Kodi tidzayankha chiyani mu usiku wathu oyamba m’manda: Imam (mtsogoleri) wathu ndi ndani?

Kodi tidzayankha chiyani mu usiku wathu oyamba m’manda: Imam (mtsogoleri) wathu ndi ndani?

بسم الله الر حمن الرحیم

Padakali pano tiri m’masiku a mwezi wa Ramadhan, mausiku a Lailatul Qadr, masiku okhudzana ndi anthu osalakwa mu umoyo wawo onse omwe ali akunyumba ya mtumiki Muhammad (A.S). masiku omwe Imam Ali (A.S) adakhapidwa ndi lupanga la mankhwala – poison – mumzikiti komanso masiku a kuphedwa kwake. Ameneyu ndi munthu amene adamupatsa Mulungu mwayi omakagawira anthu abwino Jannah komanso oyipa Jahannama.
Mwachoncho tikupepesa kwa Asilamu onse pano padziko lapansi chifukwa cha zovuta zomwe zidatigwerazi m’masiku amenewa. Komanso tikumupempha Mulungu kuti afulumizitse kubwera kwa mtsogoleri wanthawi yathu yemwe ali Imam Mahdi (A.A.T.F).
Tatiyeni m’masiku amenewa tikhale pa tebulo la Quran pomwe tidzakambirane ena mwa ma Aya a bukhuli kuchokera mu Surat Nabai yomwe ikupezeka kumayambiliro kwa Juz yomaliza ya 30 ya Quran yolemekezeka, yomwe ikuyamba ndi kuti:

عم یتساءلون، عن النبإ العظیم، الذی هم فیه مختلفون، کلا سیعلمون، ثم کلا سیعلمون

Kodi anthu akufusana fusana zachiyani? Akufusana za nkhani yomwe ili yaikulu kwambiri. Nkhani yayikulu yake yomwe iwo akusemphana ndi kusiyana maganizo pokhudzana ndi nkhani imeneyo. Nkhaniyi sidzangokhala chonchi, ndithudi adzazindikira posachedwapa. Kenakonso ndithudi adzazindikira posachedwapa.

Kutanthauza kuti posachedwapa kwa iwo zidzawonekera poyera zowona zake.
Kodi chinthu chimenechi ndi chinthu chanji? Kodi nkhani imeneyi ndi nkhani yanji yomwe asilamu onse akhala akusemphana ndi kutsutsana maganizo pokhudzana ndi mtendere umenewo, pokhudzana ndi nkhani yaikulu imeneyi?
Kodi ndi Mulungu? Ayi. Chifukwa asilamu onse amakhulupilira za Mulungu m’modzi.
Kodi ndi mtumiki wa chisilamu Muhammad (S.A.A.W)? ayi. Asilamu onse amakhulupilira ndi kuvomereza za Mtumiki wa chisilamuyu.
Kodi ndi Quran? Ayi.
Nkhani yaikulu muchipembedzo cha chisilamu yomwe asilamu adasemphana maganizo ndi kumakangana, ndi nkhani yokhudzana ndi utsogoleri, Khilafah ndi Imamah wa Amirul muminin Ali Ibn Abi Talib (A.S).
Imam Ali (A.S) pankhondo ya Siffin adanena kuti:

أنا النبأ العظیم الذی فی اختلفتم و فی خلافتی تنازعتم

Ine ndiye nkhani yaikulu ija yomwe inu mudasemphana komanso mudakangana pokhudzana ndi ulowa m’malo wanga”

Nkhani yaikulu yomwe anthu adasemphana maganizo ndi Ali (A.S), Khilafah ndi Imamah pambuyo pa mtumiki wa Mulungu (S.A.A.W) ndikusemphananso ndi ma Aya, Hadith ndi maumboni omwe akulozera ndi kutsimikizira za Utsogoleri wa Ali ibn abi Talib (A.S) pambuyo pa mtumiki.
Nkhani imeneyi sidzangokhala chonchi mpakana kalekale.
M’bale okondedwa amene ukuwerenga padakali pano, Quran ikulongosola kuti nkhani yomwe mudasemphana ndi kutsutsana maganizoyi kufikira mpakana pano, sidzangokhala choncho mukutsutsanabe mpakana tsiku la Qiyamah ayi.
Pompano komanso posachedwa mudzazindikira kuti chilungamo chiri ndi ndani?

کلا سیعلمون

Ndithudi adzazindikira posachedwapa.

Mudziko la Barzakh, komwe mizimu yathu ikupita pambuyo posamuka kuchoka mudziko lino lapansi ndi lakutha. Posachedwapa tidzakala tikusamuka kuchoka mudziko lapansili. Pomwe tidzakhala tikulowa m’manda mutsiku loyamba pomwe azikatifunsa. M’mandamu tidzayenera kukwanitsa kuyankha kuti:
Kodi bwana wako ndi ndani?
Kodi mneneri wako ndi ndani?
Kodi bukhu lako ndi chiyani?
Nanga kodi Imam wako ndi ndani?
Apa ndipomwe zizadziwika kuti yemwe amayenera kuti akhale Imam wako ndi ndani. Kenakonso kachiwiri patsiku la Qiyamah zizadziwikanso kuti ndi ndani amayenera kukhala Imam wako.
Tsiku loyamba la m’manda ndi lowopsya kwambiri chifukwa ndi tsiku lomwe lizamudziwitsa munthu kuti kuyambira pamene wangoikidwapo umoyo wake ndi otani. Ndi wabwino kapena oyipa.
Mwachoncho ndi pofunika kuti m’mausiku a Qadir amenewa tipemphe kwa Mulungu kuti:
Ee Mulungu wanga! ikani imfa yanga kuti idzakhale ndiri pachiwongoko.
Ee Mulungu wanga! Ndivereni chisoni kuti tsiku langa loyamba m’manda, tsiku lomwe ine ndidzakhala ndiri ndekha popanda ondithandiza, ndidzapambane komanso ndidzapulumutsidwe kuchokera m’malo opweteka amenewa.
Quran yanena kale kuti nkhani imeneyi sidzangokhala chonchi ayi.
Anthu omwe adakhazikika ndi kutsatira utsogoleri weniweni wa Ali (A.s) adzazindikira pomwe adzawona ndi maso awo kuti adali ndi chikhulupiliro chenicheni ndipo ankanena zowona.
Koma tsoka lidzakhala kwa omwe dzanja lawo silidafike kwa Imam Ali (A.S) ndipo m’malo mwake adagogoda khomo la nyumba ina posakhala khomo la Ali (A.S).
Pali Hadith ina yomwe ikunena kuti:
…Fufuzani kuchokera kum’mawa kufikira kumadzulo kwa dziko zokhudzana ndi utsogoleri wa Ali (A.S).
Palibe kuzindikira kwabwino komwe mungakupeze pokhapokha kudutsira mwa Ahalbait (A.S) omwe ali ma Imam okwana khumi ndi awiri 12.
Tonsefe tidzafunsidwa tsiku loyamba la m’manda kuti kodi nkhani yaikulu ija ndi chiyani? Ndi munthu uti yemwe adali wamkulu pambuyo pa mtumiki Muhammad (S.A.A.W)?
Kodi ine ngati msilamu ndidzayankha chiyani?
Ngati ine ndiri msilamu wa Shia ndidzayankha kuti Imam Ali (A.S) ndi yemwe adali wamkulu komanso oyenera kumutsatira pambuyo pa mtumiki Muhammad (S.A.A.W) ndipo sindidatsatire kapena kukhulupilira utsogoleri ochita kulanda ayi.
Kodi omwe adamutenga Shafi, Hambali, Maliki ndi Hanafi, kukhala Imam wawo adzakwanitsa kumutchula yemwe adali munthu oyenera kumutsatira pambuyo pa mtumiki kapena ayi?
Kumeneko kulibe kubisa kapena kuwapusitsa ofunsa ayi.
Adzafunsa ofunsawo kuti kodi simudamumve mtumiki akunena kuti:

من کنت مولاه فهذا علی مولاه

“Wina aliyense yemwe ine ndidali mtsogoleri wake, uyu Ali ndi mtsogoleri wake”.
Kodi simudawerenge kuchokera m’mabukhu a Shia komanso mabukhu a Ahalsunna kuti mtumiki olemekezeka (S.A.A.W) pazomwe zidachitika pa malo otchedwa Ghadir, adanyamula dzanja la Ali (A.S) pakati pa chinantindi cha anthu ndipo adanena kuti wina aliyense amene ine ndidali mtsogoleri wake adziwe kuti Ali adzakhala mtsogoleri wake.
Adzakufunsani mutsiku loyamba m’manda kuti kodi simudawerenge Aya ya Quran kuti:

انما ولیکم الله و رسوله و الذین آمنوا الذین یقیمون الصلاة و یؤتون الزکاة وهم راکعون

“Ndithudi mtsogoleri wanu ndi Mulungu, Mtumiki ndi anthu okhulupilira, anthu ake omwe amayimiki mapemphero ndipo amapereka Zakat ali chiwelamire (panthawi ya mapemphero)”.
Kodi simudawerenge kuchokera m’mabukhu osiyanasiyana kuti Ayayi idatsika polongosola za utsogoleri wa Ali (A.S) pambuyo pa mtumiki wathu (S.A.A.W).
Ndichifukwa chiyani simudamutenge Ali (A.S) kukhala mtsogoleri wanu?
Adzafunsa zimenezi mu tsiku loyamba m’manda. Ndipomwe munthu akasowa kothawira pankhani imeneyi.
Kodi simudawerenge aya yomwe ikunena kuti:

فقل تعالوا ندع أبناءنا و أبناءکم و نساءنا و نساءکم و أنفسنا و آنفسکم

“Awuze – iwe mtumiki – bwerani tiyitane ana athu ndipo inu muyitane ana anu, akazi athu ndi akazi anu ndinso mitima yathu (ife eni ake) komanso mitima yanu (inu eni)”.
Simudawone kuti panthawi yomwe akhirisitu aku dera la Najran ankatsutsa za utumiki mtumiki, kodi mtumiki ndi munthu uti yemwe adamuyika kukhala mtima wake (iye mwini)?
Akhirisitu adali akudikilira kuti kodi mtumiki abwera ndi ndani? kodi chisilamu chizazidziwitsa bwanji kwa akhirisitu kuti ichi ndicho chisilamu chenicheni? Anthu adawona kuti mtumiki adabweretsa anthu omwe adali okondedwa komanso owandikirana kwambiri ndi iye. Imam Hasan, Imam Husein, Fatima al-Zahra, Imam Ali (A.S) ndi iye mtumiki (S.A.A.W) ndi omwe adapezeka pa mtsutsowo.
Kodi simudawerenge kuchokera m’mabukhu osiyana siyana kuti mtumiki adanena kuti:

أنا مدینة العلم و علی بابها

“Ine ndi mzinda wa maphunziro ndipo Ali ndi khomo lake”.

Munthu sadzalowa mu mzinda umenewu pokha pokha atadutsira kwa Ali (A.S).
Ine monga msilamu ndikuyenera kutenga malamulo a chisilamu kuchokera kwa mtumiki wa Mulungu, mwachoncho ngati munthu dzanja lake silifika kwa Ali Ibn Abi Talib (A.S) ndiye kuti sadafike kwa mtumiki (S.A.A.W).
Kodi inu simudawerenge Hadith yomwe idalembedwa kangapo konse m’mabukhu osiyana siyana kuti mtumiki adali akumuwuza Ali kuti:

أنت منی بمنزلة هارون من موسی إلا أنه لا نبی بعدی

“Ali okondedwa wanga! Iwe uli kwa ine ngati momwe adaliri Haroon kwa Mussa kupatula kuti pambuyo pa ine palibenso mtumiki wina ayi”.

Haroon adali mchimwene, mlowa m’malo , gavanala wa Mussa (A.S) ndipo Haroon ndi yemwe adasiyiridwa zonse zokhudzana ndi mtundu wa ana a Izrael koma Samiriy ndi yemwe adamukankhira Haroon kumbali powayitanira anthu kugwadira ng’ombe. Kodi simudawerenge Hadithiyi?
Pankhani yokhudzana ndi ulemelero wa Ali (A.S)
Kodi simudawerenge Aya ya Quran yomwe ikuti:

والسابقون السابقون أولئک المقربون

Kodi ndi ndani yemwe adayamba kukhulupilira za mtumiki Muhammad (S.A.A.W) ndi Chisilamu ndipo olo ndi pang’ono pomwe kuyambira nthawi yomwe adabadwa sadagwadirepo mafano? Kupatula kuti adali Ali Ibn Abi Talib (A.S).
Kodi simudawerenge mu Quran Aya yomwe ikuti:

یاأیها الرسول بلغ ما أنزل إلیک من ربک و إن لم تفعل فما بلغت رسالته

“Ee iwe mtumiki! Lalika zomwe zakutsikira iwe kuchokera kwa bwana wako ndipo ngati siutero ndiye kuti siudafikitse komanso siudakwanitse utumiki wako”.

Kodi mwayiwala nkhani ya Ghadir kuti m’ngelo Jibril adatsika kokwana katatu ndi kumamuwuza mtumiki wa Mulungu kuti:
Ee iwe mtumiki! Fikitsa kwa anthu zomwe zachokera kwa Mulungu wako.

و إن لم تفعل فما بلغت رسالته

Aya ikupitiliza kunena kuti:
“Ngati siufikitsa ndi kuwawuza anthu nkhani yokhudzana ndi utsogoleri ndi u Imamah wa Ali ndiye kuti utumiki wako siwudachitike”.

Munthu amene angamukankhe Ali (A.S) kumbali ndiye kuti Mulungu wake ndi Mulungu amene adzatha kumuwona ndi maso ake pa tsiku la Qiyamah.
Utumiki udzakhala ukutsutsidwa ndi kukanidwa.
Malamulo a Mulungu (Ahkam) adzakhala akutsutsidwa.
Zikhulupiliro zidzakhala za bodza.
Mwachoncho iwe mtumiki usawope kulalika nkhani imeneyi chifukwa cha kuti:

و الله یعصمک من الناس

“Ndipo Mulungu adzakuteteza kuchokera kwa anthu (omwe adzafuna kukubweretsera mavuto chifukwa cha nkhaniyi)”.

Mulungu akudziwa kuti panthawi yomwe mtumiki adzifikitsa uthengawu kwa anthu, makalata ambiri adzalembedwa, mabukhu adzalembedwa omwe adzakhala akulongosola kuti adzamukankhe bwanji Ali (A.S) kumbali pakusakhala kwake mtsogoleri, koma Mulungu ndiyemwe adzasunga ndi kuyang’anira nkhani imeneyi. Fikitsa nkhani imeneyi ndipo Mulungu adzakuteteza.
Zowonadi ndipomwe tikuwona kuti pankhani yokhudzana ndi Sahifa Mal’un yoyamba pomwe ankafuna kumupha mtumiki wa Chisilamu munjira ya pakati pa mzinda wa Madina ndi Makka, Mulungu adamuteteza mtumiki.
Ee iwe amene uli mu tsiku lako loyamba m’manda! Kodi siwudawerenge mu Quran Aya yomwe ikuti:

یا أیها الذین آمنوا اتقوا الله وکونوا مع الصادقین

“Ee inu okhulupilira! Muwopeni Mulungu ndipo khalani ndi anthu onena zowona”.

Kodi anthu onena zowona omwe akuwalongosola mu Ayayi ndi ndani mu Ummah wa chisilamu pambuyo pa mtumiki (S.A.A.W)?
Zikupezeka mu bukhu la Ahalsunna la Sahih Muslim kuti Ali (A.S) adanena kuti:
“Ngakhalenso inuyo maganizo anu adali oti ine ndi wabodza”.
Kodi Sadiq (wachilungamo ndi onena zowona) ndi ndani? Kodi ndi Ali Ibn Abi Talib (A.s) kapena ndi ena?
Kodi inu simudawerenge kuti mtumiki wa Mulungu (S.A.A.W) adanena kuti:

إنی تارک فیکم الثقلین کتاب الله و عترتی أهل بیتی لن یفترقا حتی یردا علی الحوض

“Ndithudi ine ndikukusiyirani zinthu ziwiri zolemera (za mtengo wa patali), bukhu la Mulungu (Quran) ndi akunyumba kwanga (Ahalbait) sizidzasiyana, mukazigwirizitsa ziwirizi ndithudi mpakana kalekale simudzasochera ndipo mpakana zidzandipeza ine pa chitsime cha Hawz patsiku la Qiyamah.
Funso apa ndi lakuti:
Bukhu la Mulungu zowonadi lili m’manja mwathu kodi mtumiki wa Mulungu (S.A.A.W) adalakwitsa polankhula mawu amenewa kuti powonjezera Quran mugwirizitsenso akunyumba kwanga? Kodi padakali pano palibe Ahalbait? Ndichifukwa chiyani simudakhulupilire za Imam Mahdi (A.A.T.F) kukhala mtsogoleri komanso Imam wa Nthawi yanu?
Kodi simudawerenge m’mahadith ambiri pomwe mtumiki wa Mulungu (S.A.A.W) akunena kuti:

إنما مثل أهل بیتی کمثل سفینة نوح من رکبها نجا و من تخلف عنها غرق

“Ndithudi chitsanzo cha Ahalbait anga chiringati chombo cha Nowa (A.S) aliyense yemwe adakwera chombo chimenechi adapulumuka ndipo yemwe adasemphana nacho adamira”.
Munthu yemwe adasemphana ndi chombo chimenechi ngakhale atakhala mwana wa Nowa (A.S) kapena munthu yemwe angafune kukwera pa phiri lokwera kwambiri adzamira.
Mtumiki (S.A.A.W) adatiwonetsa kale njira ya chipulumutso komwe kuli kutiwuza gulu lomwe lili lopambana kuchokera m’magulu 73 omwe adawanena kuti adzapezeka mu Ummah wake. Mwachoncho ngati munthu osatenga njira yachipulumutso imeneyi pambuyo poti zawonekera poyera kwa iye limenelo ndi vuto lake.
Nkhani imeneyi idzafunsidwa mu usiku oyamba wa m’manda. Ngati munthu wayankha yankho lolondola ndiye kuti ndi zabwino zokhazokha koma ngati sitidzapereka yankho lolondola chidzachitike ndi chiyani?
Tidanena kale kuti ife ndi alendo padziko lino la pansi ndipo tiri ndi nthawi yochepa kwambiri, zotsatira zake ndi kunong’oneza bondo basi.
Ee inu akulu akulu olemekezeka amene simudawatenge Madh’hab a Ahalbait (A.S) kukhala njira yanu yoyenera kutsata! Ngati mu usiku oyamba wa m’manda mwathu adzatifunsa kuti kodi simudawerenge Hadith iyi yomwe idanenedwa mochuluka m’mabukhu ovomerezeka anu omwe, mudzayankha chiyani?

إن هذا الأمر لا ینقضی حتی یمضی فیه اثنی عشر خلیفة

“Chimbedzochi sichidzatha kufikira kuti mudzadutse muchipembedzochi ma Khalifah (atsogoleri) okwana khumi ndi awiri (12)”.

Kutanthauza kuti kufikira kuti chipembedzo cha Chisilamu chiripo ma Khalifah okwana 12 ayenera kukhalapo potenga ulamuliro wa chipembedzo ndi kukhala atsogoleri.
Tikuyenera kuti tiwatchule ma Khalifawa mayina awo kuti ndi ndani?
Kodi simudawerenge Aya ya Quran kuti:

کل شیئ أحصیناه فی إمام مبین

“China chirichonse tidachisunga mwa Imam owonekera poyera”.

Kodi Imam owonekera ameneyu yemwe akutchulidwa mu Surah Yasin ndi ndani?
Ndichifukwa chiyani sitidazipezere Imam mpakana pano?
Mulungu akulankhula mu Quran yolemekezeka kuti:

یوم ندعوا کل أناس بإمامهم

“Kumbukirani tsiku limene tidzawayitana anthu onse (patsiku la Qiyamah) ndi Imam wawo”.

Imam ameneyu ndi ndani?
Anthu omwe mudamutenga Malik, Abu Hanifa, Shafi ndi Hambali kukhala atsogoleri anu, kodi Quran ndi yomwe idakuwuzani kuti muwatenge iwo kukhala atsogoleri anu? Kapena hadith idakuwuzani kuti muwatenge iwo kukhala atsogoleri anu?
Mukuwatsatirawo ndi anthu omwe adabadwa pambuyo pa zaka 80 chimwalilireni mtumiki wa Mulungu (S.A.A.W).
Kodi zidzakhala bwanji kwa asilamu omwe adalipo atsogoleriwa asadabadwe?
Munthu amene akufuna kumulungosola mtumiki wa Mulunguyu ndi amene olo ndi pang’ono pomwe sadamuwone mtumiki.
Koma chikhulupiliro cha chisilamu chenicheni chikuti chiyani?
Chikuti panthawi imene mtumiki wa Mulungu kapena mlowa m’malo akusankhidwa ndi Mulungu kukhala mtsogoleri, alinso ndi mlowa m’malo wake ndipo mlowa m’maloyo akusankhidwanso ndi Mulungu. Mwachoncho anthu ndi cholinga chofuna kuthetsa mavuto awo akuyenera kupita kwa munthu uyu amene akusankhidwa ndi Mulungu kukhala mtsogoleri wawo. Ndipo wadziwitsidwanso kwa anthu ndi mtumiki kapena mtsogoleri wa pambuyo pake.
Mtsogoleri ameneyu ndiye mtsogoleri weniweni.

یوم ندعوا کل أناس بإمامهم

“Kumbukirani tsiku limene tidzawayitana anthu onse (patsiku la Qiyamah) ndi Imam wake”.

Ameneyu ndiye Imam akufunidwa mu Ayayi. Ndi chifukwa chiyani sitidaganizebe mpakan pano?
Quran ikuchita kulongosola mowonekera poyera kuti:

قل کفی بالله شهیدا بینی و بینکم و من عنده علم الکتاب

“Nena iwe (mtumiki kwa anthu okanirawo) kuti: Wakwanira Mulungu kukhala mboni kwa ine ndi inu ndi yemwe ali ndi kuzindikira kwa bukhu”.

Ndichifukwa chiyani simudapite ndi kukasankha chinthu chomwe Mulungu akuchisankha ndi mtumiki wake kukhala chowakwanira. Kodi yemwe ali ndi kuzindikira kwa bukhu ndi ndani?
Ndichifukwa chiyani simudamutenge munthu amene angathe kukuthandizani inu pa mavuto a uzimu, chipembedzo, adziko ndi zina zotero? Musankheni iye kukhala m’thandizi kwa inu chifukwa chakuti iye ndi amene ali mlumikizi pakati pa inu ndi Mulungu.
Kodi simudamve zokhudzana ndi Surah Tawbah kuti poyamba mtumiki adamupatsa Abubakar kuti akawawelengere anthu aku Makka, panthawi imene adanyamuka ali mnjira, mngelo Jibril adamutsikira mtumiki (S.A.A.W) ndipo adamuwuza kuti uthenga umenewu palibe amene angawufikitse kwa anthu okanira kupatula kuti ukhale iwe mwini kapena munthu ochokera mwa iwe.
Mtumiki wa Chisilamu adamuwuza Ali (A.S) kuti iwe pita kwa Abubakar ukalande Surah ija chifukwa chakuti ndi Mulungu amene watsitsa uthenga umenewu. Kutanthauza kuti Ali (A.S) ndi yemwe adali ochokera mwa mtumiki (S.A.A.W).
Ndi chifukwa chiyani munthu sakukhala ndi funso pamenepa kuti kodi Abubakar sadali ochokera mwa mtumiki? Ngati mtumiki adamutumiza Ali kuti akalande Surah ija kuchokera kwa Abubakar ndiye kuti Sadali ochokera mwa mtumiki. Ndiye ndi chifukwa chiyani Abubakar sadali ochokera kwa mtumiki wa Mulungu?
Ndichifukwa chiyani sitidadzifunse funso limeneli? Kodi usiku oyamba m’manda mwathu tidzakwanitsa kuyankha kuti sitimadziwa kumachita kuti zimakhala zikukambidwa ndi anthu ambiri? Komanso padziko lino lapansi mukadatha kupeza njira zosiyana siyana zomwe zikadatha kukuthandizani pokulongosolerani zinthu ngati zimenezi.
Kodi simudamve kuti Khalifa oyamba adali akunong’oneza bondo kumapeto a umoyo wake pomwe ankati:
“pali ntchito zitatu zomwe ndidapanga zikadakhala bwino ndikadapanda kupanga”
Imodzi mwa ntchito zitatuzo ndi:
“ndikadapanda kutsekula nyumba ya Fatima (S.A), ndikadapanda kuwotcha nyumba yake, ndikadapanda kuyalutsa ulemu wake”
Fatima amene mkwiyo wake ndi mkwiyo wa Mulungu ndi mtumiki wake ndipo mkwiyo wa Mulungu ndi mtumiki uli ndi mavuto apano padziko lapansi ndi tsiku lomaliza.
Ndichifuka chiyani sitikudzifunsa kuti kodi iye adapanga zoipa zazikulu bwanji kunyumba ya Fatima (S.A) kuti mpakana akhale akudandaula ndi kunong’oneza bondo chonchi kumapeto a umoyo wake? Ndikumati bola ndikadapanga kutero.
Adapitiriza mukudandaula pomwe amati:
“ndikadapanda kuvomereza utsogoleri omwe adandipachika nawo pa Saqifah”
Ndichifukwa chiyani sitikumadzifunsa kuti kodi iye chomwe amadandaula ndi chiyani? Ndimayesa utsogolera, Khilafah, ndi Wilayat amasankha ndi anthu kuti ndi m’mene angafunire amusankhe munthu yemwe akumufuna.
Kodi chipembedzo cha mtumiki wathu okondedwa ndi chapansi choncho komanso chopanda ndondomeko kuti munthu wina aliyense ndi m’mene angafunire anene kuti ndikhala Khalifa kapena sindikhala?
Khilafat, Imamat ndi Wilayat ndi chinthu chomwe Mulungu wapamwamba ndiyemwe amasankha.
Kodi Khalifah oyamba adali wachisoni kwambiri ku chisilamu kuposa mtumiki kuti kumapeto a umoyo wake adasankha mlowa m’malo wake? Kodi mtumiki sadasankhe mlowa m’malo?
Kodi Khalifah Wachiwiri adali wachisoni kwambiri ku chisilamu kuposa mtumiki kuti kumapeto a umoyo wake adasankha mlowa m’malo wake koma mtumiki sadasankhe?
Kodi amenewa ndi mawu olemera bwanji?
Kodi simudamve kuchokera m’mabukhu ovomerezeka kwambiri osakhala a Shia zokhudzana ndi nkhani zimenezi.
Padakali pano sitiri ndi cholinga chonena adilesi ya zimenezi kuti zikupezeka kuti, koma tangoyerekezani kuti ndi usiku wanu oyamba m’manda.
Usiku oyambawu ndi usiku omwe anthu amene sadali munjira yowongoka azikati:

رب ارجعونی لعلی أعمل صالحا فیما ترکت

“Bwana wanga ndibwezeretseni ine padziko kuti ndikapange zabwino pa zomwe ndidasiya”.

Ndipomwe adzayankhidwa kuti:

کلا إنها کلمة هو قائلها و من ورائهم برزخ إلی یوم یبعثون

“Ayi sichoncho, amenewo ndi mawo chabe omwe iye akungowalankhula ndipo pambuyo pawo kuli Barzakh – yomwe iwo akakhalako – mpakana tsiku lomwe azadzutsidwa kuchokera m’manda”.
Sizingatheke, tidakupatsani nthawi ndi mpata ndi zonse zoyenelera ndipo tidafikitsa chiwongoko kwa inu koma chifukwa cha tsankho lanu simudamve pa zomwe njira ya chilungamo imanena.
Kodi simudamve kuti panthawi yomwe Abubakar adamuvutitsa mwana wa mkazi wa mtumiki, Fatima (S.A) adamuwuza mwamuna wake Ali (A.S) kuti anthu amene adandimenya ine, adawotcha nyumba yanga, adapangitsa kuti mwana wanga Muhsin aphedwe ali m’mimba mwanga sindikufuna kuti adzapezeke nawo panthawi yakundiika ine m’manda.
Kodi munthu amene adapanga zinthu zoterezi kwa bwana wa amayi ku Jannah angakhale Khalifa wa asilamu?
Ndichifukwa chiyani simukukawona nokha m’mabukhu anu kumene? Ndichifukwa chiyani simudafufuze nokha kuti mukawone kuti kodi zomwe zikunenedwazi ndi zowona kapena bodza?
Simudamve kuti Khalifa wachiwiri nthawi yaitali ali mu Shirk asadalowe chisilamu, adali akuwavutitsa akazi a asilamu ndi kuwamenya, munthu amene kale lake lidali Shirk, kumwa mowa ndi kuvutitsa anthu omwe adali asilamu.
Kodi munthu otereyu angakhale Khalifa wa asilamu? Chabwino zingatheke kunena kuti walowa chisilamu ndipo ndi msilamu koma osati mpakana kufika pa mlingo oti ndi Khalifa wa asilamu.
Titayang’ana kwa atumiki onse, kodi pali mtumiki amene kale lake lidali Shirk ndikupondereza?
Ndichifukwa chiyani olo ndi pang’ono pomwe sitidaganize? Bwanji tikungowonetsa tsankho lopanda phindu?
Zingatheke munthu amene akumunena mtumiki kuti wapenga sakudziwa chomwe akulankhula, kukhala Khalifa wa asilamu?
Panthawi yomwe mtumiki wa Mulungu adanena kuti ndibweretseleni cholembera ndi pepala kuti ndikulembereni chinthu chomwe simudzasochera mpakana kalekale komanso simudzakangana, ndichifukwa chiyani Khalifa wachiwiri Umar adadzuka nanena kuti musiyeni munthu ameneyu wapenga ndi matenda sakudziwa chomwe akulankhula. Mtumiki yemwe samalankhula zopanda phindu komanso zachabe mukakhalidwe kena kalikonse komwe angakhale nako, alibwino, akudwala kapena wagona kumene ndipo china chirichonse chomwe iye amalankhula chidali Wahay (uthenga wa Mulungu).

وما ینطق عن الهوی إن هو إلا وحی یوحی

Kodi munthu amene akumunena mtumiki kuti wapenga angakhale Khalifa wa mtumiki?
Kodi munthu amene adapangitsa kuti maswahaba a mtumiki okwana 15000 kapena 20000 adzaphedwe patsogolo pake angakhale ovomerezedwa ndi Mulungu komanso mtumiki wake ndikumati ndi Khalifa wa asilamu?
Ndichifukwa chiyani tangokhala sitikupita kukafufuza za munthu amene munthawi yake ya utsogoleri adapondereza anthu ambiri muchisilamu ndipo mapeto ake anthu ambiri maswahaba a mtumiki adabwera kuchokera Madera osiyana siyana ndikusonkhana kunyumba yake ndikumati munthu ameneyu watuluka muchisilamu ndipo mapeto ake asilamu omwewo ndi omwe adakhamukira kunyumba yake ndikumupha. Yemwe ali Khalifa wachitatu.
Ngati maganizo a anthu omwe adali akukhala munthawi ya Khalifa wachitatu omwe adali maswahaba a mtumiki ndi oti iye adatuluka muchipembedzo ndipo mapeto ake ndikumupha – kufikira kuti asilamu sadalole kuti mtembo wake uyikidwe pafupi ndi mtumiki wa Mulungu, Abubakar ndi Umar, mtembo wake udakhala masiku atatu uli pansi kenako adamuyika m’manda mwa Ayuda ndipo adayikidwa usiku. Pambuyo pake Muawiyah adawakulitsa manda asilamu ndipo nthawi imeneyo ndipomwe zidawoneka kuti ali m’manda mwa asilamu – ndiye maganizo a munthu ngati ine akhala otani pa munthu ameneyu?
Funso ndi lakuti ngati maganizo a asilamu anthawi imeneyo omwe ali maswahaba maganizo awo adali otere pa munthu ameneyu, nanga kulibwanji ine munthu wamba komanso pambuyo poti padutsa zaka zambiri kufikira pomwe ndiripa, kodi ndikuyenera kufufuza bwanji pokhudzana ndi chipembedzo changa?
Ndichifukwa chiyani sindidapite kukafufuza kuti kodi mawu omwe ndikuwamvawa ndi zowona kapena bodza?

کانت بیعة أبی بکر فلتة وقی الله من المسلمین شرها فمن عاد إلی مثلها فاقتلوه

“Kudachitika kumuvotera ndi kumusankha Abubakar mopupuluma ndi mopanda kuganiza Ndipo Mulungu adachotsa kuyipa kwake kuchokera kwa asilamu ndipo munthu amene adzapanga zinthu ngati zimenezi mudzamuphe”.
Kodi chinthu chomwe chikupangidwa popanda kuganiza ndi nzeru mkati mwake, chingakhale ndi gawo mchipembedzo cha Chisilamu?
Ndichifukwa chiyani simudakafufuze zokhudzana ndi nkhani imeneyi kuti ndi zowona kapena bodza?
Ngati zingakhale zowona kodi ife tidzamvamo chiyani kuchokera munkhani imeneyi?
Pomwe tikuwona kuti Khalifah oyamba nthawi zambiri adali akunena kuti:

أقیلونی أقیلونی فلست بخیرکم وعلی فیکم

“Ndichotsereni chinthu chomwe mudandipachika nacho chifukwa chakuti ine siwabwino kwa inu kumachita kuti Ali ali pakati panu”.

Sitikudziwa kuti ndi chifukwa chiyani adalankhula mawu amenewa zimenezo zikhale apo. Koma ndi zodziwika bwino kuti adalankhula mawu amenewo kuti ndichotsereni utsogoleriwu chifukwa ine siwabwino kwa inu panthawi yomwe Ali (A.S) ali pakati panu.
Ndichifukwa chiyani sitidapite kukaganiza bwino lomwe kuti munthu amene ali Khalifa wa asilamu, yemwe amayenera kuti akhale munthu ozindikira ndi wanzeru kwambiri kuposa anthu ena, nthawi zambiri ndichifukwa chiyani adali akunena kuti:

لولا علی ابن أبی طالب لهلک عمر

“Pakadapanda Ali Ibn Abi Talib, Umar akadawonongeka”.

Kodi ndi zomveka kuti munthu amene akuyenera kukhala Khalifa wa asilamu, akhale ndi kuzindikira kochepa poyerekeza ndi asilamu onse? Ndiyesa akuyenera kukhala munthu ozindikira bwino lomwe pa masunna a mtumiki wa Mulungu ndi bukhu la Mulungu kuti adzathe kuzigwiritsa ntchito bwino komanso moyenera mudziko la asilamu?
Ndichifukwa chiyani simudapite kukafufuza kuti munthu amene angaukire Khalifa wa asilamu ndiye kuti watuluka muchipembedzo cha Chisilamu?
Kodi pa nkhondo ya Siffin, Muawiya sadaukire ndi kusemphana ndi Khalifa wa asilamu yemwe ali Imam Ali (A.S), Khalifa amene utsogoleri wake udali wamphamvu komanso wachilungamo kuposa ma Khalifa onse omwe anadutsa?
Pomwe asilamu onse adabwera mu mzikiti ndi kuvotera utsogoleri wa Ali Ibn Abi Talib (A.S) koma iye sadapange.
Ngati munthu amene akusemphana ndi kulimbana ndi Khalifa wa asilamu ndiye kuti simsilamu nanga kulibwanji kukhala Khalifa wa asilamu?
Kodi Muawiya adabweretsa mavuto akulu bwanji mu Chisilamu?
Ena mwa mavuto omwe adabwera mu Chisilamu chifukwa cha Muawiya, ndiko kupha chidzukulu cha mtumiki, bwana wa anyamata ku Janna komanso bwana wa anthu ofera munjira ya Mulungu yemwe ali Husein Ibn Ali (A.S) ndi kuwayendetsa mtunda wawutali anthu akunyumba ya mtumiki wathu ndi Zainab (S.A).
Kodi munthu ngati ameneyu tingamutenge kuti ndi msilamu? Kodi ali ndi gawo mu Chisilamu? Nanga kulibwanji kukhala kwake Khalifa wa asilamu?
Usiku wathu oyamba m’manda adzatifunsa kuti Aya yoti:

ذلک الکتاب لا ریب فیه هدی للمتقین

“Ili ndi bukhu lomwe mulibe chikayiko mkati mwake, ndi chiwongoko kwa anthu omuwopa Mulungu”.

Zowonadi mulibe chikayiko m’bukhu limeneli ndipo ndi chiwongoko.
Funso ndi loti:
Kodi akamati bukhu akutanthauza kuti chiyani? Bukhu lake ndi lomweli la mapepalali lomwe lili m’manja mwathu padakali pano kapena bukhu la Mulungu lake lomwe lili lolankhula lomwe ntchito yake ndi kulongosola zomwe ziri m’bukhu?
Ngati lingakhale bukhu lake lamapepalali ndiye kuti padzakhala mafunso ambiri kwabiri komanso chikayiko.
Nanga poti Quran tiri nayo mpakana pano sidakwanitse kuthetsa mikangano, kusemphana ndi kutsutsana maganizo komwe kulipo pakati pa asilamu!
Panthawi yomwe mtumiki wa Mulungu (S.A.A.W), adali ndi moyo, padalibe mkangano ndi kusemphana maganizo pakati pa asilamu, chifukwa chakuti mtumiki wa Mulungu amalongosola zenizeni zomwe zabwera mubukhuli. Kutanthauza kuti mtumiki adali Quran yolankhula (Qur’an Naatiq).
Ee akamberembere (Munafiqiin) adalipo koma palibe chomwe adapanga pofuna kusokoneza matanthauzo enieni a Quran.
Pomwe mtumiki adamwalira, bukhunso la Mulungu lolankhula lidapita. Nthawi iyinso ndi yomwe anthu adali ndi udindo oti apeze bukhu lolankhula pambuyo pa mtumiki lomwe lidzatha kuwawuza iwo matanthauzo enieni a bukhu la mapepalali. Koma zomvetsa chisoni ndi zakuti pomwe mtumiki adamwalira, bukhu lolankhula lidakankhidwa kumbali.
Ndichifukwa chiyani sitidaganize kuti tanthauzo la aya imeneyi ndi chiyani? Ngati Quran iri chiwongoko nanga ndi chifukwa chiyani asilamu akusemphana maganizo?
Kodi Quran yomweyi siyomwe ikudzilongosola yokha kuti mwa ine muli ma Aya ofanana fanana omwe simungathe kuwamva bwino lomwe matanthauzo ake kupatula anthu omwe ali ozama mukuzindikira?
Ndi chifukwa chiyani simudapite kuti mukawafufuze anthu omwe ali ozama pakuzindikira? Ndichifukwa chiyani simudapite kukamupeza mtsogoleri wa anthu owopa Mulungu pambuyo pa mtumiki Muhammad (S.A.A.W)? ndichifukwa chiyani simudayitenge Quran yolakhula yomwe ikulongosola bwino matanthauza a Quraniyi?
Kodi simudamve mu Hisitore kuti chimodzi muzochitika zomwe zidali zoyipitsitsa kwambiri pambuyo pa mtumiki wa Mulungu, ndiko kupha kopanda chisoni Swahaba wa mtumiki yemwe amatchedwa kuti Malik Ibn Nuwairah kudutsira mwa anthu omwe adali ndi gawo mu Ulamuliro opondereza.
Khalid Ibn Walid adamuwona mkazi wa Malik Ibn Nuwairah. Chifukwa chakuti mkazi wake adali owoneka bwino, adapha mwamuna wake yemwe ndi Malik, anadula mutu wake ndikuwuyika pamaso pa anthu ndipo mapeto ake adapanga chiwelewere ndi mkazi wake kenako adabwelera ndipo Khalifa oyamba adamubereka kumbuyo ndi kumumuteteza munthu ameneyu ponena kuti:

إجتهد و أخطأ

“Adapanga Ijtihad koma adalakwitsa”.

Ndichifukwa chiyani simukufufuza kuti muwone kuti kodi Khalifa oyamba adanenadi zimenezi kapena ayi? Ngati adanena kodi ine zidzanditanthauzira chiyani?

و ما أنا إلا کأحدکم فإذا رأیتمونی قد استقرت فتبعونی فإن زغت فقومونی

“Ine ndiri ngati m’modzi wa inu kumene, mukandiwona kuti ndiri mu njira ya chiwongoko nditsatireni ndipo ndikakhota ndi ongolereni chifukwa chakuti nthawi zina ndi makhala ndi Satana yemwe amandilowelera mwachoncho mukandiwona kuti ndakwiya muzinditalikira”
Khalifa amene alibe Ismah (kusachimwa), Khalifa amene Satana akumulowelera, Khalifa amene yekha akumanena kuti nthawi zina amandibwelera Satana ndipo mukandiwona kuti ndakwiya muzinditalikira, kodi Khalifa ameneyu angakhale Khalifa wa mtumiki, mtumiki wake amene idamutsikira Aya yakuti:

انما یرید الله لیذهب عنکم الرجس أهل البیت و یطهرکم تطهیرا

Kodi mathero ake a mtumiki ameneyu angakhale chonchi? Sizingatheke olo ndi pang’ono pomwe.
Kodi mu usiku wathu oyamba m’manda akamadzatifunsa kuti inu mudamva kuti mtumiki wa Mulungu (S.A.A.W) kumapeto a umoyo wake adakhazikitsa gulu la asilikali motsogozedwa ndi Usamah Ibn Zayd, ndipo mtumiki adawayika anthu omwe patsogolo pake adazitcha kuti ndi ma Khalifa a mtumiki, mu gulu la asilikaliwa kuti Usamah yemwe adali ndi zaka 18 akhale mtsogoleri wawo ndipo adawalamula kuti atsatire zomwe iye angawalamule ngati mtsogoleri. Mapeto ake anthu aja sadatsatire zonena za mtumiki ndipo adabwelera kunkhondo. Mtumiki adawatembelera anthu omwe adabwelera kunkhondowa posamutsatira Usamah pomwe adati?

لعن الله من تخلف عن جیش أسامة

“Mulungu awatembelere anthu omwe asemphana ndi gulu la Usamah”.
Ndi chifukwa chiyani sitidaganize kuti anthu amene mtumiki sadawasankhe kumene kukhala atsogoleri ankhondo ndipo m’malo mwake awalamula kuti akhale pansi pa ulamuliro wa Usamah mwana wa zaka 18 kukhala mtsogoleri wawo, kodi zingatheke anthu amenewa kukhala ma Khalifa a asilamu pambuyo pa mtumiki?
Ndipo Usamah mukululankhula kwake ankati: “Mtumiki wakulamulani kuti mumve zonena za ine”.
Chabwino, kameneka kadali kagulu kakang’ono kwambiri, koma mtumiki sakuwawona anthu amenewa kuti angakhale atsogoleri a gulu laling’onoli, nanga kuli bwanji Ummah onse wa asilamu?
Ndichifukwa chiyani sitidaganize kuti ndindani mwa ma Khalifawa adakwanitsa kutsata ma Sunna onse a mtumiki popanda kupungula kapena kuwonjezera?
Asilamu omwe siali Shia, amanena kuti mtumiki sadasankhe Khalifa wa pambuyo pake, kutanthauza kuti kwa iwo Sunna ya mtumiki pa utsogoleri idali kusasankha Khalifa.
Ngati zili choncho ndiye kuti Khalifa oyamba adaphwanya Sunna ya mtumikiyi chifukwa choti adasankha Khalifa wa pambuyo pake.
Khalifa wachiwiri adapanga mosemphana ndi Khalifa wachiwiri komanso mosiyana ndi mtumiki.
Iye adakhazikitsa Shura. Iyi ndiye Bidiah inanso, kodi sizimanenedwa kuti Bidiah ina iliyonse ndi ya kumoto?
Ndipo mapeto azimenezi adathera kwa Uthman yemwe tanena kale kuti asilamu kumene ndi omwe adamupha ndikukawuponya mtembo wake ku manda a ayuda.
Ndichifukwa chiyani sitidaganize kuti munthu amene angalimbane ndi kutsutsana ndi Khalifa wa mtumiki ndiye kuti walimbana ndi chisilamu kwenikweni Khalifa wake yemwe ali ovomerezeka ndi Mulungu komanso mtumiki wake.
Nkhondo ya Jamal komanso nkhondo ya Siffin idachitika chifukwa cha zomwezi komwe kuli kuwukira Khalifa wa asilamu yemwe adasankhidwa ndi Mulungu.
Ndichifukwa chiyani sitidatsatire zizindikiro za njira ya chiwongoko pambuyo pake ndipo chimodzi mwa zizindikirozo ndiko kutilongosolera kuti Ammar ali ndi chilungamo ndipo chilungamo chiri ndi iye.
Panthawi imene Ammar akulimbana ndi gulu la anthu ku nkhondo ndipo iye adali akuwayitanira ku chilungamo pomwe iwo adali akumuyitanira ku moto, zomwe mapeto ake akuphedwa ndi anthu omwe adanenedwa ndi mtumiki wa Mulungu kuti ndi anthu oyipitsitsa komanso opyola muyeso.
Ndichifukwa chiyani sitidaganize kuti kodi Ammar adamupha ndi ndani? Zomwe zidzatipangitsa kuti tidziwe kuti anthu omwe amawanena mtumiki ndi ndani kuti tiwatalikire.
Mwachidule, Ammar ndi amene adali ndi Imam Ali (A.S) pa nkhondo ya Siffin ndipo adaphedwa ndi asilikali a Muawiya.
Funso ndi lakuti: Ndichifukwa chiyani timamutenga Muawiya kukhala Khalifa wa asilamu? Muawiya wake amene adamuyika mwana wake Yazid kukhala Khalifa wa asilamu pambuyo pake ndipo Yazid wake amene adapandukira ndi kuwononga nyumba ya Mulungu Kaaba, adawononga mzinda wa mtumiki Madinah ndipo adapha Husein Ibn Ali (A.S) yemwe ali bwana wa ine ndi inu ku mtendere wa Mulungu.
Zolankhula ndi zambiri.
Ndichifukwa chiyani sitikuwasankha Madh’hab a Ahalbait (A.S) kukhala njira yathu yoyendamo? Madh’hab amene ngati ukufuna kupemphera uwonetsetse kuti Imam wa Swalayo ndi wachilungamo. Ngati Imam siali wa chilungamo ndipo amapanga machimo akulu akulu kapena amakakamila kupanga machimo ang’ono ang’ono, siukuyenera kupemphera kumbuyo kwake.
Zodandaulitsa ndi zoti tikuwasiya Madh’hab ngati amenewa ndikupita ku Madh’hab ena omwe amanena kuti osati Imam wa Salat yekha koma kuti ngakhale Khalifa kumene atha kukhala munthu opondereza.
Khalifa wake amene akukwanitsa kupha mwana okondedwa wa mtumiki, Khalifa amene akulimbana ndi kumenyana ndi munthu amene Quran ikumunena kuti ndi Nafs (mtima) wa mtumiki ndi kuwavutitsa komanso kupha ma Swahaba ambiri.
Kodi pali kusiyana bwanji pakati pa Madh’hab a Ahalbait (A.S) ndi Madh’hab oterewa?
Hadith ya mtumiki yomwe ikupezeka m’mabukhu osiyana siyana komanso ovomerezeka a Ahalsunna, pomwe mtumiki amanena kuti:

من مات و لم یعرف إمام زمانه مات میتة الجاهلیة

“Munthu yemwe angamwalire asakumudziwa mtsogoleri wa nthawi yake ndiye kuti wamwalira mu Imfa ya umbuli”

Kutanthauza kuti wamwalira ali okanira. Hadith imeneyi ikulamula iwe ndi ine kuti tisankhe mtsogoleri wa nthawi yathu.
Kodi inu abale anga okondedwa, mtsogoleri wa nthawi yanu yemwe ali ovomerezedwa ndi Mulungu ndi ndani?
Ndichifukwa chiyani sitidaganize kuti kodi Imam wa Fatima al-Zahra (S.A) ndi ndani?
Kodi ndi Abubakar kapena Umar omwe adamukwiyitsa iye kufikira kuti adamwalira kapena Imam wake ndi wina?
Ndichifukwa chiyani sitidamutenge yemwe adali Imam wa Fatima (S.A) kukhala Imam wathu?
Nkhani ikuwoneka kuti ndi yaitali, koma nkhani yathu ndi yotani padakali pano?

عم یتساءلون، عن النبإالعظیم، الذی هم فیه مختلفون، کلا سیعلمون، ثم کلا سیعلمون

Kodi anthuwa akufusana fusana za chiyani? Zankhani yaikulu kwambiri, nkhani yake yomwe sidzangokhala chonchi osadziwika chowona chake, anthu ndi kumangokanganabe. Mulungu adatipatsa kuzindikira ndi zida zosiyana siyana zomwe zingatithandize ife podziwira zinthu, mwachoncho sipatali iyayi, koma kuti ndiposachedwa tidzazindikira zowona za nkhani yaikuluyi.
Posachedwapa tidzazindikira zowona zake. Nthawi yoyamba ndi usiku oyamba wa m’manda mwathu pomwe tizikafunsidwa kuti Imam wathu ndi ndani? ukadzalephera kuyankha ndiye kuti zotsatira ndi zotani?

کلا سیعلمون

“Sichoncho iyayi adzazindikira posachedwapa”.

Kenako tidzafunsidwanso kachiwiri lomwe lili tsiku lomaliza

ثم کلا سیعلمون

“kenako ndithudi adzazindikira posachedwa”.

Kumapeto kwa Surat Nabai kuli Aya yomwe ikunena kuti:
یوم یقوم الروح و الملائکة صفا
Tsiku la Qiyama ndi nthawi imene angelo onse adzakhala ali chiyimire m’mizera.

لا یتکلمون إلا من أذن له الرحمن

Palibe amene akalankhula kupatula anthu amene Mulungu adawapatsa kapena adzawapatsa chilolezo cholankhula patsikulo.

Odzalankhula patsikuli akuyenera kudzakhala anthu omwe ali apamwamba kuposa angelo.
Kodi tirinso ndi anthu omwe ali apamwamba kuposa angelo? Ee alipo.
Ngati olemekezeka bambo wa anthu Adam (A.S) angelo adamupangira Sajda ndiye kuti palibe kukayikira ndithudi Adam (A.S) ndi wapamwamba kuposa angelo.
Palibe yemwe angatsutse kuti mtumiki wathu omaliza Muhammad (S.A.A.W) ndi wapamwamba kuposa olemekezeka Adam (A.S). Chonchonso ma Khalifa omwe adabwera pambuyo pa mtumiki, omwe adasankhidwa ndi Mulungu alinso ndi ulemelero umenewu.
Ife padakali pano tikulankhula za Imam wa nthawi amene Surat Qadr ikulankhula zokhudzana ndi iye kuti:

تنزل الملائکة و الروح فیها

“Amatsika angelo mu usiku umenewo”.

Kodi angelo ayenela kumutsikira ndani? Munthu wamba? Ndi zosatheka zimenezo.
Angelo amayenera kumutsikira mtumiki wa Mulungu. Nanga poti padakali pano mtumiki palibe?
Ee mtumiki palibe koma Khalifa wa mtumiki yemwe adasankhidwa ndi Mulungu, yemwe amapanga zinthu ndi chilamulo cha Mulungu alipo. Imam alipo, Imam wake ndi amene ngati siumudziwa ndiye kuti wamwalira ndi imfa yaumbuli (okanira).
Imam amene tikumulongosola apayu ndi yemwe uja amene akutchulidwa mu Surat Yasin kuti:

و کل شیئ أحصیناه فی إمام مبین

“Ndipo china chirichonse tidachisunga mwa Imam owonekera poyera”.
Imam ameneyu ndi amene adzakuyikira umboni kuti ndiwe ndani ndipo udali pa chilungamo kapena ayi? Ngati momwe Aya ikunenera pa za amene akuwona ntchito zathu komanso omwe ali mboni kwa ife.

و قل اعملوا فسیری الله عملکم وسوله و المؤمنون

“Ndipo awuze (iwe mtumiki) kuti gwirani ntchito ndipo Mulungu, mtumiki wake ndi anthu okhulupilira akuwona ntchito zomwe mukupanga”.

Ndi zachidziwikira kuti Mulungu sanama ayi. Mwachoncho zoti iye akuwona ndi zachidziwikire kwa wina aliyense, zotinso Mtumiki amawona ntchito zathu palibe yemwe angatsutse.
Koma nkhani ndi yakuti anthunso okhulupilira amawona ntchito zathu kodi zimenezi ndi zowona?
Kutanthauza kuti Mulungu anthu amenewa wapatsa mphamvu zoti azitha kuwona ntchito za anthu ena.
Kodi okhulupilirawa ndi ndani? asilamu komanso okhulupilira ndi ambiri kodi tiziti ife asilamu timawona zomwe ena amapanga?
Ee ntchito zomwe amapanga mowonekera ndi maso timaziwona, koma zomwe amapanga mobisika?
Nkhani yaikulu yagona pamenepa kuti kodi ndi anthu okhulupilira ake ati omwe Mulungu akuwapatsa mphamvu zoti aziwona ntchito za ine ndi inu ndikukhala mboni zathu?
Ndi anthu ake okhawo amene pambuyo pa mtumiki olo ndi pang’ono pomwe sadamukhumudwitse mtumiki kapena kupanga zosemphana ndi lamulo lake komanso muzichitochito zawo mulibe kuwonetsa Kufr kapena Shirk.
Ndi okhulupilira ake amene Mulungu adawapatsa mtendere wakusakhala kwawo ochimwa mu umoyo wawo wonse pomwe Quran ikunena kuti:

انما یرید الله لیذهب عنکم الرجس أهل البیت و یطهرکم تطهیرا

Mosabisa okhulupilira amenewa ndi omwe ali ma Imam komanso alowa m’malo osankhidwa ndi Mulungu pambuyo pa mtumiki.
Abale anga! Usiku oyamba m’manda mwathu ndi nthawi yopweteka komanso yovuta kwambiri. Ndikoyenera kuti tiganize bwino komanso tigwiritse ntchito bwino mawu amene akulongosoledwa apawa kuti atha kutithandiza ife kuti tisakakumane ndi zoterezi komanso tiwugwiritse ntchito bwino umoyo umenewu.
Mu Hadith ina mudanenedwa kuti umoyo wadziko lapansi siwungafaniziridwe ndi china chirichonse. Chifukwa chiyani?
Chifukwa chakuti ndi umoyo omwewu munthu atha kukhonzera umoyo wake wachisangalalo chosatha (Jannah) komanso atha kudzikhonzera kunong’oneza bondo kosatha (Jahannama).

ذلک الیوم الحق

“Tsiku la Qiyama ndi tsiku la chilungamo chokha chokha”.

Kulibe kupusitsa kapena kupanga chinyengo. Dzanja lidzayamba kulankhula, mwendo udzayamba kulankhula, maso, mphuno, mimba, makutu, khungu zidzalankhula koma kuti thupi lonse.

فمن شاء اتخذ إلی ربه مآبا

“Yemwe wafuna adzatenga malo kwa bwana wake”.

Kodi Mulungu adakuwuza zotsatira ndani pambuyo pa mtumiki?
Zomwe iye adasankha kapena zomwe anthu adasankha?

إنا أنذرناکم عذابا قریبا

“Ndithudi ife tikukuchenjezani za mavuto apafupi”.

Limeneli ndi tsiku limene lidzayang’ane kale la munthu kuti kodi panthawi imene anthu adali padziko lapansi chilungamo chidali chiyani? Nanga munthuyo adatsatira chiyani?
Imam Khomeini akunena kuti Hadith Thaqalain ikukwanira kukhala umboni okwanira kwa anthu onse adziko la pansi.
Nditsiku lomwe anthu akafunsidwa kuti kodi adali otsatira Ahalbait (A.S) kapena ayi?

یوم ینظر المرء ما قدمت یداه و یقول الکافر یا لیتنی کنت ترابا

“Ndi tsiku limene munthu adzayang’ana zomwe adatsogoza ndi manja ake ¬– zomwe adachita – ndipo adzalankhula munthu okanira kuti bola ndikadakhala dothi”

Munthu amene wamva ndi kudziwa za Madh’hab achilungamo a Ahalbait (A.S) koma adabisa adzanena kuti bola ndikadakhala dothi.
Zidanenedwa mu Hadith kuti Ali Ibn Abi Talib (A.S) ndi Abu Turab (bambo a dothi).
Limodzinso mwa mayina omwe angatchulidwire ma Shia ndi Turab (dothi). Chifukwa chakuti dothi lili ndi maubwino ambiri komanso apamwamba koma anthu samazindikira za ma ubwino amenewa.
Mkaka omwe munthu akumwa ukuchokera ku dothi, zipatso zomwe akudya zikuchokera ku dothi, masamba kumene, nyama yomwe akudya ikuchokera ku dothi. Nanga zinthu zosiyana siyana zomwe munthu akugwilitsa ntchito kuti umoyo wake uyende monga kumangira nyumba ndi kupangira zovala ndi zokwera kumene zikuchokera kuti?
Zowonadi umenewu ndiwo ulemelero omwe Shia alinawo pokhala ndi bambo pambuyo pa mtumiki wathu Muhammad (S.A.A.W) yemwe ali bambo wadothi.
Ndipomwe mdani akuwona kuti Shia ali ndi kuzichepetsa komanso kupilira kufikira kuti adagwirizitsa popanda mantha Madh’hab awo mpakana adali akuteketedwa komanso akuteketedwabe pansi pa mapazi ngati dothi kumene monga momwe tikuwonera m’mayiko a Pakistan, Syria, Egypt, Iraq, Bahrayn ndi mayiko ena.
Ee Mulungu wathu! fikitsani mofulumira kuwonekera kwa Imam Mahdi (A).

 

 

 

 

Add new comment