(OLEMEKEZEKA ABULFADHL ABBAS (A.
Kufikira kuti olemekezeka Fatimat Zahra (a.s) ali moyo, Imam Ali (a.s) sadakwatirenso mkazi wina ayi. Ngati momwenso zidalili kuti mtumiki wathu olemekezeka kufikira kuti olemekezeka Khadijah (s.a) alimoyo, sadakwatirenso ndi mkazi wina ayi.
Koma ndi momwe zidakhalira kuti Fatimat Zahra (s.a) sadakhalitse mnyumba mwa Imam Ali (a.s), ndipo zikunenedwa kuti adakhala mnyumba mwa Ali (a.s) zaka zokwana zisanu ndi zinayi (9) zokha basi ndipo mapeto ake adaphedwa moponderezedwa ndi anthu omwe amazitcha kuti asilamu.
Pambuyo pomwalira Fatimat Zahra (s.a) Imam Ali (a.s) adakwatirapo kangapo konse ndipo zimayenera kutero kumene.
Kukwatira kwake nthawi zina kumachitika motere, tsiku lina lake adapita kwa mchimwene wake wamkulu yemwe amatchedwa kuti Aqiil.
Aqiil yemwe ali mchimwene wake wa Imam Ali (a.s) adali ndi mbiri yoti amadziwa bwino mitundu ya anthu a mtundu wa ma Arab ndi mbiri zawo.
Koma apa funso loti chifukwa chiyani Ali (a.s) adapita kwa mkulu wake Aqiil kumachita kuti iye ndiyemwe adali ozindikira kwambiri pachina chirichonse pakati pa anthu anthawi yake? Lidzayenera kuyankhidwa munthawi yake osati pano ayi.
Apa ndikungolosola zomwe zidachitika munthawiyo.
Imam Ali (a.s) adamuwuza mchimwene wake Aqiil kuti ndikufuna kuti mundipezere kuchokera mmitundu ya ma Arab mtundu omwe uli wamphamvu komanso osawopa kuti ndikwatire ndi mkazi ochokera ku mtundu umenewo.
Aqiil ndi kuzindikira komwe adali nako adayamba kafukufuku wake kumitundu ya ma Arab ndipo mapeto ake adamuwuza Imam Ali (a.s) zotsatira za kafukufuku wake kuti:
“ Ali okondedwa wanga, ndakusankhira mkazi yemwe kuyambira agogo ake onse akuchimuna omwe adapita mpakana agogo ake onse akuchikazi, adali anthu amphamvu ndi osawopa munthawi yawo kumtundu wa ma Arab”
Mzimayi ameneyu adali ndani?
Adali mzimayi yemwe amatchedwa kuti Fatima ochokera kumtundu wa Kilaab.
Momwe Hisitore ikunenera pa za mtundu wa mzimayi ameneyu ndi zoti:
Fatima adali mwana wa Hizam yemwe adali munthu wamphamvu odziwika munthawi yake, Hizam adali mwana wa Khalid, Khalid adali mwana wa Rabiah, Rabia adali mwana wa Wahid, Wahid adali mwana wa Kaab, Kaab adali mwana wa Amir ndipo Amir adali mwana wa Kilaab mpakana omwe adapita onse adali anthu amphamvu munthawi yawo.
Mapeto ake Imam Ali (a.s) adakwatira ameneyu yemwe adafufuzidwa mtundu wake ndi mchimwene wake.
Zotsatira za ukwati umenewu ndiko kubadwa kwa ana okwana anayi (4) ndipo ana onse adali amuna ndipo wamkulu mwa iwo adali Abbas (a.s).
Tikati tiwone bambo a ana amenewa ndi zodziwika bwino kuti Imam Ali (a.s) adali ndi mphamvu zochuluka bwanji. Komanso amayi awo adali ochokera ku mtundu otani.
Mwachoncho ndi zachidziwikire kuti ana amenewa adzakhala ndi mphamvu zotani ndithudi adzayenera kutengera makolo awo m’machitidwe. Ndiye ana amenewa sadali ana wamba ayi. Adali ana odziwika pamaso pa mtundu wa ma Arab ku Madinah.
Mwachoncho mzimayi ameneyu ngakhale kuti dzina lake lidali Fatima koma chifukwa chokhala ndi ana amphamvu chonchiwa, amayi a mzinda wa Madina adamupatsa mzimayiyu dzina loti Ummul Banin.
Banin pa chilankhula cha chiyarabu ndi kuchulukitsa kwa Ibn ndipo tanthauzo lake ndiye kuti mayi wa ana amuna. Kukhala ngati kuti ana amenewa poyerekeza ndi ana ena adali opambana komanso apamwamba kwambiri pamanso pa aliyense.
Mwana wamkulu yemwe ali Abbas (a.s) adakhala umoyo wake zaka zokwana 34 ndipo pa ana anayiwa ndi Abbas yekha yemwe adapeza mwayi okwatira.
Iye adakwatira ndi mwana wa Abdullah ibn Abbas yemwe amatchedwa kuti Nubabah.
Ngakhale kuti pali kusiyana maganizo kuti kodi Abbas adali ndi ana angati. Koma zomwe ziri zodziwika bwino ndi zoti zotsatira za banja limeneli kudabadwa ana okwana awiri amuna.
Oyamba adali Fadhil ndipo wachiwiri ndi Ubaidullah ibn Abbas ibn Ali ibn Abitwalib (a.s).
Pachifukwa choti mwana oyamba adali otchedwa kuti Fadhil, ndi chikhalidwe kwa ma Arab kuti bambo amadziwika ndi dzina la mwana wamkulu oyamba. Mwachoncho olemekezeka Abbas (a.s) adadziwika ndi dzina loti Abul Fadhil Abbas.
Mapeto ake adaphedwa pa Karbala ali ndi zaka zokwana 34 podzipereka chifukwa choteteza chisilamu, potetezanso zinthu zina monga:
Qur’an yomwe ili njira yachiwongoko, nyali yachiwongoko yemwe ali Imam Husein (a.s) ndi utsogoleri osankhidwa ndi Mulungu.
Manda a iyeyu ali pafupi ndi manda a mchimwene wake Imam Husein (a.s) omwe padakali pano ndi malonso omwe amapitako anthu ambiri kukawona manda ake (Ziyarah) komwe kuli ku Karbala.
Izi zidali chidule cha umoyo wa olemekezeka ameneyu amene adabadwa pa 4 m’mwezi wa Shaban mu chaka cha 28 chisamukire mtumiki (s.a.a.w).
Kodi padakali pano tikufuna kulongosola zotani?
Chifukwa cha ulemelero ndi upamwamba omwe olemekezeka Abbas (a.s) alinawo, ndi zambiri zomwe tingalongosole zokhudzana ndi iye koma kuti padakali pano tikufuna tilongosolerane zinthu ziwiri zokha basi.
Zinthu ziwiri zimenezi ndi zofunika kwambiri chifukwa choti zinanenedwa kuchokera kwa munthu amene ali osachimwa mu umoyo wake onse yemwe ali Imam, mboni ya Mulungu komanso Khalifah wa Mulungu.
Chimodzi mwa zinthu ziwirizi chikupezeka mu bukhu la Biharul Anwar/ volume 44/ pa tsamba 298 ngakhalenso kuti nkhani imeneyi inanenedwanso ndi Sheikh Saduq mu bukhu la Alkhiswal, Hadith ya 101.
Kodi Hadith ikuti chiyani?!
Pambuyo pa zomwe zidachitika pa Karbala, Imam Ali mwana wa Imam Husein (a.s) yemwe amadziwikanso ndi dzina loti Sajjad, tsiku lina lake ali limodzi ndi omutsatira ake adali kuyenda mumzinda wa Madinah. Kenako adakumana ndi mwana wa amalume ake yemwe ali Ubaidullah ibn Abbas akusewera ndi anzake.
Panthawi yomwe adamuwona iye, zidamupangitsa Imam Sajjad kuti akumbukire zomwe zidachitika pa karbala. Imam Sajjad (a.s) adati:
“Tsiku loyipitsitsa kwambiri mu umoyo wa mtumiki lidali tsiku la Uhud, lomwe malume ake omwe amatchedwa kuti Asadullah Hamzah, adaphedwa momvetsa chisoni kwambiri. Pambuyo pa tsiku la Uhud tsikunso lomwe lidali lopweteka komanso loipitsitsa kwa mtumiki lidali tsiku la Mu,Utah (nkhondo ya Mu’utah) lomwe mwana wa amalume ake yemwe amatchedwa kuti Jaafar adaphedwa pomwe adamupha ndi kumudula manja ake awiri kuchokera m’mapewa”.
Imam Sajjad (a.s) atalongosola izi adapitiriza nati:
لا یوم کیوم الحسین
“Inde tsiku la Uhud lidali lovuta ndinso lopweteka, ee tsiku la Mu’utanso lidali lowawa kwambiri kwa mtumiki (s.a.a.w) koma kupweteka kwa masiku awiriwa sikungafanane ndi kupweteka kwa tsiku lomwe bambo anga Husein (a.s) adaphedwa”.
Chifukwa chake ndi ichi:
ازدلف الیه ثلاثون الف رجل یزعمون من هذه الأمة کل یتقرب الی الله عزوجل بدمه
“Ine ndidali pomwepo ndipo ndidawona ndi maso angawa anthu okwana 30,000 amuna omwe amazitcha kuti ndi ochokera mu Ummah wa chisilamu. Onse adawawukira bambo anga ndi cholinga choziwandikitsa kwa Mulungu ndipo adapha bambo anga mowapondereza”.
Imam Sajjad (a.s) pambuyo powonetsa madandaulo ake adakumbukira amalume ake Abbas (a.s) ndipo adati:
رحم الله عمی عباس لقد آثر و أبلی و فدی أخاه بنفسه حتی قطعت یداه فأبدل الله بهما جناحین یطیر بهما مع الملائکة فی الجنة کما جعل لجعفر بن ابی طالب علیهما السلام.
“Mulungu apangire chisoni malume anga Abbas chifukwa chakuti adadzipereka ndipo adadziyika m’mavuto ndi chipsyinjo ndinso adapereka nsembe mwini wakeyo kwa mchimwene wake (Husein), mpakana adadulidwa manja ake awiri kufikira kuti Mulungu adamusinthira manja akewo pomupatsa mapiko awiri omwe azikawulukira nawo pamodzi ndi angelo ku mtendere ngati momwe zidachitikira kwa Jaafar mwana wa Abutwalib (a.s)”.
Mtumiki (s.a.a.w) adanenapo zimenezi pokhudzana ndi Jaafa ibn Abitwalib (a.s) panthawi yomwe adaphedwa ku nkhondo ya Mu’utah podulidwa manja ake kuti:
“Ine ndikumuwona Jaafar kuti Mulungu wamupatsa mapiko awiri ndipo akuwulukira nawo limodzi ndi angelo mu Jannah. Mwachoncho ndikulongosola kwa mtumiki kumeneku Jaafar adadziwika kuti Jaafar Twayyar (Jafaar owuluka)”.
Imam Sajjad (a.s) pokhudzana ndi abbas (a.s) adapitiriza ponena kuti”
و إن للعباس عند الله عزوجل منزلة یغبطه بها جمیع الشهداء یوم القیامة
“Ndipo ndithudi Abbas kwa Mulungu ali ndi ulemelero ndi malo apamwamba omwe anthu onse ophedwa mu njira ya Mulungu adzakhumbira ndi kulakalaka kuti atakhalaa nawo pa tsiku lomaliza”.
Mwina nthawi zina inu ndi ine tingalankhule mopyola muyeso posakhala m’mene zinthu ziliri lomwe lili bodza, koma mawu awa akuchokera pakamwa pa munthu yemwe samanama, osalakwa umoyo wake onse yemwe mulungu adamuchotsera uchimo wina ulionse mu umoyo wake komanso munthu yemwe ali mboni ya Mulungu ndi osankhidwa wake kukhala mtsogoleri wa anthu.
Mwachoncho ndikuwonjezera kuti tikanangokhala ndi zokhazi pokhudzana ndi ubwino wa Abbas (a.s) zikukwanira pa ubwino omwe iye alinawo.
Chinthu chachiwiri chomwe ndikufuna kulongosola padakali pano ndi zoti:
Kuphedwa kwa Imam Husein (a.s) kudachitika pa 10 mwezi wa Muharram, tsiku lomwe limatchedwa kuti Ashura. Koma m’mene zikuwonekera mu Hisitore, zimenezi zimayenera kuchitika madzulo a tsiku la 9, lomwe limatchedwa kuti Tasuua.
Ndi kulongosola uku:
Panthawi yomwe Ibn Ziyad adawuzidwa kuti Umar Saad akuchedwa kumupha Imam Husein (a.s), podziwa kuti Imam Husein (a.s) adafika ku Karbala pa 2 Muharram pomwe Umar Saad ndi gulu lake la nkhondo adafika pa 3 mwezi omwewu.
Kuchoka pa 2 kukafika pa 9 kapena pa 10 ndi nthawi yaitali kwambiri amayenera kupanga mofulumira pomupha Imam Husein (a.s). koma chifukwa chakuti Umar Saad kwina amafuna ulamuliro opondereza kwinanso amafuna Mulungu posamupha Imam Husein (a.s), mwachoncho m’mausiku ambiri adali akukambirana ndi Imam Husein (a.s).
Mwachoncho panthawi yomwe Ibn Ziyad adamva zimenezi, adamutumiza Shimr mu tsiku la 9 ndipo adamuwuza kuti ngati Amur Saad angaganize zomupha Husein, uyenera kumuthandiza koma ngati akuchedwa kutero ndipo akuwonetsa kufowoka, iweyo udzakhale mtsogoleri wa gulu la nkhondo ndipo ukawutenga udindowo, udzayambe kuthana ndi Amur ibn Saad kenako udzamuphe Husein.
Shimr atafika ku Karbala madzulo a tsiku la 9, adamuwuza Amur ibn Saad za ntchito yomwe wabwelera ndi udindo wake. Umar Ibn Saad atamva izi, adayankha kuti ndipitiliza udindo umenewu.
Munthawi imeneyi Imam Husein (a.s) potengera ndi momwe Hisitore ikunenera, adakhala pansi pafupi ndi tenti lake atayika manja ake pa mabondo ndipo mutu wake adayika pamwamba pa manja ake ali m’maganizo.
Sitikudziwa kuti ankawona chiyani m’maganizo ake.
Fumbi lidali litafalikira penapaliponse ku Karbala.
Olemekezeka Zainab (s.a) atawona momwe adakhalira mchimwene wake, adapita pafupi ndi iye ndipo adamukodola paphewa ndi kumuwuza kuti tawona kutsogolo kwako.
Imam Husein (a.s) atadzutsa mutu wake, adawona kuti gulu la asilikali a Umar ibn Saad lakhonzeka kufuna kumupha iye ndipo fumbilo lidachuluka chifukwa cha unyinji wa Asilikali a Umar ibn Saad.
Apa ndipomwe Imam Husein (a.s) adamuitana mchimwene wake Abbas (a.s) ndipo adamuwuza mawu ena ake zikadakhala kuti tili ndi mawu okhawo pokhudzana ndi Abbas (a.s), zikukwanira pofuna kuwonetsa ulemelero omwe iye alinawo.
Mawu amenewo adali otani?
Adamuwuza kuti:
ارکب بنفسی أنت یا أخی حتی تسألهم عما جائهم
“Podzipeleka kwa ine, kwera iwe mchimwene wanga mpaka ukawafunse iwo cholinga chomwe abwelera”.
Apa sitikufuna kuti tilongosole zonse zomwe zidachitika nthawi imeneyo monga kuti kodi mdani adatsekereza bwanji kuti Abbas akumane ndi iwo kufikira kuti kulimbana kumeneku kudafika tsiku lotsatira lake lomwe liri Ashura.
Apa tiwonenso kuti ndi Imam yekha yemwe ali osalakwa amene angalankhule mawu omwe ali m’mwambawa, kumulankhulira mwana wamkulu wa olemekezeka Ummul banin.
Kutanthauza kuti kodi olemekezeka Abbas (a.s) adali munthu ofunikira bwanji kwa Imam Husein (a.s) kuti pakati pa anthu onse omwe adali ndi Imam, iye yekha ndi amene adasankhadwa.
Mwachoncho ngati ife nthawi zina timamva zonenedwa ngati zimenezi kuchokera kwa akulu akulu mu Hisitore, tisamadabwe kwambiri ayi.
یوم ابوالفضل استجار به الهدی والشمس من کدر العجاج لثامها
Nthawi ya Ashura ndi nthawi imene Husein (a.s) amene ndi nyali ya chiwongoko akuti: “Ndinaphelera kwa Abbas, pomwe nkhodo ya Ashura imatha pokomera mdani, ndipo dothi ndi fumbi lidali litafalikira dera la Karbala ndipo kuwala kwa dzuwa kudabisika ndi fumbi, nthawi imeneyi ndi nthawi imene ine Husein ndidathawira kwa Abbas (a.s).
Izinso ndi zomwe zikuyikira umboni kuti kodi olemekezeka Abbas (a.s) ali ndi ulemelero ndi upamwamba otani.
Koma kuti pali zambiri zomwe tingakambe zokhudzana ndi olemekezekayu zomwe zikuyenera kulongosoledwa munthawi ina.
Kodi Abbas adali ndani?
Add new comment