Ulemelero ndi ubwino wa mwezi wa Ramadhan
Mukunenedwa mu Versi ya 185 kuchokera mu Surah Albaqarah kuti:
شهر رمضان الذی أنزل فیه القرآن هدی للناس و بینات من الهدی و الفرقان، فمن شهد منکم الشهر فلیصمه، ومن کان مریضا أو علی سفر فعدة من أیام أخر، یرید الله بکم الیسر و لا یرید بکم العسر...
“Mwezi wa Ramadhan omwe Quran idatsitsidwa, Quran yomwe ndi chiwongoko kwa anthu komanso imawawunikira anthu njira yachiwongoko ndinso ndi chisiyanitso pakati pa bodza ndi chilungamo. Ndiye kwayemwe wawuona mweziwu mwa inu, ayenera kusala ndipo yemwe ali odwala kapena kuti ali paulendo adzayenera kubweza m’masiku ena. Mulungu akufuna kufewetsa kwa inu ndipo sakufuna kuti pakhale chipsyinjo kwa inu ayi…
Mwezi wa Ramadhan ndi mwezi omwe Quran idatsika ngati momwe yenenera Ayah ili m’mwambayi.
Kutanthauza kuti mwezi wa Ramadhaniwu kupezeka kwake ndi kwakukulu kwambiri kuposa miyezi ina yonse kufikira kuti Quran ikutsika m’mwezi umenewu.
Zowona zake ndi zoti Quran ikutsika, zomwe zikutanthauza kuti mphatso yapamwamba mukuzindikira chinachirichonse ya Umulungu, Mulungu wayitsitsa mphatso imeneyi m’mweziwu kukhala yowalandilira akapolo ake okondedwa. Mulungu watitumizira ife anthu apadziko lapansi chinthu cha mtengo wapatali ndinso chapamwamba.
Chinthu chapamwamba kutitsikira ife apansi ndicholinga choti chitinyamule ifenso kuti tikhale apamwamba osati apansi ayi.
Mwezi wa Ramadhan omwe anthu ali alendo a Mulungu, Mulunguyo akuwalandira bwino anthu ake okhulupilira powatumizira Quran.
Quran yomwe ikulongosola chinachirichonse.
Quran yomwe iri chiwongoko kwa anthu.
Ife anthu ndife apaulendo kupita ku umoyo osatha ndipo masiku ochepa a umoyo wathu pano padziko lapansi atha posachedwapa. Mwina mawa kapenanso lero lomwe lino.
Anthu ena omwe adabadwa zaka zapitazo adatisiya, adamwalira. Ifenso tiyembekezere kudzamwalira.
Kodi m’masiku amenewa tikuyenera kupanga zotani?
Kodi tizindikira bwanji pa zinsisi zakupezeka kwa dzikoli?
Quran ndi gome (tebulo) la mulungu.
Quran ndi mphatso ya Mulungu kwa ife.
Quran yomwe ikutisonyeza ife kuti tiyenda bwanji.
Quran ndi chiwongoko kwa anthu ndipo imatiwalitsira njira yachilungamo.
Koma kuti mbiri ina yomwe Quran ilinayo ndiko kudutsira mukugwirizitsa bukhuli ndi Ahalbait (A.S) omwe ali olongosola zenizeni za Quran, ndipomwe munthu angadziwe kuti kodi ayende munjira iti? Nanga ayende bwanji?
Munthu akumapeza njira kuchokera muzinthu ziwirizi kufikira kuti munthu akuyenda nawo pa ulendo umenewu koyamba. Kuyenda pa ulendo kamodzi kukutanthauza kuti, Padziko lapansi pano munthu akungokhala kamodzi kokha basi ndipo palibe kuyesa kaye kenako ndikudzakhala zenizeni ayi ndipo mapeto ake munthu akupambana kudutsira mukugwirizitsa zinthu ziwiri zija.
Ayayi ikupitilira kunena kuti munthu yemwe wawuona mweziwu (kutanthauza kuti wamupeza) ayenera kusala.
Ndiofowoka bwanji anthu amene sakugwiritsa ntchito mwezi umenewu bwino posala, ndipo mapeto ake osapeza nawo mwayi okhala nawo patebulo lotambasuka ndi lodzadza ndi mitendere ya Mulungu limeneli.
Koma zowona zake ndi zakuti, ngakhale Mulungu adatilamula ife kusala m’mwezi umenewu koma zotsatira zabwino za kusalaku zikubwelera kwa ife eni ake osati Mulungu ayi chifukwa chakuti iye samafunikira chinachirichonse kwa ife.
Mulungu samafunikira mapemphero omwe anthu okhulupilira amapanga chifukwa chakuti Mulungu ndi olemera. Koma apa funso ndi loti nanga ndichifukwa chiyani iye akutiyitanira ife kuti tizipanga mapempheto komanso tizipanga zinthu zomwe ziri zovuta? Ndikutinso tisadutse malire mu umoyo wathu watsiku ndi tsiku?
Zonsezi ndi mayeso a Mulungu.
Amenewa ndi malamulo omulimbikitsira munthu, komanso ndi malamulo omwe ayikidwa ndi cholinga choti munthu okhulupilira adzasiyane ndi osakhulupilira.
Ngakhale ziri choncho koma malamulo a chipembedzo cha chisilamu ndi malamulo amene amatsatana ndi chilengedwe komanso nzeru za munthu ndinso amangidwa pamwamba pa kuphweka posawavutitsa anthu ndikusawayikira chipsyinjo mu umoyo wawo.
Ngati munthu ali ndi vuto, akudwala, , mzimayi yemwe akuyamwitsa mwana, mzimayi yemwe ali ndi pakati, nkhalamba ndi wina aliyense amene alibe kukwanitsa , Mulungu wachisoni adawayikira anthuwa malamulo ena ogwirizana ndi iwo.
فمن کان منکم مریضا أو علی سفر فعدة من أیام أخر
Munyengo yadzuwa ngati munthu kungamubweletsere vuto kusala ngakhale kuti ayenera kusunga ulemelero wamwezi wa Ramadhan posapanga zinthu zosayenera, adzayenera kusala m’miyezi ina yomwe nyengo yake ndiyosatentha kwambiri komanso mausana ake ndi afupi.
Ndipo ngati nthawi ina iliyonse sangakwanitse kusala, munthu ameneyo ali ndi malamulo ena.
لا یکلف الله نفسا إلا وسعها
Mulungu amamupatsa munthu ntchito mofananira ndi kukwanitsa
Palibe malamulo muchisilamu oposa kukwanitsa komwe munthua alinako.
یرید الله بکم الیسر و لا یرید بکم العسر
Mulungu akukufunirani inu kupepuka muzintchito zanu ndipo sakukufunirani chipsyinjo ayi.
Malamulo onse achisilamu adakhazikidwa ndicholinga choti munthu akhale pa mtendere ndi ufulu, ngakhale malamulo a Mulungu omwe anthu ena chifukwa cha zolinga ndi matenda omwe alinawo, akusemphana ndi kumatsutsana nawo, zomwe zili zodandaulitsa kwambiri.
Mwachitsanzo lamulo lakunyonga munthu yemwe akufalitsa chiwonongeko padziko lapansi.
Kodi ndi anthu ake ati omwe akumatsutsana ndi lamulo lakunyonga posakhala kuti omwe amaterowo ndi anthu omwe lamulo lakunyongedwali likuperekedwa kwa iwo kumene?
Anthu akupha omwe lamulo lakunyongedwa likuyikidwa kwa iwo ndi omwe amatsutsana ndi lamulo limeneli.
Malamulo a Mulungu omwe anthu ambiri amakonda kutsutsanawo ndiwo malamulo amene angatenge gawo lalikulu kwambiri pofuna kulongosola ndi kukhonza umoyo wapagulu.
Ndipomwe Mulungu akupitiriza mu Ayayi kuti malamulo omwe tatumizawa, ngati munthu akudwala kapena ali paulendo, ndiye kuti kusala kwachotsedwa kwa iye ndipo m’malo mwake adzabweze m’masiku ena.
Ndipo ngati munthu angasemphane ndi lamulo limeneli, komwe kuli kufuna kuti asamvere ndikuti asemphane ndi chilamulo cha Mulungu, ndicho chiwonongekocho chimenecho.
Tikamati Ibadah zimatanthauza kuti kumvera ndi kutsatira chinachirichonse chonse chomwe Mulungu wanena.
Ibadah sindiye kuti m’mene mtima wanga wafunira.
Malamulo a Mulungu ndi otani?
Akuti ngati uli kumudzi kwanu, uyenera kusala.
Ngati uli paulendo usasale ayi ndipo kusala ndi Haram komanso kutero ndizomwe zikunthauza kuti Bidiah chifukwa ukupanga chinthu chomwe Mulungu wakuletsa, kutanthauza kuti sizili muchipembedzo ayi koma iwe ukuzitenga zimenezi kukhala ngati chipembedzo.
Pomwe tikudziwa bwino lomwe kuti akamati Bidiah, ndiye kuti kulowetsa muchipembedzo chinthu chomwe chiri chakunja kwa chipembedzo.
Mulungu wapamwamba adatiyikira ife okhulupilira malamulo ofewa chonchiwa ndipo ndikoyenera kuti tikhale othokoza chifukwa cha chisoni cha Mulungu chimenechi.
Ngakhale kuti sitingathe kudziwa cholinga cha malamulo amenewa koma panthawi yomwe zidzawonekera kwa ife zolinga za malamulo amenewa chifukwa cha zotsatira zabwino zomwe malamulowa alinawo, ndipomwe munthu adzakhala othokoza kwambiri kuti Mulungu ndi wachisoni bwanji potifunira ife zabwino.
Kodi Mulungu adatitumizira ife malamulo otani, omwe akutifikitsa ife ku umoyo wachisangalalo chosatha.
Mwezi wa Ramadhan ndi mwezi wamadalitso.
Mwezi umene madalitso ochokera kumwamba akutsika omwe alibe mathero.
Mwezi wachikhululuko.
Nthawi inayake yaitali (chaka chonse) ife anthu tidakhala tikupanga machimo osiyanasiyana ambiri koma Mulungu adatiyikira mwezi umenewu kukhala mwayi kwa ife kuti tizitsuke machimo omwe tidapanga.
Munthu akadadziwa ubwino wa mwezi wa Ramadhan, bwezi akulakalaka kuti:
“Umoyo wanga onse ukadakhala mwezi wa Ramadhan”
Munthu akutsukidwa m’mwezi umenewu.
Mwezi otsika Quran zomwe zikutanthauza kuti mwezi umenewu ukuyenera kukhala ndi ulemelero waukulu kwambiri kuti mpakana Quran itsike m’mweziwu.
Ngatinso momwe alili mtumiki wathu okondedwa (S.A.A.W) ndi akunyumba kwake Ahalbait (A.S) chifukwa chakuti ayah yoti:
کل شیئ أحصیناه فی إمام مبین
Chinthu china chirichonse tidachisunga mwa Imam owonekera poyera.
Ikukamba za iwo. Apa ndipomwe tingadziwenso kuti Imam wa kwa munthu ndi owonekera poyera chabe kuti anthuwo ndi omwe sakupita kwa Imamuyo.
Iwo ndi anthu omwe akulongosola zowona za bukhu lolemekezekali. Chifukwa chakuti Mulungu adawadalitsa powapatsa kuzindikira pa chinachirichonse. Mwachoncho ngati Quran ili:
تبیان لکل شیئ
Yolongosola chinachirichonse
Ndiye kuti Imam mtumiki kapena Imam ayenera kuzindikira bwino lomwe zonse zomwe ziri m’bukhuli.
Mwezi wa Ramadhan muli mausiku a Qadr. M’mausiku amenewa ndimomwe chinachirichonse chokhudzana ndi umoyo wamunthu chimawerengedwa muchaka chimenecho ndipo chinachirichonse chimayenera kusayinidwa ndi Imam Mahdi (A.A.T.F). uwu ndi udindo omwe adapatsidwa ndi Mulungu. Surah Qadr ikuyikira umboni pankhaniyi.
Ndimwezi umene nyali imodzi kuchokera munyali zowala khumi ndi ziwiri inabadwa. Kubadwa kwanyali yachiwiri kuchokera kwa Ahalbait (A.S) yemwe ali Imam Hasan Mujtaba (A.S).
Mwachoncho kuwonjezera kuti ndife alendo a Mulungu m’mwezi umenewu, ndifenso alendo a Imam Hasan Mujtabah (A.S) pomwe pali pa 15 mwezi wa Ramadhan.
M’masiku a Qadr, pomwe pali pa 19, 21 ndi 23, ndipomwe munthu akupempha kwa Mulungu kudutsira mwa mtima wa mtumiki yemwe ali Imam Ali (A.S).
أنفسنا و أنفسکم
Pali tanthauzo lalikulu kwambiri kupezeka kwa kuphedwa kwa Imam Ali (A.S) m’masiku a Qadr. Ndipomwe munthu afune asafune m’masiku amenewa akulumikizanso ndi Imam wake.
Mukulongosola kwina, munthu amene m’masiku amenewa sadzalumikizana ndi Imam Ali (A.S) ndiye kuti sadakumane nawo mausiku a Qadr.
Mwezi wa Ramadhan ndi mwezi umene Ummul Muuminin omwe ali mayi a olemekezeka Fatima Alzahra Hazrat Khadijah (S.A) adamwalira.
Mwezi wa Duwa.
Mwezi ochezera omwe munthu munthawi yonse yausiku ankagona koma chifukwa chakudya dakwi akukakamizidwa kudzuka munthawi ya usikuwu yomwe ili Ibadah.
Kukoma komwe anthu a Mulungu amakhala akukupeza muchaka chonse chifukwa chakuchezera kwawo podzuka nthawi ya usiku ndikumapanga Ibadah, Mulungu akumuyikiranso njira munthu waulesi kuti akhale okakamizidwa kuti nayenso akupeza nawo kukoma kumeneku podzuka nthawi yausiku ndi cholinga chodya dakwi.
Ndizosangalatsa bwanji kuti mpweya wanu m’mwezi umenewu ndi Ibadah.
Shaytan wamangidwa m’mwezi umenewu.
Mwezi omwe munthu akuchapidwa. Pomwe mtima wamunthu wadzadza ndi litsilo ndinso udzimbiri wamachimo komanso chifukwa choti munthu waiwala tsiku lomaliza kuti akawerengedwa zintchito zake.
Tayiwala kuti tsiku lina lake nkhope ndi thupi lathu lonse zidzakwiliridwa.
Tayiwala kuti tiri ndi tsiku loyamba la m’manda.
Tayiwala kuti kuli mafunso omwe tidzayenera kuyankha.
Koma kusala kumamukumbutsa munthu za tsiku lomaliza (Qiyamah) ndi mavuto atsiku limeneli.
Kusala kumafewetsa mzimu wa munthu.
Kusala kumatsekula maganizo ndi nzeru za munthu.
Kusala kumamufikitsa munthu pa kumuwopa Mulungu (Taqwah) pomwe Taqwah imamupatsa munthu luntha ndi kuzindikira.
Ndizachidziwikire kuti galimoto ikada ndi fumbi ndicholinga choti iyere, amayipitsa kumalo ochapitsa magalimoto. Chimodzimodzinso ife anthu kuchapidwa kwathu pambuyo poti tadetsedwa ndi machimo muchaka chonse ndiwo masiku okwana makumi atatu 30 omwe timasala m’mwezi olemekezekawu.
M’masiku 30 amenewa tikufuna kuti zinthu zomwe zidali zololedwa kwa ife (Halal), tizipange kukhala zoletsedwa (Haram).
Koma zimenezi ndizosangalatsa bwanji?! Mulungu amamukonda bwanji kapolo wake?!
Munthu amene chinthu chomwe chidali choletsedwa kwa iye chifukwa cha Mulungu ndikuchipanga chinthu cha Halalicho kukhala choletsedwa kwa iye, ndithudi palibenso kukayikira kuti sichidzakhala chovuta kwa iye kutalikirana ndi chinthu chomwe chiri cha Haram.
Munthu amene madzi kwa iye akukhala Haram m’mwezi umenewu ndithudi sadzamwa mowa.
Munthu amene sakudya zakudya za Halal ndithudi sizidzakhala zovuta kwa iye kusiya zinthu za Haram.
Munthu amene kukhala malo amodzi ndi mkazi wake akukupanga kukhala Haram kwa iye chifukwa chakusala ndithudi adzaphunzira kuti asapange chiwerewere.
Ndithudi munthu amene azadzitchinjiriza kuchokera ku zinthu za Haram.
Tanena kale kuti mwezi umenewu ndi mwezi omwe munthu akukhala mlendo ndipo mwini nyumba ndiye Mulungu.
Kodi Mulungu ameneyu ndi mphawi kapena olemera? Ndizachidziwikire kuti ndi olemera. Kodi Mulungu olemera adzamulandira bwanji munthu? Ndi chinthu chanji chomwe angatibweletsere pokhala kuti ndife alendo?
Akamalongosola tanthauza la mawu oti Ramadhan omwe akuchokera muliwu loti Ramadha muchilankhulo cha chiluya, zikunenedwa kuti akamati Ramadha ndiye kuti mvula yoyamba yomwe imagwa munthawi ya dzinja yomwe imachotsa fumbi lomwe lidabwera chifukwa cha nyengo ya dzuwa pambuyo poti china chirichonse chadzadza ndinso chakutidwa ndi fumbi.
Mwezi wa Ramadhan chifukwa cha madalitso osatha omwe akubwera kuchokera kwa Mulungu wapamwambamwamba ndikutitsitsira ife, mzimu wamunthu omwe udadzadza ndi machimo, fumbi, litsilo ndi dzimbiri umachapidwa ndi kutsukidwa.
M’mwezi umenewu munthu amakumbukira anthu osauka. Mtima wa munthu umakhala ofewa komanso wachisoni.
Kapenanso kuti tanthauzo lina la Ramadhan ndiye kuti kutentha. Kutentha komwe mwala umatenthedwa chifukwa cha dzuwa.
Kutanthauza kuti chiyani?
Kutentha kwa dzuwaku, kumachotsa zoyipa ndi nyasi zomwe zidali pamwala umenewu.
Kukhala ngati kuti Ramadhan kwa munthu, ndi kutentha komwe kumamuchitikira munthu ndicholinga choti machimo ndi zonyasa zake ziwotchedwe, komanso chinthu chomwe chimamupangitsa munthu kuti azipanga machimo chiwotchedwenso.
Zinthu zoipa zomwe zidakhazikika pa mzimu, mtima ngakhale thupi kumene zimachoka chifukwa chakusala.
Inu mukudziwa bwino lomwe kuti kusala kuli ndi ubwino wanji.
Kupilira kwa munthu kumawonjezereka. Madzi ali patsogolo pako uli ndi ludzu koma uyenelera kupilira.
Ena mwa maubwino omwe kusala kulinako ndi oti, Matenda ambiri a mthupi mwa munthu amachoka.
Mavutonso a mumtima mwathu amatha.
Kuganiza kwathu kumatsekuka.
Njala imapangitsa kuti thupi lamunthu likhale ngati mzimu.
Mphunzitsi wamkulu otchedwa kuti Ziyayi, polongosola hadith ya Miirajiyah, pokhudzana ndi zotsatira za njala, akulongosola kuti anthu omwe Mulungu adawapatsa luntha amanena kuti:
“Mzimu wanthu chifukwa chakudya kwambiri umakhala thupi – kutanthauza kuti mzimu omwe udali opepuka komanso ofewa, umalemera mwachoncho siungathe kuwuluka komanso siungathe kupanga ntchito zake moyenera – ndipo thupi la munthu chifukwa chakudya pang’ono limakhala mzimu”.
Izi ndi zomwe zimachitika m’mwezi wa Ramadhan.
Imodzi mwa mahadith a mtumiki ikulongosola kuti adafika munthu wina wake panthawi yomwe udawoneka mwezi wa Ramadhan, adanena kuti:
“Wabwera Ramadhan”
Olemekezekawo adati:
“Osanena kuti wabwera Ramadhan koma unene kuti mwezi wa Ramadhan wabwera”.
Uku kudali kuwonetsa ulemelero wa mwezi umenewu. Zomwe zikutitanthauzira kuti munthu asangonena kuti Ramadhan powutchula mwezi umenewu zomwe zidzakhala ngati kuti wanyoza ndinso wapanga chinthu cholakwika kwambiri koma ayenera kunena kuti mwezi wa Ramadhan.
M’mwezi umewu muli mausiku a Qadr. M’masiku amenewanso muli usiku omwe Imam Ali Ibn Abi Twalib (A.S) adakhapidwa ndi lupanga la poison pamutu pake.
Ndithudi udatchedwa mwaziwu kuti mwezi wa Ramadhan chifukwa chokhala ngati kuti umasungunula machimo ndikuwafafaniza.
Munthu chifukwa chanjala zimamupangitsa kuti ndi pang’ono pomwe aziganiza bwino pokumbukira anthu anjala, makamaka pokumbukura tsiku lomaliza.
Ayah ina mu Quran ikulongosola kuti:
یآ أیها الذین آمنوا کتب علیکم الصیام کما کتب علی الذین من قبلکم لعلکم تتقون.
Ee Inu anthu amene mwakhulupilira! zalembedwa kwa inu kusala kukhala kokakamizidwa .
Koma kuti kusalaku kuli kokakamizidwa kwa anthu omwe akhulupilira ndipo kwa anthu omwe sadakhulupilire sichikakamizo ayi.
Chotinso tidziwe ndi chakuti kusala ndi Ibadah yomwe ikusiyana ndi ma Ibadah ena chifukwa chakuti kusala sindiye kuti munthu apange ntchito ina yake ayi, koma kuti asiye kupanga ntchito zina zake.
Monga Swala pomwe munthu sakufunikira kuwerenga Surah Fatiha, Surah ina iriyonse, kupanga Dhikr, Rukuu, Sajdah, Qunut ndi zina zotero.
Mwachoncho mukusala mulibe gawo lakupanga zinthu moziwonetsera (Riya) ndipo ngati kulipo ndikochepa kwambiri.
Munthu sakuyenera kunama, kutukwana, kujeda, kutsatira zofuna za mtima wake ndi zina zotero. Kukhala ngati ali pakati pa iye mwini ndi Mulungu wake.
Mwachoncho imafunikira chikhulupiliro chokwera kwambiri. Ndi munthu yekhayo yemwe angasale yemwe ali ndi chikhulupiliro chakwera kwambiri.
Ee inu anthu omwe mwakhulupilira! Apa Mulungu ndi zachidziwikira kuti amalankhula ndi anthu omwe ali atumiki, aneneri, ma Imam ndi anthu osankhika ndi Mulungu chifukwa chakuti palibe kukayika kuti iwo ndi anthu okhulupiliradi zenizeni mwa Mulungu.
Kodi ife padakali pano ndife okhulupiliranso? Ngati tiri choncho ndiye kwakakamizidwa kwa ife kusala ndipo tiyenera kutero.
Kodi Mulungu siyemwe ali osafunikira pa mamphero athu ndi kusala kwathu? Ndiye Mulungu ameneyu akufuna chiyani potikakamiza ife kuti tisale? Mulungu yemwe ali ndi luntha losatha akuzindikira chomwe akupanga.
Akuti zakakamizidwa kwa inu kusala ngati momwe zidakakamizidwira kwa anthu omwe adalipo inu musadabwere ndicholinga choti mukhale anthu omuopa Mulungu.
Ee, kusalaku kudalinso kokakamizidwa ku zipembedzo zonse zomwe zinadutsa. Chipembedzo cha chiyuda, chipembedzo cha chikhirisitu ndi zina zotero.
Olemekezeka Yesu (A.S) nawonso ankasala.
Zotsatira za kusala ndiko kukhala anthu owopa Mulungu Taqwa.
Ndinthawi yanji yomwe munthu amapanga machimo? Panthawi yomwe munthu ali ndi mphamvu zochuluka. Munthawi imeneyi ndi pomwe munthu amatsatira chilakolako chake, amapita kumachimo ndi zina zotero.
Munthu yemwe ali ndi mphamvu ndi yemwe amapondereza ena.
Imodzi mwa maphindu ndi zotsatira zomwe kusala kulinako, mphamvu yopanga machimo, kupondereza, kunama ndi … imachepa. Gawo la unyama limachepa ndipo mapeto ake mphamvu ya uzimu ndi umulungu imawonjezereka mwa munthu.
Munthu amakhala ngati zolengedwa zadziko lokwera ngati angelo. Kutanthawuza kuti munthu amafika pa mlingo weniweni wa Taqwa. Mwachoncho munthu alibenso mphamvu yopondereza anthu ena, kutanthauza kuti munthu alibenso mphamvu yopanga tchimo.
Kusala kumamupatsa munthu Taqwa, Taqwa imamupatsa munthu kuzindikira ndipo Taqwa imamupatsa munthu mphamvu yosiyanitsa pakati pachabwino ndi choyipa.
Kusala kuli ndi zotsatira zabwino kwambiri kwa munthu.
Zotsatira zabwino pa uzimu. Zotsatira zabwino pa thupi. Zina mwa izo ndiko kuubweza mtima potsatira chilakolako, kubweza ndi kuyang’anira maso, kuyang’anira lilime, kuyang’anira dzanja, kuyang’anira khutu ndi zina zotero.
Kodi zimenezi ndi zosangalatsa bwanji?
Nthawi ina tizanena kuti kodi mtumiki akulongosola zotani pankhani yokhudzana ndi mwezi umenewu.
شهر دعیتم إلی ضیافة الله
Ndi mwezi omwe mwaitanidwa kukhala alendo a Mulungu
Mulungu akulongosola mu Quran yolemekezeka kuti:
لا یحب الله الجهر بالسوء من القول إلا من ظلم
Mulungu sakusangalatsidwa kuti munthu alankhule zoyipa za mnzake kupatulako yemwe waponderezedwa.
Kutanthauza kuti munthu amene waponderezedwa ali ndi ufulu olankhula pakuponderezedwa kwake ndipo ayenera kutero.
Imam Swadiq (A.S) polongosola Ayah imeneyi atafunsidwa kuti tipatseni chitsanzo cha munthu yemwe waponderezedwa amene akuyenera kulankhula chifukwa chakuponderezedwa kwake.
Imam Swadiq (A.S) adati:
من إضاف قوما فأساء فی ضیافتهم
Munthu amene akuwaitana alendo koma osawalandira bwino powapatsa zinthu zoyenera.
Kutanthauza kuti alendowo ngati sadapatsidwe zoyenera kupatsidwa ngati alendo, ndithudi ali ndi ufulu oti alankhule chifukwa chakusalandiridwa bwino ndi eni nyumbawo.
فلا جناح علیهم فیما قالوا فیه
Palibe vuto linalilironse pa zomwe angalankhule
Atha kulankhula kuti:
Adatiitana koma sadatilandire bwino ndipo sadatipatse zoyenera kutipatsa ngati alendo.
Ndiye tikudziwa bwino lomwe kuti Mulungu ndi osafunikira olo ndi pang’omno pomwe, ndiye osafunikirayu watiitana ndipo ngati satilandira bwino kodi chingatike ndi chiyani? Ngati satipatsa zoyenera kutipatsa ngati alendo ake kodi chingachitike ndi chiyani?
Koma tikudziwa bwinonso kuti Mulungu m’mwezi umenewu watilandira bwino ndipo watipatsa zinthu zabwino kwambiri.
Kodi Mulungu watilandira bwanji m’mwezi umenewu?
Mulungu akutipezeketsera kusangalala kosatha kwathu m’mwezi umenewu.
Mulungu akutipatsa mphatso yabwino pakuzindikira kosatha komwe kuli kutitsitsira bukhu loyera la Quran, komwe kuli kutipatsanso Ahalbait (A.S).
Munthu mu mausiku a Qadr omwe Quran ikutsika, akupita kunyumba ya Imam Mahdi (A.A.T.F), Imam Ali (A.S) ndi Fatima Alzahra (S.A).
قد أقبل إلیکم شهر الله بالبرکة والرحمة والمغفرة
Wakufikirani mwezi wa Mulungu ndi mtendere, chisomo ndi chikhululuko.
Tikumupempha Mulungu kuti:
Inshaallah atipange ife kukhala anthu ogwiritsa ntchito bwino mwezi umenewu.
اللهم صل علی محمد وآل محمد و عجل فرجهم
Add new comment