Kupha mtundu wa asilamu mu mzinda wa Bermeh+zithunzi zopweteka mumtima
Kufalitsa zithunzi zopweteka mtima za kuwotcha asilamu adziko la Bermeh kumachita kuti mayiko achisilamu ena chidwi chawo chonse angoika pa nkhani yokhudzana ndi zomwe zikuchitika ku dziko la Siriya ndipo akumakamba zakuphedwa kwa anthu adzikoli. Nthawi zonse ma wailesi ndi ma Television awo akuwagwiritsa ntchito polongosola zochitika ku dzikoli. Zoterezi zikudzutsa mafunso ambiri ndipo yankho lake kuchokera pachiyambi ndi lodziwika.
Masiku angapo apita, kwamvekanso nkhani yokhudzana ndi kuphedwa kwa asilamu dera la Bermeh. Dziko lomwe likulamulidwa ndi asilikali ndipo chirichonse chokhudza ulamuliro wadzikoli chili m’manja mwa asilikali. anthu ambiri mudzikoli ndi ma Hindu (abatiya) ndi ma Budha ndipo iwo apatsidwa chilolezo kuti chinthu chomwe ali ndi ufulu kuchipanga m’mene angathere ndiko kupha asilamu onse adzikoli.
Kupha komwe kwachitika posachedwapa ndi ma Hindu komanso ma Budha oyipitsitsa m’midzi ndi m’mizinda ya kumpoto ndinso kumadzulo kwa dzikoli, kumachita kuti asilikali ndi apolisi adzikoli ali m’mbali m’mbali akuyang’ana, anthu atsankho lachimbedzo (ma Hindu ndi ma Budha) oyipitsitsa adaphwasula midzi ya asilamu ndipo kuwonjezera kuwotcha manyumba awo, adawotcha asilamu ambiri ali ndi moyo, adapanga zachisembwere ndi atsikana ndi azimayi achisilamu ndipo ena adawathamangitsa kuchokera m’madera awo.
Asilikali olamula dziko la Mynmar m’malo moyankha pamchitidwe wachinyama wa ma Hindu ndi ma Budha oyipitsitsawa, adawatenga asilamu adzikoli kuti ndi anthu omwe adasamukira ku dzikoli popanda chilolezo ndipo ayenera kusankha chinthu chimodzi pa zinthu ziwirizi; kapena atuluke mudzikoli apo ayi adzipereke ku matenti a anthu ogwidwa.
Chiwelengero cha asilamu omwe akhudzidwa ndi mchitidwe wa anthu oyipitsitsawa omwe akuthandizidwa ndi dzikoli chikupitilira 800,000 ndipo sizikudziwika kuti mabungwe oyang’anira za ufulu wa anthu pankhani imeneyi apangapo chiyani komanso sakudziwika komwe ali.
Musadawone zithunzizi, tikupepesa kwambiri chifukwa chaululu omwe ukukubweletserani pakuyang’ana zithunzizi.
Kuchokera ku ABNA, SHIA ONLINE ndi SHIA NEWS
Add new comment