Kufanana pakati pa mtumiki Isa – yesu – (a.s) ndi Imam Husein (a.s)
http://tvshia.com/farsi/images/emamhoseyn%2031.jpg
- Olemekezeka Yesu (a.s) mwana wa Maryam – Maliya – (s.a) adali oyeretsedwa.
Nayenso Husein (a.s) mwana wa Fatima (s.a) adali oyeretsedwa.
- Mtumiki Yesu (a.s) adali mwana wa mzimayi amene angelo ankamuyitana kuti:
(يا مَرْيَمُ إِنَّ اللَّهَ اصْطَفاكِ وَطَهَّرَكِ وَاصْطَفاكِ عَلى نِساءِ الْعالَمِينَ).(آل عمران/
42)
Ee Maryam! Mulungu wakusankha ndipo wakuyeretsa ndinso ndiwe wapamwamba kuposa amayi onse adziko lapansi.
Husein (a.s) nayenso ndi mwana wa mzimayi olemekezeka yemwenso angelo ankamulankhula ndipo ndi mzimayi opambana kuposa azimayi onse padziko lapansi.
- 3. Yesu (a.s) ndi mzimu wa Mulungu komanso adalengedwa ndi Mulungu.
Nayenso Husein (a.s) ndi nyali ya Mulungu ndinso khomo la mtendere ndi chisomo cha Mulungu.
- Yesu (a.s) ndi mwana wa mzimayi yemwe adali wapamwamba kuposa azimayi adziko lonse lapansi munthawi yake.
Nayenso Husein (a.s) ndi mwana wa mzimayi yemwe ndi wapamwamba kuposa azimayi onse pano padziko lapansi ndi kumwamba komwe.
- Olemekezeka mtumiki Yesu (a.s) adali otalikirani ndi zadziko lapansi, ankayika miyala kukhala choyedzamira nthawi yogona (pilo)
Nayenso Husein (a.s) adapeleka mutu wake munjira ya Mulungu ndipo adalibe thupi lake ataphedwa lidalibe mutu kuti athe kutsamila pamwala kukhala pilo.
- Olemekezeka Yesu (a.s) ankavala zovala zachisangalalo (Eid).
Pomwe Husein (a.s) adavulidwa zovala zake ndi adani munjira ya Mulungu.
- Yesu (a.s) ankakhutitsidwa ndi chakudya chochepa.
Pomwe Husein (a.s) asadaphedwe adakhala masiku atatu akumanidwa madzi ndi chakudya.
- Yesu (a.s) adalibe chuma choti akadatha kusunga.
Imam Husein (a.s), ngakhale tenti yake adayiwotcha kufikira kuti pambuyo pophedwa adamuvula ndi kuwotcha zovala zake.
- Yesu (a.s) adalibe mwana kuti ngati mwana wakeyo angaphedwe iye zunzike mumtima.
Pomwe mwana wa Imam Husein (a.s) chifukwa chakuphedwa mu njira ya Mulungu, adamufowoketsa Imam Husein (a.s) ndipo dziko linamudera kwambiri ndi ululu wakuphedwa mwana wake, komabe adalimba mtima ndi kupilira.
- Olemekezeka Yesu (a.s) mthunzi wake udali kulowa kwa dzuwa ndi m’banda kucha dzuwa litatsala pang’ono kutuluka.
Pomwe thupi la Imam Husein (a.s) lidakhala masiku atatu lili padzuwa.
- Yesu (a.s) chokera chake chidali mapazi ake awiri ndipo omugwilira ntchito ake adali manja ake.
Pomwe Imam Husein (a.s) ndi munthu yemwe mutu, manja ndi mapazi ake adazitaya mu njira ya Mulungu ndipo chale chake adani adachidula ndi cholinga chofuna kuchotsa mphete yomwe idali kuchala chake.
Add new comment