Kodi Wahabi ndi ndani?

Kodi Wahabi ndi ndani?

Mudzina la Mulungu wachifundo wachisoni chosatha

Salam alaikum, nthawi zonse tiri okufunirani zabwino inu abale okondedwa.
Tisanayambe kulankhula zokhudzana ndi chisilamu, kumayambiliro m’magawo angapo tidzakambirana zokhudza gulu la WAHABIYYAT.
Chifukwa chonena kuti padakali pano gawo lalikulu lofalitsa ndi kulalikira za chisilamu liri m’manja mwa gulu la WAHABIYYAT ndipo anthu omwe sakudziwa zambiri zokhudza chisilamu angaganize kuti chisilamu ndiye chimenechi chomwe akumachiwona chikulalikidwachi.
Kumachita kuti gulu la WAHABIYYAT, lidatenga pamwamba pa chisilamu ndi kuvala chovala cha chisilamu ndipo m’mawonekedwe ndikumakhala  ngati chisilamu koma limagwiritsa ntchito mawonekedwe amenewo polimbana ndi chisilamu.
Pali mizu iwiri ya chipembedzo cha chisilamu yomwe asilamu onse amayivomereza kupatulako gulu la WAHABIYYAT, ndipo gulu limeneli limawatcha asilamu onse kuti ndi ma KAFIR chifukwa chovomereza mizu imeneyi ndipo iwo ntchito yawo yaikulu ndiko kuyesetsa kuti malamulo awiri ali m’musiwa awakhazikitse ndi cholinga chofuna kufafaniza mizu iwiri ija.
Ndipo munthu amene sadzavomereza malamulo awiriwa adzamupatsa chigamulo choti aphedwe:
Lamulo loyamba ndi loti; manda ena aliwonse a atumiki ndi anthu ogwira ntchito zabwino pamaso pa mulungu agumulidwe ndi kufafanizidwa ndipo iwo akadakwanitsa akadathanso kufafaniza manda a mtumiki wathu Muhammad (s.a.a.w).
Zowona zake ndi zoti iwo amanena kuti manda a mtumiki wa chisilamu adapangitsa kuti anthu m’malo molunjika ndi kuyikira chidwi kwa Mulungu akumalunjika ku manda a mtumiki.
Kumachita kuti kulunjika kwa mtumiki ndiko kulunjika kwa Mulungu kumene, kupempha kudutsira kwa mtumiki ndiko kupempha kwa Mulungu kumene chifukwa choti Mulungu ndiyemwe adapeleka ulemelero ndi mphamvu imeneyi kwa iye komanso adamupatsa kuzindikira. Ma Hadith ndi ma Aya akutsimikizira pankhani imeneyi.
Koma ma WAHABIY kuchokera pansi pa mtima ali ndi udani ndi mtumiki.
Kodi cholinga chawo podana ndi mtumiki wa chisilamu ndi chiyani?
Kuti dzina la mtumiki wa chisilamu lisapezeke padziko.
Afafanize zizindikiro za mtumiki wa chisilamu.
Kuti afafanize, awononge ndi kuphwanya manda a mtumiki.
Kuti atsitse pansi ulemelero ndi upamwamba wa uzimu wa mtumiki wa chisilamu.
Kuti amubweletsere vuto mtumiki wa chisilamu ndi kumuyipitsa.
Ma WAHABIY ndi omwe akumapanga zonsezi.
Ma WAHABIY ndi omwe ali adani enieni a chisilamu omwe abisala kuseli kwa chisilamu.
Tangowonani abale anga momwe adamunyozera mtumiki. Papezeke munthu aziti tiphwanye manda a mtumiki wa Mulungu ndiye kuti tipeza malipiro ambiri kwa Mulungu (THAWAB), kumachita kuti akumasunga zizindikiro za aYuda mudzina loti akusunga zizindikiro za mbiri yakale.
Kumachita kuti mukuyang’ana kwa Qur’an, aYuda ndi mdani wamkulu wa chisilamu.
Imeneyi ndiyo ntchito yaikulu yomwe ma Wahabiy akumawagwilira aYuda.
Enanso mwa anthu olemba ndi kufufuza za mbiri yakale (Hisitore) ndi ma umboni omwe alinawo amakhulupilira kuti gulu la Wahabiy lidapangidwa ndi ayuda ndi cholinga chokhazikitsa zolinga za aYuda mu dziko la chisilamu.
Wahabiy ndi munthu amene amakamba zokhudzana ndi Yazid amati “ Yazid ndi Amirul Muuminin (mtsogoleri wa anthu okhulupilira).
Wahabiy ndi munthu amene amalemba bukhu lokhudzana ndi Yazid ndi kumalongosola ubwino wa Yazid.
Yazid amene adawononga nyumba ya Mulungu Kaaba, ndikuwaloleza asilikali ake zakuphwasula ndi kuwononga mzinda wa mtumiki wa Mulungu Madinah ndi kuti apange zoyipa ndim’mene angathere. Ndipo chitsanzo chimodzi chochepa pantchito yoipa imeneyi ndi iyi; komwe kudali kupangitsa kuti atsikana okwana 1000 omwe adali osakwatira ndikupatsidwa pakati mapeto ake kubadwitsa ana opanda bambo (kudutsira mu kugonana nawo). Iye adamupha Imam Husein (a.s) (yemwe ali chidzukulu cha mtumiki). Ndi munthu amene ankawagulitsa atsikana ndi akazi a asilamu kumsika. Ndi munthu yemwe nthawi zonse adali chidakwa ndi kuledzera ndi mowa ndipo ankakwatira ndi abale ake. Iye adali kupanga  chinachirichonse choipa ndipo panthawi yomwe adamupha mwana wa Fatima (a.s) (mwana wamkazi wa mtumiki) Husein adati “Ndawabwezelera agogo anga omwe adaphedwa m’manja mwa Muhammad”.
Mukulankhula kwina kutanthauza kuti, iye adawononga Kaaba chifukwa cholimbana ndi Mulungu.
Chifukwa cholimbana ndi mtumiki wa Mulungu adawononga Madinah pa chochitika chomwe chidachitika pamalo otchedwa Harrah.
Ndi cholinga cholimbana ndi Ahal Bait (a.s), adamupha Imam Husein (a.s) yemwe adachemeleredwa mu ma Aya ambiri a Qur’an ndipo adabaya ndi mabango mitu ya anthu omwe adaphedwa limodzi ndi Husein (a.s) ndikumayizungulilitsa m’matawuni ndi m’mizinda.
Iye ankamwa mowa ndi cholinga cholimbana ndi malamulo achisilamu ndipo adali akupanga chinachirichonse choyipa momwe angathere.
Tsopano tawonani, zomwezi ndi zomwe akumapanga ma Wahabiy.
Lelonso ngati momwe lidaliri dzulo, Makkah ndi Madinah ali m’manja mwa Yazid ndi anthu omutsatira Yazid.
Cholinga cha ma Wahabiy ndi ichi; kufuna kuwononga manda a mtumiki wa Mulungu ngati momwe adawonongera manda ambiri a asilamu, ngatinso momwe adamuphera Imam Husein (a.s).
Cholinga cha ma Wahabiy ndikokufuna kuti dzina la mtumiki wa chisilamu lisapezeke. Ndipo zomwe zikuikira umboni pa zimenezi ndiwo mawu awo omwe amati  “Muhammad adafa ndipo adathera pomwepo” ndikumapitiriza kunena kuti “ndipo ndodo yanga ilibwino kuposa manda akewa”.
Cholinga cha ma Wahabiy ndi choti wina aliyense yemwe angatchule dzina la mtumiki ndikumati ee! Mtumiki wa Mulungu (Ya Rasula llah) ayenera kuphedwa, magazi ake ndi ololedwa (Halal) kukhetsedwa, chuma chake ndi Halal kulandidwa ndipo banja lankenso ndi Halal kulandidwa ngati momwe adapangira Yazid pa Karbala ndi akazi a asilamu ophedwa ndi Imam Husein (a.s).
Chabwino tangoyerekezani kuti munthu akufuna kudana ndi chisilamu kodi angapange zoyipa kuposera zimenezi?
Inu tawonani m’mene akuwonongera ndi kupha anthu mu dera la Gaza mu dziko la Palestin. Tawonani munthu aliyense yemwe ali ndi umunthu ngakhale kuti alibe chipembedzo koma ali ndi chilengedwe choyera, akuyesetsa pofuna kuthetsa zimenezi koma Wahabiy ndipomwe akuthandiza dziko la Isiraeli.
Mudziko la Siriya mukupangidwa zoyipa zambiri. Anthu osalakwa ndi osowa chitetezo akuwapha, ndipomwe Wahabiy akutulutsa lamulo loti akazi adziko la Tunisia apite kumeneko ndikuti akapange Jihad ya chiwelewere ndi kuwapanga Halal akazi a dziko la Siriya kuti azipanga banja ndi zigawenga komanso anthu owukira dziko la Siriya. Komanso akumalengeza kuti apange zoipa mudzikoli ndim’mene angathere.
Mdani wa zipembedzo zonse adapanga Filimu yomunyoza mtumiki wa chisilamu (s.a.a.w) mpakana kufikira kuti akhirisitu omwe ali opanda tsankho adali odandaula ndi kukhudzidwa chifukwa cha nkhani imeneyi, koma Wahabiy akupereka lamulo loti kupanga Jihad ndi kumenyana ndi anthu amenewa ndi zoletsedwa (Haram) komanso kupanga ziwonetsero polimbana ndi opanga Filimuwo ndi Haram.
Anthu ofuna ufulu atopa ndi kupondereza mwachoncho akuima ndi kumalimbana ndi kupondereza. Pomwe ma Wahabiy akutulutsa lamulo loti kulimbana ndi boma ngakhale liri lopondereza ndi Haram chifukwa choti mtsogoleri ngakhale atakhala opondereza ndi zokakamizidwa kumutsatira (Wajibu al-Tabaiyyah). Ndipo munthu oyima polimbana ndi mtsogoleri opondereza ayenera kuimbidwa mulandu chifukwa choti munthu ameneyu sakusangalatsidwa ndi chisangalalo ndinso chifuniro cha Mulungu. Chifukwa chakuti mtsogoleriyo ali chifukwa cha mphamvu ya Mulungu ndipo ngati inu Muli munthu wachipembedzo muyenera kusangalala ndi ulamuliro wa munthu ameneyu.
Njira yomwe ankagwiritsa ntchito ma Bani Umayya powanamiza ndi kuwapusitsa anthu osazindikira ndiyomwe akumagwiritsa ntchito ma Wahabiy ndipo akufuna kufika pa zolinga zomwe ankafuna Yazid.
Zidalembedwa m’maHadith zokhudzana ndi ma Bani Umayya kuti, Abu Sufiyan adamenya nkhondo ndikulimbana ndi mtumiki, Muawiya adalimbana ndi Ali (a.s), Yazid adalimbana ndi kumenyana ndi Husein ndipo mapeto ake munthu ochokera ku mtundu wa Sufiyan ndi yemwe adzalimbana ndi Imam Mahdi (a.j) akadzabwera. Pomwe tikamawona tikupeza kuti munthu yemwe ali Sufiyani zowona zake ndi munthu yemwe akuyesetsa pofuna kukwaniritsa zofuna ndi zolinga za aYuda omwe ali ma Wahabiy.
Munthu yemwe angamalongosole ubwino wa Yazid ndiye kuti akutsimikizira ndi kuvomereza zikhulupiliro ndi zichitochito za Yazid ndipo ngati angakwanitse adzapanga zonse zomwe Yazid adali kupanga ngati momwe akupangira padakali pano.
Kumaphulitsa ndi kumapha anthu ndi kuwononga zomangidwa zoyeretsedwa za chisilamu ndinso kuthandiza anthu omwe akumapha asilamu.
Inu tawonani kuti Yazid yemwe adali omwa mowa (chidakwa) adakhala mtsogoleri wa asilamu, mukayang’anaso mbali ina mupeza kuti munthu yemwe akuzitcha kuti othandiza ku Madinah ndi ku Makkah (Khadimul al- Haramayni) akumamenyetsa kapu yake yomwera mowa ndi kapu ya mowa ya munthu yemwe adawononga mayiko awiri a chisilamu (Iraq ndi Afghanistan).
Inu tangoyang’anani kuwononga komwe kulipo pankhani ya chiwelewere ndi chuma kwa anthu akubanja la Saudi.
Chabwino, kodi amenewa ndi ndani? Khadimul al-Haramayn ndi anthu omwe akuzitcha kuti ndi amlowa mmalo a mtumiki wa Mulungu.
Ndi munthu uti mfulu yemwe sanganyasidwe ndi chisilamu ngati chimenechi?
Chuma cha mafuta a dziko la Hijaz chomwe chikuyenera kugwiritsidwa ntchito kulimbitsa ndi kupititsa patsogolo chisilamu, chuma chambiri chomwe asilamu chaka ndi chaka amakhala akupititsa mudziko loyeretsedwali, chikugwiritsidwa ntchito yochiwonetsa chisilamu kuti ndi chipembedzo cha nkhanza ndi kulimbikitsiranso magulu aumbanda ndi zipolowe omwe akhala akupha asilamu.
Gulu la Wahabiy ndi lokhazikitsidwa ndi kupangidwa ndi mayiko akuluakulu okalamba omwe akulamula mopondereza ndi cholinga choti zofuna ndi zolinga za mayiko amenewa zizichitika kudutsira mugulu lomwe liri mkati mwa chisilamu pomwe liri kunja kwa chisilamu.
Kodi anthu akuluakulu ndi maSheikh adali ndi mphamvu zochuluka bwanji pofuna kuwalongosolera anthu za gulu limeneli ndipo tikadatha kupanga ntchito zambiri bwanji polimbana ndi gulu limeneli koma nthawi yambiri yatithera.
Wahabiy mapeto ake akufuna kuti amufikitse munthu pa mulingo oti azipha asilamu mmene angathere ndikutinso adzipha anthu osalakwa moipitsitsa kwambiri.
Dziwani izi kuti gulu la Wahabiy ladzibisa povala chovala cha chisilamu koma ngati tingafune kuyesa ndicholinga choti tidziwe zenizeni za gululi, tatiyeni tiwone kuti munthu ngati ameneyu yemwe akulankhula za chisilamu (Wahabiy) kodi ndi msilamudi kapena ayi poyang’ana zizindikiro ziri mmusizi:
Choyamba ndi choti Wahabiy amakhulupolira kuti ndi zoletsedwa (Haram) kukawona ndi kupanga ziyara manda amtumiki komanso kupempha kudutsira mwa mtumiki (Tawassul) ndipo zonsezi ndi chifukwa choti iwo samakhulupilira zoti atumiki ali ndi ulemelero waukulu pamaso pa Mulungu, kumachita kuti asilamu onse amakhulupilira kuti atumiki ali ndi ulemelero wapamwamba pamaso pa Mulungu komanso ndi anthu osankhika ndipo asilamu onse amakhulupilira kuti udindo wa atumiki siumapunguka komanso kutsika olo ndi pang’ono pomwe ngakhale atachoka padziko lino (kumwalira).
Ndipo ichi ndicho chikhulupiliro cha Qur’an pomwe ikulankhula kunena kuti: سلامعلی  وح فی العالمین “Mtendere ukhale kwa Nuh (Nowa) mpaka kalekale”, سلام علی ابراهیم “Mtendere ukhale kwa Ibrahim”, سلام علی موسی و هارون “Mtendere ukhale kwa Musa ndi Haroon”, سلام علیه یوم ولد و یوم یموت و یوم یبعث حیا “Mtendere ukhale kwa iye (yesu) kuyambira tsiku lomwe anabadwa ndi tsiku lomwe adzamwalira kufikiranso tsiku lomwe adzadzutsidwa kuchokera m’manda kukhalanso wamoyo”. Ndipo msilamu aliyense mmapempharo ena aliwonse amati

 السلام علیک ایها النبی و رحمه الله و برکاته “mtendere ndi chisomo cha Mulungu chikhale kwa iwe, ee! Mneneri wa Mulungu”.
Chabwino, kodi ma Salam onsewa sindiye Ziyara imeneyo?
Kapenanso mu bukhu lolemekezeka la Qur’an, Mulungu adakakamiza kumupatsa Salam mtumiki wa Mulungu. Qur’an ikunena kuti;
یا ایها الذین آمنوا صلوا علیه و سلموا تسلیما “ee! Inu amene mwakhulupilira, mupemphereni zabwino iye (mtumiki) ndipo mupatseni mtendere (Salam) kumupatsa mtendere kwenikweni”. Mulungu akukakamiza kumupatsa mtendere mtumiki koma ma Wahabiy akuti مات فات “adafa ndipo adathera pomwepo” mwachoncho maSalam amenewa ndi kumuphatikiza Mulungu ndi zinthu zina (Shirk) ndipo mapeto ake akumati “Munthu amene mukumupangira Ziyarayu ndi wakufa mwachoncho alibe phindu lina lililonse ndipo munthu opanga ziyarayo ayenera kuphedwa.
Mawu a maWahabiy alibenso mkati mwake kupatula kupusitsa ndi kuwasokoneza anthu basi ndi kulimbana ndi mzimu wa zipembedzo zonse komwe kuli kukhulupilira za umoyo wa mmanda pambuyo poti munthu wamwalira komanso komwe kuli kukhulupilira za mayiko obisika ndipo Mulungu akulankhula mu Qur’an kunena kuti الذین یومنون بالغیب “Anthu omuwopa Mulungu ndi omwe amakhulupilira za zobisika”.
Kutanthauza kuti iwo (Wahabiy) amakhulupilira za zinthu zokhazo zomwe zikupezeka pano padziko lapansi ndi zomwe zikuwoneka ndi maso ndipo amatsutsa ndi kumakanira zakupezeka kwa zinthu zosaoneka ndi maso zomwe ziri zobisika mpakananso kukanira za kupezeka kwa mzimu, zomwe tidzalongosolabe zokhudzana ndi nkhani ngati zimenezi.
Gulu la Wahabiy limakhulupilira kuti Mulungu alingati zolengedwa ndipo angathe kuwonedwa ndi maso yemwe wakhala pa mpando wake. Kutanthauza kuti Mulungu wa malire yemwe amafunikira zinthu zina. Kumachita kuti chikhulupiliro chimenechi chimatsutsana ndi nzeru, maHadith komanso maAya aQur’an, pomwe ikunena kuti
 فاینما تولوا فثم وجه الله “ndipo kwina kulikonse komwe mungatembenukire kuli Mulungu ndi ulemelero wake”.
Mzimu wa zipembedzo zonse umakhulupilira kuti dziko ndi munthu ziri ndi magawo awiri, gawo la thupi ndi gawo la uzimu ndipo Ifa ndiko kuchoka kwa mzimu wa munthu mthupi mwake kupita kudziko lina. Panthawi imene munthu akungowona kuti zinthu zikupezeka pokhala ndi thupi ndipo sakukhulupilira kuti palinso zinthu zina zomwe zikupezeka posakhala ndi thupi, mapeto ake amakaniranso zakupezeka kwa Mulungu posakhala ndi thupi ndipo iye amati Mulungunso ali ndi thupi, mwachoncho munthu yemwe wamwalira amamutenganso kuti wathera pomwepo.
Kenako wakufayo alibenso udindo ndi ulemelero wina uliwonse ngakhale atakhala mtumiki wa Mulungu, kuwonjezeranso apo iye amakanira za tsiku lomaliza (Qiyamah) chifukwa choti wakufayo amawola ndi kusanduka dothi ndipo dothi limasintha ndikukhala chipatso kapenanso kukhala udzu ndipo udzu ndikudyedwa ndi nyama ndipo mapeto ake nyama ndikudyedwa ndi munthu.
Munthu wakufa uja amakalowa mu chipatso kenako chipatso ndi kukalowa mwa munthu wina ndikumayendelera mpakana kuti pamapeto pake ndi zonsamvekanso kuti kukhale Qiyamah, mwachoncho ndiye kuti kulibenso dziko lina kupatula dziko lapansili.
Tsopano tifika pa mawu omwe aja aYazid pomwe amanena kuti “palibe Wahay (uthenga wa Mulungu) omwe udabwera ngakhale mngelo Jibril, ndinso zoti kuli Mulungu ndi zabodza ndipo chipembedzo ndi chida chofuna kuwabera ndi kuwalamulira anthu osazindikira basi.
Mwachoncho ngati dziko lapansi lokha ndi lomwe lilipo ndipo kulibe Qiyamah, nanga ndiye ngakhale kupanga ziyara ngakhale pa manda amtumiki zingatanthauze chiyani?
Palibenso Qiyamah, mwachoncho mutha kupanga tchimo lina lilironse lomwe mukufuna komanso mutha kumwera limodzi ndi Bushi komanso mutha kupeleka chilolezo choti asilamu aphedwe ndipo munthu amene sangavomereze zimenezi mupheni chifukwa choti akutisokoneza zochita zathu. Mwachoncho maSheikh ndi onse omwe sakuvomereza za mawo amenewa ndi anthu okanira (Kufar).
Ndipo palibe kusiyana kuti asilamu adziko la Miyanmar azimwalira ndi njala kumachita kuti chuma chomwe chimayenera kuti chigwire ntchito pofalitsa chisilamu padakali pani zikugwiritsidwa ntchito powathandiza anthu oipitsitsa komanso ana a ufumu wa Saudi pomapangira zisangalalo zopanda pake ndi ma Biliyoni ndikumapanga chinachirichonse choyipa chomwe angathe.
Kuyendera ndi kukawona manda a atumiki ndi Haram, kumachita kuti Qur’an ikunena kuti یا ایها الذین آمنوا اتقوا الله وابتغوا الیه الوسیلة “ee! Inu amene mwakhulupilira, khalani omuwopa Mulungu ndipo funafunani njira ndi cholinga chodziwandikitsa kwa Mulungu”, ndiye pangakhale njira yapamwambanso iti kuposa atumiki oyera aMulungu.
Samhudi yemwe ali Sheikh ndi ophunzira wamkulu wa Ahalsunnah akutilongosoera nkhani ina kunena kuti “kupempha chithandizo kudutsira mwa mtumiki wa chisilamu ali moyo kapenanso atamwalira ndi Haram”.
Chodabwitsa ndi chosangalatsa ndi choti Mulungu mu Aya yotsatana ndi Aya ya mmwambayi akunena kuti:
 ان الذین کفروا لو ان لهم ما فی الارض جمیعا و مثله معه لیفتدوا به من عذاب یوم القیامة ما تقبل منهم و لهم عذاب الیم
“Ndithudi anthu amene akanira ndikusafufuza ndi kusatsatira njirayo, ngakhale atapeleka nthaka yonse kuti apulumuke kuchokera kumoto, sadzalandilidwa ndipo ali ndi mavuto opweteka kwambiri”.
Tawonani kuti kodi anthu amanewa awononga bwanji? Qur’an ikunena kuti pelekani Salam ndipo pezani njira, ndipomwe ma Wahabiy akuti Ziyara ndi kufunafuna njira (Tawassul) ndi Haram komanso Shirk ndipo mapeto ake oteroyo ayenera kuphedwa.
Ndi chifukwa chiyani amanena zimenezi?
Chifukwa choti مات فات mtumiki adafa ndipo adathera pomwepo!
Inu tangowonano kuti chaputala chomwe chili chachikulu mu Qur’an yomwe ili Sura Baqarah. Kodi Surayi ikuti chiyani?
Amodzi mwa mawu akulu omwe akupezeka mu Sura ya Baqarah ndi oti, Mulungu atafuna atha kuika mphamvu mu chinthu chakufa ndipo chakufacho chingakhale ndi mphamvu zochuluka mpakana chingathe kudzutsa chinthu china chomwe chidafa kale. Tayang’anani nkhani ya ng’ombe ya ana aIzrael kuti ng’ombe yomwe idali yakufa, idadzutsa munthu yemwe adali wakufa.
Chabwino, padakali pano ine ndimufunse munthu wina aliyense kuti kodi pali munthu yemwe anganene kuti mphamvu zomwe zidali ndi ng’ombe yakufa zingapose mphamvu za mtumiki wachisilamu?
Ngati Mulungu akulamula kuti funafunani njira yofikira kwa iye, mmalo ena akutinso, pelekani mtendere kupeleka mtendere kwenikweni, ndikutinso mtendere ukhale kwa iye kuchokera tsiku lomwe anabadwa kufikira tsiku lomwe adzamwalira, kodi kumupatsa Salamu mtumiki yemwe wamwalira ndi Shirk? Kapena ndicho chikhulupiliro cha Qur’an komanso umodzi wa Umulungu?
Qur’an muAya ina ikuti
  لاتقولوا لمن یقتل فی سبیل الله اموات بل احیاء و لکن لاتشعرون
“Musawanene anthu omwe amwalira kuti ndi akufa koma kuti ndi amoyo chabe kuti inu simukudziwa ayi”.
Tsopano ngati ife talamulidwa kuti timupatse Salamu mtumiki wa Mulungu ndipo iye siwakufa koma kuti ndi wamoyo motsatana ndi Aya yoti  و اذا حییتم بتحیة فحیوا باحسن منها او ردوها “Panthawi yomwe mwapatsidwa mtendere ndi ulemelero yankhani mofananira kapena yankhani mwabwino kuposa momwe akupatsirani” ndipo ife talamululidwa kupeza njira ndi cholinga chokafika kwa Mulungu, tsopano kumupangira Salamu mtumiki ndi kumutenga iye kukhala njira yokafikira kwa Mulungu ndi Shirk?
Moti mtumiki wa chisilamu alibe mphamvu kuposa ng’ombe ya ana aIzrael?
MaWahabiy akumati “mtumiki adamwalira, samamva ndipo palibe chomwe angapange mwachoncho wina ndikumapitiriza pomati ndodo yomwe ili m’manja mwanga ndi yamphamvu ndipo manda amtumiki alibe mphamvu chifukwa choti mtumiki mmanda mwake adasanduka dothi ndipo adathero pomwepo mwachoncho dothi lilibe upamwamba olo ndi pang’ono pomwe ndi ... kumachita kuti Qur’an pokhudzana ndi chovala cha mtumiki Yusuf (a.s) ikuti chovalachi chidali ndi mphamvu kufikira kuti chidachiza maso amtumiki Yaqub (a.s) ndikumuwonetsa koma ma Wahabiy akumati manda amtumiki wathu Muhammad (s.a.a.w) alibe mphamvu komanso ali pansi kuposa chovala cha mtumiki Yusuf (a.s).
Kuphempha chikhululuko kwa Mulungu kudutsira mwa atumiki aMulungu ndi kulankhulana ndi mzimu wawo ndi Shirk.
Mu bukhu lotchedwa Khulaswatu al-Kalam pa tsamba la 230 zikunenedwa kuchokera kwa Muhammad AbdulWahab (yemwe ali mtsogoleri wa ma Wahabiy) kuti iye nthawi zonse pokhudzana ndi mtumiki wachisilamu ankati: “Mtumiki samamva” choncho mmodzi mwa omutsatira ake ankatinso
 عصای هذه خیر من محمد لانه ینتفع بها فی قتل الحیة و محمد قد مات و لم یبق فیه نفع و انما هو طارش و مضی
“Ndodo yangayi imagwira ntchito kuposa Muhammad chifukwa choti ndodo yanga ingathe kugwiritsidwa ntchito pophera njoka koma Muhammad adafa ndipo adatha ndipo palibe chomwe amamva kuti mpakana athe kupereka phindu kwa ena”.
Ife mukukambirana kwathuku, tidzalongosola zizindikiro zomwe zidzatithandiza kuti tisiyanitse pakati pa msilamu ndi Wahabiy.
Mukuyang’ana kwachidule ngati tikufuna kudziwa kuti kodi ndi ndani yemwe ali Wahabiy nanga ndi ndani yemwe ali msilamu, titha kulongosola izi kuti:
Asilamu onse amavomereza za kuwapangira Ziyarah atumiki ndi anthu ochita zabwino munjira ya Mulungu kupatulako ma Wahabiy.
Asilamu onse amalemekeza manda a atumiki ndi anthu opanga zabwino kupatulako ma Wahabiy.
Asilamu onse amavomereza zopemphera (Swala) pafupi ndi manda kupatulako maWahabiy.
Asilamu onse amavomereza za kupempha chikhululuko kwa Mulungu kudutsira mwa mizimu ya atumiki kupatulako ma Wahabiy.
Asilamu onse amavomereza zakuti titha kupeza madalitso kuchokera muzizindikiro za atumiki kupatulako maWahabiy.
Asilamu onse amavomereza zakuti titha kulumbilira kudutsira mwa atumiki kupatulako maWahabiy.
Asilamu onse samamutenga Muhammad Abdul Wahab ndi Ibn Taymiyyah kukhala atsogoleri awo muchipembedzo kupatulako maWahabiy.
Asilamu onse amamutenge yense yemwe ali msilamu kuti ndi msilamu ndipo magazi ndi chuma cha wina ndi mzake ndi Haram kuwonongedwa kupatulako maWahabiy omwe amati munthu yemwe Sali Wahabiy ndiye kuti simsilamu ndipo kupha asilamu omwe Sali ngati iwo muchikhulupiliro ndi zokakamizidwa (Wajib).
Asilamu onse amavomereza za kuzindikira pa zobisika komwe atumiki alinako kupatulako maWahabiy.

Zikomo kwambiri khalani opambana nthawi zonse.

 

Add new comment