Kulongosola zokhudzana ndi Ayah (versi) ya Mawaddat (chikondi kwa akunyumba ya mtumiki)
[قُلْ لا أَسْئَلُكُمْ عَلَیْهِ أَجْراً إِلاَّ الْمَوَدَّةَ فِی الْقُرْبى ]؛ شورى (42)، آیه 23
Nena iwe mtumiki kuti; olo ndi pang’ono pomwe palibe malipiro omwe ndikufuna kuchokera kwa inu pa utumiki wangawu, kupatula chikondi kwa abale anga (kuwakonda Ahalbait anga).
Mu chaputala (Surah) cha Shuara, Mulungu akuwawuza atumiki ena monga olemekezeka Nuh (Nowa), Lot ndi Hud ponena kuti; awuzeni anthu kuti sitikufuna malipiro a utumiki wathu.
[إِنْ أَجْرِیَ إِلاَّ عَلى رَبِّ الْعالَمِینَ]
Ndipo atumiki onse adalamulidwa kuti afotokozere mtundu wawo kuti ife sitikufuna malipiro pa utumiki wathu koma mu chaputala cha Shura, mtumiki wathu olemekezeka Muhammad (s,a,a,w) adalamulidwa ndi Mulungu kuti afune malipiro pa utumiki wake ndipo omwe amanena kuti mtumiki (s.a.a.w) sadafune malipiro pa utumiki wake amalakwitsa. Ayah ya Qur’an ikuchita kunena mowonekera poyera kuti:
[قُلْ لا أَسْئَلُكُمْ عَلَیْهِ أَجْراً إِلاَّ الْمَوَدَّةَ فِی الْقُرْبى ]
Kutanthauza kuti malipiro a mtumiki omaliza kuchokera kwa anthu ndi kuwakonda akunyumba yake (Ahalbait) ndipo tanthauzo la mawu oti Mahabbat ndiye kuti chikondi chenichenii.
Mwachoncho ndi koyenera kunena kuti:
1. Mtumiki wa Mulungu (s.a.a.w) adafuna malipiro.
2. Mtumiki wa Mulungu adafuna malipiro kuchokera kwa anthu molamulidwa ndi Mulungu.
3. Malipiro a mtumiki siadali adziko lapansi ayi, koma kuti chikondi kwa abale ake (Ahalbait).
Kulozera kwa Chaputalachi pa zakufuna malipiro ndi zochita kuwonekera poyera kwambiri, chifukwa chakuti pankhani yosafuna malipiro achotsapo ndipo ngati pazinthu zokanidwa ngati zina zachotsedwa, zotsatira zake ndi zoti zochotsedwazo ndiye kuti zavomerezedwa.
Mwachitsanzo pomwe inu mukuti: lero kunyumba yathu sadabwere munthu olo ndi m’modzi yemwe kupatula bambo anga, zotsatira zake ndi zoti munthu yemwe adabwera kunyumba yanu ndi bambo anu. Ndiye ngati Ayah ikunena kuti: nena kuti sindikufuna malipiro kupatulako chikondi kwa akunyumba yanga, zikutanthauza kuti chikondi cha anthu kwa akunyumba ya mtumiki ndiwo malipiro a utumiki.
Pofuna kudziwa zambiri, ikirani chidwi pa zomwe zikulongosoledwa pansizi:
Ahalsunna ali ndi ma Sheikh awiri akuluakulu omwe ndi:
1. Zamakhshariy; iye ndi mtsogoleri wa Tafsir (kumasulira Qur’an) kwa anthu odziwa za Tafsir a Ahalsunna ndipo adamwalira muchaka cha 528 chisamukire mtumiki (hj). Iye ndi mlembi wa bukhu la Tafsir lodziwika ndi dzina loti Alkashaf lomwe liri mayi wa mabukhu a Tafsir a Ahalsunna walJamaa ndipo ndi zosatheka kwa Ahalsunna kumupeza munthu yemwe samavomereza za Zamakhshariy ndi bukhu lake Alkashaf.
2. Fakhr Raziy; iye ndi mlembi wa bukhu la Tafsir la Alkabir lomwe liri bukhu la mphamvu kwambiri pa mabukhu onse a Tafsir a Ahalsunna. Zowonadi Fakhr Raziy adali katakwe, mwina ankakwanitsa tanthauzo la chiganizo (sentence) chimodzi ndikulisintha kukhala kakhalidwe kokwana 7 kapena 8 komanso kakhalidwe kosiyana siyana. Iye pankhani yokhudzana ndi kulongosola mawu ndi matanthauzo a ziganizo adalibe ofanana naye kwa Ahalsunna ndipo padalibe munthu oganiza komanso ozama kwambiri kuposa iye.
Tsopano funso ndi loti kodi akunyumba kwa mtumiki (s.a.a.w) ndi ndani?
Zamakhshariy mu bukhu lake la Alkashaf an Haqaiq Ghawaamidh al-Tanziil, pomasulira Ayah ya 23, Surah Shura akunena kuti, mawu oti Qur,baa mu ayayi akutanthauza kuti abale ake a mtumiki (s,a,a,w). Fakhr Raziy pambuyo polongosola mawu a Zamakhshariy adalemba mu bukhu la Altafsiiru al-Kabiir wa Mafaatiihu Alghaib pansi pa Ayah 23, Surah Shura kuti:
[و اَنَا اقول آلُ محمدصلى الله علیه وآله هُم الذین یَوول امرهم الیه فكل مَن كان امرهم الیه اشدّ و اكمل كانوا هم الآل و لا شك انّ فاطمةَ و علیاً و الحسن والحسین كان التعلّق بینهم و بین رسول اللَّه صلى الله علیه وآله اشدَّ التعلّقات و هذا كالمعلوم بالنقل المتواتر فوجب اَن یكونوا هم الآل... اَمّا غیرهم فهل یدخلون تحت لفظ الآل فمختلفٌ فى]
Ndipo ine ndi kuti: “abale a Muhammad, ndi anthu omwe ali owandikirana ndi mtumiki ndipo yense amene akuwandikirana kwambiri ndi mtumiki komanso kuwandikirana kwake ndi mtumiki ndikukhala kokwana ndiye kuti adzakhala wakunyumba ya Mtumiki. Ndipo palibe chokayikitsa kuti kulumikizana kwa Fatima, Ali,Hasan ndi Husein ndi mtumiki ndi kwakukulu kwambiri koposa wina aliyense. Monganso momwe Hadith yokhudzana ndi nkhani imeneyi idanenedwera mochuluka ndi ma Swahabah. Chiwelengero cha anthu omwe adatenga Hadithiyi chikupitilira 1000, ndiye kuti ndi zoyenera kuti anthu anayiwa akhale akunyumba ya mtumiki. Koma nkhani ndi yoti kodi kupatula anthu anayiwa, anthu enanso ndi akunyumba ya mtumiki? Pali kusemphana maganizo pankhani imeneyi.
Adanena nkhani mwini wa bukhu la Alkashaf (Zamakhshariy) kuti ndithudi panthawi yomwe idatsika Ayayi, anthu adafunsa kuti: “Ee! Mtumiki wa Mulungu, ndi abale ako ati omwe kwakakamizidwa kwa ife kuwakonda”? Mtumiki adati: Ali, Fatimah ndi ana awo awiri (Hasan ndi Husein). Apa zadziwika kuti anthu anayiwa ndiwo abale ndi akunyumba a mtumiki (s.a.a.w) omwe anenedwa mu Ayah ndipo ngati zadziwika choncho ndi zokakamizidwa (Wajib) kuwasiyanitsa ndi anthu ena powakonda ndi kuwalemekeza ndipo pali ma Hadith ena omwe akulozera ndi kutsimikizira pa kukakamizidwa kulemekeza ndi kukonda anthu amenewa. Imodzi mwa ma Hadith omwe akulozera pazimenezi ndi iyi; mtumiki (s.a.a.w) adali kumukonda kwambiri Fatimah (s.a) ndipo ankati: Fatimah ndi theka la thupi langa; ndipo yemwe angamuvutitse iye ndiye kuti wandivutitsa ine. Chifukwa choti nkhaniyi idatengedwa ndi akuluakulu ambiri. Zatsimikizika kuti mtumiki (s.a.a.w) ankamukonda Ali, Hasan ndi Husein (a.s) ndipo pomwe zadziwika chonchi ndi zokakamizidwa kwa anthu onse (Ummah) kuti apange chimodzimodzi ngati mtumiki powakonda iwowa. Qur’an ikunena kuti: ndithudi mtumiki wa Mulungu ndi chitsanzo kwa inu. Izi zikuchokera mu bukhu la Alkashaf an Haqaiq Ghawaamidh al-Tanziil, pansi pa Ayah 23, Surah Shura.
[و رَوى صاحب الكشاف انّه لَمّا نزلت هذه الآیة قیل یا رسول اللَّه مَن قرابتك هؤلاء الّذین وجبت علینا مودّتهم؟ فقال على و فاطمه و ابناهما، فثبت انّ هؤلاء الأربعة اقارب النبىّ صلى الله علیه وآله و اذا ثبت هذا وَجَب ان یكونوا مخصوصین بمزید التعظیم و یدل علیه وجوه:... الثانى: لا شك انّ النبىّ صلى الله علیه وآله كان یُحبّ فاطمةعلیها السلام قال صلى الله علیه وآله فاطمة بضعة منّى یؤذینى ما یؤذیها و ثبت بالنقل المتواتر اَنّ رسول اللَّه صلى الله علیه وآله انّه كان یحبُّ علیا والحسن والحسین و اذا ثبت ذلك وجب على كل الأمّة مثله... لقد كان لكم فى رسول اللَّه اسوة حسن]
Nayenso Fakhr Raziy adalembanso kuti:
Adatenga nkhani mwini bukhu la Alkashaf kuchokera kwa mtumiki (s.a.a.w) kuti:
مَن مات على حبّ آل محمد ماتَ شهیدا
1- Munthu yemwe angamwalire akuwakonda Ahalbait ndiye kuti wamwalira ngati (Shahiid) munthu ofera kunkhondo munjira ya Mulungu.
مَن مات على حبّ آل محمد مات مغفوراً له
2- Yemwe angamwalire akuwakonda Ahalbait a Mtumiki ndiye kuti wamwalira ali okhululukidwa ndi Mulungu.
مَن مات على حبّ آل محمد مات تائباً
3- Munthu yemwe angamwalire akuwakonda akunyumba ya mtumiki ndiye kuti wamwalira ali olandiridwa kulapa kwake.
مَن مات على حبّ آل محمد مات مؤمناً مستكمل الایمان
4- Munthu yemwe angamwalire ali ndi chikondi ndi akunyumba a mtumiki ndiye kuti wamwalira ali okhulupilira weniweni komanso chikhulupiliro chake chiri chokwana.
مَن مات على حبّ آل محمد بشّره ملك الموت بالجنّة
5- Yemwe angamwalire akuwakonda Ahalbait a mtumiki, mngelo wa imfa adzamusangalatsa ndi Jannah.
مَن مات على حبّ آل محمد فتح له فى قبره بابان الى الجنّةr
6- Yemwe angamwalire akuwakonda akunyumba ya mtumiki, adzamutsekukira m’manda mwake makomo awiri aku Jannah.
مَن مات على حبّ آل محمد جعل اللَّه قبره مزار ملائكة الرحم]
7- Yemwe angamwalire akuwakonda akunyumba ya mtumiki, Mulungu adzamupangila manda ake kukhala malo opanga ziyarah (kumuyendela) angelo a mtendere. Ndiye ngati manda a bwenzi wa Ahalbait a mtumiki (s.a.a.w) angakhale malo opangapo ziyarah angero a mtendere, ndiye manda a iwo (Ahalbait) angakhale otani? Tidziwenso kuti pali Hadith ina yomwe ikunena kuti Munthu yemwe angamuyendere Husein (a.s) ku manda ake, ziri ngati munthu yemwe wamuyendera Mulungu ku mpando wake wachifumu (Arsh).
Kenako Zamakhshariy adatenganso ma Hadith okhudzana ndi kukana kuwakonda akunyumba ya mtumiki. kutanthauza adatenganso ma Hadith okhudzana ndi kudana ndi akunyumba ya mtumiki (s.a.a.w) kuti:
من مات على بغض آل محمد جاء یوم القیامة مكتوباً بین عینیه آیس مِن رحمةاللَّه.
1- Munthu yemwe angamwalire ali ndi udani ndi akunyumba ya mtumiki, adzabwera pa tsiku lomaliza atalembedwa pakati pa maso ake kuti otalikirana ndi mtendere wa Mulungu.
Kutanthauza kuti mdani wa Ahalbait m’mayiko awiri (dziko la pansi ndi Akhirah). Adzakhala otulutsidwa muchisomo cha Mulungu chifukwa choti ngati imodzi mwazintchito zake idzalandiridwa ndiye kuti mtendere wa Mulungu udzamukhudza ngati momwe Ayah ikunenera kuti:
[ورحمتى وسعت كلّ شى ء]
Ndipo mtendere wanga ndi otambasuka pa china chirichonse
Kumachita kuti iye adzakhala otaya mtima pa chisomo cha Mulungu.
من مات على بغض آل محمد مات كافراً.
2- Munthu yemwe angamwalire akudana ndi akunyumba ya mtumiki, ndiye kuti wamwalira ali munthu okanira (Kaafir).
من مات على بغض آل محمد لم یشمّ رائحة الجنّة.
3- Munthu yemwe angamwalire akudana ndi akunyumba ya mtumiki, sadzamva fungo la kumtendere.
Izi ndi zomwe adatenga mwini wa bukhu la Alkashaf (Zamakhshariy)
Umboni wina ndi oti Fakhr Raziy akutenganso Hadith ina kunena kuti:
انّ الدّعاء للآل منصب عظیم و لذلك جُعل هذا الدعاء خاتمة التشهد فى الصلاة و هو قوله اللّهم صلّ على محمد و على آل محمّد و هذا التعظیم لم یوجد فى حق غیر الآل فكل ذلك یدل على انّ حب آل محمد واجب
Ndithudi kuwapangira Duwa Ahalbait a mtumiki (s.a.a.w) ndi chinthu chachikulu kwambiri mwachoncho ndi chifukwa chake zidayikidwa kumapeto kwa Tashahud pa Swalah kuti wina aliyense azinena mawu oti:
اللّهم صلّ على محمد و على آل محمّد
Magulu onse a Ahalsunnah ali chimodzimodzi ngati gulu la Shia, amamufunira zabwino mtumiki ndi akunyumba yake mu Tashahud pa Swala ndipo onse amazitenga zimenezi kuti ndi zokakamizidwa (Wajib). Kupeleka ulemu waukulu kumeneku, sikudamuchitikirepo wina aliyense kupatulako akunyumba a mtumiki (s.a.a.w). ndiye zonsezi zikuyikira umboni kuti kuwakonda akunyumba ya mtumiki ndi chikakamizo kwa aliyense.
Kudutsiranso m’maumboni ena ochekora kwa mtumiki olemekezeka (s.a.a.w) ndi chifukwa chake onse anzathu a Ahalsunnah popanda kuchotsera (mpakananso Wahabiy), amadzichemelera kuti ife timawakonda akunyumba ya mtumiki (s.a.a.w). Mogwirizana ndi kumva kwa nzeru, chikondi chitha kukanidwa komanso chitha kuvomerezedwa. Kutanthauza kuti ngati mumamukonda munthu wina wake, ndi koyenera kuti mudzadanenso ndi mdani wake.
Tsopano funso ndi loti, kodi kumukonda Ali mwana abi Twaalib (a.s) kukugwirizana bwanji ndi Muawiyah? yemwe adawalamula anthu kuti alembe dzina la Ali (a.s) kunsi kwa nsapato zawo kuti lizipondedwa ndi mapazi awo komanso adawalamula olalikira kuti azimunyoza Ali (a.s) kumayambiliro kwa ulaliki wawo ndipo ngati osatero adzalandira chilango. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti chiyani?
Kufikira nthawi ya ulamuliro wa Umar mwana wa Abdul azizi, kumunyoza Ali (a.s) pa Khutbah ndi pa ulaliki kumapitilirabe ndipo iwo ankamutembelera Ali (a.s). Kodi zikugwirizana bwanji kumukonda Ali (a.s) komwe kwalembedwa mu mabukhu aja ndi kumutembelera komanso ndi kuponda dzina la Ali (a.s) komanso kumenya nkhondo ndi Ali pa nkhondo ya Sifiin?
Mwachoncho ndi koyenera kuti mtsutso omwe ukuwonekawu uyankhidwe. Kapena anene kuti Ali ndiye wachilungamo kapena Muawiyah. Kodi ndi zotheka kumukonda wakupha ndi ophedwa? Ndi zotheka bwanji kuti uziwakonda bamboo ako omwe aponderezedwa pophedwa komanso kumukonda munthu yemwe wapha bambo ako? Zowona zake za chikondi ndi izi ponena kuti;
[سلم لمن سالمكم و حرب لمن حاربكم؛ موالى لمن والیتم معادٍ لمن عادیتم؛ محب لمن احبكم مغبض لمن ابغضك]
Ndidzakhala pa mtendere ndi munthu yemwe wakupatsani mtendere ndipo ndidzamenya nkhondo ndi munthu yemwe adzamenya nkhondo ndi inu, ndidzamutsatira munthu yemwe wakutsatirani ndipo ndidzadana ndi munthu yemwe wadana ndi inu, ndidzamukonda munthu yemwe adzakukondani inu komanso ndidzakhala okwiya ndi munthu yemwe adzawonetsa mkwiyo kwa inu.
Zotsatira zake ndi zoti, kapena kumusiya Muawiyah kapena Ali (a.s). Koma mogwirizana ndi ma Hadith ochuluka okhudzana ndi Ali (a.s) ndizosatheka kumusiya Ali ibn abi Twalib.
Funso apanso ndi loti ngati inu muli owakonda anthu anayiwa (Ali, Fatimah, Hasan, Husein) ndiye kuti Muawiyah mukumutenga ngati ndani? kodi tizimukondanso? Akuti Muawiyah ndi amalume a okhululupiliraمعاویه خال المؤمنین Chifukwa choti mchemwali wake adali mkazi wa mtumiki. Kodi zimenezi ndi zomveka? Nanga kodi chimenechi chakwanira kukhala chifukwa?
Chigamulo chiri ndi inu abale anga okondedwa.
Mulungu akusungeni ndikuti atiwongole tonsefe Ishaallah.
Add new comment