Syria: اذا جاء نصر الله و الفتح... (chikadzafika chipulumutso cha Mulungu ndi kupambana…)
Asilikali a dziko la Syria pambuyo pa masiku angapo polimbana ndi gulu lowukira dzikoli, apambana pokwanitsa kuthetsa anthu opandukira motheratu mudera la Alqusair.
Wailesi ya kanema ya nkhani ya Almayadiin yalengezanso kuti asilikali a dziko la Syria ndi omwe ali ndi mphamvu zonse poyang’anira mzinda wa Alqusair.
Kumbuyoku kwalengezedwanso za kuthawa kwa anthu opandukira kuchokera mudera la Alqusair ndi kutsogola kwa asilikali a dzikoli.
Dera la kumadzulo kwa Alqusair ndiwo malo omwe adali omaliza omwe amasonkhana anthu ambandawa omwe adalandidwa ndi asilikali a dziko la Syria atawapanikiza kotheratu.
Dera la Alqusair lomwe liri kumadzulo kwa dziko la Syria ndinso mzinda wa Himsi, masabata awiri apitawa, kudali kulimbana kwakukulu pakati pa asilikali a Syria ndi ambandawa
Miyezi 6 yapitayi, gulu lokanira la Wahabiy lidapha anthu owandikira 1000 omwe amakhala m’midzi ya Shia mudera la Alqusair ndipo anthu ambiri adawakakamiza za kusiya midzi yawo ndi kuthawo.
Miyezi yapitayi, mtsogoleri wa gulu la Hizbullah mu dziko la Lebanon Hasan Nasrallah, kangapo konse adawopyseza pa zakupha anthu a Shia omwe ali mudera la Alqusair koma anthu okanira amenewa ndipomwe adawonjezera kupanikiza popha anthu omwe akukhala m’midzi ya derali.
Mbali inanso tikuwona kuti pakuzeka gulu la ukapirikoni la ulamuliro wankhanza wa Zayonisti mudera la Alqusair, zomwe zikupangitsa kuti gulu la Hizbullah lisathe kupanga chirichonse pofuna kuthandiza anthu omwe akukhala m’midzi ya Alqusair.
Gulu la ulamulilo wa nkhanza wa Zayonisti lomwe likupezeka muderali, wadula kulumikizana konse kwa mawailesi pakati pa asilikali a Syiria ndi gulu la Hizbullah.
Add new comment