chidule cha zoyipa zomwe Wahabi akupanga padakali pano mudzina la chisilamu poyipitsa chipembedzochi 

 

بسم الله الرحمن الرحیم

من قتل نفسا بغیر نفس أو فساد فی الأرض فکأنما قتل الناس جمیعا

Mulungu wapamwambamwamba akulankhula mu bukhu lake lolemekezeka kuti:

“ Amene angaphe munthu osalakwa kapena kuwononga padziko la pansi, ziri ngatiwapha anthu onse adziko la pansi".

Muchisilamu kupondereza ndi kuvomereza kuponderezedwa ndi zoletsedwa Haram.
Kudzipha ndi kupha anthu ena osalakwa ndizoletsedwa muchisilamu.
Kugwiritsa ntchito zida zakupha anthu oponderezedwa mwaunyinji monga Bomb ndi zina zotero ndizoletsedwa muchisilamu.
Ndi m’malo angapo okha omwe zaloledwa kupha motsatana ndi chilamulo cha chisilamu komanso motsatana ndi nzeru pofuna kukhazikitsa chilungamo.
Mwachitsanzo:
Ngati munthu wapha munthu wina mwadala ndipo zatsimikiziridwa ku khoti, chisilamu chikupeleka chisankho ndi mwayi kubanja lofedwa, ndicholinga chofuna kukhazikitsa chilungamo. Atha kusankha pakati pa kubwezera kuti ophayo nayenso aphedwe (Qiswas), kapena kutenga ndalama zomwe zalengezedwa kwa banja lakuphalo kuti apereke (Diyah) kapena kukhululuka kumene.
Mwachoncho kupha muchisilamu ndikoletsedwa ndipo kumatengedwa kuti ndi imodzi mwa machimo akuluakulu, kaya munthu wachita kudzipha yekha kapena kuchotsa pakati (komwe kuli kupha mwana wakhanda), kupha anthu osalakwa kapenanso kupha zinyama chifukwa chongosangalatsidwa, izinso ndizoletsedwa.
Kodi chisilamu ndi chabwino komanso ndi chachisoni bwanji?
Kuchokera pa nthawi imene dziko la Iran lidapambana polimbana ndi adani ndikukhala ndi ulamuliro udzilamulira pa wokha, Satana wamkulu – Amereka ndi maiko oipitsitsa omwe adagwirizana nawo muzochitika adabwera ndipo adayesetsa moipitsitsa kuti abweretse vuto ndikuwononga ndikuchiipitsa chipembedzo cha chisilamu ndi chiphunzitso cha Ahalbait (A.S). chifukwa chakuti amadziwa kuti kuima kumeneku polimbana ndi kupondereza chidzakhala chitsanzo kwa anthu ofowoketsedwa ndi oponderezedwa polimbana ndi maiko opondereza ndi odzikweza.
Tikudziwa bwino lomwe kuti padakali pano likulu la chiphunzitso cha Ahalbait kapena kuti chiphunzitso cha Shia ndi Iran.
Mwachoncho pofuna kuthetsa zimenezi adabwera ndikuyesetsa poliyipitsa dziko la Iran pamaso pa anthu kuti wina aliyense wakumva ndi kuwona aziti Iran ndi dziko loipa komanso lakupha.
Ndipomwe tikuwona kuti pambuyo poti dziko la Iran lapambana, Amereka ndi maiko ena ambiri otsatira amereka, adayesetsanso pobweretsa vuto ndi kumapanga ziwembu zosiyanasiyana pomapha ndi kuwopsyeza anthu otsatira Ahalbait (A.S) adzikoli omwe adagwira ntchito yaikulu kwambiri polimbana ndi adani achisilamuwa mpakana kupambana, ndicholinga choti mchitidwe ndi maganizo olimbana ndi maiko opondereza uchoke m’maganizo mwa anthu ndi kuti anthu ena adzikoli abwelere m’mbuyo.
Komanso mapeto ake anthu amaiko ena padziko lapansi akhale ndi mantha komanso atengerepo phunziro kuti wina aliyense opanga mchitidwe oterewu adzakumana ndi zinthu zoterezi ndikutinso asakhale ndi maganizo abwinowa komwe kuli kulimbana ndi maiko opondereza.
Ntchito ina yomwe adapanga ndiko kugawanitsa pakati pa asilamu pokhazikitsa nkhondo yapakati pa Sunni ndi Shia ndi kuwasiyanitsa asilamuwo ndicholinga choti asadziwe zomwe zikuchitika pakati pawo (kutanthauza kuti asilamu adziko lina asadziwe zomwe zomwe zikuwachitikira asilamu ena) zomwe zidzapangitsa kuti pasakhale mgwirizano wina uliwonse pakati pawo ndipo zotsatira zake adani achisilamuwa adzapeze zolinga zawo zoipa mosavuta.
Kugawanitsa maiko a chisilamu, kumachita kuti kuchokera m’mawu a olemekezeka mtumiki wathu Muhammad (S.A.A.W) omwe adatifika ife, ina mwa mahadith ake akulongosola kunena kuti:

من سمع مسلما ینادی یا للمسلم فلم یجبه فلیس بمسلم

Kutanthauza kuti:

Ngati m’modzi mwa asilamu akuitana msilamu mzake kuti Ee! Msilamu mzanga ine ndikuponderezedwa ndithandize ndipo ngati osamuyankha (osamuthandiza), ndiye kuti wakumvayo olo ndi pang’ono pomwe simsilamu ayi.

Apa choti tingadziwe ndichakuti, kuthandiza kuli munjira zosiyana siyana.
Nthawi zina munthu angathandize popereka ndalama Sadaqah, nthawi zina chifukwa choti alibe chopereka komanso kuti ali kutali atha kupanga Duwa kumene powapemphera zoipa adani a asilamuwo kuti awonongedwe ndi mkwiyo wa Mulungu komanso ndikuti asilamu ndi anthu oponderezedwa ndi ofowoketsedwa apulumutsidwe ndi chisomo cha Mulungu.
Ngakhalenso kuti zinanenedwanso kuchokera kwa mtumiki wathu okondedwa mawu ofananira amenewa kuti:

من سمع رجلا ینادی یا للمسلم فلم یجبه فلیس بمسلم

Kutanthauza kuti oyitanayo ngakhale asakhale msilamu, akhale wachipembedzo china ngati akufuna chithandizo, ndiye munthu amene akuyitanidwayo ndi msilamu mwadzina chabe (apa sitikufuna kulongosola kuti oyitanidwayo akhale okhulupilira weniweni chifukwa chakuti okhulupilira weniweni pankhaniyi udindo wakenso ndi wina) ndipo akumva kuitanaku, koma osayankha komanso osamuthandiza oponderezedwayu, ndiye kuti iye simsilamu ayi.
Ndiye choyamba chake ndi choti abwera pofuna kuipitsa dziko lachisilamu la Iran.
Kenako adayesetsanso kuti agawanitse mayiko achisilamu kuti asilamu asalumikizane ndikukhala anthu ogwirizana.
Ndipo mapeto ake mbali inanso adabwera ndikuyipitsa chiphunzitso cha Ahalbait (A.S) (Shia) ndikuchidziwitsa kwa anthu adziko lapansi kuti Shia ndiye kuti kupha ndi umbanda. zonsezi ndicholinga chofuna kuchisinthanitsa chisilamu chenicheni ndi chisilamu chabodza, chisilamu chenicheni chake chomwe chakhazikika komanso chayima mwamphamvu pa bukhu la Quran ndi chiphunzitso cha Akunyumba ya mtumiki (S.A.A.W.) – Ahalbait (A.S) kumachita kuti iwo ndi omwe ali akupha akuluakulu adziko lino lapansi komanso ndi omwe akupanga zinthu zoyipitsitsa kwambiri m’mayiko osiyanasiyana mudziko lino lapansi.
Tangowonani, kodi ndi ndani omwe adakhazikitsa nkhondo ya dziko lonse lapansi ndipo ndi anthu ambiri bwanji osalakwa omwe adaphedwa munkhondo imeneyi moponderezedwa komanso ndi zinthu zochuluka bwanji zomwe zidawonongeka zomwe sizingathenso kubwezeretsedwa?!
Kodi tikamakamba zokhudzana ndi zida zowopsya zikuluzikulu ngati Atomic bomb zili m’manja mwa ndani padakali pano?
Nanga padakali pano ndi ndani omwe akuwatenga anthu adziko lapansi ngati akapolo pomawalamula momwe akufunira ndipo ngati osapanga zomwe akufuna ndiye kuti akumana ndi mavuto osaneneka?
Kodi ndi ndani omwe akulanda ndikuba chuma cha mayiko ofowoketsedwa?
Nanga kodi ndende zikulu zikulu komanso zowopsya kwambiri padakali pano zili m’manja mwandani kapenanso kuti ziri m’mayiko ake ati? Gwantanamo ku Amereka, Qatwif ku Saudi Arabia ndi …
Nanganso ndi ndani omwe padakali pano ali pakalikiliki kupanga zida zakupha anthu mwaunyinji munthawi yochepa?
Ntchito inanso yaikulu yomwe adapanga, ndiko kutembenuza nkhope ya chisilamu kudutsira mukutembenuza matanthauzo a zina mwa ziphunzitso za chisilamu.
Mwachitsanzo pomwe chisilamu chikunena kuti payenera kukhala kubwezera (Qiswas) kapenanso kuti pakhale Jihad polimbana ndi adani achisilamu.
Adabwera ndikutembenuza matanthauzo amawu amenewa.
Chabe kuti iwo amayesetsa kupeza anthu omwe kuzindikira kwawo pa chipembedzo cha chisilamu ndikochepa, nawaphunzitsa ziphunzitso za chisilamu motembenuza.
Adabwera ndikukhazikitsa chisilamu cha Amereka ndicholinga choti chisilamu cha amerekachi chifowoketse chisilamu chenichenichi ndikuti chibwezeretse m’mbuyo kupita patsogolo kwa chisilamu.
Adakhazikitsa chisilamu chomwe ntchito yake ndi kufowoketsa chisilamu choyera, kulimbikitsa kukanira za Mulungu, ndikumapanga zofuna za anthu omwe ali okanira mudziko la chisilamu ndi asilamu.
Mukulankhula mwachindunji ndi mowonekera poyera, iwo adakhazikitsa chisilamu cha Wahabi, Alqaedah, Talban, Salafiy Takfiriy, mudziko la chisilamu ndikuwayitanira anthu kuchisilamu chimenechi kapena kuti anthu aziganiza mumchitidwe wamagulu amenewa ndikumawapatsa chithandizo anthuwo kotheratu, zomwe mapeto ake adafika ndikupeza zolinga zawo popanda kuti eni akewo apezekemo m’malo omwe asilamuwo amakhala.
Ntchito za Wahabi mudziko la chisilamu
1- Kusiyanitsa ndi kudanitsa pakati pa asilamu.
2- Kupha asilamu powanamizira kuti ndi anthu okanira Mulungu komanso omuphatikiza Mulungu ndi zinthu zina.
3- Kulimbikitsa Kufr ndi Shirk.
4- Kuwayipitsa asilamu ndi chisilamu kumene.

mgeirizano-wa-Saudi-dni-Amereka

Inu tangowonani kuti kodi m’mayiko achisilamu mukuchitika chiyani? Ku Iraq, Pakistan, Afghanistan, Egypt, Syria, Bahrayn, Hijaz (Saudi Arabia) ndi ….
Nthawi zina munkangomva kuti pali gulu lina la anthu omwe muchikhulupiliro chawo amamutenga Mulungu kuti ali ndi thupi, samakhulupilira upamwamba ndi ulemelero omwe atumiki ndi anthu a Mulungu alinawo monga momwe zikuwonekera poyera mu bukhu lolemekezeka la Quran pa zaulemelero wawo.
Ndipo mapeto ake amamutenga mtumiki wathu olemekezeka Muhammad (S.A.A.W) ngati munthu wamba komanso ndikumutsitsa pomulongosola ndi kumudziwitsa kwa asilamu kuti ankapanga machimo (ochimwa).
Munkangomva kuti muchisilamu cha Wahabi, mukuchitika zinthu zambiri ndipo pali malamulo odabwitsa, ankhanza komanso odandaulitsa kwambiri omwe akuperekedwa ndi akuluakulu awo ndipo ali ndi Hisitore yodandaulitsa kwambiri.
Munkangomva kuti Wahabi mudziko la Hijaz (Saudi Arabia), Karbala, Najaf, Twaif ndi … adapanga zotani.
Koma tsopano ndizoti mukuchita kuwona ndi maso anu kuti akupeleka lamulo loti aziwononga manda a anthu abwino ndi olemekezeka pamaso pa Mulungu.
Zotsatira za lamulo limeneli ndikomwe kuli kuwononga ndi kuphwanya manda a ana amtumiki wachisilamu mu dziko la Iraq.
Zotsatira za lamuloli ndiko kuphwasula manda a munthu olemekezeka Swahabah wa mtumiki mu dziko la Syria ndikutulutsa mtembo wake ndipo mpakana pano sizikudziwika kuti adawupititsa kuti.
Zotsatira zake ndiko kupha moipitsitsa anthu pogwiritsa ntchito zida zankhondo padziko lapansi.
Akupanga zimenezi potsatira lamulo lomwe alinalo ngakhale kuti lamuloli lilibe kochokera kwake m’mabuku ndi muchiphunzitso cha chisilamu.
Akubwera ndikudula khosi lamunthu ndikung’amba chifuwa chake ndikutulutsa mapapo ake ndikuluma.
Kodi zimenezi sichiphunzitso cha umbuli chomwechija chomwe adali nacho Abu Sufiyan ndi mkazi wake Hind?
Munkangomva zimenezi kuti mu Hisitore zidachitika zoterezi koma tsopano mukuchita kuwona ndi maso anu. Anthu amenewa abwelera ku umoyo wa umbuli bwanji?
Palibe tsiku lomwe lingadutse popanda kumvapo kuti ku Iraq, Pakistan, Afghanistan, Egypt, Syria, Hijaz (Saudi Arabia), Bahrain ndi… kwachitika zoipitsitsa kwambiri popha anthu omwe ali asilamu.
Kodi ndi munthu wake uti mfulu yemwe sanganyasidwe ndi mchitidwe ngati umenewu?
Tangowonani m’mene dziko la Saudi Arabia likuthandizira dziko la Israel mudera la Gaza, Karanah Bakhtariy, Lebanon ndi Palestine. Atsogoleri opepera ndi zinthu za zii adziko la Saudi Arabia olo ndi pang’ono pomwe palibe chomwe adapangapo potsutsa ndi kulimbana ndi machitidwe a Israel.

Saudi-kuthandiza-Israel

Kapenanso kumawamenya asilamu omwe amapanga ziwonetsero mudziko la Saudi chifukwa choti amatsutsa mchitidwe omwe anthu ena adapanga popanga filimu yomunyoza mtumiki wathu.
Kodi dziko la Saudi lathandiza bwanji zida popha asilamu ku dziko la Bahrain?
Limeneli ndi vuto lalikulu kwambiri mudziko lachisilamu ndipo chifukwa chazimenezi ndikoyenera kuti diso la asilamu lilire magazi.
CHITHUNZI
Wahabi ndi chisilamu chomwe chidapangidwa ndi mayiko odzikweza okalamba.
Zodandaulitsa kwambiri ndi zoti Wahabi, likupita patsogolo ndi ndalama za mafuta ndinso chuma cha asilamu chomwe chaka ndi chaka chimakhala chikulowa ndi asilamu mudziko la Hijaz (Saudi Arabia) ndikumagwa m’matumba awo, ndipo mapeto Wahabi ndi chisilamu chomwe chikuwononga kwakukulu chipembedzo cha chisilamu.
Kodi nthawi yake siimeneyi kuti tichimvetsetse ndi kuchidziwa chiWahabi?
Kodi timayenera kutulutsa ndalama zochuluka bwanji kuti tichilongosole chi Wahabi kwa anthu adziko lapansi makamaka asilamu?
Anthu awo (mafumu adziko la Saudi Arabia) omwe akuzitenga ndi kumazichemelera kuti ndiosunga makiyi anyumba ya Mulungu, siali kathu koma kungopatulako kuti ndi anthu omwe ali ankhanza ndinso okakala mtima kwambiri omwe akupitiriza njira ndi mchitidwe wa Yazid.
Kodi timayenera kutulutsa ndalama zochuluka bwanji?
Eni akewo adabwera ndipo adatsimikizira zimenezi kudziko lapansi.
Tawonani zomwe zikuchitika mu dziko la Syria, kuphulitsa ndi kuziphulitsa komwe kukuchitika ndi anthu omwe akupusitsidwa ndikutumidwa ndi magulu amenewa pakati pa anthu omwe akuswali mumzikiti. Kodi zimenezi ndi zochepa?! Kodi kukhetsedwa kwa magazi a munthu ndi zochepa?

من قتل نفسا بغیر نفس أو فساد فی الأرض فکأنما قتل الناس جمیعا

Imam Khomeiniy ali ndi mawu poyankha zomwe zidachitika kwa anthu aku Iran omwe adaphedwa ku Haj, malo omwe ngati munthu akupita ndi kukapanga Haj ndikukamuyankha Mulungu ponena mawu oti LABAIK, alibe ufulu komanso sakuloledwa kupha chinthu, ngakhale udzudzu utatera padzanja lake siali ololedwa kupha udzudzuwo, siali ololedwa kudzipweteka ayi.
Kodi anthu olamula mudziko la Saudili adapanga zinthu zoipitsitsa bwanji pa malo olemekezekawa munthawi ya Haj?
Kodi pangakhale tchimo lalikulu kuposa ili?

 

{flvremote}{/flvremote}

 

Kupha unyinji wa anthu aku Iran pamalo olemekezeka kwambiri yomwe ili nyumba ya Mulungu (KABAH), munthawi yabwino kwambiri, mukaphedwe komvetsa chisoni omwe adapita ndicholinga chokapanga Haj.
Udindo waukulu mudziko lachisilamu polimbana ndi mchitidwe oterewu padakali pano uli m’manja mwa ma Sheikh ndi ma Ulama akuluakulu a Ahal Sunna Waljamaa.
Akuyenera kuyima polimbana ndi gulu lopangidwa mwabodza ndipo akuyenera kuchotsa dontho lakuda limeneli muchisilamu.
Wahabi olo ndi pang’ono pomwe palibe ulemu omwe wachisungira chisilamu.
Pelekani lamulo (Fatwa) kwa ma Wahabi ngati momwe adapelekera lamulo Shia kwa gulu la Bahaay.
Mapeto ake Wahabi palibe Halal yomwe sadzayipanga kusakhala Haram ndipo palibe Haram yomwe sadzayipanga ndi kusakhala Halal.
Imam Khomeiniy akuti:
“Ngati zingakhale kuti timukhululukire Sadam Husein ndi Amereka, koma olo ndi pang’ono pomwe sitingawukhululukire ulamuliro wamtundu wa Saudi”
Amereka idapanga zinthu zoyipitsitsa kwambiri, zida zowopsya zomwe zimapha anthu mwaunyinji, zoperekedwa ndikuthandizidwa ndi dziko la Amereka ndi kupha komwe adapanga kwa anthu oponderezedwawa, kuphulitsa ndege yonyamula anthu apaulendo ya dziko la Iran, zowopsya zomwe adapanga Sadam Husein popha anthu adziko la Iran okwana 400,000,zonsezi zikhale mbali ina, koma Imam Khomeiniy akuti:
“Ulamuliro wamtundu wa Saudi udapanga zoyipitsitsa komanso zopweteka kwambiri kuposa zomwe Amereka ndi Sadam adapanga”
Anthu amenewa adaphwanya kuwala ndi kuyeretsedwa kwa chipembedzo cha chisilamu. Kodi mukufuna tiwalongosole ndani posakhala iwo?! Zonse tikunenazi umboni wake padakali uli penapaliponse.
Wahabi lopangidwa ndi mayiko opondereza okalamba, lili padziko lapansi lino ndicholinga chofuna kukwaniritsa zofuna za Satana wamkulu ndi kupondereza mudziko la chisilamu.
Zikhulupiliro zoipa, malamulo owopsya, mchitidwe wankhanza ndi anthu ena osakhala iwo polimbana ndi chisilamu.
Ndithudi munthu amene angachokere mayiko omwe kulibe chisilamu ndikumva za chisilamu chomwe iwo akuchilongosolachi komanso akuyesetsa ndikumachifalitsa penapaliponse, anganyasidwe ndi chisilamu ngati chimenechi.
Kutanthauza kuti chiyani?
Kutanthauza kuti Wahabi akuwononga kwakukulu chisilamu chathuchi. Akuwononga chisilamu ndikuwafowoketsa asilamu kuchokera mkati, powagawanitsa, kuwayambanitsa, ndi kuwamenyanitsa zomwe zikupangitsa kuchepa kwachiwelengero cha asilamu ndi kumawawonetsera asilamu kuti chisilamu ndiye zomwe tikupangazi.
Akumanena Allahu Akbar, Lailaaha illa Allah, kwina akudula mutu wamunthu ndikung’amba mimba yake ndikutulutsa mtima wake ndikuluma ndi mano ake ndikumadya.
Pambuyo pa kuima kwa asilamu polimbana ndi ulamulilo wa dziko lankhanza ndi lopondereza la Egypt, zomwe zidaika bata ndi mtendere wadziko la Isiraeli pachiwopsyezo, mayiko opondereza akuwulaya ndi mayiko azungu adakhala pakalikiliki pofuna kuthandiza dziko la Isirael adakhala pampungwepungwe.
Israel lomwe liri dziko lankhanza lalikulu, dziko labodza lalikulu, maikowo atawona kuti dziko la Isiraeli lili pachiwopsyezo, adafuna kuti alande dera lonse lomwe liri pakati pa mitsinje iwiri ya Euphrates ndi Tigris koma mapeto ake ataona kuti nawonso alipachiwopsyezo, adaganizo zokhazikitsa chisokonezo m’mayiko awiri omwe ali owandikirana ndi dziko la Isiraeli, Egypt ndi Syria.
Adapanga zotheka kuti pakhale kusagwirizana pakati pa asilamu, ndikuti mukhale chiphunzitso cha Wahabi omwe kumbuyo kwawo akuthandizidwa ndi Zionist.
Mukudziwa bwino lomwe kuti chiyambi cha Wahabi chikulumikizana moyipa kwambiri ndi Yahud komanso ndi mayiko opondereza okalamba.
Pitani mukawerenge History yake.
Kodi kupeza kwake mphamvu Wahabi kudali kotani?
Pomwe mudzawona kuti adabwera kudutsira mukupha anthu osalakwa, adalanda dziko la Hijaz, ndikuwukira mayiko achisilamu popha asilamu ochuluka kwambiri ndipo mapeto ake ndikusintha dzina la Hijaz polisinthanitsa ndi dzina la mtundu wa anthu omwe adagwirizana m’machitidwe ndi mchikhulupiliro ndi Wahabi omwe uli mtundu wa Saudi, zomwe zikutanthauza kuti olamulira wadzikoli, udzakhala kwa yekhayo yemwe ali ochokera kumtundu umenewu ndipo munthu wina ochokera mudzikoli osakhala wamtunduwu alibe ufulu okhala mtsogoleri wadzikoli.
Asilamu akuima polimbana ndi mchitidwe wa Isiraeli ndi Zionist m’mayiko achisilamu koma ndipomwe tikuwona kuti Wahabi, Saudi Arabia akubwera ndikumalinbikitsa ndikuthandiza mchitidwe onyasawu.
Kuchokera kudziko lalikulu kwambiri lomwe likuyitanira ku chisilamu lomwe liri Saudi Arabia tikumva zinthu zodabwitsa kwambiri.
Kodi dziko la Saudi Arabia liri ndi ndalama zochuluka bwanji pofalitsa chisilamu chabodzachi? Kodi ndalama zonsezi zikugwira ntchito yanji?
Chiphunzitso chomwe chikubwera ndikumawaphunzitsa anthu Shirk m’malo mwa Tawhid, ndikumachilongosola chisilamu kuti ndi chipembedzo chankhanza.
Inu tangowonani kuti mayiko amene muli chiphunzitso chimenechi cha Wahabi, ndipo likulu lake ndikukhala Saudi Arabia, akumabwera m’mayiko amene asilamu akukhala monzunzika chonchi ndi kumalimbikitsa ndinso kumathandiza mchitidwe oyipawu.
Kodi zimenezi ndi zobisika kwa munthu?
Kodi zopweteka zimenezi munthu akadandaule kuti?
Anthu omwe akutengedwa kuti ndi akuluakulu oyitanira chisilamu ndi omwe ali adani akuluakulu owononga chisilamu padziko lapansi.
Iwowa atembenuza zomwe versi ya Quraniyi ikunena kuti:
محمد رسول الله و الذین معه أشداء علی الکفار رحماء بینهم
Zoterezi ndi zopweteka kwambiri kuposa zomwe angapange mayiko opondereza monga Amereka pomwe akuyesetsa kumayilongosola Shirk m’malo mwa Tawhid ndikumapereka lamulo lakumapha anthu osalakwa, Zomwe zikuchitika kumayiko awiri Egypt ndi Syria ndipo Wahabi akupangadi zimenezi m’mayikowa.
Zomwe zikutsimikiziridwa ndi ena mwa Hadith kuti kumapeto kwa nthawi Imam Mahdi (A.A.T.F) asadawonekera kudzakhala kukuchitika zinthu ngati zimenezi omwe uli mchitidwe wa Sufiyaniy.
Sufiyaniy ndiye Wahabi amene akupezeka m’mayiko achisilamu ndi cholinga chofuna kukwaniritsa zofuna zake.
Kodi ku Egypt adapanga zotani?
Tangowonani kuti masiku apitawo takhala tikuwona zolembedwa m’misewu ndi m’manja mwa anthu ena ku Egypt kuti:
لا شیعة فی مصر
Kulibe Shia ku Egypt
Ndipofunikanso kunena izi:
Asangokhala anthu otsatira Ahalbait okha (Shia) omwe ayenera kulimbana ndi mchitidwe wa Wahabi koma kuti munthu wina aliyense ali ndi umunthu, ndi udindo wake kutero. Chifukwa chakuti omwe adayamba kutsutsana ndi mchitidwe umenewu ndi ma Sheikh akuluakulu kumene a Ahal Sunnah kuchokera kale polimbana ndi anthu omwe adali oyambitsa zikhulupiliro zoipazi monga pomwe amalimbana ndi Ibn Taymiyah ndipo nthawi imeneyo adalemba zambiri potsutsa maganizo ake, akuluakulu a Ahal Sunnah adaima polimbananso ndi Muhammad Abdul Wahab ndi omutsatira ake.
Ngakhale kuti Wahabi mkwiyo wake ukulunjika pofuna kulimbana ndikupha anthu otsatira Ahalbait (A.S) – Shia – koma posachedwa alinso ndimaganizo odzapereka lamulo lakupha munthu wina aliyense yemwe adzayima polimbana ndi mchitidwe wawo ndikumutenga kuti ndi Kafir.
Ndipamenenso tikuwona m’mahadithi kuti nthawi yomwe Imam Mahdi (A.A.T.F) akadzakhala pang’ono kubwera, Sufiyaniy pofuna kupha ndikupeza mutu wa Shia azidzayika mphoto zochuluka kuti wina aliyense yemwe angaphe Shia m’modzi ndiye kuti tidzamupatsa mphoto zochuluka chonchi. Koma kupitilira apo, pofuna kupeza zadziko adzafika pamlingo oti azidzaphanso anthu ochokera m’magulu ena achisilamu ndipo poyankha azidzati:
“ Awa adali ma Shia ndipo amazibisa (amapanga Taqiyah)”
Dziwani izi kuti muchikhulupiliro cha Wahabi, ndizoti wina aliyense yemwe adzatsutsana ndi iye adzapatsidwa lamulo lakuti ndi Kafir ndipo ayenera kuphedwa.
Wahabi omwe amakanira zakuzindikira kwa atumiki pa zinthu zobisika, amakanira za ulemelero ndi kuyeretsedwa komwe atumiki alinako.
Mapeto ake amati chinthu chachikulu chomwe chikupangitsa kuti Shirk idzifalikira pano padziko lapansi ndiko kupezeka manda a mtumiki wathu Muhammad (S.A.A.W) ndipo chinthu chachikulu chomwe chingapangitse kuti Shirk imeneyi ithe yomwe idzakhala njira yodziwandikitsa kwa Mulungu pochotsa Shirk imeneyi, ndiko kugumula manda a mtumiki.
Wahabi adakhazikitsa chisokonezo mudziko la Egypt ndipo adapanga komanso akupanga zimezi m’mayiko ambiri.
Tawonani kuti ku Pakistan kukuchitika chiyani, Iraq, Afghanistan, Syria ndi mayiko ena a chisilamu.
M’mayiko ena omwe siali achisilamu ndipo chiwelengero cha asilamu ndi chochepa, tikuwona Wahabi sakuwonekera poyera koma m’malo mwake mayiko opondereza aja ndi omwe akupezeka ndikuwonekeranso poyera. Monga m’mene zikuchitikira mudziko la Mynmar.
Ku Egypt ndi ku Syria panthawi yomwe anthu adawina polimbana ndi atsogoleri opondereza, ndipomwe tikuwona kuti Wahabi akubwera ndikusokoneza kupambana kumeneko ndipo ndikuyamba kuyambanitsa anthu mapeto ake ndikumalemba zinthu zowonetsa udani ndi anthu otsatira Ahalbait (A.S) mpakana kufikira zomwe zachitika posachedwapa zomwe ngakhale chinyama sichingachitiridwe mchitidwe oterewu.
Tsiku lokumbukira kubadwa kwa Imam Mahdi (A.A.T.F) pa 15 Shaban mudzikoli mudachitika zinthu zoyipa bwanji?! Nanga adawagawanitsa bwanji anthu adziko la Egypt ndipo zochitika zimenezi zikungopitilirabe mtsogolo kufikira kuti mtundu wa asilamu ukutha mosayembekezereka.
Gulu lochepa la anthu otsatira Ahalbait (A.S) pa tsiku la 15 Shaban ndicholinga chokumbukira kubadwa kwa Imam Mahdi (A.A.T.F) adasonkhana mnyumba mwa Sheikh wina otchedwa Hasan Shahatah, yemwe adali Sheikh wamkulu komanso ophunzira mozama wa Ahal Sunna chifukwa chakufufuza kwake powerenga mabukhu, adalowa muchiphunzitso cha Ahalbait (A.S) (Shia) ndipo anthu ambiri omwe ankabwera ndikumamvelera zina muzolankhula zake, nawonso ankapeza mwayi odziwa za chiphunzitso cha Ahalbait (A.S) mapeto ake amakhamukiranso ku chiphunzitso chogwirizana ndi umunthuchi.
Zonsezi zimachitika chifukwa choti ma Shia ndi ana a Umboni, kutanthauza kuti samalankhula zinthu zopanda umboni kapena zosemphana ndi chilengedwe ndi nzeru za munthu chifukwa ndi m’mene adaphunzitsidwira ndi Ahalbait (A.S).
Mwachifukwa ichi anthu omwe ali osochera chifukwa choti alibe zolankhula zomveka polimbana ndi chiphunzitso cha Ahalbait (A.S), alibenso njira ina yofuna kulimbana ndi anthu otsatira chiphunzitso cha Ahalbait (A.S), mwachoncho njira yokha yomwe alinayo polimbana ndi Shia ndiko kupha anthu otsatira chiphunzitsochi.
Tikamawona makanema ndi mafilimu azinthu zomwe adapangazi, munthu wina aliyense anganyasidwe kwambiri.
Tawonani zomwe zidachitika kuti anthu otumidwa ndi Wahabi opitilira 2000 adapandukira ndi kuphwanya nyumba imeneyi yomwe gulu lochepa la otsatira a Ahalbait (A.S) adasonkhanamo chifukwa chokumbukira Imam Mahdi (A.A.T.F).
Anthu amene adali akumvelera zolankhula za Sheikh ameneyu omwe ankateteza kuti Sheikhiwo asaphedwe, nawonso adaphedwa.
Adamupha Hasan Shahatah momvetsa chisoni kwambiri ndipo mapeto ake adanyoza mtembo wake nawumangilira kunjinga ya moto ndikumaukhwekhwesa mumnsewu watala.
Munthu amene angawone zoterezi angakumbukire Imam Husein (A.S) chifukwa cha zomwe zidamuchitikira.
Apa Hasan Shahatah ndi anthu opitilira 2000 pomwe anthu okwana 20,000 pa Karbala kulimbana ndi anthu 72, kodi kumeneko kudachitika zotani?
Tsiku lobadwa Imam wanthawi yathu ino adalisandutsa ndikukhala tsiku lamagazi.
Kodi nanga ku Syria kudachitika zotani?
Ine ndikupempha abale okendedwa asilamu anzanga kuti awalongosolere anthu zinthu zimenezi. Uwu ndi mwayi wathu oti tithe kuwawuza anthu ena zinthu ngati zimenezi.
Mulungu apa akutipatsa mwayi munthawi ndi malo osiyanasiyana kuti tithe kulongosola ndi kuwawuza anthu zoyipa zomwe zikuchitika m’mayiko achisilamu padziko lino lapansi.
Kodi munthu amene akuzitenga kuti ndiwachilungamo, angapange zinthu zoyipa ngati zimenezi?, angapange mchitidwe umenewu?
Unyinji wa anthu ochuluka chonchi ubwere ndikupha munthu m’modzi ndi kuyalutsa mtembo wake pambuyo pophedwa.
Tatiyeni tiwone ku dziko la Syria.
Nubel ndi Alzahra, medera ang’onoang’ono awiriwa mudziko la Syria, komwe kukuchitika zowopsya zikuluzikulu popha anthu osalakwa. Komwe padakali pano anthu am’maderawa, nkhondo yaikulu yomwe alinayo ndiko kungopeza madzi ndi chakudya kuti asamwalire.

Nubel-Alzahra

Kodi m’maderawa mukuchitika chiyani?
Ndichifukwa chiyani tikuphimbidwa ndi zomwe zikulengezedwa ponkhudzana ndi zinthu zimenezi ndipo tatsalira kwambiri pofuna kudziwa zomwe zikuchitika m’mayikomu.
Ndichifukwa chiyani tikuphimbidwa posadziwa zomwe zikuchitika ku dziko la Syria pomwe zowona ndi machitidwe a Saudi Arabia, Wahabi ndi Salafiy Takfiriy zikuwonekera poyera.
Nanga apa ndichifukwa chiyani sitikulankhula zokhudzana ndi anthu omwe ali ndichikhulupiliro cha umodzi wa Mulungu monga akhirisitu?

Wahabi, Salafiy Takfiriy akupha ndikudula mitu ya akhirisitu awiri ku Syria uku akunena kuti ALLAHU AKBAR, Bismillah, Alhamdulillah ndi …

{flvremote}http://tvshia.com/farsi/up-files/videos/soriyeh/tvshia%20soriyehok.flv{/flvremote}

Chifukwa chonena kuti anthu ngati amenewa akumatengedwa ndikumawapha ndi tchimo loti adapezeka ndi manambala afoni omwe amayimba polimbana ndi mchitidwe oyipawu ndipo ena mwa iwo adali otsatira Ahalbait (A.S) (Shia).
Ena mwa machitidwe a Wahabi omwe ali otsatira Yazid Ibn Muawiyah, akumatenga mpeni ndikumugwiritsa m’manja mwana wam’ng’ono kuti amenye ndikuzinga mutu wamunthu.
Akubwera ndikumupanga mwana ochepa, osalakwa kukhala wakupha ngati chinyama chakutchire.
Kumupatsa mwana wamng’ono chikwanje kuti adule mutu wa msilamu powugagada

{flvremote}http://tvshia.com/farsi/up-files/videos/soriyeh/tvshia%20soriyeh4ok.flv{/flvremote}

Zikuwoneka ngati mukupezeka kwawo olo ndi pang’ono pomwe mulibe mtima ndi chisoni.
Tangowonani kuti akumutenga mwana wam’ngono ndikumumangilira kenako ndikupha mayi ndi bambo ake iye akuwona ndi maso ake.
Kumangilira amwana wa zaka zitatu ndi tcheni ndikupaha bambo ndi mayi ake akuwona ndi maso

Kumangilira-mwana-wa-mng'ono-ndi-kupha-makolo-ake-

Kupha mwana wa zaka zitatu pomunyonga

kumangilira-mwana-wazaka-zitatu

Kodi ku Syria kukuchitika zotani popha anthu osalakwa, ana, amayi ndi amuna kumene. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani.
Wahabi adapeleka lamulo loti ndi Halal wina aliyense yemwe angamupeze osakhala ochokera mwa iwo, apange naye chinachirichonse chomwe akufuna ngakhale kumupha kumene. Kodi zimenezi zikutathauza chiyani?
Gulu lowukira lomwe alipanga mudzikoli mudzina loti akulimbana ndi ufulu wawo, siali kanthu kungopatulako kuti ndi anthu omwe ali ngati zinyama mwinanso kuposa nyama yakutchire.
Kupha msilikali wachisilamu oteteza dziko lachisilamu ndikutulutsa mtima wake ndikuluma komanso kudya.

{flvremote}http://tvshia.com/farsi/up-files/videos/soriyeh/tvshia%20soriyeh5ok.flv{/flvremote}

kupha mwana wam’ng’ono pomuganizira kuti ndi Dajjal ndikumudula mutu wake.

kuzinga-mwana-wana-pomuganizira-kuti-ndi-Dajjal

Chifukwa chiyani zonsezi?
Anthu amene akumamutenga mtumiki Muhammad (S.A.A.W) kuti ndi mtumiki wawo, m’mene angafunire akupereka lamulo loti aphwanye manda a olemekezeka Hazrat Zainab (A.S) ku Syria. Posachedwapa adayika Bomb yolemera 500 kg m’manda a olemekezekayu yomwe mwamwayi adayipeza nayichotsa.
Kupereka lamulo (Fatwa) logumula manda a olemekezeka Zainab (S.A) mwana wamkazi wa Fatima Alzahara (S.A) yemwe ali mwana wa mtumiki wathu Muhammad (S.A.A.W).

Lamulo-la-kugumula-manda-a-Zainab-(s.a)

Kufukula manda a Swahabah okondedwa wa mtumiki (S.A.A.W) Hujr Ibn Uday (A.S) ndikutulutsa mtembo wake ndikuwuyalutsa

kufukula-manda-a-Swahabah-wa-mtumiki

Zomwe adapanga pofukula manda a Swahabah olemekezeka wa mtumiki HUJR ibn UDAY ndikutulutsa mtembo wake, alinso ndi cholinga choti apange chimodzimodzi pa manda omwe ali ku Egypt, Syria ndi Iraq.
Kodi chisilamu achiyipitsa bwanji popereka lamulo (Fatwa) la Jihad ya chiwerewere.
Ndichifukwa chiyani sitikutengapo gawo powawuza anthu kuti chisilamu sizomwe Wahabi akupanga, kapena sizomwe iwo akulamula.
Kukhala chete kumeneku ndi zinthu zomwe satana wamkulu akusangalala nazo.
Akazi opanga Jihad yachiwerewere potsatira lamulo la Wahabi

Akazi-okapanga-Jihad-ya-chiwerewere-ku-Syria

Kuwawuza akazi aku Tunisia kuti apite ku Syria akapange Jihad yachiwerewere ndicholinga chofuna kuyika chikoka kwa anthu ena kuti akalowe nawo mugulu la anthu akupha omwe akuwukira dziko lachisilamuli.
Pomwe tikuwona kuti ku Tunisia komweko amayi omwe adamva lamulo limeneli adati:
“ Ngati chisilamu ndichotere ndiye ife ndi onyasidwa ndi chisilamu chimenechi”.
Mapeto ake ndi oti adapanga gulu lankhondo la akazi kuchokera kudziko la Tunisia opanda Hijab, osavala, akumadzilemba pamatupi awo ndikumawotcha mbendera zolembedwa mawu oti; Laa ilaha illa Allah.
Kuwotcha mbendera yolembedwa Laa ilaha illa Allah

zimayi-kuwotcha-mbendera-yolembedwa-Laailaha-

Komwe kuli kunyoza chiphunzitso chachisilamu ndikuyalutsa ulemelero ndi kuyeretsedwa kwa chisilamu.
M’modzi mwa anthu akuphawa atagwidwa pomufunsa ankayankha ponena kuti amawapatsa ndalama zokwana 700 Dollars kuti akadule mutu wamunthu yemwe ali otsatira Ahalbait (A.S) (Shia).

{elvremote}http://tvshia.com/farsi/up-files/videos/soriyeh/tvshia%20soriyeh2ok.flv{/flvremote}

Tatiyeni tibwelere ku Hadith ija yomwe ikunena kuti:

من سمع مسلما ینادی یا للمسلم فلم یجبه فلیس بمسلم

{flvremote}http://tvshia.com/farsi/up-files/videos/soriyeh/tvshia%20soriyeh3ok.flv{/flvremote}

Kutanthauza kuti ngati patapezeka munthu msilamu akuyitana kuti Ee! Inu asilamu ndithandizeni, ngakhale atakhala kuti ali kutali bwanji koma wakumvayo osamuyankha ndiye kuti simsilamu ayi.
Ntchito yochepa yomwe tingapange pothandiza kwa munthu ameneyo, ndiko kulengeza kwa ena kuti adziwe pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana, kusonkhanitsa anthu, alembi alembe, ojambula zithunzi ajambule, atola nkhani alengeze, wina aliyense ndi m’mene angathere muzilankhulo zosiyanasiyana ndi mukakhalidwe kosiyanasiyana awonetsere poyera mchitidwe oyipawu.
Panthawi imene dziko la Iran lidayima ndikupambana polimbana ndi ulamuliro opondereza, Satana wamkulu adayesetsa kuti awononge chisilamu chomwe chikutsatira chiphunzitso cha Ahalbait (A.S) ndi Quran koma anthu olimba ndi odziwa kufunikira kwa chipembedzo chawo adayima ndikulimbana ndi mchitidwewu ndipo mapeto ake anthuwo adaphedwa, komabe ngakhale adaphedwa adapeleka ulemelero ku chisilamu ndipo chisilamu chidapeza umoyo wina olimba polimbana ndi anthu opondereza.
Mwachoncho ina mwa ntchito zomwe tingapange. ndikukumbukira anthu onse omwe akuphedwa munjira ya Mulungu pofuna kulimbitsa chimbedzo chathuchi m’mayiko achisilamu ndi m’madera m’mene asilamu akukhala.
Tichitepo kanthu powazenga mlandu anthu akuphawa.
Tikuyenere kuzenga mlandu ma Sheikh ndi ma Ulama a Wahabi omwe akupeleka malamulo (Fatwa) osemphana ndi chipembedzo chathu komanso osemphana ndi umunthuwa.
Tiyenera kuimba mlandu mayiko amene akulimbikitsa mchitidwe oterewu makamaka mayiko achisilamu omwe akudzinamiza kuti ndi asilamu ndipo lalikulu lake ndi Saudi Arabia.
Padakali pano anthu akuphawa akumadzitcha kuti ife ndi ma Sufiyaniy. Sitikudziwa kuti ndichifukwa chiyani akunena zimenezi. Koma zowona zake ndi zakuti zinanedwa kuti Imam Mahdi (A.A.T.F) akadzatsala pang’ono kubwera, kudzapezeka mchitidwe wa gulu la Sufyani kudziko la Syria ndipo adzapeza mphamvu.
Ndipo tikuwona kuti akumapeleka lamulo loti mukabweretsa mutu wa Shia, tidzakupatsani ndalama zochuluka chonchi.
Kodi ngati tikumamva pa TV ndi pa mawailesi munkhani kuti mtundu wa Shia ndi owukira komanso wakupha, Tatiwuzeni ndikuti komwe mudamvapo munkhanimo kuti gulu la Shia lapha posakhala kuti nthawi zonse timangomva kuti laphedwa kapenanso kuti laphulitsidwa mwina panthawi yopemphera kapenanso panthawi yomwe amapita kukawona manda a m’modzi mwa anthu akunyumba ya mtumiki wathu Muhammad (S.A.A.W). Kuwonjezeranso apo ndipomwe tikuwonanso kuti ena mwa anthu omwe akudzitcha kuti asilamu enieni akupeleka lamulo lakupha pomwe muchiphunzitso cha Shia mulibe zoterezi.
Tikumupempha Mulungu kuti afulumizitse chipulutso chake pomuwonetsera Imam Mahdi (A.A.T.F).

Ndemanga
Chisilamu sizimenezi ayi. Apa ndipomwe msilamu aliyense angathe kudziwa ndikutsimikizira kuti ali pachiwopsyezo chachikulu kwambiri komanso ndipo zidzamutsimikizira kuti zowonadi muchisilamu muli magulu osiyanasiyana ndipo asangonamizidwa ndi kupusitsidwa kuti bola ali msilamu ayi. Ndipomwe wina aliyense ali ndi udindo oti adziwe gulu lomwe ali ndi zikhulupiliro zake komanso asangovomereza zikhulupiliro zina zirizonse mudzina lachisilamu popanda umboni omveka bwino.
Chizindikiro chabwino posemphana ndi magulu oyipawa
Mukadzawona chisilamu chomwe chidzakhala chikukulamulani zinthu zowonetsa nkhanza, kupanda chisoni, kupeleka lamulo lakupha anthu otsatira magulu ena achisilamu osalakwa ngakhale atakhala akunja kwa chisilamu, kudana ndi anthu azipembedzo zina omwe sakulimbana ndi chisilamu, kugemula ndi kunyoza magulu ena a chisilamu kapena anthu azipembedzo zina, kulamula ndi kulankhula zinthu zosemphana ndi nzeru ndi umunthu – Chifukwa chakuti umunthu ndi nzeru ziri ndi munthu wina aliyense mwachoncho aliyense owona zinthu ngati zimenezi adzanyasidwa nazo ngakhale atakhala kuti munthuyo simsilamu – kulankhula zinthu zopanda umboni wa Quran, Hadith kapena nzeru, zadziweni kuti chimenecho sichisilamu chenicheni chomwe mtumiki Muhammad (S.A.A.W) adabwera nacho choyera komanso chachisoni, koma kuti zimenezo ndi zakunja kwa chisilamu ndipo zabwera muchisilamu mwabodza ndipo zadziwoka ndi dzina loti chisilamu ndichifukwa chake chikutchedwa kuti chisilamu koma zowona zake sichisilamu ayi chifukwa chakuti tiribe zisilamu zambiri mpakana tizinena kuti chisilamu chabodza kapena chisilamu chakupha, chisilamu checheni ndi zina zotero.
Dziwaninso kuti Quran ndi nzeru komanso umunthu sizimatsutsana ayi, mwachoncho mutha kudzawonanso kuti wina wake akukuwuzani zinthu zoyipa ndipo akubweretsa umboni wa Quran ndi hadith, mukadzawona kuti zonena zake zikusemphana ndi nzeru ndiye kuti mwina Hadithiyo ndiyopeka kapena apo ayi akugwiritsa ntchito umboniwo pamalo osayenera kapenanso akutanthauzira umboniwo mogwirizana ndi zolinga zake osati momwe umboniwo ukunenera.

Add new comment