Wahabi akuti zomwe zidamuchitikira Fatima (S.A) ndi bodza chifukwa Ali (A.S) adakhala chete

Wahabi akuti zomwe zidamuchitikira Fatima (S.A) ndi bodza chifukwa Ali (A.S) adakhala chete

بسم الله الرحمن الرحیم

Tikupepesa kwa mtsogoleri wa nthawi yathu ino Imam Mahdi (A.A.F.S) ndi asilamu onse chifukwa cha kufika kwa masiku omwe Imam Ali Ibn Abi Talib (A.S) adakhapidwa ndi lupanga la mankhwala (poison) ndi kuphedwa.
Limodzi mwa mafunso omwe amakhala akufunsidwa kuchokera kwa Wahabi pofuna kutsutsa pankhani ya kuphedwa kwa Hazrat Fatima al-Zahra (S.A)n ndi loti:
Panthawi yomwe anthu adapita kukaphwanya nyumba ya olemekezeka Fatima al-Zahra (S.A), ndichifukwa chiyani Amirul Mu’uminina Ali (A.S) sadalimbane ndikumenyana nawo anthu amenewa pofuna kuteteza banja lake? Ndichifukwa chiyani adakhala chete popanda chochita?
Zina mwa mbiri zomwe olemekezeka Ali (A.S) ali nazo ndi zoti;
Iye ndi yemwe adatsekula chitseko cha Khaibar.
Iye ndi amene adamugonjetsa Amur ibn AbduWod.
Chisilamu chidapita patsogolo chifukwa cha lupanga lake polimbana ndi anthu okanira.
Ngati zilichoncho, panthawi yomwe anthu adakhamukira kukaphwanya nyumba ya Fatima al-Zahra (S.A), kodi Ali (A.S) adalibe mphamvu yolimbana ndi anthu amenewa?
Kodi iye panthawi imeneyi adali ndi mantha?
Kodi iye adalibe udindo oteteza banja lake?
Wahabi pambuyo pofunsa mafunso amenewa modabwa, mapeto ake amanena kuti:
Ali amene tikumudziwa ife munkhondo zosiyanasiyana monga; Uhud, Badr, Khandaq, Khaibar ndi malo ena ndichifukwa chiyani sakuteteza banja lake? Zomwe ngakhale mu mabukhu a Hisitore sizidapezekemo kuti iye adateteza mkazi wake.
Mwachoncho Ali ameneyu monga momwe tikumudziwira mumphamvu zake, ndithudi amayenera kuti ateteze mkazi wake.
Mwachoncho chifukwa choti mafunso amenewa alibe yankho, nkhani yakupandukira kunyumba ya Fatima al-Zahra (S.A) ndi yabodza komanso yopeka.
Izi ndi zomwe amalongosola Wahabi pofuna kutsutsa nkhani imene idachitikayi.
Ife padakali pano tiri ndi mayankho angapo pamafunso amenewa.
Choyamba chomwe tiyenera kupanga ndi chakuti, tilifufuze bwino bwino funso limeneli mkati mwake kuti:
Kodi yemwe akufunsa funso limeneli ndi ndani?
Nanga ali ndi cholinga chanji pofunsa funso limeneli?
Kodi pofunsa funsoli akufuna kupeza yankho kapena kuti alibe chiyembekezo choti pangakhalenso kulankhula ndi kuyankha pafunsoli, ndipo mapeto ake chifukwa choti palibe yankho lake, ndiye kuti nkhani imeneyi ndi yabodza komanso yopeka.
Kawiri kawiri anthu otsatira chiphunzitso cha Wahabi omwe adatsatira zochitika za Saqifah, samafunsa funsoli ndi cholinga choti apeze yankho, koma kuti amafunsa ndi cholinga choti atsutse nkhani yodandaulitsa yomwe idamuchitikira mwana wa mtumiki Muhammad (S.A.A.W) Fatima al-Zahra (S.A).
Imeneyi ndi fundo yoyamba yomwe munthu wina aliyense ofuna kudziwa chilungamo ayenera kuidziwa.
Ife ngakhale tingakwanitse kuyankha funsoli kapenanso osakwanitsa kuyankha, koma nkhani yokhudzana ndi kupandukira, kuyalutsa komanso kumenya ndi kuvulanza Fatima al-Zahra (S.A) ndi zina zotero, ndi yodziwika bwino komanso ndiyovomerezeka kwa wina aliyense yemwe akudziwa za Hisitore ya chisilamu.
Olemekezeka Fatima al-Zahra (S.A) adamenyadwa, chitseko cha nyumba yake chidaphwanyidwa ndi kuyatsidwa moto, ndipo adabayidwa mimba yake ali oyembekezera zomwe zidapangitsa kuti msomali wa chitseko udabaya mwana yemwe adali m’mimba mwake otchedwa Muhsin (A.S) ndipo adamwalira ali m’mimba komanso mapeto ake Fatima al-Zahra adayamba kudwala kwambiri chifukwa chabala limenelo ndipo mapeto ake posakhalitsa adamwalira momvetsa chisoni.
Olemekezeka Fatima al-Zahra (S.A) adakwiya chifukwa cha ma Khalifah awiri (oyamba ndi wachiwiri) ndipo adatalikirana ndi iwo.
Kukwiya kwa Fatima al-Zahra (S.A) ndi kukwiya kwa Mtumiki wathu ndipo kukwiya kwa mtumiki wathu Muhammad (S.A.A.W) ndi kukwiya kwa Mulungu, pomwe mkwiyo wa Mulungu ndiwo mavuto akulu kuyambira pano padziko lapansi mpakana tsiku lomaliza.
Zonsezi ndi zodziwika komanso zovomerezeka ngakhale kuti funso lija layankhidwa kapenanso osayankhidwa. Koma Inshaallah funso limeneli liyankhidwa.
Zonsezi ndi zodziwika bwino lomwe kufikira kuti panthawi yomwe olemekezeka Fatima al-Zahra (S.A) adatalikirana ndi kukwiyitsidwa ndi Khalifah oyamba ndi wachiwiri, adamuwuza mwamuna wake Ali (A.S) kuti ndikadzamwalira udzandisambitse usiku, udzandimveke nsanda usiku, udzandipemphelere usiku komanso udzandiyike m’manda usiku ndicholinga choti zisazadziwike kuti ndidayikidwa kuti ndipo anthu patsiku la Qiyamah adzayikire umboni kuti ndidakwiyitsidwa ndi kuvutitsidwa ndi oyamba komanso wachiwiri.
Tikuwonanso kuti Fatima al-Zahra (S.A) sadawatenge iwo kukhala atsogoleri ake ndipo sadatsatire zochita ndi zonena zawo.
Adalamula kuti ayikidwe usiku ndi cholinga choti panthawi yomwe munthu wina aliyense opita ku Madinah akafika pa manda a maswahabah nayamba kufunsa kuti manda awa komanso awa ndi andani? Ndipo akadzayankhidwa kuti mwini wake ndi ndani? adzakhala odabwa powona kuti manda awina aliyense alipo koma manda a munthu amene ali wapamwamba kwambiri pambuyo pomwalira mtumiki yemwe ali Fatima al-Zahra (S.A), manda ake sakupezeka.
Zonsezi ndi cholinga choti munthu akapanda kuwapeza manda ake adzayambe kufufuza za nkhani imeneyi kuti ndi chifukwa chiyani zilichoncho ndipo pofufuza yankho lake adzakumane ndi njira yomwe ili yachilungamodi omwe ndi Madh’hab a Ahalbait (A.S).
Koma ndicholinga choti tiyankhepo mongolozera pankhani imeneyi tidzagwiritsa ntchito mabukhu akuluakulu ovomerezeka a Ahalsunnah monga, bukhu la Sahih Muslim, Sahih Bukhariy, Musnad Ahmad Hambaliy ndi bukhu la Musnad Fatima Suyuti.
Nkhani ya kupandukira kunyumba kwa Fatima al-Zahra (S.A)
1- Kuchokera mu bukhu la Sahih bukhari, Hadith 3913 komanso bukhu la Sahih Muslim, Hadith 3304.

فوجدت فاطمة علی أبی بکر فی ذلک فهجرته فلم تکلمه حتی توفیت

Awa ndi mawu omwe akupezeka m’mabukhu odalirika kwa Ahalsunna.
Funso lathu kwa anthu omwe akufunsa mafunso amenewa ndi loti:
Ndi chifukwa chiyani Fatima al-Zahra (S.A) sadalankhulane ndi Abubakar komanso Umar kufikira kuti adamwalira? Chidachitika ndi chiyani?
2- Kuchokera mu Sahih Bukhariy ndi Musnad Ahamad,

فغضبت فاطمة بنت رسول الله فهجرت أبا بکر فلم تزل مهاجرته حتی توفیت

Adakwiya Fatima mwana wa mtumiki ndipo adatalikirana ndi Abubakar, ndipo kutalikirana ndi Abubakar kudapitilira kufikira kuti adamwalira
Apa okondedwa anga ndipofunika kukhala oyang’anitsitsa kwambiri chifukwa chakuti zonsezi tikuzilongosola kuchokera m’mabukhu a Ahalsunnah kumachitika kuti eni ake mabukhuwa akusemphana ndi nkhani zomwe ziri m’mabukhu awo kumene.
Ndipomwe tikuwona kuti ngakhale adayesetsa kuyambira kale kufuna kufafaniza chilungamo m’mabukhu awo kumene komabe mpakana pano chilungamo chikupezekabe m’mabukhuwa.
Fatima (S.A) amene ndi momwe Hadith ya mtumiki (S.A.A.W) ikunenera mowonekera poyera kuti mkwiyo wake ndi mkwiyo wa mtumiki ndi Mulungu ndipo mkwiyo wa Mulungu ndiwo mavuto adziko lapansi lino mpakana ku Akhirah, apa zikuchita kuwonekera poyera kuti iye adakwiyitsidwa ndi oyambayo, adatalikirana naye mpakana adamwalira ndipo sadalole kuti munthu adziwe kuti manda ake ali kuti.
3- Kuchokera mu bukhu la Musnad Fatima Suyuti, mukulongosoledwa nkhani kuti:
Abubakar akuchita kunena mowonekera poyera kuti mu umoyo wanga ndidapanga ntchito zitatu, bwanji ndidakapanda kupanga zimenezi!

وددت أنی لم أفعلها

Zikadakhala bwino kwambiri ndikadapanda kutsekula khomo la nyumba ya Fatima mwaupandu ndikuyatsa khomo la nyumbayi ndikulowa mnyumba ndikumutulutsa Ali Ibn Abi Talib mwamphamvu kuti akandivotere utsogoleri wanga, zomwe zidapangitsa kuti Fatima avulale ndipo kuvulala kwake zidapangitsa kuti mwana yemwe adali m’mimba mwake amwalire komanso zidapangitsa kuti posakhalitsa Fatima adamwalira yemwe ali mwana wa mtumiki wachisilamu.
China ndichoti zikadakhala bwino bwanji patsiku la Saqifah – pomwe adabwera ndikundipachika nawo ukhalifah – ndikadawapachika nawo utsogoleriwu iwo. Zaka ziwiri ndi miyezi ingapoyi yomwe ine ndakhala pa utsogoleri ndi yofunikira bwanji kuti mpakana ine ndidapanga zinthu zimenezi.
Palibe munthu yemwe angakanire nkhani imeneyi, kaya tidzakwanitsa kapena sitidzakwanitsa kuyankha funso la Wahabi lija.
Koma yankho lathu pa funso limeneli ndi lotani?
Yankho lomwe ife tidzapereka pano ndithudi wina aliyense yemwe siali Shia, adzayenera kumvetsetsa chifukwa chakuti umboni wathu utha kukhala wa nzeru kapena Qur’an kapenanso umboni omwe watengedwa kuchokera m’mabukhu osakhala a Shia.
Chikhulupiliro choyamba chomwe Shia alinacho ndichoti:
Imam amayenera kusankhidwa ndi Mulungu ndipo Imamuyo samayenera kupanga chinthu pokhapokha atalamulidwa ndi Mulungu ndipo samayenera kupanga zinthu mwa iye yekha ngati momwe zidachitikira kwa Musa (A.S) ndi yemwe adayenda naye yemwe amatchedwa kuti Khizr (A.S). kodi ndi chifukwa chiyani amapanga zimenezo?
Khizr (A.S) poyankha ankati ndikupanga izi ndi chilamulo cha Mulungu.

الإمام مأمور من عند الله

Ndi chifukwa chiyani Amirul mu’uminina (A.S) sadapange chirichonse ndipo adangokhala chete?
Chifukwa chakuti iye ndi Imam komanso Khalifa wa Mulungu ndipo amapanga zinthu ndi chilamulo cha Mulungu.
Kodi Mulungu adapanga chiyani pakuzitukumula komwe Iblis adapanga?
Kodi Mulungu adalibe mphamvu?
Kodi Mulungu siadali wachisoni kwa akapolo ake kuti Iblis ndiyemwe adzasokoneza akapolo ake ndikuwayitanira kukuwononga ndi uchimo?
Zonsezi Mulungu ankadziwa koma ndi chifukwa chiyani adakhala chete ndikuvomereza pempho la Satana Iblis?
Umboni wina uliwonse omwe mungakhale nawo pankhani yosamubweza Iblis pazochita zake ndiwomwenso ungaperekedwe pankhani ya kusatulutsa lupanga kwa Imam Ali (A.S) polimbana ndi anthu amenewa.
Mulungu ali ndi luntha komanso Mulungu amawayesa mayeso akapolo ake. Mulungu akufuna kuti zinthu ziyende monga mwachilengedwe. Pali lunthu lonzama kwambiri posamuletsa Iblis (Satana) zochitika zake.
Imam Ali (A.S) nayenso adakhala chete ndipo sadatenge lupanga ndi kulimbana nawo komanso kuwapha anthu amenewa chifukwa chakuti amapanga zinthu muchilamulo cha Mulungu komanso pali luntha (Hikmah) ina yake pazimenezi.
Mwachoncho ngati Ali (A.S) akupanga zinthu potsatira chilamulo cha Mulungu, ndipo limodzi mwa malamulo amenewa ndiko kukhala chete pa zomwe zidamuchitikira Fatima (S.A), kuti ee Ali! Ukuwona kuti Fatima akumenyedwa, ukuwona kuti akuvutitsidwa koma uyenera kupilira.
Malo angapo onse mtumiki wathu adakhala akumuwuza Ali (A.S) kuti iwe kwa ine uli ngati momwe Haroon adaliri kwa Musa (A.S).
Kodi Qur’an ikuti chiyani pankhani imeneyi?
Kodi olemekezeka mtumiki Musa (A.S) adagwira ntchito yaikulu komanso yotopetsa bwanji pofuna kuwapulumutsa ana a Izraeli? Koma Haroon ndi chifukwa chiyani adakhala chete posawabweza anthu kuchokera kukugwadira ng’ombe ya Samiriy?
Yankho ndi chifukwa chomwe mudzapereka pankhani ya Haroon ndi lomwe lidzaperekedwa pankhani ya Ali (A.S).
Izi ziri choncho chifukwa choti olemekezeka Ali (A.S) kwa mtumiki wathu (S.A.A.W) ali ngati momwe Haroon adaliri kwa Musa (A.S).
Umboni wina pankhaniyi
Ndichifukwa chiyani Ali (A.S) adakhala chete?
Ndifunsepo kaye omwe akumakanira nkhani imeneyi ndikumatulutsa funso limeneli pofuna kutsutsa.
Mtumiki wa Mulungu (S.A.A.W) adakhala zaka zokwana 13 ku Makkah, munthawi imeneyi mtumiki adali akuwawona anthu omwe adali omutsatira ake akuphedwa ndi kumavutitsidwa koma palibe chomwe adapanga polimbana ndi anthu omwe ankapanga zimenezi. Mtumiki amene adali ndi mphamvu kuposa wina aliyense kufikira kuti Ali (A.S) akulongosola kuti nkhondo ikafika povuta tinkathawira kwa mtumiki (S.A.A.W). ndichifukwa chiyani pazomwe zimachitikazi mtumiki (S.A.A.W) sadalimbane ndi anthu amenewa?
Pepani kwambiri abale anga tikuzitchinjiriza kwa Mulungu pomunenera mawu awa mtumiki wathu kuti, chifukwa chakukhala chete kwake, kodi adali opanda mphamvu? Kodi adalibe chisoni kwa amayi, ana ndi amuna omwe amavutitsidwawa?
Olemekezeka Sumayya ndi Yasir adavutitsidwa ndi kuphedwa momvetsa chisoni pomakhwekhwesa mitembo yawo, ndichifukwa chiyani mtumiki (S.A.A.W) adakhala chete?
Zomwe zimamupangitsa mtumiki kuti asapange chirichonse pazomwe zimachitikazi ndizomwenso zidapangitsa Ali (A.S) yemwe ali mtima wa mtumiki kuti akhale chete.
Umboni wina
Ndichifukwa chiyani Ali (A.S) adakhala chete?
Choti mudziwe ndichakuti Ali (A.S) yemwe ali mlowa m’malo wa mtumiki (S.A.A.W) pambuyo pake, siwosankhidwa ndi anthu muchikhulupiliro chathu.
Kodi angadziwe bwanji kuti ndi ndani yemwe ali oyenera kukhala mtsogoleri wa pambuyo pa mtumiki ndikumupatsa ufulu okhala Khalifa wa mtumiki?
Kodi ife anthu tiri ndi ufulu wanji pankhani ya utsogoleri wa Mulungu?
Ulamuliro ndi wa Mulungu ndipo Mulunguyo ndiyemwe amamusankha munthu kukhala Khalifah ngati momwe zimakhaliranso kwa mtumiki kuti ndiyemwe amasankha munthu kukhala mtumiki.
Ife anthu ndi ndani pankhani ya umulungu?
Ali (A.S) ndi mlowa m’malo – Khalifah – wa mtumiki (S.A.A.W) pambuyo pake kudutsira muchilamulo cha Mulungu.
Ali simtsogoleri wa anthu ayi.
Ali (A.S) chifukwa chakukhala kwake mlowa m’malo wa mtumiki, ayenera kumva zonena za mtumiki (S.A.A.W).
Mtumiki (S.A.A.W) adali atamuwuza kale Ali (A.S) polosera zomwe zidzachitike pambuyo pake mtumiki kodi pambuyo pake chidzachitika ndi chiyani kuchisilamu? Chidzawachitikire ndi chiyani akunyumba kwanga? nanga iwe chidzakuchitikira ndi chiyani?
Kutanthauza kuti kodi nyumba ya Wahay idzachitiridwa chiyani? Nyumba yomwe ija yomwe Qur’an poyilongosola nyumba imeneyi ikuti:

فی بیوت أذن الله أن ترفع و یذکر فیها اسمه

Mulungu akupereka chilolezo kuti dzina lake litchulidwe komanso linyamulidwe
Mulungu wayinyamula nyumba imeneyi.
Mtumiki adalozera kale kuti kodi nyumba imeneyi idzakumana ndi zotani.
Mtumiki (S.A.A.W) pambuyo pomuwuza Ali (A.S) zomwe zidzachitika adati:

علیک بالصبر علی ما ینزل بک و بها

Udzayenera kupilira pazomwe zidzikufikira iwe ndi iye (Fatima al-Zahra).
Udzayenera kupilira pa zonse zomwe zidzakufikira iwe ndi Fatima mpakana utadzakumana ndi ine.
Zowonadi, kodi ndi mavuto ochuluka bwanji omwe Imam Ali (A.S) adakumana nawo kuchokera pomwe mtumiki (S.A.A.W) adamwalira kufikira nthawi yomwe iye adasiyana ndi dziko lino.
Kufikira kuti iye Imam (A.S) polozera za mavuto omwe adakumana nawo ndikupilira komwe adali nako adali kunena kuti:
“Ndidapilira kukhala ngati kuti minga ili m’maso mwanga ndipo fupa landiima pakhosi”.
Kufikiranso nthawi yomwe adakhapidwa ndi lupanga la mankhwala (poison) ankalankhula kunena kuti:

فزت و رب الکعة

Ndapambana chifukwa cha bwana wa Kabah.
Mtumiki (S.A.A.W) adamuwuza Ali (A.S) kuti:
“Pambuyo pa ine mtundu wa Quraish udzakubweretsera mavuto, kukuvutitsa ndi kukupondereza".
فإن وجدت أعوانا فجاهدهم
“koma ukadzapeza okuthandiza, udzalimbane nawo ndikumenyana nawo”.
و قاتل من خالفک بمن وافقک
“kudutsira mwa anthu omwe adzakuvomereza udzamenyane ndi anthu omwe adzasemphana ndi iwe”.
Koma zonsezi zidzayenera kuchitika nthawi yanji? Panthawi yomwe udzapeza okuthandiza.
Pomwe tikuwona kuti limodzi mwa mavuto omwe Amirul muminina (A.S) adakumana nawo ndiko kupanda omuthandiza kapena kuchepa kumene muchiwelengero chawo.
Ndipo mtumiki (S.A.A.W) ankanena kuti ukadzapanda kumupeza okuthandiza udzayenera kupilira.
و لا تلق بیدک إلی التهلکة
“Osadziyika pachiwonongeko ndi dzanja lako”
Kutanthauza kuti osayika moyo wako pachiswe, chifukwa chakuti ukuyenera kukhala ndi moyo chifukwa cha chisilamu.
Kenako mtumiki (S.A.A.W) adanena kuti:
"Iwe kwa ine uli ngati momwe adaliri Haroon kwa Musa (A.S).
Ngati momwe Haroon adaliri mchimwene, mlowa m’malo wa Musa kufikira kuti Haroon adatsala pang’ono kuti aphedwe. Chonchonso iwe ndi Haroon kwa ine ndi Ummah wanga.
Ngati momwe adayankhira olemekezeka Haroon (A.S) kuti”
إن القوم استضعفونی و کادو یقتلوننی
“ndithudi anthu andifowoketsa ndipo adatsala pang’ono kuti andiphe”.
Iwenso Ali anthu adzakufowoketsa, ulibe okuthandiza mwachoncho udzayenera kupilira.
Panthawi yomwe zidachitika zoterezi komwe kuli kuphwanya nyumba ya Fatima (S.A), Imam Ali (A.S) adamutembenukira wachiwiriyo namuwuza kuti:
یا بن الصهاک لولا کتاب من الله سبق و عهد عهده إلی رسول الله لعلمت أنک لا تدخل بیتی
“Ee iwe mwana wa Sahak! Pakadapanda bukhu la Mulungu (lamulo la Mulungu) ndi phangano (langizo) lomwe adandisiyira ine mtumiki wa Mulungu, ndithudi ukadadziwa kuti siukadalowa mnyumba mwanga”.
Yankho lina tikulipezanso kuchokera m’mawu a mtumuki (S.A.A.W) pomwe amanena kuti:
فإن وجدت أعوانا فجاهدهم و قاتل من خالفک بمن وافقک
Kodi Amirul mumminina Ali (A.S) akadalimbana ndi anthu amenewa pothandizidwa ndi anthu angati?
Zidanenedwa kuti adali ndi anthu okwana 40, malo ena zidanenedwa kuti adali ndi anthu okwana 400, zidanenedwanso kuti adali ndi omuthandiza okwana 4000.
Tikuwona kuti chinamtindi cha anthu chidakhamukira kukaphwasula nyumba ya Fatima (S.A), Ali (S.A) yemwe adali yekha kodi akadatha kulimbana bwanji ndi chiwunyinji cha anthuchi?
Akadatenga lupanga ndikulimbana komanso kumenyana ndi anthu amenewa, ndithudi chisilamu chikadawonongeka ndipo gulu lambiri la asilamu likadaphedwa.
Kapenanso kuti akadalimbana nawo ndipo mapeto ake ndikuphedwa, kodi chikadachika ndichiyani ku Chisilamu pambuyo pakuphedwa kwake?
Fatima al-Zahra (S.A) adali akupita m’manyumba a maswahaba a mtumiki (S.A.A.W) kokwana mausiku 40, ndikumawafunsa kuti:
kodi mwayiwala nkhani ya Ghadir? Kodi mwayiwala kuti mtumiki (S.A.A.W) adanyamula dzanja la Ali (A.S) ndipo adanena kuti:
من کنت مولاه فهذا علی مولاه
“Amene ine ndidali mtsogoleri wake, ndiye uyu Ali ndi mtsogoleri wake”.
Imam Ali (A.S) adalibe omuthandiza.
Ndipomwe iye mwini wake akulongosola powonetsera zomwe adakumana nazo ndi momwe adapililira zipsyinjo zimenezi ponena kuti:
Chifukwa cha zomwe ndidakumana nazo ndidawusiya ulowa m’malo (Khilafah) ndipo ndidaganiza mozama kwambiri kuti ndimenye nkhondo ndidzanja lalifupi (kupanda chithandizo) komanso popanda mthandizi, ndidawona kuti ndibwino kuti ndipilire pa ulamuliro oponderezawu. Nthawi imene nkhalamba zidali za mantha, mnyamata adakhala ngati okalamba ndipo okhulupilira adali pamavuto ndi pachipsyinjo kwambiri chifukwa cha ulamuliro oponderezawu, mwachoncho ndidapilira kukhala ngati kuti minga idali m’maso mwanga ndipo fupa lidali pakhosi panga. zomwe zimandipangitsa kuti ndisalankhule komanso ndisawone.
Kodi iwe Ali umayenera kutani panthawi imeneyi?
“Ndidawona kuti kudzibweza pankhani imeneyi ndicho chidali chinthu chanzeru ndipo ndidapilira”. Ndidawona ndi maso anga kuti ndalandidwa zomwe mtumiki (S.A.A.W) adandisiyira (omwe uli utsogoleri) kufikira kuti nthawi ya oyambayo idadutsa. Koma ndidapilira ngati momwe mtumiki adaliliri pakupilira. Inenso ndidalamulidwa kupilira chifukwa chakuti ndine Waswiy (mlowa m’malo wa mtumiki).

فاستقم کما أمرت
فاصبر صبرا جمیلا
فاصبر لحکم ربک
فاصبر علی ما یقولون واهجرهم هجرا جمیلا

Ali (A.S) yemwe adali wamphamvu zosaneneka polimbana ndi adani, mosayembekezereka akukhala mlimi, akukhala okumba chitsime komanso akukhala othilira minda ya anthu omwe adali akunja kwa chisilamu kuti mbewu zimere bwino.
Ndichifukwa chiyani Amirul munina Ali (A.S) akudzitsitsa kuchoka komwe adali kuja ndikukazifikitsa pamenepa?
Onsewa ndi mafunso omwe akudikira mayankho.
Fundo ina ndiyonena kuti kodi ngati Ali (A.S) akadatenga lupanga ndikumenyana ndi anthu amenewa, kwa iye kudali phindu lanji?
Chifukwa cha mphamvu zomwe adali nazo akadawapha onsewo.
Ndi m’mene chisilamu chidaliri ndi adani ochuluka omwe amafuna kuchithetsa, kodi zimenezi zikadakhala zanzeru?
Kodi Ali (A.S) akadayankha chiyani pamaso pa Mulungu ndi mtumiki (S.A.A.W) chifukwa chakuthetsa chisilamuku?
Ali (A.S) akadamenyana ndi anthu amenewa, zikadapangitsa kuti olemekezeka Fatima al-Zahra (S.A) aphedwe mukulimbana kumeneku ndipo mapeto ake anthu omwewa akadabwera ndikumanena kuti mwawona Ali adasemphana ndi mtsogoleri wanthawi yake ndipo mapeto ake tidapha banja lake. Zomwe zikadapangitsanso kuti Ahalbait (A.S) atulutsidwe muchisilamu.
Pakulimbana kumeneku ndithudi Imam Ali (A.S) ndi olemekezeka Fatima (S.A) akadaphedwa.
ZidachitikApo ngati zimenezi.
Pomwe tikuwona kuti Ammar Yasir Swahabah weniweni wa mtumiki (S.A.A.W), yemwe adali kutumikira mumzikiti wa mtumiki. Tsiku lina lake mtumiki wa Mulungu (S.A.A.W) adamuwona Ammar Yasir ndipo adati:
Ammar ali ndi chilungamo ndipo chilungamo chiri ndi Ammar, mwachoncho kuphedwa kwa Ammar ndiye kuti chilungamo chikuphedwanso.
Idzafika nthawi yomwe kudzachitika nkhondo yomwe anthu oyipitsitsa adzakupha iwe ndipo iwo adzakuyitanira iwe ku Jannah ndipo iwo chifukwa chakuphedwa m’manja mwawo udzawayitanira ku Jahannama (kumoto).
Idafika nkhondo ya Siffin, mbali ina kuli Muawiyah ndipo mbali ina kudali Ali (A.S). kodi Ammar – yemwe mtumiki (S.A.A.W) adamunena kuti ali ndi chilungamo ndipo chilungamo chiri ndi iye – amayenera kukhala mbali ya ndani?
Panthawi yomwe Ammar adaphedwa, anthu ambiri ndipomwe adazindikira kuti kodi chilungamo chidali kwandani?
Anthu ambiri adazindizikira kuti ngati anthu ambali zonse ziwiri amapemphera, kodi ndi anthu ati omwe adali ma Munafiqiina ndipo ndi ndani omwe adali asilamu enieni?
Anthu adamuwuza Muawiyah kuti:
“Pali Hadith yotereyi kuchokera kwa mtumiki wa Mulungu (S.A.A.W) pokhudzana ndi Ammar, iye adali mbali ya Ali (A.S) ndipo waphedwa ndi gulu la Asilikali athu. Kodi titani pamenepa?”
Anthu ena omwe adali ochenjera pakamwa zomwe zikuwonetsa kuti adali otsatira a Muawiyah m’machitidwe adati:
“Ife sitidamuphe Ammar, koma kuti Ali ndiyemwe wamupha iye chifukwa chakuti Ali ndi yemwe adamubweretsa Ammar kunkhondo kuno ndipo mapeto ake waphedwa. Mwachoncho munthu amene wamupha Ammar ndi Ali Ibn Abi Talib. Mwachifukwa chimenecho anthu omwe adawanena mtumiki kuti ndi oyipa, opondereza, opyola malire ndi iwo ndipo ife ndi omwe tiri pachilungamo.
Imam Ali (A.S) adayankha motere:
“Ngati zingakhale kuti Ammar waphedwa chifukwa choti ife ndi omwe tidamubweretsa kunkhondo ndipo tamupha ndi ife, ndiye kuti Hamza Sayyida Shuhada sadamuphe ndi anthu ma Mushrikina omwe adali makolo a Muawiyah (Abu sufiyan ndi mkazi wake Hindi) koma kuti yemwe adamupha Hamza ayenera kukhala mtumiki wa Mulungu chifukwa iye ndi amene adamubweretsa Hamza kunkhondo.
Tatiyeni tibwelere kunkhani yathu yomwe tikuyankha pafunso lomwe Wahabi akufunsa pofuna kutsutsa zomwe zidamuchitikira Fatima al-Zahra (A.S).
Imam Ali (A.S) akadakhala kuti adatenga lupanga ndikulimbana ndi anthu amenewa ndithudi anthu omwewo akadanena kuti:
“Ali waukira Khalifa wa mtumiki wa Mulungu ndipo tamupha komanso zimayenera kutero chifukwa chakusemphana kwawo ndi Khalifah mwachoncho onse amayenera kuphedwa”.
Chomwe muyeneranso kudziwa apa ndi choti Khalifa wachiwiri ndiyemwenso adayesetsa kuti Saqifa ndi zomwe zidachitika pamenepo zichitikedi.
Nkhani yokhudzana ndi kumusankha Abubakar kudachitika mwadzidzi komanso yosemphana ndi nzeru.
Zowonadi padali zoyipa koma Mulungu adasunga zoyipa zimenezo. Keneko pambuyo pomusankha Abubakar podziwa kuti siidali njira ya umulungu adanena kuti:
“Kuyambira apa asadzapezekenso munthu osankha atsogoleri munjira imeneyi ndipo amene adzateroyo mudzamuphe”
Anthu amenewa adali akudziwa kudutsira m’mabukhu akale monga bukhu la Torah, Injiil ndi ena kuti Ali Ibn Abi Talib (A.S) ali ndi chikhalidwe komanso mbiri za Haroon. Ali Ibn Abi Talib (A.S) ali pamphambano.
Amayenera kuti akhazikitse ndi kuteteza ufulu wake pobwezera ndi kulimbana nawo zomwe mapeto ake zimatanthauzira kuwonongeka kwa Chisilamu. Kapenanso kuti amayenera kusankha kupilira ndi kukhala chete pa ulamuliro wanthawi yochepa wadziko lapansiwu kuti mpakana nthawi yake idzakwane.
Zowonadi Ali (A.S) adali ndi mphamvu za umulungu ndipo akadatha kubwezera popanda chovuta china chirichonse, koma powonjezera kuti ali ndi mphamvu alinso ndi luntha la umulungu (Hikmah).
Abale anga okondedwa! Inu nokha tangodziyikani munthawi ya chisilamu kuti nthawi yomwe Imam Ali (A.S) adali, kodi chisilamu chidali bwanji?
Iyi ndi nthawi yomwe ku Madinah kudali anthu ma Arab omwe adali ma Munafiqiina ngati momwe aya ikunenera kuti:
و ممن حولکم من الأعراب منافقون و من أهل المدینة مردوا علی النفاق
“ndipo ena mwa ma Arab omwe ali m’mbali m’mbali mwanu ndi ma Munafiqiina ndipo kuchokera mwa anthu aku Madinah palinso anthu omwe akhamukira ku Nifaq.
Munafiqiina ndi adani akuluakulu pa chisilamu omwe akubisa zinthu m’mitima mwawo pofuna kuwapanga chinyengo asilamu.
یحذر المنافقون أن تنزل علیهم سورة تنبئهم بما فی قلوبهم
“Munafiqun akuwopa kuti ingatsikire iwo Aya yomwe ingafotokoze ndi kuwulula zomwe abisa m’mitima mwawo”.
Atumiki onyenga ambiri omwe adabwera monga Musaylimah Kadhab, ndicholinga chosokoneza chisilamu.
Mafumu akuluakulu a Rome ndi Iran omwe adali ndi cholinga chofuna kugumula ndi kugwetsa chisilamu.
Anthu okanira omwe adali mu mizinda ya Makkah ndi Madinah. Komanso anthu okanira omwe amawoneka m’mawonekedwe a chisilamu monga Abusufiyan.
Anthu ena omwe adatuluka muchisilamu chifukwa chakukana kwawo kupereka Zakat.
Tikamakamba zokhudzana ndi ma Swahabah a mtumiki (S.A.A.W) omwe adali pafupi ndi iye, ndizachidziwikire kuti tidzatchulapo Abubakar, Ali (A.S) Umar, Uthman, Ammar, Abudhar, ndi ena otero. Mwachoncho ngati anthu amenewa adzapezeka kuti akumenyana kapena kulimbana ndiye zizadziwika kuti chisilamu sichilungamo ayi ndipo mtumiki (S.A.A.W) adalephera kuwalera otsatira ake ndipo onse adali akulimbana chifukwa cha ufumu wanthawi yochepa wa dziko lapansi.
Kupyoleranso apo chisilamu chidali ndi adani akulu akulu awiri omwe adali ayuda ndi akhirisitu.
Quran ikulongosola mowonekera poyera mu Surat albaqarah, versi 120 kuti:
لن ترضی عنک الیهود ولا النصاری حتی تتبع ملتهم
“Olo ndi pang’ono pomwe sadzasangalala nawe ayuda komanso akhirisitu mpakana utawatsatira iwo chipembedzo chawo”.
Kodi mukakhalidwe kameneka ndi adani ochuluka chonchi, Ali (A.S) amayenera kutani?
Akadapanda kusunga pamwamba pa chisilamu komwe kuli kusalimbana ndi kusamenyana ndi anthu owukirawo pofuna kusawonetsera kuwonongeka komwe chisilamu chidali nako, ndithudi chisilamu chonse chikadatheratu kudutsira mukulowelera komwe adani onse achisilamu omwe tawatchula aja akadakhala nako pambuyo powona kuti ma Swahabah ayamba kumenyana.
Imam Ali (A.S) akuyikira umboni pankhaniyi polongosola chifukwa chomwe sadayimire polimbana ndi anthu amenewa kuti:
لولا مخافة الفرقة بین المسلمین و أن یعودوا إلی الکفر و یبور الدین، لکناعلی غیرنا کنا لهم علیه
Ndidakhala chete ndipo sindidalimbane nawo chifukwa chowopa kugawikana pakati pa asilamu ndipo anthu ambiri omwe adangolowa chisilamu kumene akadabwelera ku Kufur ndipo chisilamu chikadathera pomwepo. Mapeto ake adani akadatipambana.
Yankho lina lomwe tingapereke ndi loti:
Mu bukhu la Hisitore la Tarikh altabari la Ahal sunnah vol 2, tsamba 676, muli nkhani yomwe ikulongosoledwa kuti:
Panthawi yomwe ma Swahabah oyera adawona kuti Uthman mu ulamuliro wake akupanga zinthu zosemphana ndi Sunna komanso zonena za mtumiki wa Mulungu (S.A.A.W), gulu la asilamu lidamukhamukira uthman ndikumupha.
Zikunenedwa kuti munthu yemwe amadziwika ndi dzina loti Sudan Ibn Hamran adabwera ndi gulu lake ndipo adakhamukira ku nyumba ya Uthman. Sudan Ibn Hamran adadula chala cha mkazi wa Uthman… (apa pali mawu ena omwe sitingathe kuwalongosola koma yemwe akufuna akawone bukhu lomwe talitchula lija) kenako adamupha Uthman.
Funso apa ndi lakuti:
Ndichifukwa chiyani Uthman yemwe ali Khalifa wachitatu sadalimbane ndi anthu opandukirawo pofuna kuteteza mkazi wake? Ndichifukwa chiyani sadatenge lupanga ndikumenyana ndi anthu amenewa?
Umboni wina uliwonse omwe ungaperekedwe poyankha chifukwa chomwe Uthman adakhalira chete, umboni omwewonso kapena chifukwa chomwechonso ndi chomwe chidzaperekedwa pakukhala cheti kwa Imam Ali (A.S).
Tanena kale m’bale wanga kuti Wahabi akulitulutsa funso lija ndicholinga choti tilephere kuyankha ndipo tikalephera kuyankha adzanene kuti nkhani yopandukira kunyumba ya Fatima (S.A) ndi kumumenya komanso kuphedwa kwamwana ndi yabodza ndinso ndi yopeka.
Fundo ina ndiyakuti:
Mu bukhu la Siratu Nabawi la Ibn Hisham vol 2, tsamba 162, muli nkhani yomwe ikulongosoledwa kuti:
Panthawi imene Khalifah oyamba Abubakar adalowa chisilamu ndipo nthawi imeneyo Khalifah wachiwiri adali asadalowe chisilamu, imodzi mwa ntchito zomwe umar adali kupanga ndiyakuti, adali kuvutitsa asilamu ndi kuwamenya. Nthawi ina yake Abubakar adamuwona Umar akumenya mkazi chifukwa chakuti adalowa chisilamu ndipo amamumenya ndicholinga choti atuluke chisilamu. Adamumenya kwambiri mzimayi uja kufikira kuti adatopa chifukwa chakumumenya nthawi yaitali ndipo mapeto ake Umar adati:
“Sindikukumenya chifukwa choti ndatopa kukumenya”
Funso apanso ndi loti:
Ndichifukwa chiyani Abubakar adakhala chete ndipo sadatulutse lupanga polimbana ndi Umar pofuna kuteteza msilamu uja?
Chifukwa chomwe chingatulutsidwe ndi ma Wahabi poyankha funso limeneli, chidzakhalanso chifukwa chomwe Ali (A.S) adakhalira chete.
Nkhani inanso yomwe iri yofunikira kwambiri kuti tiyidziwe pofuna kuyankha funso la Wahabi ndi yakuti:
Kodi ndi ndani mu Hisitore ya chisilamu adanena kuti Ali (A.S) adakhala chete ndipo sadatulutse lupanga polimbana ndi anthuwa? Kodi ndizotheka kuti angokhala chete?
Zidachita kunenedwa m’mabukhu ambiri monga bukhu la Ruhul Maani (Alusi) vol 3, tsamba 124 kuti:
Ali (A.S) adalimbana ndi Umar pakhomo panyumba ndipo adamugwetsa Umar pansi, Ali (A.S) adamumenya chibakela kumaso ndipo adatsimikiza zofuna kumupha koma adakumbukira mawu a mtumiki (S.A.A.W).
فهم بقتله و ذکر قول رسول الله
Ndipo tikuwona kuti chifukwa china akuchilongosola ndi mwini wake Ali (A.S) pomwe akuti:
یا بن الصهاک لولا کتاب من الله سبق و عهد عهده إلی رسول الله لعلمت أنک لا تدخل بیتی
“Ee iwe mwana wa Sahak! (Umar ibn Khataab) Pakadapanda bukhu la Mulungu (lamulo la Mulungu) ndi phangano (langizo) lomwe adandisiyira ine mtumiki wa Mulungu, ndithudi ukadadziwa kuti siukadalowa mnyumba mwanga”.
لولا مخافة الفرقة بین المسلمین و أن یعودوا إلی الکفر و یبور الدین، لکناعلی غیرنا کنا لهم علیه
Ndidakhala chete ndipo sindidalimbane nawo chifukwa chowopa kugawikana pakati pa asilamu ndipo anthu ambiri omwe adangolowa chisilamu kumene akadabwelera ku Kufur ndipo chisilamu chikadathera pomwepo. Mapeto ake adani akadatipambana.
Akulankhulanso mu Nahjul Balagha kuti:
فأمسکت یدی حتی رأیت راجعة الناس فخشیت إن لم أنصر الإسلام و أهله أری فیه ثلما و هدما
“Ndidabweza dzanja langa kufikira kuti ndidawawona anthu akubwelera ku Kufur kuchokera kuchisilamu, ndidawopa kuti ngati sinditeteza chisilamu ndi asilamu, ndikuwona kuti muchisilamu mudzakhala chiwonongeko ndi kugumuka”.
Ndidawona kuti ndibwino kuti ndipilire ngakhale Fatima al-Zahara (S.A) aphedwe koma ndibwino kuti chisilamu chitetezedwe komanso chisungidwe, chifukwa ndi nthawi yomwe ndidawawona anthu okanira akuwayitanira asilamu ku Kufur ndi kukanira ndipo chisilamu chidali chikutha ndipo vuto lakutha kwa chisilamu ndi lalikulu kwambiri kuposa vuto lakuphedwa kwa Fatima al-Zahra (A.S).

 

 

 

 

 

Add new comment