Kumudziwa Hazrat Khadijah (S.A)
بسم الله الرحمن الرحیم
ألم یجدک یتیما فآوی و وجدک ضالا فهدی و وجدک عائلا فأغنی
M’mwezi olemekezeka wa Ramadhan pa tsiku la khumi (10), tsiku lomwe adamwalira olemekezeka Khadijah (S.A).
Ife mutsiku limeneli chifukwa chakumwalira kwa olemekezekawa timakhala pachisoni kwambiri kufikira kuti ngakhale mtumiki wathu okondedwa (S.A.A.W) adachitcha chaka chomwe Hazrat Khadijah (S.A) adamwalira kuti chaka cha madandaulo (Amul Huzn).
Mwachoncho ifenso padakali pano ndife odandaula.
Amuna ndi amayi onse ayenera kumuyika mzimayi ameneyu kukhala chitsanzo chawo pakupilira, kutukuka ndi pa usilamu wawo ndikudutsa njira yomwe olemekezekawa adadutsa.
Tiyenera kuti tipititse patsogolo kuzindikira kwathu pokhudzana ndi olemekezeka Khadijah (S.A).
Msilamu wina aliyense yemwe alipo, adalipo komanso yemwe adzabwere kutsogoloko, ali msilamu chifukwa cha ntchito yosanenedwa ya olemekezeka ameneyu.
Chifukwa chakuti pakadapanda kupezeka Hazrat Khadijah (S.A) mu Hisitore komanso padakapanda kulimbira kwake ndi ntchito yomwe adayigwira, ndithudi sibwenzi chisilamu chitapita patsogolo.
Inde! Tikudziwa bwino lomwe kuti mtumiki wathu okondedwa adali ndi ulemelero wapamwamba mu uzimu, izo zikhale pambali. Koma kuti ntchito yoitanira anthu kuchiwongoko iyende bwino, pamafunikanso zinthu zina zadziko lapansi monga chuma.
Zikunenedwa mu bukhu lolemekezeka la Quran kuti:
ألم یجدک یتیما فآوی و وجدک ضالا فهدی و وجدک عائلا فأغنی
“kodi Mulungu sadakupeze iwe – mtumiki – uli wamasiye ndiye adakupatsa malo okhala? Ndipo adakupeza iwe uli osochera ndipo adakuwongola? komanso adakupeza uli osauka koma adakulemeretsa?
Kutanthauza kuti Mulungu adamupeza mtumiki alibe chuma choti akadagwiritsira ntchito popititsa patsogolo chipembedzo koma Mulungu adamulemeretsa kudutsira mwa olemekezeka Khadijah (S.A).
Zidanenedwanso mu Hadith ina kuchokera kwa Ahalbait (A.S) kuti kusafunikira chinthu ndi kulemera komwe mtumiki adali nako, kudalipo kudutsira muchuma chomwe Mulungu adamupatsa Hazrat Khadijah (S.A).
Olemekezeka Khadijah (S.A) popanda kudandaula komanso popanda chiyembekezero china chirichonse adapereka chuma chake kwa mtumiki komanso munjira ya Mulungu.
Zimenezi sizochepa ayi.
Ife sitikuwonapo mu mbiri yakale – Hisitore – kuti padali munthu ngati Olemekezeka Khadijah (S.A) yemwe adapereka chuma chonse munjira ya Mulungu. Kufikira kuti panthawi yomwe amamwalira, palibe chomwe chidatsala mu chuma chake ngakhale mlingo wansalu okwana nsanda yake kumene.
Zonse adazipereka munjira ya Mulungu kufikira kuti palibe chomwe chidatsala m’manja mwake.
Sitikudziwa kuti kodi mtumiki wa Mulungu adapanga zotani ndi chuma chimenechi? Koma zomwe tikudziwa ndi zoti, dera lomwe anthu adali munthawi ya mapeto a umbuli, kupha ana akazi, nkhondo zochuluka pakati pawo, kupondereza, kufalitsa uchimo padziko lapansi ndi zina zotero, zonsezi ndi cholinga chofuna kupeza zadziko lapansi.
Kodi mtumiki adzausintha bwanji mtundu oterewu? Kodi apange zotani komanso akhale ndi chiyani pofuna kusintha mzinda umenewu?
Sitikudziwa kuti mtumiki adapanga chiyani ndi chuma cha Olemekezeka Khadijah (S.A).
Adawaombola akapolo, adapawapatsa umoyo wabwino anthu osauka, adawathandiza anthu osowa ndi zina zotero.
Padakali pano dziko lapansi likufunikira anthu ozindikira omwe ali olemera kuti apereke chuma chawo munjira ya Mulungu ndi kuti amenye nkhondo ndi kulimbana ndi chuma chawo.
Padakali pano ife asilamu tikufunikira kuti tivomereze za upamwamba omwe Olemekezeka Khadijah (S.A) adali nawo ndi kuti titengerepo phunziro.
Munthu amene tanena kale kuti adataya chuma chonse munjira ya Mulungu kufikira kuti olo ndi pang’ono pomwe palibe chomwe chidatsala ngakhale mlingo okwana nsanda yake.
Tikutha kuwona zomwe zidachitika mudziko la Iran munkhondo yadziko lonse yoyamba. Mdani pofuna kuwakokera anthu kuchikhulupiliro chosocheretsa cha Bahayi, adabwera ndikuwapatsa chakudya anthu omwe adali opanda chakudya, anjala ndipo kudutsira munjira imeneyi anthu ambiri ndi mitundu ina ya nthawi imeneyo idakhala yotsatira gulu la Bahayi.
Ku Somalia panthawi yomwe kudabwera chilala mu zaka zapitazo, ndi chiyani ife asilamu sitidathe kuwugwiritsa ntchito bwino mwayi umenewu pofuna kuthandiza asilamu anzathu?! Komwe akhirisitu adabwera ndikugwiritsa ntchito mwayi umenewu pomwe atsikana ndi ana achisilamu adali kulandira chakudya kuchokera m’manja mwa akhirisitu namawapapasa ndi manja awo achithandizo pa mitu yawo.
الناس عبید الإحسان
“anthu ndi akapolo a ntchito zabwino”
Ndi lamulo la chipembedzo chathu kuti gawo lina la chuma chathu tichipereke kwa anthu osowa ngakhale atakhala kuti siasilamu ndi cholinga choti mtima wawo uwandikire ku Chisilamu.
Kuyitanira ku chipembedzo cha Mulungu ngakhale kuti kumafunikira Taqwa, Ikhlas, kumafunikiranso chuma chochuluka ndikuchipereka mu njira ya Mulungu. Ngakhale munthu yemwe akufuna kusonkhanitsa chuma pano adziko lapansi, njira ina yomwe amatsata ndiko kupereka gawo la chuma chake kwa ena.
Chimodzi muzolinga za kusala ndiko kukumbukira anthu osauka. Tikumbukire kunena kuti anthu amenewa sakutha kudya, kumwa, kuvala, kuseka ndi kusangalala pano padziko chifukwa chakuti alibe ndalama.
Koma munthu wa masomphenya ndi ozindikira yemwe angapeze phunziro kuchokera kwa Olemekezeka Khadijah (S.A), chisangalalo chake amachigawa.
Imodzi mwa mbiri zomwe Olemekezeka Khadijah (S.A) alinayo ndi Ummul Fuqaraa, kutanthauza kuti mayi wa osauka ndi osowa.
Zikukhala ngati kuti anthu osauka ndi osowa ali ndi mayi omwe dzina lawo ndi Khadijah (S.A).
Tanena kale kuti munthu amene akufunafuna umoyo wadziko ndikusonkhanitsa chuma chake amayenerabe kuti apereke chopereka – Infaaq – ngakhale yemwe alibe amakumbukira kuthandiza ena ngati atapeza kangachepe.
Pali Hadith yomwe ikutsimikizira pa zimenezi kuti:
من قدر علیه رزقه فلینفق مما آتاه الله
“Munthu amene chakudya chake chachepetsedwa – umoyo wake ndi ovuta – ayenera kupereka kuchokera muzomwe Mulungu wamupatsa.
Ngakhale zitakhala zochepa.
Kupereka munjira ya Mulungu, zili ngati mulimi amene ngati akufuna kuchulukitsa mbewu zake, akufunikira kupilira ndi maphunziro (kuzindikira).
Mulimi amenewu chifukwa cha kuzindikira komwe ali nako, ali ndi chitsimikizo ndi chikhulupiliro kuti akadzala nthangala imodzi ndiye kuti adzakolola zochuluka kwambiri.
Munthu amene akupereka munjira ya Mulungu ngakhale ndi pang’ono pomwe akufunikiranso kupilira ndi Ikhlas. Mapeto ake adzawona kuti Mulungu adzamupatsa zochuluka kukhala ngati kuti wadzala ndipo panthawi imeneyi akukolola zochuluka.
Amenewa ndi malamulo a Quran ndipo Olemekezeka Khadijah (S.A) adapanga zoterezi.
Kodi adali ndi chuma chochuluka bwanji? Pomwe zikunenedwa kuti chuma chake chidali chikunyamulidwa ndi ngamila zokwa 70,000. Kodi chuma chochuluka chonchi chifunikira anthu antchito ochuluka bwanji? Nanga katundu yemwe wanyamulidwayo ndi ochuluka bwanji? Nanganso akufunikira nthaka yayikulu bwanji?
Koma zonsezo adazipereka munjira ya Mulungu. Zimenezi ndi zomwe zikutisonyezera ife kuti kodi nzeru zake zidali zowala komanso zamphamvu bwanji. Komwe kudali kusakakamira za dziko.
Anthu omwe amakakamila za dziko ndithudi ndi omwe ali pachiwonongeko chachikulu kwambiri.
Pali Hadith yomwe ikuchokera kwa Imam Hasan Askariy (A.S) kuti:
“ Nzeru za anthu zikadagwira ntchito bwino, dziko lapansi likadakhala lotayika (ngati nyumba yomwe idagwa kalekale).
Chifukwa chiyani zikadakhala chonchi?
Chifukwa chakuti ife omwe tikukhala pano pa dziko lapansi, pomwe tiri pa ulendo opita kudziko losatha, tikadazindikira zimenezi tikadayesetsa ndi m’mene tikadakwanitsira kuti tigwire ntchito yathu chifukwa cha dziko losathalo.
Ngatinso momwe zikunenedwera mu Hadith ina yodziwika bwino kuti:
“ Gwirani ntchito padziko lapansi ngati mudzakhala mpakana kalekale – ndicholinga chofuna kupeza zofunikira za umoyo wadziko lapansi – ndipo ligwilireni ntchito dziko losatha – pofuna kupeza chisangalalo chosatha – ngati mumwalira mawa.
Ndiye ngati zanenedwa kuti tikhala umoyo wapano padziko lapansi nthawi yaitali, palibe kufunikira kofulumira kuti tigwire ntchito mopupuluma.
Tithamangira kuti?! Tidakalipo ndipo nthawi ndi yambiri.
Zomwe zidzapangitsa kuti munthu asakhale ndi chidwi chogwira ntchito.
Ife padakali pano tiri ndi lamulo la anthu apaulendo omwe akungodutsa mudzikoli.
Anthu omwe ali ngati Olemekezeka Khadijah (S.A) amadziwa kuti sakuyenera kusiya chinthu paulendewu ndipo asadanyamuke pa siteji imeneyi akuyenera kutumiziratu katundu wawo komwe akupita. Mapeto ake panthawi yomwalira amakhala akusamuka pa ulendewu popanda katundu owalemeretsa. Pomwe anthu ena siali chonchi.
Sitidzakhala umoyo wathu onse mpakana kalekale pa siteji imeneyi. Imeneyi ndi sitiji chabe yomwe pakangodutsa nthawi yochepa ukhala ukusamutsidwa kupita kudziko lina. Koma zomvetsa chisoni ndi zakuti onse atangwani pongoligwilira ntchito siteji imeneyi.
Ifika nthawi posachedwapa pomwe azikuwuza kuti tiye uzipita. Ndipo iwe uzifunsa kuti ndizipita kuti?! Ndipomwe udzayankhidwa kuti nyumba yathu komanso kokhala kwathu sikuno ayi.
Zowonadi Mulungu adamupeza mtumiki alibe chirichonse koma adamulemeretsa kudutsira mu chuma cha Olemekezeka Khadijah (S.A).
Pokhudzana ndi Olemekezeka Khadijah (S.A) ndipomwe tikuwonanso mu Baibulo kuti mukulongosoledwa zokhudzana ndi Olemekezeka Khadijah (S.A).
Mtumiki wa Mulungu pomulongosola Olemekezeka Khadijah (S.A) powerenga kuchokera mu Baibulo la chiluya akunena kuti:
نسله من مبارکة و هی مونسة أمک فی الجنة
“Mtundu – Ummah – wake ndi ochokera mwa Mubarakah ndipo iye ndi yemwe azidzawachezetsa amayi ako ku mtendere”
Mubarakah ameneyu atha kukhala Olemekezeka Khadijah (S.A) kapenanso atha kukhala Hazrat Fatima Zahra (S.A).
Zowonadi kuti mtundu wa mtumiki wa chisilamu, uli ochokera kwa Olemekezeka Khadijah (S.A). pomwe tikuwona kuti akubadwitsa mwana wake olemekezeka Fatima (S.A) ndikumupereka ku mtundu wa chisilamu.
Zowonadi Olemekezeka Khadijah (S.A) ndi omwe azidzamuchezetsa Hazrat Mariyam – mayi Mariya – (S.A) omwe ali mayi a mtumiki Yesu (A.S) ku Jannah.
Kupezeka kwa Olemekezeka Khadijah (S.A) ndi kwakukulu komanso kwa pamwamba kwambiri kufikira kuti mwa iye mukupezeka kukwanira pokhala mkazi wa mtumiki wa mtumiki (S.A.A.W), kuwonjezeranso apo kukwanitsa kulandira kuwala kwa mwana olemekezeka Fatima Zahra (S.A).
Kuwala kumene kudalibe kwa mtumiki wina aliyense, kuwala komwe kukuperekedwa kwa mtumiki wathu chifukwa chakuziyeretsa kwake mtumiki, kuwala komwe palibe mtumiki yemwe adapatsidwa. Kuwala kumene kudasungidwa chifukwa cha mtumiki wathu ndipo mapeto ake kuwala kumeneku kudafika ndi kubadwa kudutsira mwa Olemekezeka Khadijah (S.A).
Kupezeka kumene kungathe kukhala mkazi wa mtumiki ndi kukhalanso kupezeka kotuluka mkati mwake atsogoleri ndi ma Imam okwana 11, sikupezeka kwapansi ayi.
Zowonadi chibelekero cha Olemekezeka Khadijah (S.A) ndi choyera kuti mpakana zizichitika zoterezi. Kupezeka kwake ndi kwapamwamba kwambiri.
Ndipo tikupeza kuti imodzi mwa mbiri zomwe Olemekezeka Khadijah (S.A) alinayo ndi Twahirah kutanthauza kuti oyera.
Tangowona nthawi yomwe amakhala amayi a anthu ena omwe adazitchanso kuti ndi Khalifah wa mtumiki Muawiyah, yemwe mayi ake adali Hind, tawonani nthawi yomweyi ndi yomwe amakhala Olemekezeka Khadijah (S.A) koma adali akutchedwabe kuti Twahirah.
Tayesani pakati pawo anthu amenewa kuti ankakhala bwanji.
Apanso tinene izi kuti upamwamba omwe Olemekezeka Khadijah (S.A) alinawo, sichifukwa choti adangokhala mkazi wa Mtumiki (S.A.A.W).
Chifukwa chakuti tikutha kuwona kuti mu Hisitore kudali akazi a atumiki omwe adanenedwe ndi kudzudzulidwa ndi Quran.
Ulemelero siukubwera chifukwa chongolumikizana ndi mtumiki wa Mulungu kapena kungokhala ubale wakubadwana.
Tawonani kuti olemekezeka mtumiki Lot (S.A) ndi olemekezeka mtumiki Nowa (A.S) adalinso ndi akazi, koma akaziwo akudzudzulidwa chifukwa cha mchitidwe wawo oyipa mu Quran.
Ndipomwe tikuwonanso mbali inayo kuti mkazi wa Farao akuchemeleredwa ndi kuyamikiridwa ndi Quran. Zonsezi osati chifukwa chakulumikizana komwe kudalipo pakati pa iye ndi Farao.
Mwachoncho kupezeka kwa ulemelero wa Olemekezeka Khadijah (S.A), sichifukwa choti adangokhala mkazi wa mtumiki basi. Ngakhale kuti ndi zinthunso zonyaditsa kwa iye kukhala mkazi wa mtumiki chifukwa chakuti adawugwiritsa bwino ntchito utumiki umenewu. Pomwe tikuwona kuti panthawi yomwe Olemekezeka Khadijah (S.A) ali ndi moyo ndipo mtumiki adali akumukumbukira Olemekezeka Khadijah (S.A) mu umoyo wake onse.
Kupezeka kwa Olemekezeka Khadijah (S.A) kwa mtumiki kudali kwapamwamba kwambiri kufikira kuti mtumiki akuchitcha chaka chomwe olemekezekayo adamwalira kuti Amul Huzn (chaka cha madandaulo).
Mtumiki akamakumbukira Olemekezeka Khadijah (S.A), mtima wake udali kudzadza ndi madandaulo, kufikira kuti ena mwa akazi a mtumiki akawona zoterezi ankadana nazo ndikumayankhula monyogodola ponyoza Olemekezeka Khadijah (S.A) kuti:
“Mulungu m’malo mwa nkhalamba yaikaziyo, adakupatsa akazi achitsikana okongola. Ndi chifukwa chiyani umakumbukira Khadijah chonchi? Ndi chifukwa chiyani ukumamuphera nkhosa ndikumawapatsa abwenzi ake?”
Mtumiki poyankha ndipomwe akunena kuti:
“khalani chete palibe chomwe mukudziwa kuti Khadijah adali ndani. panthawi imene munthu wina aliyense sadakhulupilire za utumiki wanga iye adakhulupilira za ine. Adapereka chuma chake munjira yanga”.
Amirul Mu’uminina Ali (A.S) mu Khutbah yotchedwa Qasiah akunena kuti:
“Mtumiki wa Mulungu adanena kuti Mulungu patsiku kangapo konse chifukwa cha Khadija amakhala akunyadira pamaso pa angelo kuti: mukukumbukira panthawi yomwe ndinkafuna kulenga munthu oyamba padziko kuti adzakhale mlowa m’malo wanga padziko lapansi ndipo inu munkatsutsana ndi zimenezi chifukwa chakuti mumandigwadira ndi kumandiyeretsa ndipo ine ndidanena kuti:
إنی أعلم ما لا تعلمون
“Ine ndimadziwa zomwe inu simumadziwa”. Chimodzi mwazinthu zomwe simunkadziwa ndi ichi kuti kuchokera mumsana wa Adam – Abulbashar – (A.S) mudzabwera kupezeka kwa pamwamba ngati Khadijah. Tawonani angelo anga cholengedwa chimenechi.
Olemekezeka Khadijah (S.A), Ummul Mu’uminina.
Mulungu adali kunyadira pamaso pa angelo kangapo konse patsiku.
Kodi ndi ma Salamu ochuluka bwanji omwe mngelo wa uthenga olemekezeka Jibril (A.S) adali kumupatsira mtumiki kuti ukatipelekere Salamu kwa Khadijah (S.A).
Quran yanena zowonadi kuti:
ألم یجدک یتیما فآوی و وجدک ضالا فهدی و وجدک عائلا فأغنی
Koma zomvetsa chisoni ndi zakuti pali anthu ena omwe akuyesetsa kufuna kunyoza ndi kuchepetsa ulemelero ndi upamwamba omwe olemekezekawa ali nawo.
Mtendere ndi madalitso a Mulungu apite kwa olemekezeka Khadijah Ummul muminina.
Add new comment