Ana okwana 200 ali mundende ya boma lankhanza la Aalkhalifah

 

Ntchito zomwe ofesi ya ukazembe yadziko la Bahrain ikupanga monga kulengeza kuti anthu asiye kupanga ziwonetsero ndi kusonkhani m’misewu ikuluikulu, zikupangitsa kuti kubweza moto kwa anthu kupite patsogolo polimbana ndi ulamuliro opondereza ndi wankhanza wa Aalkhalifa.
Mlembi wa nyuzi pepala wadziko la Bahrain wafotokoza nkhani yakupezeka kwa ana ang’ono ang’ono okwana 200 mundende ya boma loponderezali.
“Abbas Busufwan” pakukambirana komwe kudali pakati pa iye ndi Television ya nkhani ya Al’alam, iye kuwamanga anaku akukutenga kuti ndi gawo lina la ndale la ulamuliro wankhanzawu pofuna kulimbana ndi anthu otsutsana ndi boma lankhanzali. Iye adati: “kufikira padakali pano pali ana ambiri omwe akuvutitsidwa ndi kulangidwa ndi bomali”.
Iye wanena mosabisa kuti: “Ntchito zomwe ofesi ya ukazembe yadziko la Bahrain ikupanga monga kulengeza kuti anthu asiye kupanga ziwonetsero ndi kusonkhana m’misewu ikuluikulu, zikupangitsa kuti kubweza moto kwa anthu kupite patsogolo polimbana ndi ulamuliro opondereza ndi wankhanza wa Aalkhalifa”.
Adawonjezeranso ponena kuti: “kupitilira kwa nkhanzaku, kukupangitsa anthu adzikoli kuti kutsutsana ndi kudana kwawo ndi bomali kuzipitilirabe ndipo chitsanzo chake chidali kuwononga 4ways yaikulu ya Al-Dawar komwe bomali lidapanga zomwe zidapangitsa kuti anthu adzuke polimbana ndi kutsutsana ndi mchitidwe oterewu”.
Busufwan adapitiriza nati: “zimene bomali likupanga olo ndi pang’ono pomwe sizidzapangitsa kuti anthu asiye kupanga ziwonetsero ayi koma m’malo mwake zidzawonjezera kuti  anthu azisonkhanabe m’misewu mwa unyinji wawo”.
Kuchokera ku Shia online

Add new comment