kukhala asilamu!
“Yambani mwadziwa kaye chilungamo nokha ndi pomwe muzawadziwa omwe akutsatira chilunga, musawadziwe anthu kaye pofuna kudziwa chilungamo. Kutanthauza kuti musayambe mwamuvomera munthu kuti ndi wachilungamo pomwe chilungamocho simudachidziwe”.
Mwachidule, ife (Shia) timawalemekeza maswahaba oyera omwe ali ovomerezedwa ndi kusangalalidwa ndi mtumiki kwambiri osati omwe adakhala mwachinyengo ndi mtumiki ndipo pambuyo pake namamuvutitsa ndi kumamukwiyitsa.
Kuyankha pa zomwe adawonjezera Sheikh Abdullah Jibrin pa fundo yomweyi kuti Shia chifukwa choti samatsatira ndi kugwiritsa ntchito ma bukhu a Bukhari ndi Muslim momwe mwagona Sunna ya mtumiki ndiye kuti iwo ndi ma Kafir komanso Najs posatsatira Sunna ya mtumikiyi.
Ee zowonadi ife (Shia) sitimagwiritsa ntchito ma bukhu amenewa. Nditsatira bwanji bukhu lomwe ndiribe chilolezo choganiza pa zomwe ziri mkati mwake?
Ma Sheikh akuluakulu a Ahalsunna adatulutsa lamulo loti:
Kuganiza pa zomwe ziri m’mabukhuwa ndi Bidiah. Kutanthauza kuti munthu alibe chilolezo choganiza mkati mwa mabukhuwa ndipo kuteroko ndi tchimo.
Zitheka bwanji kuti ndiligwiritse ntchito bukhu lomwe silikundithandiza ine pakuzindira kwina kulikonse, kuzindikira komwe kumabwera pambuyo pakuganiza? Pomwe tikumupeza Mulungu powonjezera kuti iye akudziwa kuti zomwe zabwera mu Quran ndi chilungamo chokha chokha, akuwayitara ndi kuwakakamizabe anthu za kuganiza mozama mu bukhu lolemekezekali ndipo ndikumati ganizani mukapeza kuti ndi zowona zitsatireni. Kumachitadi kuti zonse ziri mu Quran ndi chilungamo chokha chokha ndipo munthu alibe kothawira komanso sangabweretse umboni omveka kuposa Quran.
Ngati Mulungu akundilamula kuganiza mu bukhu lake ndiye kulibwanji bukhu lomwe likulembedwa ndi munthu? Munthu yemwe nthawi ina iliyonse akupenekeredwa kuti atha kulakwitsa? Kodi bukhu lake likuyenera kufufuzidwa ndi kuganiziridwa mozama bwanji?
Apanso ndi pomwe munthu ayenera kufufuza ndi cholinga choti adziwe kuti kodi m’mabukhumu muli chiyani mpakana chilolezo choganiza sichikuperekedwa? Ndithudi pali kanthu abale anga.
Tikamafufuza ndi kuwerenga zomwe ziri m’bukhuli tikupeza kuti pogwiritsa ntchito ma bukhu awiriwa, tidzatha kupeza umboni oti Khalifa oyamba, wachiwiri ndi wachitatu adali achinyengo, a uchimo, komanso abodza.
Ndi ma bukhu amenewa, mutha kupeza umboni oti Khalifa wa chitatu ankamunena mtumiki kuti musiyeni musamumvere matenda amupengetsa komanso mudzatha kupeza umboni oti mlembi wa bukhu la Sahih Bukhari sakumutenga Ali (A.S) kuti ndi Khalifa wachinayi.
Ngakhale kuti asilamu ambiri sadziwa bwino za utsogoleri wa Ali (A.S) kuti ndi ochokera kwa Mulungu komabe ndi pang’ono pomwe amadziwa kuti iye adali Khalifa wachinayi.
Ndipo ma bukhu amenewa azakutsimikizirani kuti Fatima al-Zahra (S.A) – bwana wa amayi ku Jannah – adakwiyitsidwa ndi Khalifa oyamba komanso wachiwiri ndipo mapeto akenso mudzapeza umboni oti mkwiyo wa Fatima (S.A) ndi mkwiyo wa mtumiki ndi Mulungu zomwe zotsatira zake ndi matembelero a mtumiki ndi Mulungu.
Zowonadi izi ndi zina mwa zinthu zomwe zidawapangitsa akuluakuluwo kuti aletse kuganiza ndi kufufuza zomwe ziri m’mabukhuwa chifukwa akudziwa kuti munthu adzakumana ndi zimenezi mapeto ake akadzazindikira adzadana nazo kwambiri.
• Fundo yomaliza ndi yoti Sheikh Jibrin akunena kuti Shia ndi Kafir chifukwa chakuti amawatenga Ahalsunna kuti ndi Najs.
Ilinso ndi bodza la mkunkhuniza lomwe akuligwiritsa ntchito pofuna kuwaphera ma Shia.
Dziwani kuti akamati Najs apa, akutanthauza kuti adabadwa mu njira yosayenera mwachidule adabadwira muchigololo zomwe zingawapangitse kuti asakhale ma Imam a Swalat ya pagulu komanso asakhale atsogoleri. Mwachoncho umve umenewu mwanjira ina iliyonse ndi osachoka mpakana kalekale.
1- Choyamba choti tidziwe ndi chakuti ma Sheikh ambiri akuluakulu omwenso ndi ma Imam (atsogoleri) a Swalat a Shia, kumayambiliro adali a Sunni. Munthu amene ali ndi Najs imeneyi sangakhale Imam wa Swala mpakana kalekale. Nanga ma Sheikh athuwo ndi chifukwa chiyani akumakhala atsogoleri a Swala? Ndipo palibe zomwe zimanenedwa kuti Najs yatha chifukwa choti wakhala Shia.
2- Shia akukhulupilira kuti munthu amene wapita ku HAJ ndipo sadapenge Haj Nisa ndiye kuti ndi Haram kuti akhale ndi mkazi kapena mwamuna wake malo amodzi ndipo ngati angatero ana obadwawo adzakhala obadwira munjira ya Haram.
Zowonadi lamuloli lilipo, koma choti mudziwe ndi chakuti lamuli likungokhudza anthu ake omwe ali ma Shia chifukwa chakuti ndi omwe adakhulupilira lamuloli osati anthu omwe siali Shia. Kutanthauza kuti munthu wa Shia ngati sapanga Haj Nisa ndiye kuti zotsatira zake ndi zimenezo.
Chifukwa chakuti wina aliyense amapakanga zinthu motsana ndi chikhulupiliro chake, chomwechonso amakwatira motsana ndi chikhulupiliro kapena chikhalidwe chake.
Kodi tithe kuwanena ana onse omwe makolo awo sadapite ku Haj – akhale a Shia kapena a Sunni – kuti ndi obadwira munjira ya Haram mwachoncho ndi Najs? Ndi zosatheka zimenezo. Ndithudi ana obadwawo ndi obadwira munjira ya Halal.
3- Tinenenso apa kuti anthu a chipembedzo kapenanso a mtundu wina uliwonse amapanga zinthu motsatira zikhulupiliro ndi zikhalidwe zomwe alinazo.
Kutanthauza kuti yemwe ali msilamu ayenera kupanga zomwe chisilamu chikunena ndipo akapanda kutero ndiye kuti ngati kuli kukwatira, ana obadawo adzabadwira munjira yosayenera komanso yosavomerezedwa ndi chisilamu komwe kuli kubadwira munjira ya Haram ndipo adzakhala ndi Najs ija yoti sangathe kukhala Imam wa Swala kapena mtsogoleri wa anthu.
Ngati munthuyo ali mkhirisitu adzayenera kutsatira ndondomeko yomwe akhirisitu amatsatira kuti anthu akwatirane ndipo akatero chisilamu chizawadziwa ana obadwawo kuti ndi obadwira munjira yovomerezeka chonchonso ngati satsatira za chipembedzo chawo ndiye kuti anawo adzabadwira munjira yosavomerezeka.
Izi ndi zachidziwikire chifukwa timawona kuti pakati pa anthu a mitundu yosiyana siyana, ngati munthu sadatsatire chikhalidwe chawo kapena chikhulupiliro chawo pankhani yokwatira, anthu achikhalidwecho kapena chikhulupilirocho samasangalatsidwa ndi zoterozo ndipo amawatcha anthu oterowo kuti achikunja chifukwa choti asemphana ndi chikhalidwe chawo.
Nkhani ndi yaikulu kwambiri koma apa timafuna kutsimikizira yankho la chiwiri lija.
Mwachoncho ife asilamu makamaka anyamata amasiku ano omwe ali asilamu, tiyenera kuyang’anitsitsa kwambiri. Tisapange zinthu zomwe zidzapangitsa kuti ana athu omwe adzakhale obadwira munjira yosayenera komanso yosavomerezeka ndi chisilamu pomwe ana achikhirisitu ndi mitundu ina adzakhala obadwira munjira yovomerezeka ndi chisilamu ngati makolo awo adatsatira zomwe chipembedzo chawo chidanena.
Ndizowawa kwambiri kuti tidzawononge tsogolo la ana athu iwo asadabadwe. Kodi kupondereza kumeneku kudzakhala kwakukulu bwanji kwa ana athu?
Ndiye zonsezi timafuna kuyankha kuti:
Shia olo ndi pang’ono samawatenga a Sunni kuti ndi Najs, koma kuti m’malo mwake a Shia omwewo ndi omwe ana awo adzakhala a Najs ngati sadzatsatira malamulo omwe Madh’hab awo akunena komwe kuli kusapanga Haj Nisa komanso kwa munthu yekhayo yemwe wapita kukapanga Haj. Dziwaninso kuti Haj imaneyi ikungopezeka ku Madh’hab athu okha basi. Ndiye wa Sunni zimukhudza kumachita kuti alibe mtundu wa Haj umenewu?
Add new comment